Malembo Oyera
2 Nefi 4


Mutu 4

Lehi alangiza ndi kudalitsa mbumba yake—Amwalira ndipo ayikidwa m’manda—Nefi alemekeza mu ubwino wa Mulungu—Nefi aika chidaliro chake mwa Ambuye kosatha. Mdzaka dza pafupifupi 588–570 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, ine, Nefi, ndikulankhula za maulosi amene atate anga alankhula, za Yosefe, amene adatengedwa ku Igupto.

2 Pakuti taonani, iye adalosera moonadi za mbewu yake yonse. Ndipo maulosi amene iye adalemba, si ochuluka kwambiri. Ndipo adalosera za ife, ndi mibadwo yathu yamtsogolo; ndipo zalembedwa pa mapale a mkuwa.

3 Kotero, atate anga atatsiriza kulankhula za maulosi a Yosefe, adaitana ana a Lamani, ana ake aamuna, ndi ana aakazi, ndipo adati kwa iwo: Taonani, ana anga aamuna, ndi ana anga aakazi, omwe ali ana aamuna ndi aakazi a mwana wanga woyamba, ndikadakonda kuti inu mumvere mawu anga.

4 Pakuti Ambuye Mulungu adanena kuti: Ndipo pamene inu mudzasunga malamulo anga inu mudzachita bwino m’dzikolo, ndipo pamene inu simudzasunga malamulo anga, mudzachotsedwa pamaso panga.

5 Koma taonani, ana anga aamuna ndi aakazi, sindingathe kutsikira kumanda anga, koma ndikusiyirani mdalitso; pakuti taonani, ndikudziwa kuti ngati muleredwa m’njira imene muyenera kuyendamo simudzapatukamo.

6 Kotero, ngati muli otembeleredwa, taonani, ndikusiyirani mdalitso wanga, kuti thembelerolo lichotsedwe pa inu ndi kuyankhidwa pamitu ya makolo anu.

7 Kotero, chifukwa cha dalitso langa Ambuye Mulungu sadzalora kuti muonongeke; kotero, iye adzakhala wachifundo kwa inu ndi kwa mbewu zanu kunthawi zonse.

8 Ndipo zidachitika kuti atamaliza kulankhula kwa ana aamuna ndi aakazi a Lamani, adachititsa ana aamuna ndi aakazi a Lemueli kuti abweretsedwe pamaso pawo.

9 Ndipo adanena nawo, nati, Taonani, ana anga aamuna ndi aakazi, amene muli ana aamuna ndi aakazi a mwana wanga wamwamuna wachiŵiri; taonani ndikusiyirani inu mdalitso womwewo umene ndidasiya kwa ana aamuna ndi aakazi a Lamani; kotero, simudzawonongedwa konse; koma pamapeto pake mbewu yanu idzadalitsidwa.

10 Ndipo zidachitika kuti atate anga atatsiriza kulankhula kwa iwo, taonani, adalankhula kwa ana a Ismaeli, inde, ndipo ngakhale a m’nyumba yake yonse.

11 Ndipo atatha kuyankhula nawo, adayankhula kwa Samu, nati: Odala iwe, ndi mbewu yako; pakuti udzalandira dziko monga m’bale wako Nefi. Ndipo mbewu yako idzawerengedwa pamodzi ndi mbewu yake; ndipo udzafanana ndi m’bale wako, ndi mbewu yako monga mbewu yake; ndipo udzakhala wodala masiku ako onse.

12 Ndipo zidachitika kuti atate anga, Lehi, atayankhula ndi banja lawo lonse, monga mwa kumvelera kwa mtima wawo ndi Mzimu wa Ambuye umene unali mwa iwo, adakalamba. Ndipo zidachitika kuti adamwalira, naikidwa.

13 Ndipo zidachitika kuti pasadapite masiku ambiri atamwalira, Lamani ndi Lemueli ndi ana a Ismaeli adakwiya ndi ine chifukwa cha malangizo a Ambuye.

14 Pakuti ine, Nefi, ndidakakamizidwa kuyankhula kwa iwo, monga mwa mawu ake; pakuti ndidalankhula zinthu zambiri kwa iwo, ndiponso atate anga, asadamwalire; zambiri za izo zalembedwa pa mapale anga ena; pakuti gawo la mbiri yakale lidalembedwa pa mapale anga ena.

15 Ndipo apa ndimalemba zinthu za moyo wanga, ndi malemba ambiri amene amazokotedwa pa mapale a mkuwa. Pakuti moyo wanga ukondwera ndi malemba; ndipo mtima wanga umalingalira iwo, ndi kuwalemba kuti ana anga aphunzire komanso kuti awapindulire.

16 Taonani, moyo wanga umakondwera ndi zinthu za Ambuye; ndipo mtima wanga umasinkhasinkha kosalekeza pa zimene ndidaziona ndi kuzimva.

17 Komabe, pakusamala kanthu za ubwino waukulu wa Ambuye, pakundionetsa ntchito zake zazikulu ndi zodabwitsa, mtima wanga umafuula: Iwe munthu womvetsa chisoni amene ndili! Inde, mtima wanga uli ndi chisoni chifukwa cha thupi langa; moyo wanga uli ndi chisoni chifukwa cha mphulupulu zanga.

18 Ndazingidwa, chifukwa cha mayesero ndi machimo omwe amandifikila mosavuta.

19 Ndipo pamene ndifuna kukondwera, mtima wanga umabuula chifukwa cha machimo anga; koma ndidziwa amene ndimamukhulupilira.

20 Mulungu wanga wakhala mthandizi wanga; Wanditsogolera m’masautso anga m’chipululu; ndipo wanditeteza pa madzi akuya kwakukulu.

21 Iye wandidzaza ine ndi chikondi chake mpaka kudzadza thupi langa.

22 Wasokoneza adani anga, kuwapangitsa kuti agwedezeke pamaso panga.

23 Taonani, wamva kulira kwanga usana, ndipo wandipatsa chidziwitso kudzera m’masomphenya a usiku.

24 Ndipo usana ndidalimbika mukupemphera kwamphamvu pamaso pake; inde, mawu anga ndidakweza pamwamba; ndipo angelo adatsika nanditumikira.

25 Ndipo pa mapiko a Mzimu wake thupi langa lanyamulidwa pa mapiri aatali kwambiri. Ndipo maso anga awona zinthu zazikulu, inde, ngakhale zazikulu kwambiri kwa munthu; tero ndidauzidwa kuti ndisalembe izo.

26 O ndiye, ngati ndawona zinthu zazikulu, ngati Ambuye m’kudzichepetsa kwake kwa ana a anthu wayendera anthu m’chifundo chochuluka chotere, mtima wanga uliliranji, ndipo moyo wanga ukhaliranji m’chigwa cha chisoni, ndipo thupi langa kufooka, ndipo mphamvu zanga kulefuka chifukwa cha masautso anga?

27 Ndipo ndidzagonjeranji kuuchimo chifukwa cha thupi langa? Inde, chifukwa chiyani ndiyenera kupereka mpata kwamayesero, kuti woipayo akhale ndi malo mu mtima mwanga kuti awononge mtendere wanga ndi kusautsa moyo wanga? Ndikwiyiranji chifukwa cha mdani wanga?

28 Galamuka, moyo wanga! Osagweranso mu tchimo. Kondwera, Iwe mtima wanga, osaperekanso malo kwa mdani wa moyo wanga.

29 Usakwiyenso chifukwa cha adani anga. Osafooka mphamvu zanga chifukwa cha masautso anga.

30 Kondwera, iwe mtima wanga, ndi kufuula kwa Ambuye, ndi kunena, O Ambuye, ndidzakutamandani kwa nthawi zosatha; inde, moyo wanga udzakondwera mwa Inu, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.

31 O Ambuye, kodi mudzaombola moyo wanga? Kodi mudzandilanditsa m’manja mwa adani anga? Kodi mundipanga ine kuti ndizigwedezeka pakaoneka tchimo?

32 Zipata za gahena zitsekedwe mosalekeza pamaso panga, chifukwa mtima wanga wasweka ndipo mzimu wanga olapa! O Ambuye, simudzatseka zipata za chilungamo chanu pamaso panga, kuti ndiyende m’njira ya kuchigwa, kuti ndikhale wokhwima mu njira yolunjika!

33 O Ambuye, kodi mundizinga mu mwinjiro wa chilungamo chanu! O Ambuye, kodi mundikonzera njira yopulumukira kwa adani anga! Kodi mudzawongola njira yanga pamaso panga! Kodi simundiyikira chondipunthwitsa pa njira yanga- koma kuti mundikonzere njira yanga pamaso panga; ndipo musatchinge njira yanga, koma njira za mdani wanga.

34 O Ambuye, Ndakhulupilira mwa Inu, ndipo ndidzakhulupilira mwa Inu kosatha. Sindidzaika chikhulupiliro changa m’dzanja la thupi; pakuti ndidziwa kuti wotembeleredwa ali iye amene aika chikhulupiliro chake m’dzanja la thupi. Inde, wotembeleredwa ali iye amene aika chikhulupiliro chake mwa munthu amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amthandize.

35 Inde, ndidziwa kuti Mulungu adzapatsa modzala manja kwa iye wapempha. Inde, Mulungu wanga adzandipatsa, ngati sindipempha cholakwika; kotero, ndidzakweza mawu anga kwa inu; Inde, ndidzafuulira kwa inu, Mulungu wanga, thanthwe la chilungamo changa. Taonani, mawu anga adzakwera mpaka kalekale kwa inu, thanthwe langa ndi Mulungu wanga wosatha. Ameni.

Print