Malembo Oyera
2 Nefi 24


Mutu 24

Israeli adzasonkhanitsidwa ndipo adzasangalala ndi mpumulo wa dzaka chikwi—Lusifara adaponyedwa kuchokera kumwamba chifukwa cha kuukira—Israeli adzapambana kwa Babulo (dziko lapansi)—Fananitsani Yesaya 14. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Pakuti Ambuye adzam’chitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israeli, ndi kuwakhazikitsa m’dziko lakwawo; ndipo achilendo adzadziphatikiza wokha ndi iwo, ndipo adzamamatira ku nyumba ya Yakobo.

2 Ndipo anthu adzawatenga, ndi kuwafikitsa ku malo akwawo; inde, kuchokera kutali mpaka kumalekezero a dziko lapansi; ndipo adzabwelera ku maiko awo alonjezano. Ndipo a nyumba ya Israeli adzakhala nawo, ndipo dziko la Ambuye lidzakhala la atumiki ndi adzakazi; ndipo adzatengedwa ndende ndi amene adali andende; ndipo adzawalamulira owavuta.

3 Ndipo zidzachitika kuti mutsiku limenelo Ambuye adzakupumitsa iwe kuchisoni, ndi ku mantha ako, ndi ku ukapolo wovuta umene udapangitsidwa kutumikira.

4 Ndipo zidzachitika patsiku limenelo kuti, udzayimbira kwa mfumu ya ku Babulo mwambi uwu, nati: wopondeleza wathadi bwanji, mzinda wagolidi wathadi!

5 Ambuye wathyola ndodo ya oipa, ndodo zachifumu za wolamulira.

6 Iye amene adakantha anthu ndi ukali ndi chikwapu chosalekeza, iye amene adalamulira maiko mokwiya, angosautsidwa opanda omulanditsa.

7 Dziko lonse lapansi lapuma, ndipo liri duu, iwo ayamba kuimba nyimbo.

8 Inde, mitengo ya mlombwa ikondwera ndi iwe, ndiponso mikungudza ya ku Lebanoni, ndi kunena: Chigonekedwere iwe pansi, palibe wogwetsa wakwera kudzalimbana nafe.

9 Kunsi kwa gahena kwagwedezeka chifukwa cha iwe kuchingamira kubwera kwako; kukuukitsira iwe akufa, ngakhale onse akulu akulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m’mipando yawo mafumu onse a maiko.

10 Wonse adzayankhura nati kwa iwe: kodi iwe wakhalanso ofooka ngati ife? Kodi iwe wafanana ndi ife?

11 Kudzikuza kwako kwatsitsidwa ku manda; ndi phokoso la mingoli yako siikumveka; ndipo mphutsi zayalidwa pansi pa iwe, ndipo mphutsi zakukuta iwe.

12 Wagwa bwanji kuchokera kumwamba, Iwe Lusifara, mwana wa m’banda kucha! Wagwetsedwa pansi iwe, amene udalefula maiko!

13 Pakuti iwe udati mumtima mwako; ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m’mbali za kumpoto;

14 Ndidzakwera pamwamba pa mitambo; ndidzafanana ndi Wam’mwambamwamba.

15 Koma udzatsitsidwa kunsi kwa gahena, kumalekezero a dzenje.

16 Iwo amene akuona iwe adzayang’anitsitsa iwe, ndipo adzalingalira za iwe, ndipo adzati: kodi uyu ndiye munthu amene adagwedeza dziko lapansi ndi kugwedeza maufumu?

17 Amene adapangitsa dziko lapansi ngati chipululu, ndi kuwononga mizinda yake, ndipo sadatsegule nyumba za akaidi ake?

18 Mafumu onse a maiko, inde, onsewo, ogona mu ulemelero, aliyense kunyumba kwake.

19 Koma iwe wataidwa kunja kwa manda ako ngati nthambi yonyansa, ndipo ngati wotsala a iwo ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira ku miyala ya kudzenje; monga ngati mtembo wopondedwa ndi mapazi.

20 Iwe sudzaphatikizidwa nawo m’manda, chifukwa iwe waononga dziko lako ndi kupha anthu ako; mbewu ya anthu ochita zoipa siidzadziwika konse.

21 Konzekerani kuphedwa kwa ana ake, chifukwa cha mphulupulu za atate awo, kuti iwo asadzadzuke, kapena kutenga dziko, kapena kudzadza dziko lapansi ndi mizinda.

22 Pakuti ine ndidzawaukira, atero Ambuye wa Makamu, ndikuwononga Babulo dzina ndi otsala, ndi mwana wamamuna, ndi chidzukulu chachimuna, atero Ambuye.

23 Ndidzapangaponso pokhala nungu, ndi madziwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsache la chiwonongeko, atero Ambuye wa Makamu.

24 Ambuye wa Makamu walumbira, nati: Ndithu monga ndaganizira, momwemo zidzachitika; ndipo momwe ndapangira uphungu, momwemo chidzakhazikika—

25 Kuti ine ndidzabweretsa Asiriya mu dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzamupondereza ndi phazi; pomwepo gori lake lidzachoka pa iwo, ndipo katundu wake adzachoka pa mapewa pawo.

26 Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse lapansi; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa kwa maiko onse,

27 Pakuti Ambuye wa Makamu wapanga uphungu, ndipo ndani adzauthetse? Ndipo dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibwenze?

28 M’chaka chimene mfumu Ahazi adamwalira kudali katundu ameneyu.

29 Usakondwere iwe, Filisitiya yense, chifukwa ndodo ya yemwe adakumenyera iwe yathyoka; pakuti m’muzu wa njoka mudzatulukira mphiri, ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.

30 Ndipo oyamba kubadwa wa aumphawi adzadya, ndi osauka adzagona pansi mosaopa; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndipo wotsala ako adzaphedwa.

31 Lira, Iwe chipata; fuula; iwe mzinda, iweyo, Filisiti yense wasungunuka; pakuti padzabwera utsi ochokera ku mpoto, ndipo palibe adzakhala yekha mnyengo zake zoikika.

32 Kodi adzayankhanji amithenga a maiko? Kuti Ambuye wakhazikitsa Ziyoni, ndipo wosauka a anthu ake adzakhulupiliramo.

Print