Malembo Oyera
2 Nefi 26


Mutu 26

Khristu adzatumikira kwa Anefi—Nefi aoneratu za chiwonongeko cha anthu ake—Iwo adzayankhula kuchokera ku fumbi—Amitundu adzamanga mipingo yonama ndi magulu azachinsinsi—Ambuye aletsa kupanga zaunsembe zolakwika. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo Khristu akadzauka kwa akufa adzadzionetsera yekha kwa inu, ana anga, ndi abale anga; ndipo mawu amene adzayankhule kwa inu adzakhala lamulo lomwe inu mudzachite.

2 Pakuti taonani, Ndikunena kwa inu kuti ndaona mibadwo yambiri ikutha, ndipo padzakhala nkhondo zikuluzikulu ndi mikangano pakati pa anthu anga.

3 Ndipo akadzabwera Mesiya padzakhala zizindikiro zoperekedwa kwa anthu anga pa kubadwa kwake, ndiponso pa kufa kwake ndi chiukitso; ndipo lalikulu ndi loopsya lidzakhala tsikulo kwa anthu oipa, pakuti adzaonongedwa; ndipo adzaonongedwa chifukwa iwo adatulutsa aneneri, ndi oyera mtima, ndikuwagenda miyala, ndi kuwapha; kotero kulira kwa mwazi kwa oyera mtima kudzakwera kumwamba kwa Mulungu kuchokera pansi pa nthaka motsutsana nawo.

4 Kotero, onse amene ali wodzikweza, ndi amene akuchita zoipa, tsiku limene lirinkudza lidzawatentha iwo, atero Ambuye wa Makamu, pakuti adzakhala ngati chiputu.

5 Ndipo iwo amene amapha aneneri, ndi oyera mtima, kuya kwa dziko lapansi kudzawameza, atero Ambuye wa Makamu; ndipo mapiri adzawaphimba iwo, ndi akamvuluvulu adzawatengera kutali iwo, ndipo nyumba zidzawagwera ndikuwaphwanya iwo mzidutswa ndi kuwapera ngati ufa.

6 Ndipo adzayenderedwa ndi mabingu, ndi mphenzi, ndi zivomelezi, ndi chiwonongeko cha mitundu yonse, pakuti moto wa mkwiyo wa Ambuye udzayaka pa iwo, ndipo adzakhala ngati chiputu, ndipo tsiku lirinkudza lidzawanyeketsa, atero Ambuye wa Makamu.

7 O, ululu ndi kuwawida kwa moyo wanga chifukwa cha kutaika kwa anthu anga wophedwa! Pakuti ine, Nefi, ndachiona ichi, ndipo chikadandipsereza ine pamaso pa Ambuye; koma ndikuyenera kufuulira kwa Mulungu wanga: Njira zanu ndi zachilungamo.

8 Koma taonani, olungama amene amvera mawu a aneneri, ndipo samawawononga, koma amayang’anira kwa Khristu ndi kukhazikika mwa zizindikiro zomwe zapatsidwa, posaona za mazunzo onse—taonani, ndi amenewa amene sadzawonongedwa.

9 Koma Mwana wa Chilungamo adzaonekera kwa iwo; ndipo adzawachiritsa, ndipo adzakhala ndi mtendere ndi iye, kufikira mibadwo itatu idzapita, ndipo ambiri mwa m’badwo wachinayi adzapita m’chilungamo.

10 Ndipo zinthu izi zikadzatha, chiwonongeko chofulumira chidzafikira kwa anthu anga; pakuti posaona za kupwetekeka kwa m’moyo mwanga, ndaziona izi; kotero, ndikudziwa kuti zidzachitika; ndipo iwo akudzigulitsa wokha pachabe; pakuti mphotho ya kunyada ndi kupusa kwawo iwo adzakolola chiwonongeko; chifukwa iwo adzipereka kwa mdyerekezi ndi kusankha ntchito za mu m’dima m’malo mwa kuwala, kotero akuyenera kupita ku gahena.

11 Pakuti Mzimu wa Ambuye siudzalimbana ndi munthu nthawi zonse. Ndipo pamene Mzimu wasiya kulimbana ndi munthu, pamabwera chiwonongeko chofulumira, ndipo izi zimawawitsa moyo wanga.

12 Ndipo monga ndidayankhula zokhudzana ndi kutsimikizira kwa Ayuda, kuti Yesu ndiye Khristu yemweyo, zikuyenera kuti Amitundu atsimikiziridwenso kuti Yesu ndiye Khristu, Mulungu wa Muyaya;

13 Ndipo iye adzionetsera kwa anthu onse amene akhulupilira mwa iye, mwa mphamvu ya Mzimu Woyera; inde, kwa mafuko onse, maiko, chinenero ndi anthu, kuchita zamphamvu zozwizwitsa, zizindikiro ndi zodabwitsa, pakati pa ana a anthu malingana ndi chikhulupiliro chawo.

14 Koma taonani, ndikunenera kwa inu zokhudzana ndi masiku omaliza; zokhudzana ndi masiku amene Ambuye Mulungu adzabweretsa zinthu izi kwa ana a anthu.

15 Patatha izi, mbewu yanga ndi mbewu ya abale anga idzacheperachepera m’kusakhulupilira, ndipo idzakanthidwa ndi Amitundu; inde, akadzatha Ambuye Mulungu atawazinga mowazungulira, ndipo adzawazinga ndi phiri ndi kukweza linga motsutsana nawo, ndipo iwo akadzagwetsedwa pansi mu fumbi, ngakhale kuti palibe, koma mawu a wolungama adzalembedwa, ndipo mapemphero a wokhulupirika adzamveka, ndipo iwo amene acheperachepera m’chikhulupiro sadzaiwalidwa.

16 Pakuti iwo amene adzawonongedwe adzayankhula kuchoka m’nthaka, ndipo mawu awo adzakhala otsika kuchokera ku fumbi, ndipo mawu awo adzakhala monga a munthu wa mizimu yobwebweta; pakuti Ambuye Mulungu adzampatsa iye mphamvu, kuti adzanong’one zokhudza iwo, ngakhale ngati kuti zikuchokera pansi pa nthaka; ndipo mawu awo adzanong’ona kuchokera m’fumbi.

17 Pakuti akutero Ambuye Mulungu: Adzalemba zinthu zimene zidzachitidwa pakati pawo, ndipo zidzalembedwa ndi kutsindikizidwa mu buku, ndipo iwo amene acheperachepera m’chikhulupiliro sadzakhala nazo, pakuti amafunafuna kuti awononge zinthu za Mulungu.

18 Kotero, ngati iwo amene awonongedwa awonongedwa mofulumira: ndipo khamu la oopsa awo adzakhala ngati mankhusu amene atha—inde, motere akutero Ambuye Mulungu: zidzakhala mu kamphindi, mwadzidzidzi—

19 Ndipo kudzachitika kuti iwo amene acheperachepera m’chikhulupiliro adzakanthidwa ndi dzanja la Amitundu.

20 Ndipo Amitundu akwezedwa m’kunyada kwa maso awo, ndipo apunthwa chifukwa cha kukula kwa mwala wawo owapunthwitsa, kuti adzimangira mipingo; komabe, iwo amachepsa mphamvu ya zozwizwa za Mulungu, ndi kudzilalikira wokha nzeru zawo ndi kuphunzira kwawo, kuti apeze cholowa ndi pakupondeleza anthu wosauka.

21 Ndipo pali mipingo yambiri yomangidwa imene imapangitsa nsanje, ndi kaduka, ndi njiru.

22 Ndipo palinso magulu a chinsinsi, ngakhale ngati nthawi yakale, molingana ndi magulu a mdyerekezi, pakuti iye ndiye adayambitsa zinthu zonsezi; inde oyambitsa kupha, ndi ntchito za mu mdima; inde, ndipo amatsogolera iwo powamanga pakhosi ndi chingwe cholimba, kufikira atawamanga iwo ndi zingwe zolimba kwa muyaya.

23 Pakuti taonani, abale anga okondedwa, ndikunena kwa inu kuti Ambuye Mulungu samagwira ntchito mu mdima.

24 Iye sapanga chirichonse kupatula kuti zithandize dziko lapansi: pakuti iye amakonda dziko lapansi, ngakhale kuti adapereka moyo wake omwe kuti akope anthu onse kwa iye. Kotero, iye salamulira aliyense kuti asalandire nawo chipulumutso chake.

25 Taonani, kodi iye amafuulira kwa wina aliyense, kuti: Chokani kwa ine? Taonani, ndikunena kwa inu, Ayi; koma iye amati: Bwerani kwa ine inu malekezero onse a dziko lapansi, gulani mkaka ndi uchi, opanda ndalama ndi opanda mtengo.

26 Taonani, kodi iye adalamula wina aliyense kuti achoke m’masunagoge, kapena kuchoka m’nyumba zopembedzera? Taonani, ndikunena kwa inu, Ayi.

27 Kodi iye adalamula wina aliyense kuti asatenge nawo gawo la chipulumutso chake? Taonani ndikunena kwa inu, Ayi; koma iye wapereka izi mwa ulele kwa anthu onse; ndipo iye walamula anthu ake kuti akuyenera kukopa onse ku kulapa.

28 Taonani, kodi Ambuye adalamula wina aliyense kuti asatenge nawo ubwino wake? Taonani ndikunena kwa inu, Ayi; koma anthu wonse ali ndi mwayi wina monga mzake, ndipo palibe woletsedwa.

29 Iye akulamula kuti pasakhale zaunsembe zolakwika, pakuti, taonani, zaunsembe zolakwika ndi zakuti anthu amalalikira ndi kudziika wokha ngati kuwala kwa dziko lapansi, kuti apeze cholowa ndi matamando adziko lapansi; koma iwo safunafuna ubwino wa Ziyoni.

30 Taonani, Ambuye adaletsa chinthu ichi; kotero, Ambuye Mulungu adapereka lamulo kuti anthu wonse akhale ndi chikondi, chikondi chimene ndi chikondi cha Yesu Khristu. Ndipo pokhapokha atakhala ndi chikondi ali chabe. Kotero, ngati ali ndi chikondi, sadzalola ogwira ntchito mu Ziyoni kuti awonongeke.

31 Koma ogwira ntchito mu Ziyoni adzagwira tchito chifukwa cha Ziyoni, pakuti ngati agwira chifukwa cha ndalama adzawonongeka.

32 Ndiponso, Ambuye Mulungu adalamula kuti anthu asaphe; kuti asaname; kuti asabe; kuti asatchule dzina la Ambuye Mulungu wawo pachabe; kuti asachite kaduka; kuti asakhale ndi njiru; kuti asakangane wina ndi mzake; kuti asachite zadama; ndipo kuti asachite zirizonse mwa zinthu izi; pakuti yense wochita izi adzawonongeka.

33 Pakuti zonse zoipazi sizichokera kwa Ambuye; pakuti iye amachita zimene ziri zabwino kwa ana a anthu; ndipo sachita kanthu kalikonse pokhapokha zikhale zomveka kwa ana a anthu; ndipo akuwaitana iwo onse kuti abwere kwa iye ndi kutenga nawo ubwino wake; ndipo saletsa aliyense kubwera kwa iye, wakuda ndi oyera, omangidwa ndi omasuka, wamwamuna ndi wamkazi; ndipo amakumbukira achikunja; ndipo onse ndi ofanana kwa Mulungu, onse Ayuda ndi Amitundu.

Print