Malembo Oyera
2 Nefi 31


Mutu 31

Nefi anena chifukwa chimene Khristu adabatizidwira—Anthu akuyenera kutsatira Khristu, kubatizidwa, kulandira Mzimu Woyera, ndi kupilira kufikira chimaliziro kuti apulumutsidwe—Kulapa ndi ubatizo ndi chipata cha njira yolunjika ndi yopapatiza—Moyo wamuyaya umabwera kwa iwo amene amasunga malamulo atabatizidwa. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano ine, Nefi, ndikumaliza uneneri wanga kwa inu, abale anga okondedwa. Ndipo sindingathe kulemba koma zinthu zochepa zokha, zimene ndikudziwa kuti zikuyenera kuchitika ndithu; ngakhalenso sindingathe kulemba koma mawu ochepa chabe a m’bale wanga Yakobo.

2 Kotero, zinthu zimene ndalemba zandikwanira ine, kupatula kukhala mawu ochepa wokha amene ndikuyenera kuyankhula zokhudzana ndi chiphunzitso cha Khristu; kotero, ndidzayankhula kwa inu momveka, molingana ndi kumveka kwa uneneri wanga.

3 Pakuti moyo wanga ukondwera ndi zomveka; pakuti moteremu Ambuye Mulungu amagwira ntchito pakati pa ana a anthu. Pakuti Ambuye Mulungu wapereka kuwala kwa chidziwitso; pakuti iye amayankhula kwa anthu molingana ndi chiyankhulo chawo ndi chidziwitso chawo.

4 Kotero, ndikufuna kuti mukumbukire kuti ine ndayankhula kwa inu zokhudzana ndi mneneri uja amene Ambuye adandionetsa ine, amene akuyenera kudzabatiza Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, amene adzachotsa machimo adziko lapansi.

5 Ndipo tsopano, ngati Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, iye pokhala oyera, adayenera kubatizidwa ndi madzi, kuti akwaniritse chilungamo chonse, Inu nanga, tikufunikira kochuluka bwanji ife, pokhala opanda chiyero, kuti tibatizidwe, inde, ngakhale ndi madzi!

6 Ndipo tsopano, ndidzakufunsani inu, abale anga okondedwa, kodi ndi pati pamene Mwana wa Nkhosa wa Mulungu adakwaniritsa chilungamo chonse pobatizidwa ndi madzi?

7 Kodi simudziwa kuti iye adali oyera? Koma ngakhale iye adali oyera, iye adaonetsa kwa ana a anthu kuti, molingana ndi thupi adadzichepetsa yekha pamaso pa Atate, ndi kuchitira umboni kwa Atate kuti iye adzakhala omvera kwa iye mu kusunga malamulo ake.

8 Kotero, atatha kubatizidwa ndi madzi Mzimu Woyera udatsikira pa iye mu mawonekedwe a nkhunda.

9 Ndiponso, zidaonetsa kwa ana a anthu kulunjika kwa njira, ndi kupapatiza kwa chipata, chimene iwo ayenera kulowamo, iye atapereka chitsanzo pamaso pawo.

10 Ndipo iye adati kwa ana a anthu; Nditsateni ine. Kotero, abale anga okondedwa, kodi tingatsatire Yesu pokhapokha titakhala ofunitsitsa kusunga malamulo a Atate?

11 Ndipo Atate adati: Lapani, lapani, ndipo batizidwani mu dzina la Mwana wanga okondedwa.

12 Ndiponso, mawu a Mwana adabwera kwa ine, nati: Iye amene abatizidwa mu dzina langa, kwa iye Atate adzapereka Mzimu Woyera, monga kwa ine; kotero, nditsateni ine, ndi kuchita zinthu zimene inu mwandiona ndikuchita.

13 Kotero, abale anga okondedwa, ndikudziwa kuti ngati inu mudzatsata Mwana, ndi cholinga chonse cha mtima, osati kuchita chinyengo ndi kunyengezera pamaso pa Mulungu, koma ndi cholinga chenicheni, kulapa machimo anu, kuchitira umboni kwa Atate kuti inu mukufuna kutenga pa inu dzina la Khristu, mwa ubatizo—inde, pakutsatira Ambuye wanu ndi Mpulumutsi pansi m’madzi, molingana ndi mawu ake, taonani, pamenepo inu mudzalandira Mzimu Woyera, inde, kenako udzabwera ubatizo wa moto ndi wa Mzimu Woyera; ndipo pamenepo mudzatha kuyankhula ndi lilime la angelo, ndi kufuula matamando kwa Oyera wa Israeli.

14 Koma, taonani, abale anga okondedwa, kotero padabwera mawu a Mwana kwa ine, nati: Mutatha kulapa machimo anu, ndi kuchitira umboni kwa Atate kuti mukufuna kusunga malamulo anga, mwa ubatizo wa madzi, ndi kulandira ubatizo wa moto ndi wa Mzimu Oyera, ndi kuyankhula ndi lilime latsopano, inde, ngakhale lilime la angelo, ndipo pambuyo pa ichi n’kundikana ine, kudakakhala bwino kwa inu kuti simudandidziwe ine.

15 Ndipo ndidamva mawu ochokera kwa Atate, nati: Inde, mawu a Okondedwa wanga ndi oona ndi okhulupirika. Iye amene wapilira mpaka kumapeto, yemweyo adzapulumutsidwa.

16 Ndipo tsopano, abale anga wokondedwa, ndikudziwa mwa ichi, kuti pokhapokha munthu adzapilire kufikira chimaliziro, potsatira chitsanzo cha Mwana wa Mulungu wamoyo, sangapulumutsidwe.

17 Kotero, chitani zinthu zimene ine ndakuuzani kuti ndaziona kuti Ambuye wanu ndi Muwomboli wanu akuyenera kuchita; Pakuti chifukwa cha ichi iye wandionetsera ine, kuti inu mukadziwe chipata chimene inu mukuyenera kulowa nacho. Pakuti chipata chimene inu mukuyenera kulowa nacho chiri kulapa ndi ubatizo wa madzi, ndipo kenako kukubwera kuchotsa kwa machimo anu mwa moto ndi mwa Mzimu Woyera.

18 Ndipo pamenepo inu muli mu njira yolunjika ndi yopapatiza imene imatsogolera ku moyo wamuyaya; inde, mwalowamo pa chipata; inu mwachita molingana ndi malamulo a Atate ndi Mwana; ndipo mwalandira Mzimu Woyera, amene amachitira umboni za Atate ndi za Mwana, kufikira kukwaniritsa kwa malonjezano amene iye adapanga, kuti ngati mulowamo kudzera njira imeneyi mudzalandira.

19 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, mutalowa mu njira imeneyi yolunjika ndi yopapatiza, ndikufuna ndifunse ngati zonse zachitika? Taonani, ndinena kwa inu, Ayi: pakuti inu simudafike potero koma ndi mawu a Khristu ndi chikhulupiliro chosagwedezeka mwa iye, kudalira kwathunthu kwa zabwino za iye amene ali wamphamvu za kupulumutsa.

20 Kotero, mukuyenera kukankhira chitsogolo ndi kukhazikika mwa Khristu, kukhala ndi kuwala kokwanira kwa chiyembekezo ndi chikondi cha Mulungu ndi cha anthu wonse. Kotero, ngati mudzakankhirabe chitsogolo, kudyelera pa mawu a Khristu, ndi kupilira kufikira chimaliziro, taonani, akutero Atate: Mudzakhala nawo moyo wamuyaya!

21 Ndipo tsopano, taonani, abale anga okondedwa, iyi ndiyo njira, ndipo palibe njira ina kapena dzina loperekedwa pansi pa thambo limene munthu angathe kupulumutsidwila nalo mu ufumu wa Mulungu. Ndipo tsopano, taonani, ichi ndicho chiphunzitso cha Khristu, ndi chiphunzitso chokhacho ndi choona cha Atate, ndi Mwana, ndi Mzimu Woyera, amene ndi Mulungu m’modzi, opanda malire. Ameni.

Print