Malembo Oyera
2 Nefi 30


Mutu 30

Amitundu otembenuka adzawerengedwa ndi anthu apangano—Alamani ndi Ayuda ambiri adzakhulupilira mawu ndi kukhala okondweretsa—Israeli adzabwenzeretsedwa ndipo oipa adzawonongedwa. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano taonani, abale anga okondedwa, ndidzayankhula kwa inu; pakuti ine, Nefi, sindidzalora kuti mudziganiza kuti ndinu wolungama kuposa m’mene amitundu adzakhalire. Pakuti taonani, kupatula ngati inu musunga malamulo a Mulungu inu nonse mudzawonongedwa momwemo; ndipo chifukwa cha mawu amene ayankhulidwa simukuyenera kuganiza kuti Amitundu adzawonongeka kotheratu.

2 Pakuti taonani, ndikunena ndi inu kuti ngati ambiri mwa Amitundu womwe adzalapa adzakhala anthu apangano a Ambuye; ndipo monga ambiri mwa Ayuda amene sadzalapa iwo adzatayidwa; pakuti Ambuye sachita pangano ndi wina aliyense kupatula ndi iwo amene alapa ndi kukhulupilira mwa Mwana wake, amene ali Oyera wa Israeli.

3 Ndipo tsopano, ndinenera zina zambiri zokhudzana ndi Ayuda ndi Amitundu. Pakuti likadzabwera buku lomwe ine ndanena kuti lidzabwera, ndi kulembedwa kwa Amitundu, ndi kumatidwanso kwa Ambuye, padzakhala ambiri amene adzakhulupilira mawu amene alembedwa, ndipo adzawatenga kupita nawo kwa otsalira a mbewu zathu.

4 Ndipo pamenepo otsalira a mbewu yathu adzadziwa zokhudzana ndi ife, m’mene tidachokera ku Yerusalemu, ndipo kuti iwo ndi mbadwa za Ayuda.

5 Ndipo uthenga wabwino wa Yesu Khristu udzalalikidwa pakati pawo; kotero adzabwenzeretsedwa ku chidziwitso cha makolo awo, ndiponso kwa chidziwitso cha Yesu Khristu, chimene chidali pakati pa makolo awo.

6 Ndipo pamenepo iwo adzakondwera; pakuti adzadziwa kuti liri dalitso kwa iwo lochokera m’dzanja la Mulungu; ndipo kuti mamba awo a mdima adzayamba kugwa kuchokera m’maso mwawo; ndipo mibadwo yambiri siidzatha pakati pawo pokhapokha atakhala anthu oyera ndi okondweretsa.

7 Ndipo zidzachitika kuti Ayuda amene adamwazikana nawonso adzayamba kukhulupilira mwa Khristu; ndipo adzayamba kusonkhana pa nkhope ya dziko; ndipo monga onse ambiri amene adzakhulupilira mwa Khristu adzakhalanso anthu okondweretsa.

8 Ndipo zidzachitika kuti Ambuye Mulungu adzayamba ntchito yake pakati pa maiko wonse, mafuko, zinenero ndi anthu, kuti abweretse chibwenzeretso cha anthu ake padziko lapansi.

9 Ndipo ndi chilungamo Ambuye Mulungu adzaweruza osauka, ndi kudzudzula ndi chilungamo kwa ofatsa adziko lapansi. Ndipo adzakantha dziko lapansi ndi ndodo ya m’kamwa mwake; ndi mpweya wa milomo yake iye adzazinga oipa.

10 Pakuti nthawi ilinkudza msanga imene Ambuye Mulungu adzapangitsa kugawanika kwakukulu pakati pa anthu, ndipo oipa adzawawononga; ndipo iye adzasunga anthu ake, inde, ngakhale zitakhala kuti iye akuyenera awononge oipa ndi moto.

11 Ndipo chilungamo chidzakhala lamba wa mchiuno mwake, ndi kukhulupirika mpango wa zimpso zake.

12 Ndipo pamenepo M’mbulu idzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pamodzi ndi mwana wa mbuzi; ndi mwana wa ng’ombe, ndi mwana wa mkango, ndi choweta chonenepa, pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzadzitsogolera.

13 Ndipo ng’ombe ndi chimbalangondo zidzadya; ndipo ana awo adzagona pansi pamodzi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe.

14 Ndipo mwana woyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’pfunkha la mphiri.

15 Sizidzavulaza kapena kuwononga m’phiri langa lonse lopatulika, pakuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Ambuye; monga madzi adzadza nyanja.

16 Kotero, zinthu za dziko lapansi zidzadziwika; inde, zinthu zonse zidzadziwika kwa ana a anthu.

17 Palibe chimene chili cha chinsinsi koma kuti chidzavumbulutsidwa; palibe ntchito iliyonse yamumdima koma kuti idzaonetseredwa poyera, ndipo palibe chilichonse chimene chamatidwa koma kuti chidzamasulidwa.

18 Kotero, zinthu zonse zimene zavumbulutsidwa kwa ana a anthu zidzaulurika pa tsikulo; ndipo Satana sadzakhalanso ndi mphamvu pa mitima ya ana a anthu, kwa nthawi yaitali. Ndipo tsopano, abale anga, ndikumaliza zoyankhula zanga.