Malembo Oyera
2 Nefi 18


Mutu 18

Khristu adzakhala ngati mwala wopunthwitsa ndi thanthwe la chokhumudwitsa—Funani Ambuye, osati afiti owombedza—Tembenukirani ku chilamulo ndi ku umboni kuti mutsogoleledwe—Fananitsani Yesaya 8. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Komanso, mawu a Ambuye adati kwa ine: Tenga mpukutu wolembera waukulu, ndipo ulembepo ndi kalembedwe ka munthu zokhudzana ndi Kusakaza-Kwamsanga-Kufunkha-Kofulumira.

2 Ndipo ine ndidadzitengera mboni Zokhulupirika kuti zilembe, Uriya wa msembe, ndi Zakariya mwana wamamuna wa Yeberekiya.

3 Ndipo ndidapita kwa Mneneri wamkazi; ndipo adatenga pakati nabeleka mwana wamamuna. Ndipo Ambuye adati kwa ine: Umutchule dzina lake, Kusakaza-Kwamsanga-Kufunkha-Kofulumira.

4 Pakuti taona, mwanayo sadzadziwa kufuula, bambo anga, ndi mayi anga, chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa pamaso pa mfumu ya Asiriya.

5 Ambuye adayankhulanso kwa ine kachiwiri, nati:

6 Popeza anthu awa akana madzi a Silowa amene amayenda pang’onopang’ono, ndi kukondwera mwa Rezini ndi mwana wamamuna wa Remaliya;

7 Kotero tsopano, taonani, Ambuye abweretsa pa iwo madzi amumtsinje, amphamvu komanso ambiri, ngakhale mfumu ya Asiriya ndi ulemelero wake wonse; ndipo iye adzakwera pamwamba pa ngalande zake zonse, ndipo adzapitilira magombe ake onse.

8 Ndipo iye adzadzera pakati pa Yuda; adzasefukira ndi kupitilira, adzafikira ngakhale mkhosi; ndi kutambasula kwa mapiko ake kudzadzadza m’lifupi la dziko lako, Iwe Imanueli.

9 Gwirizanani nokha, anthu inu, koma mudzathyokathyoka m’dzidutswa; ndipo tcherani khutu inu nonse a maiko akutali; dzimangilireni m’chiuno nokha, koma mudzathyokathyoka m’dzidutswa, dzimangilireni m’chiuno nokha, koma mudzathyokathyoka m’dzidutswa.

10 Panganani uphungu, koma udzapita pachabe; yankhulani mawu, koma sadzaima; pakuti Mulungu alinafe.

11 Pakuti Ambuye adayankhula ndi ine ndi dzanja lamphamvu, ndipo wandilangiza kuti ndisayende m’njira ya anthu awa, nati:

12 Usayankhule, Chiwembu, kwa onse amene anthu awa adzachinena, Chiwembu; usaope monga mwa kuopa kwawo, kapena kuchita mantha.

13 Yeretsani Ambuye wa Makamu yekha, mumuope iye, akuchititseni mantha.

14 Ndipo iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wopunthwitsa ndi thanthwe la chokhumudwitsa cha nyumba zonse ziwiri za Israeli, khwekhwe ndi msampha wa okhala mu Yerusalemu.

15 Ndipo ambiri mwa iwo adzapunthwapo ndi kugwa, ndi kuthyoka, ndi kukodwa, ndi kutengedwa.

16 Mangani umboni, sindikiza chizindikilo pachilamulo mwa ophunzira anga.

17 Ndipo ndidzadikila Ambuye, amene wabisira nyumba ya Yokobo nkhope yake, ndipo ndidzamufunafuna iye.

18 Taonani, ine ndi ana amene Ambuye wandipatsa ndife zizindikiro ndi zodabwitsa mu Israeli kuchokera kwa Ambuye wa makamu, amene amakhala m’phiri la Ziyoni.

19 Ndipo pamene iwo adzanena kwa iwe: Funani kwa iwo amene ali ndi maula ndi afiti obwebweta ndi ong’ung’udza—kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wawo kuti amoyo adzamvere kwa akufa?

20 Ku chilamulo ndi ku umboni; ndipo ngati iwo sadzayankhula molingana ndi mawu awa, ndi chifukwa chakuti mulibe kuwala mwa iwo.

21 Ndipo iwo adzadutsa m’menemo ali ovutika ndi anjala; ndipo zidzachitika kuti pokhala ndi njala, adzakwiya wokha, ndi kutembelera mfumu yawo ndi Mulungu wao, ndikuyang’ana kumwamba.

22 Ndipo iwo adzayang’ana ku dziko lapansi, ndipo taonani mavuto ndi mdima, mdima wa zowawa, ndipo adzathamangitsidwa ku mdima.

Print