Malembo Oyera
2 Nefi 6


Mutu 6

Yakobo alongosola za mbiri ya aYuda: Ukapolo wa ku Babulo ndi kubwelera kwawo; utumiki ndi kupachikidwa pa mtanda kwa Oyera wa Israeli; thandizo lolandiridwa kuchokera kwa amitundu; kubwenzeretsedwa kwa aYuda pamene adzakhulupilira mwa Mesiya m’masiku-otsiriza. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Mau a Yakobo, m’bale wake wa Nefi, omwe adayankhula kwa anthu a Nefi:

2 Taonani, abale anga okondedwa, ine, Yakobo, nditaitanidwa ndi Mulungu, ndikudzodzedwa mu njira ya dongosolo lake loyera, ndi kupatulidwa ndi m’bale wanga Nefi, amene inuyo mumayang’ana ngati mfumu kapena mtetezi, ndipo amene mumadalira pa chitetezo, taonani mukudziwa inu kuti ndayankhula kwa inu zinthu zambiri koposa.

3 Komabe, ndikuyankhula kwa inu kachiwiri; pakuti ndikhumba ubwino wa moyo wanu. Inde, nkhawa yanga ndiyaikulu kwa inu, ndipo inu nomwe mukudziwa kuti zakhala choncho kuyambira kale. Pakuti ndakulimbikitsani inu ndi khama lonse; ndipo ndakuphunzitsani mau a atate anga; ndipo ndayankhula kwa inu za zinthu zonse zomwe zidalembedwa, kuyambira pa chilengedwe cha dziko lapansi.

4 Ndipo tsopano, taonani, ndiyankhula kwa inu za zinthu zimene ziri, ndi zimene zili nkudza; kotero, ndidzakuwerengerani mau a Yesaya. Ndipo ndi mau amene m’bale wanga wafuna kuti ndiyankhule nanu. Ndipo ndikuyankhula kwa inu chifukwa cha inu, pofuna kuti inu muphunzire ndi kulemekeza dzina la Mulungu wanu.

5 Ndipo tsopano mau amene ndidzawerenge ndi amene Yesaya adayankhula za nyumba yonse ya Israeli; kotero, akhonza kufananizidwa ndi inu, pakuti inu ndi a nyumba ya Israeli. Ndipo pali zinthu zambiri zomwe zidayankhulidwa ndi Yesaya zimene zingafanizidwe ndi inu, chifukwa inu ndi a nyumba ya Israeli.

6 Ndipo tsopano, awa ndiwo mauwo: Akutero Ambuye Mulungu: Taonani, ndidzakweza dzanja langa kwa amitundu, ndi kukweza mbendera yanga kwa anthu; ndipo adzabwera nawo ana ako aamuna m’manja mwao, ndi ana awo aakazi adzanyamulidwa pa mapewa awo.

7 Ndipo mafumu adzakulerani ndi mfumukazi zawo zidzakuyamwitsani; iwo adzakugwadirani ndi nkhope zawo zitaloza pansi, nadzanyambita fumbi la kumapazi anu; ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndi Ambuye; pakuti amene adikira Ine sadzachita manyazi.

8 Ndipo tsopano ine, Yakobo, ndiyankhura pang’ono zokhudzana ndi mau awa. Pakuti taonani, Ambuye andionetsera ine kuti iwo amene adali ku Yerusalemu, kumene ife tidachokera, adaphedwa ndi kutengedwa ukapolo.

9 Komabe, Ambuye andionetsera kuti iwo akuyenera kubweleranso. Ndipo andionetsanso kuti Ambuye Mulungu, Oyera wa Israeli, ayenera kudzionetsera yekha kwa iwo mu thupi; ndipo akadzadzionetsera yekha adzamukwapula ndi kumpachika iye, monga mwa mau amngelo amene adayankhula ndi ine.

10 Ndipo atatha kuumitsa mitima yawo ndi kukhwimitsa makosi awo kudana ndi Oyera wa Israeli, taonani, chiweruzo cha Oyera wa Israeli chidzabwera pa iwo. Ndipo tsiku lilikudza limene adzakanthidwa ndi kusautsidwa.

11 Kotero, akadzathamangitsidwa uku ndi uko, pakuti akutero mngelo, ambiri adzasautsidwa m’thupi, ndipo sadzazunzika mpaka chionongeko chifukwa cha mapemphero a okhulupilika; adzabalalitsidwa, nakanthidwa ndi kudedwa; komabe, Ambuye adzawachitira chifundo, kuti pamene iwo adzafika ku chidziwitso cha Muwomboli wawo, iwo adzasonkhanitsidwanso pamodzi ku maiko acholowa chawo.

12 Ndipo odala ndi amitundu, amene mneneri walemba za iwo; pakuti taonani, iwo ngati adzalape ndi kusamenyana ndi Ziyoni, ndi kusakhala nawo limodzi ndi mpingo uja waukulu ndi onyansa, adzapulumutsidwa; pakuti Ambuye adzakwaniritsa mapangano ake amene adapanga kwa ana ake; ndipo chifukwa cha ichi ndi chimene mneneri walembera zimenezi.

13 Kotero, iwo amene amenyana ndi Ziyoni ndi anthu apangano a Ambuye adzanyambita fumbi la kumapazi awo; ndipo anthu a Ambuye sadzachita manyazi. Pakuti anthu a Ambuye ndi iwo amene amamuyembekezera; pakuti iwo akuyembekezerabe kubwera kwa Mesiya.

14 Ndipo taonani, monga mwa mau a mneneri, Mesiya adzadzikhazikanso kachiwiri kudzawabwenza iwo; kotero, adzadziwonetsera yekha kwa iwo mwa mphamvu ndi ulemelero waukulu, ku chiwonongeko cha adani awo, pamene tsikulo lidzafika limene iwo adzakhulupilira mwa Iye; ndipo palibe okhulupilira Iye amene adzamuononge.

15 Ndipo iwo amene sakhulupilira mwa Iye adzaonongedwa ndi moto komanso namondwe, ndi zibvomelezi, ndi kukhetsa mwazi ndi mliri, ndi njala. Ndipo iwo adzadziwa kuti Ambuye ndi Mulungu, Oyera wa Israeli.

16 Pakuti a m’nsinga adzalanditsidwa kwa wamphamvu, kapena am’ndende kupulumutsidwa?

17 Koma akutero Ambuye: Angakhale am’ndende a wamphamvu adzatengedwa, ndipo ogwidwa ndi zoopsya adzawomboledwa; pakuti Mulungu Wamphamvu adzapulumutsa anthu ake apangano. Pakuti atero Ambuye: Ndidzalimbana nawo amene alimbana nawe—

18 Ndipo ndidzawadyetsa iwo amene akuzunza iwe ndi mnofu wao omwe; ndipo adzaledzera ndi mwazi wao omwe ngati ndi vinyo wotsekemera; ndipo anthu onse adzadziwa kuti ine Ambuye ndi Mpulumutsi wako ndi Muwomboli wako, Wamphamvu wa Yakobo.

Print