Malembo Oyera
2 Nefi 3


Mutu 3

Yosefe ku Igupto adaona Anefi m’masomphenya—Iye adalosera za Joseph Smith, mlosi wa m’masiku otsiriza; za Mose, amene adzapulumutse Israeli; ndi za kubwera kwa Buku la Mormoni. Mdzaka dza pafupifupi 588–570 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano ndikuyankhula kwa iwe, Yosefe, mwana wanga omaliza. Iwe udabadwira m’chipululu cha masautso anga; inde, m’masiku achisoni changa chachikulu amayi ako adakubala iwe.

2 Ndipo Ambuye akupatulirenso dziko ili kwa iwe, limene liri dziko lamtengo wapatali, kukhala cholowa chako ndi cholowa cha mbewu yako ndi abale ako, kuchitetezo chako kwa muyaya, ngati udzakhale kuti udzasunga malamulo a Oyera wa Israeli.

3 Ndipo tsopano, Yosefe, mwana wanga omaliza, amene ndakubala m’chipululu cha masautso anga, Ambuye akudalitse iwe kwa muyaya, pakuti mbewu yako siidzawonongedwa konse.

4 Pakuti taona, iwe ndiwe chipatso cha mchiuno mwanga, ndipo ine ndi chidzukulu cha Yosefe amene adatengedwa mu ukapolo ku Igupto. Ndipo aakulu adali ma pangano amene Ambuye adapanga kwa Yosefe.

5 Kotero, Yosefe adaonadi tsiku lathu. Ndipo adalandira lonjezo la Ambuye, kuti kuchokera mu chipatso cha mchiuno mwake Ambuye Mulungu adzadzutsa nthambi yolungama kwa nyumba ya Israeli; osati Mesiya, koma nthambi imene idzathyoledwe, komabe, idzakumbukiridwa m’mapangano a Ambuye kuti Mesiya adzaonetsedwa kwa iwo mmasiku otsiliza, mu mzimu wa mphamvu, m’kuwabweretsa iwo kuchoka mu mdima kufika m’kuwala—inde, kuchoka ku mdima obisika ndi kuchoka ku ukapolo kufika ku ufulu.

6 Pakuti Yosefe adachitiradi umboni, nati: Mlosi adzadzutsidwa ndi Ambuye Mulungu wanga, amene adzakhale mlosi osankhika kwa chipatso cha mchiuno mwanga.

7 Inde, Yosefe adanenadi: Akutero Ambuye kwa ine: Mlosi wosankhika ndidzadzutsa kuchokera ku chipatso cha mchiuno mwako; ndipo adzalemekezedwa pakati pa chipatso cha mchiuno mwako. Ndipo kwa iye ndidzapereka lamulo loti adzagwire ntchito kwa chipatso cha mchiuno mwako, abale ako, limene lidzakhala lofunikira kwambiri kwa iwo, ngakhale kuwabweretsa ku chidziwitso cha mapangano amene ine ndidapanga ndi makolo anu.

8 Ndipo ndidzapereka kwa iye lamulo loti iye asadzagwire ntchito ina iliyonse kupatula ntchito yomwe ndidzamulamule iye. Ndipo ndidzampanga iye kukhala wamkulu m’maso mwanga; pakuti adzagwira ntchito yanga.

9 Ndipo iye adzakhala wankulu ngati Mose, amene ndanena kuti ndidzam’dzutsa kwa inu, kuwombola anthu anga, Iwe nyumba ya Israeli.

10 Ndipo Mose ndidzam’dzutsa, kuti awombole anthu ako ku dziko la Igupto.

11 Koma mlosi ndidzadzutsa kuchokera ku chipatso cha m’chiuno mwako; ndipo kwa iye ndidzapatsa mphamvu yobweretsa mawu anga kwa mbewu ya mchiuno mwako—ndipo osati kwa kubweretsa mawu kokha, atero Ambuye, koma kwa kuwatsimikizira iwo za mawu anga, amene adzakhale atapita kale pakati pawo.

12 Kotero, Chipatso cha m’chiuno mwako chidzalemba; ndipo chipatso cha mchiuno mwa Yuda chidzalemba; ndipo chomwe chidzalembedwe ndi chipatso cha mchiuno mwako, ndiponso chomwe chidzalembedwe ndi chipatso cha mchiuno mwa Yuda, chidzakula pamodzi, mpaka kusokoneza ziphunzitso zabodza ndi kuchotsa mikangano, ndi kukhazikitsa mtendere pakati pa chipatso cha mchiuno mwako, ndikuwabweretsa iwo kuchidziwitso cha makolo awo m’masiku otsiriza, ndiponso ku chidziwitso cha mapangano anga, atero Ambuye.

13 Ndipo adzapatsidwa mphamvu kuchokera mu kufooka, mu tsiku limene ntchito yanga idzayamba pakati pa anthu anga onse, m’kubwenzeretsa iwe, O nyumba ya Israeli, atero Ambuye.

14 Ndipo umo ndi momwe adanenelera Yosefe, nati: Taonani, mlosiyo Ambuye adzamudalitsa; ndipo iwo amene akufuna kumuwononga iye adzagonjetsedwa; pakuti lonjezo ili, limene ndalandira kwa Ambuye, la chipatso cha mchiuno mwanga, lidzakwaniritsidwa. Taonani, ndili ndi chitsimikizo kuti lonjezo ili lidzakwaniritsidwa.

15 Ndipo dzina lake lidzatchedwa ngati ine; ndipo lidzakhala ngati dzina la atate ake. Ndipo adzakhala ofanana ndi ine; pakuti chinthu chimene Ambuye adzabweretse ndi dzanja lake, mu mphamvu ya Ambuye chidzabweretsa anthu anga ku chipulumutso.

16 Inde, motero adanenera Yosefe: Ndili ndi chitsikimizo cha chinthu ichi, ngakhale ndili ndi chitsikimizo cha lonjezo la Mose; pakuti Ambuye andiuza ine, Ndidzateteza mbewu yako kwa muyaya.

17 Ndipo Ambuye anena kuti: ndidzadzutsa Mose; ndipo ndidzampatsa mphamvu kwa iye mu ndodo; ndipo ndidzapatsa chiweruzo m’malembedwe. Koma sindidzamasula lilime lake, kuti adzayankhule zambiri, pakuti sindidzampatsa mphamvu polankhula. Koma ndidzalemba kwa iye chilamulo changa, ndi chala cha dzanja langa; ndipo ndidzamukonzera omuyankhulira.

18 Ndipo Ambuye adatinso kwa ine: Ndidzadzutsa chipatso cha mchiuno mwako; ndipo ndidzamukonzera womuyankhulira. Ndipo ine, taona, ndidzapereka kwa iye kuti adzalembe zolemba za chipatso cha mchiuno mwako, kwa chipatso cha mchiuno mwako; ndipo omuyankhulira wa mchiuno mwako adzalengeza izi.

19 Ndipo mawu amene iye adzalembe adzakhala mawu omwe ali oyenera mu nzeru zanga oyenera adzapite kwa chipatso cha mchiuno mwako. Ndipo zidzakhala ngati kuti chipatso cha mchiuno mwako chidafuulira kwa iwo kuchokera ku fumbi; pakuti ndikudziwa chikhulupiliro chawo.

20 Ndipo iwo adzafuula kuchokera ku fumbi; inde ngakhale kulapa kwa abale awo, ngakhale mibadwo yambiri itadutsa iwo. Ndipo zidzachitika kuti kulira kwawo kudzapita, ngakhale molingana mwa kuphweka kwa mawu awo.

21 Chifukwa cha chikhulupiliro chawo mawu awo adzapitilira kuchokera pakamwa panga kupita kwa abale awo amene ali chipatso cha m’chiuno mwako; ndipo kufooka kwa mawu awo ndidzalimbitsa m’chikhulupiliro chawo, kwa kukumbukira za pangano langa lomwe ndidapanga kwa makolo anu.

22 Ndipo tsopano, taona, mwana wanga Yosefe, moteremu ndim’mene atate anga akale adalosera.

23 Kotero, chifukwa cha pangano ili iwe ndi odalitsidwa; pakuti mbewu yako siidzawonongedwa, chifukwa iwo adzamvera mawu a mu buku.

24 Ndipo adzadzuka wina wamphamvu pakati pawo, amene adzachite zabwino kwambiri, mu mawu komanso m’machitidwe, pokhala chida m’manja mwa Mulungu, ndi chikhulupiliro chopambana, kuchita zozizwa zamphamvu, ndi kuchita chomwe chili chachikulu pamaso pa Mulungu, m’kubweretsa chibwenzeretso kwa a nyumba ya Israeli, ndiponso kwa mbewu ya abale ako.

25 Ndipo tsopano, odala ndi iwe, Yosefe. Taona, iwe ndi wamng’ono; kotero mvetsera mawu a m’bale wako, Nefi, ndipo zidzachitika kwa iwe ngakhale molingana ndi mawu amene ine ndayankhula. Kumbukira mawu a bambo wako amene akufa. Ameni.