Mutu 15
Munda wampesa wa Ambuye (Israeli) udzakhala bwinja, ndipo anthu Ake adzabalalikana—Matsoka adzafika pa iwo mu mkhalidwe wampatuko ndi kumwazikana—Ambuye adzakweza mbendera ndi kusonkhanitsa Israeli—Fananitsani Yesaya 5. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo pamenepo ndidzaimbira okondedwa wanga nyimbo ya okondedwa wanga, yokhudza munda wake wampesa. Okondedwa wanga adali ndi munda wampesa m’phiri la zipatso zambiri.
2 Ndipo adaumangira mpanda, natolatola miyala pamenepo, ndipo adadzalapo mpesa wosankhika, ndipo adamangira nsanja pakati pake, ndiponso adamangapo poponderapo mpesa; ndipo adayan’ganira kuti udzabereka mpesa, ndipo udabereka mpesa wakuthengo.
3 Ndipo tsopano, Inu okhala mu Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, weruzani, ndikukupemphani inu, pakati pa ine ndi munda wampesa wanga.
4 Ndikadachitiranso china chiyani ku munda wampesa chimene sindidachite m’menemo? Kotero, pamene ndidayembekeza kuti udzabala mpesa, iwo udabala mpesa wakuthengo.
5 Ndipo tsopano tiyeni; ndidzakuuzani zimene ndidzachitira munda wanga wampesa—Ndidzachotsamo mpanda wake, ndipo udzadyedwa; ndipo ndidzagumula khoma lake, ndipo udzapondedwa.
6 Ndipo ndidzaupasula; sindidzapaliramo kapena kulimamo, koma m’menemo mudzabwera lunguzi ndi minga; ndipo ndidzalamula mitambo kuti isagwetselepo mvula.
7 Pakuti munda wampesa wa Ambuye wa makamu ndiwo nyumba ya Israeli, ndipo anthu a Yuda ndi mtengo wake wosangalatsa; ndipo iye adayembekezera chiweruziro, ndipo taonani, msautso; kwa chilungamo; ndipo taonani, mfuu.
8 Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, kufikira sipadzakhalanso malo, kuti aikidwe paokha pakati pa dziko!
9 M’makutu anga, atero Ambuye wa makamu, zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ndipo mizinda yayikulu ndi yokongola koma yopanda okhalamo.
10 Inde, maekara khumi a munda wampesa khumi, udzangobala mbiya imodzi, ndipo mbewu yandowa idzangobala msengwa imodzi.
11 Tsoka kwa iye olawira m’mamawa, kuti atsate chakumwa chaukali, amene apitilizabe mpaka usiku, kufikira vinyo atawaledzeretsa!
12 Ndipo zeze ndi mngoli, lingaka, ndi chitoliro, ndi vinyo zili m’maphwando awo; koma sasamala konse ntchito za Ambuye, kapena kuganizirako ntchito za manja ake.
13 N’chifukwa chake, anthu anga apita ku ukapolo, chifukwa alibe chidziwitso; ndipo amuna olemekezeka awo ali ndi njala, ndipo khamu lawo lauma kukhosi ndi ludzu.
14 N’chifukwa chake, gehena wadzikulitsa yekha, ndipo watsegula kukamwa kwake popanda muyeso; ndipo ulemelero wawo, ndi unyinji wawo, ndi phokoso lawo, ndi iye amene akondwera, adzatsikira m’menemo.
15 Ndipo munthu wamba adzatsitsidwa pansi, ndipo munthu wamphamvu adzachepetsedwa, ndipo maso a odzikuza adzachepetsedwa.
16 Koma Ambuye wa makamu adzakwezedwa mu chiweruzo, ndipo Mulungu amene ali oyera adzayeretsedwa m’chilungamo.
17 Pamenepo ana ankhosa adzadya monga mwamadyedwe awo, ndipo malo abwinja la onenepa adzadyedwa ndi alendo.
18 Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zopanda phindu, ndi uchimo monga ngati ndi chingwe cha galeta.
19 Amene amati: Mulekeni iye achite changu, athamangitse ntchito yake, kuti ife tiione; ndipo uphungu wa Oyera wa Israeli uyandikire pafupi ndi kubwera, kuti ife tiudziwe.
20 Tsoka kwa iwo amene atcha choipa, chabwino, ndipo chabwino, choipa, amene amaika mdima m’malo mwa kuwala, ndipo kuwala m’malo mwa mdima, amene amaika chowawa m’malo mwa chotsekemera, ndipo chotsekemera m’malo mwa chowawa!
21 Tsoka kwa iwo odziyesa anzeru ndi ochenjera m’maso mwawo.
22 Tsoka kwa iwo amene ali amphamvu ya kumwa vinyo, ndi anthu olimba ndi kusanganiza chakumwa chaukali;
23 Amene alungamitsa oipa kuti alandire mphotho, ndi kuchotsa chilungamo cha olungama kwa iye.
24 N’chifukwa chake, monga moto umatha chiputu, ndipo malawi amanyeketsa mankhusu, muzu wawo udzakhala ovunda, ndipo maluwa awo adzauluka ngati fumbi; chifukwa iwo adataya chilamulo cha Ambuye wa makamu, ndikunyoza mawu a Oyera wa Israeli.
25 N’chifukwa chake, mkwiyo wa Ambuye wayakira pa anthu ake, ndipo watambasula dzanja lake motsutsana nawo, ndipo wawakantha iwo; ndipo zitunda zidanjenjemera, ndi mitembo yawo idang’ambika pakati pa makwalala. Pazonsezi mkwiyo wake sudachoke, koma dzanja lake lidakali chitambasulire.
26 Ndipo adzakwezera mbendera ku maiko akutali, ndipo adzawayimbira muluzi kwa iwo kuchokera kumalekezero a dziko lapansi; ndipo taonani, iwo adzabwera ndi liwiro la msanga; palibe amene adzatope kapena kupunthwa pakati pawo.
27 Palibe amene adzaodzera kapena kugona; ngakhale lamba wa m’chiuno mwawo sadzamasuka, kapena zingwe za nsapato zawo sizidzaduka;
28 Amene mivi yawo idzakhala yokuthwa, ndipo mauta awo onse opindika, ndi ziboda za akavalo awo zidzayesedwa ngati mwala, ndipo njinga zawo ngati kamvulumvulu, kubangula kwawo ngati mkango.
29 Adzabangula ngati mkango waung’ono; inde, iwo adzabangula, ndi kugwira nyama, ndipo adzainyamura bwino ndipo sipadzakhala opulumutsa.
30 Ndipo mutsikulo iwo adzabangula motsutsana nawo ngati mkokomo wa nyanja; ndipo ngati adzayang’ana kuntunda, taonani, mdima ndi chisoni, ndi kuwala kwadetsedwa m’mitambo yake.