Malembo Oyera
2 Nefi 27


Mutu 27

Mdima ndi mpatuko zidzaphimba dziko lapansi m’masiku otsiriza—Buku la Mormoni lidzabwera—Mboni zitatu zidzachitira umboni za bukulo—Munthu ophunzira adzati sangawerenge buku lomatidwa—Ambuye adzachita ntchito yabwino ndi yodabwitsa—Fananitsani Yesaya 29. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Koma, taonani, m’masiku omaliza, kapena mu masiku a Amitundu—inde, taonani maiko wonse a Amitundu ndiponso Ayuda, wonse amene adzakhamukile ku dziko lino, ndi amene adzakhale pa maiko ena, inde, ngakhale pa maiko wonse a dziko lapansi, taonani, iwo adzaledzera ndi mphulupulu ndi mitundu yonse ya zonyansa.

2 Ndipo tsikulo likadzafika iwo adzayenderedwa ndi Ambuye wa Makamu, ndi mabingu ndi chivomelezi, ndi phokoso lalikulu, ndi namondwe, ndi mphepo ya mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.

3 Ndipo maiko wonse amene amenyana ndi Ziyoni, ndi kumsautsa, adzafanana ndi loto la masomphenya a usiku; inde, kudzakhala kwa iwo, ngati munthu wanjala amene akulota, ndipo taonani akudya koma akadzuka, ndipo moyo wake uli opanda kanthu; kapena monga munthu waludzu amene alota ndipo taonani akumwa, koma akadzuka ndipo taonani ali wolefuka, ndipo moyo wake uli ndi njala; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni.

4 Pakuti taonani, inu nonse amene mukuchita zamphulupulu, khalani nokha ndi kudabwa, pakuti mudzafuula, ndi kulira; inde mudzaledzera koma osati ndi vinyo, mudzadzandima koma osati ndi chakumwa chaukali.

5 Pakuti taonani, Ambuye watsanulira pa inu mzimu wa tulo tofa nato. Pakuti taonani, mwatseka maso anu, ndipo mwakana aneneri, ndi okulamulirani, ndipo alosi waaphimba chifukwa cha mphulupulu zanu.

6 Ndipo zidzachitika kuti Ambuye Mulungu adzabweretsa kwa inu mawu a m’buku, ndipo adzakhala mawu a iwo amene adagona.

7 Ndipo taonani bukulo lidzakhala lomatidwa; ndipo m’bukulo mudzakhala vumbulutso lochokera kwa Mulungu, kuyambira pa chiyambi cha dziko lapansi ndi kumalekezero kwake.

8 Kotero, chifukwa cha zinthu zimene ziri zomatidwa, zinthu zimene ziri zomatidwa sizidzaperekedwa mu tsiku la kuipa ndi la zonyansa za anthu. Kotero bukulo lidzabisidwa kwa iwo.

9 Koma bukulo lidzaperekedwa kwa munthu, ndipo iye adzapereka mawu a mu bukulo, amene ali mawu a iwo amene adagona m’fumbi, ndipo iye adzapereka mawu awa kwa wina.

10 Koma mawu amene ali omatidwa sadzawapereka, ngakhale kupereka bukulo. Pakuti bukulo lidzamatidwa ndi mphamvu ya Mulungu, ndipo vumbulutso limene liri lomatidwa lidzasungidwa mu buku kufikira nthawi yoikika ya Ambuye, kuti likhoza kudzatuluka; pakuti taonani, amavumbulutsa zinthu zonse kuchokera pa maziko a dziko lapansi mpaka kumalekezero kwake.

11 Ndipo tsiku lirinkudza limene mawu a mu buku amene adamatidwa adzawerengedwa pamadenga a nyumba; ndipo adzawerengedwa ndi mphamvu ya Khristu; ndipo zinthu zonse zidzavumbulutsidwa kwa ana a anthu zimene zakhalapo pakati pa ana a anthu, ndi amene adzakhale kufikira kumapeto kwa dziko lapansi.

12 Kotero, pa tsiku limenelo pamene buku lidzaperekedwa kwa munthu amene ndanena, bukulo lidzabisidwa ku maso adziko lapansi, kuti maso a wina aliyense asadzalione kupatula mboni zitatu zidzaliona, ndi mphamvu ya Mulungu, pamodzi ndi iye amene bukuli lidzaperekedwa; ndipo adzachitira umboni choonadi cha bukuli ndi zinthu zimene ziri m’menemo.

13 Ndipo palibe wina aliyense amene adzaliona, kupatula ochepa malingana ndi chifuniro cha Mulungu, kuti achitire umboni wa mawu ake kwa ana a anthu; pakuti Ambuye Mulungu wati mawu a wokhulupirika akuyenera kuyankhula monga ngati kuti akuchokera kwa akufa.

14 Kotero, Ambuye Mulungu adzapitiriza kubweretsa chitsogolo mawu a mu buku; ndipo ndi pakamwa pa mboni zambiri monga zimkomera iye adzakhazikitsa mawu ake; ndipo tsoka likhale kwa iwo amene akana mawu a Mulungu!

15 Koma taonani, zidzachitika kuti Ambuye Mulungu adzanena kwa iye amene adzapereka bukulo, Tenga mawu awa amene sali omatidwa ndi kuwapereka kwa wina, kuti iye athe kuwaonetsa kwa ophunzira, nati: Werengani izi, ndikukupemphani. Ndipo ophunzirayo adzati: Bweretsa kuno bukulo ndipo ndidzawerenga.

16 Ndipo tsopano, chifukwa cha ulemelero wa dziko lapansi ndi kuti apeze cholowa iwo adzanena izi, ndipo osati chifukwa cha ulemelero wa Mulungu.

17 Ndipo munthuyo adzati: Sindingathe kubweretsa bukuli, chifukwa ndilomatidwa.

18 Pamenepo ophunzirayo adzati: Sindingathe kuliwerenga.

19 Kotero zidzachitika kuti Ambuye Mulungu adzaperekanso bukulo ndi mawu ake kwa iye amene sali ophunzira; ndipo munthu osaphunzirayo adzati: Ndine osaphunzira.

20 Pamenepo Ambuye Mulungu adzati kwa iye: ophunzira sadzawerenga izo, pakuti iwo adazikana izo, ndipo ine ndimatha kugwira ntchito yanga; kotero iwe udzawerenga mawu amene ine ndidzakupatse iwe.

21 Osadzakhudza zinthu zimene ziri zomatidwa, chifukwa ine ndidzazibweretsa mu nthawi yanga yoikika; pakuti ndidzaonetsa kwa ana a anthu kuti ine ndimatha kugwira ntchito yanga.

22 Kotero, pamene iwe udzawerenga mawu amene ine ndakulamula iwe, ndi kutenga mboni zimene ndidalonjeza kwa iwe, pamenepo udzamata bukulo kachiwiri, ndi kulibisa kwa ine, kuti ine nditeteze mawu amene iwe sudawerenge, kufikira ndidzaone kuyenera mu nzeru zanga kuti ndivumbulutse zinthu zonse kwa ana a anthu.

23 Pakuti taonani, ine ndine Mulungu, ndipo ndine mulungu wa zozizwitsa; ndipo ndidzaonetsa kwa dziko lapansi kuti ine ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse; ndipo sindimagwira ntchito pakati pa ana a anthu pokhapokha molingana ndi chikhulupiliro chawo.

24 Ndiponso zidzachitika kuti Ambuye adzati kwa iye amene adzawerenge mawu amene adzaperekedwa kwa iye:

25 Popeza anthu awa ayandikira kwa ine ndi pakamwa pawo, ndipo ndi milomo yawo amandilemekeza, koma mitima yawo ili kutali ndi ine, ndi mantha awo pa ine akuphunzitsidwa ndi malangizo a anthu.

26 N’chifukwa chake, ndidzapitiriza kuchita ntchito yodabwitsa pakati pa anthu awa, inde, ntchito yabwino ndi yodabwitsa, pakuti nzeru ya anthu awo anzeru ndi ophunzira idzatha, ndipo kuzindikira kwa anthu awo ozindikira kudzabisidwa.

27 Ndipo tsoka kwa iwo amene amafunafuna mwakuya kubisa uphungu wawo kwa Ambuye! Ndi ntchito zawo ziri mumdima; ndipo amati: Ndani akutiona ife, ndipo ndani akutidziwa ife? Ndiponso amati: Ndithudi, kutembenuza kwanu kwa zinthu kudzayesedwa ngati dongo la oumba. Koma taonani, ndidzawaonetsa iwo, akutero Ambuye wa Makamu, kuti ndikudziwa ntchito zawo. Kodi ntchito idzati za iye amene adaipanga, kuti iye sadandipange? Kapena kodi chinthu choumbidwa chinganene za iye adachiumba, iye alibe nzeru?

28 Koma taonani, akutero Ambuye wa Makamu: Ndidzaonetsa kwa ana a anthu kuti kwatsala kamphindi pang’ono ndipo Lebanoni adzasanduka munda wobalitsa, ndipo munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.

29 Ndipo tsiku limenero gonthi adzamva mawu a m’buku, ndi maso a akhungu adzaona kuchokera m’kusadziwa ndi kuchokera mu mdima.

30 Ndipo ofatsa adzachulukira, ndipo chisangalalo chawo chidzakhala mwa Ambuye, ndi osauka mwa anthu adzakondwera mwa Oyera wa Israeli.

31 Pakuti indedi monga Ambuye ali wamoyo iwo adzaona kuti oopsayo wagonja, ndipo wonyoza wapserezedwa, ndi wonse oyembekezera kuchita mphulupulu adzadulidwa;

32 Ndipo amene amapangitsa munthu kukhala ochimwa chifukwa cha mawu, ndipo amatchera msampha iye amene adzudzula pachipata, ndikumubweza wolungama ndi chinthu chachabe.

33 N’chifukwa chake, akutero Ambuye, amene adawombola Abrahamu, zokhudzana ndi nyumba ya Yakobo: Yakobo sadzachita manyazi tsopano, ngakhale nkhope yake siidzagwa.

34 Koma pamene iye akuona ana ake, ntchito ya manja anga, pakati pa iye, iwo adzayeretsa dzina langa, ndipo adzayeretsa Oyera wa Yakobo, ndipo adzaopa Mulungu wa Israeli.

35 Iwonso osochera mu mzimu adzafika pa kuzindikira, ndipo iwo amene adang’ung’udza adzaphunzira chiphunzitso.

Print