Malembo Oyera
2 Nefi 32


Mutu 32

Angelo amayankhula ndi mphamvu ya Mzimu Woyera—Anthu akuyenera kupemphera ndi kupeza chidziwitso cha iwo eni kuchokera kwa Mzimu Woyera. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, taonani, abale anga okondedwa, ine ndikuyesa kuti inu mwasinkhasinkha penapake mu mtima mwanu zokhudzana ndi zimene mukuyenera kuchita mutalowa m’njirayi. Koma, taonani, n’chifukwa chiyani mukusinkhasinkha zimenezi mumtima mwanu?

2 Kodi simukukumbukira kuti ine ndidati kwa inu kuti mutatha kulandira Mzimu Woyera mudzatha kuyankhula ndi lilime la angelo? Ndipo tsopano, mungathe kuyankhula bwanji ndi lilime la angelo pokhapokha zidali mwa Mzimu Woyera?

3 Angelo amayankhula ndi mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero amayankhula mawu a Khristu. Kotero, ndidanena kwa inu, dyelerani pa mawu a Khristu; pakuti taonani, mawu a Khristu adzakuuzani inu zinthu zonse zimene mukuyenera kuchita.

4 Kotero, tsopano nditatha kuyankhula mawu awa, ngati simungawamvetsetse kudzakhala chifukwa choti inu simumafunsa, kapena kugogoda; kotero simudalowetsedwe m’kuwala, koma mukuyenera kuwonongeka mu mdima.

5 Pakuti taonani, ndiponso ndinena ndi inu kuti ngati mulowa kudzera m’njirayi, ndi kulandira Mzimu Woyera, udzaonetsa kwa inu zinthu zonse zomwe mukuyenera kuchita.

6 Taonani, ichi ndi chiphunzitso cha Khristu, ndipo sipadzakhalanso chiphunzitso china choperekedwa kufikira atadzionetsera yekha kwa inu mu thupi. Ndipo pamene adzadzionetsera yekha mu thupi; zinthu zimene adzayankhule kwa inu mudzazisamale kuzichita.

7 Ndipo tsopano ine, Nefi, sindingayankhulenso: Mzimu wandiletsa zoyankhula zanga, ndipo ndatsala ndikulira chifukwa cha kusakhulupilira, ndi kuipa, ndi kusadziwa, ndi kusamva kwa anthu; pakuti iwo sadzafufuza chidziwitso, kapena kumvetsa chidziwitso chachikulu, pamene chapatsidwa kwa iwo momveka, ngakhale momveka monga mawu angakhalire.

8 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, ndikuona kuti inu mukusinkhasinkhabe m’mitima mwanu; ndipo zikundiwawa kuti ndikuyenera ndiyankhule nanu zokhudzana ndi chimenechi. Pakuti ngati mudzamvera kwa Mzimu amene amaphunzitsa munthu kupemphera, mukadadziwa kuti mukuyenera kupemphera; chifukwa mzimu woipa samaphunzitsa munthu kupemphera, koma amaphunzitsa iye kuti asamapemphere.

9 Koma taonani, ndikunena ndi inu kuti mukuyenera kupemphera nthawi zonse, ndipo musatope; kuti simukuyenera kuchita kanthu kalikonse kwa Ambuye pokhapokha poyamba mupemphere kwa Atate mu dzina la Khristu, kuti iye adzapatulire ntchito yanu kwa inu, kuti kuchita kwanu kukhale kwa ubwino wa moyo wanu.