Malembo Oyera
Eteri 4


Mutu 4

Moroni alamulidwa kuti amate zolemba za m’bale wa Yaredi—Sizidzaululidwa kufikira anthu atakhala ndi chikhulupiliro monga ngati m’bale wa Yaredi—Khristu alamula anthu kuti akhulupilire mawu Ake ndi a ophunzira Ake—Anthu alamulidwa kuti alape, kukhulupilira uthenga wabwino, ndi kupulumutsidwa.

1 Ndipo Ambuye adalamula m’bale wa Yaredi kuti atsike kuphiriko kuchoka pamaso pa Ambuye, ndi kukalemba zinthu zimene adaziona; ndipo zidaletsedwa kufika kwa ana a anthu kufikira iye atapachikidwa pamtanda; ndipo pachifukwa ichi mfumu Mosiya adazisunga, kuti zisafike ku dziko lapansi kufikira Khristu atadzionetsera yekha kwa anthu ake.

2 Ndipo Khristu atadzionetseradi kwa athu ake iye adalamula kuti zionetsedwe.

3 Ndipo tsopano, pambuyo pake, iwo adacheperachepera mchikhulupiliro; ndipo palibe wina kupatula Alamani, ndipo iwo akana uthenga wabwino wa Khristu; kotero ndalamulidwa kuti ndizibisenso mu nthaka.

4 Taonani, ndalemba pa mapale awa zinthu zomwezo zimene m’bale wa Yaredi adaziona; ndipo padalibe zinthu zazikulu zoonetseredwa kuposa zimene zidaonetseredwa kwa m’bale wa Yaredi.

5 Potero Ambuye iwo andilamula ine kuti ndizilembe; ndipo ndazilemba. Ndipo andilamula ine kuti ndizimate; ndiponso alamula kuti ndimatenso zomasulira zake; kotero ndamata zomasulirazo, molingana ndi malamulo a Ambuye.

6 Pakuti Ambuye adati kwa ine: Zisadzapite kwa Amitundu kufikira tsiku limene iwo adzalape mphulupulu zawo, ndi kukhala oyera pamaso pa Ambuye.

7 Ndipo mutsiku limenero iwo adzakhala ndi chikhulupiliro mwa ine, atero Ambuye, monga ngati m’bale wa Yaredi adali, kuti iwo akhale oyeretsedwa mwa ine, pamenepo ine ndidzaonetsera kwa iwo zinthu zonse zimene m’bale wa Yaredi adaona, ngakhale kuvumbulutsa kwa iwo mavumbulutso anga onse, atero Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, Atate wa kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zinthu zonse zili m’menemo.

8 Ndipo iye amene alimbana ndi mawu a Ambuye, akhale otembeleredwa; ndipo iye amene adzakana zinthu izi, akhale otembeleredwa; pakuti kwa iwo sindidzawaonetsa zinthu zazikulu, atero Yesu Khristu; pakuti ine ndi amene ndikuyankhula.

9 Ndipo pakulamula kwanga kumwamba kumatsegulidwa ndi kutsekedwa; ndipo pa mawu anga dziko lapansi lidzagwedezeka; ndipo pa kulamula kwanga okhala m’menemo adzatha, ngakhale choncho ndi moto.

10 Ndipo iye amene sakhulupilira mawu anga sakhulupilira ophunzira anga; ndipo ngati zili kuti ine sindiyankhula, weruzani iwo; pakuti mudzadziwa kuti ndi ine amene ndikuyankhula, patsiku lotsiriza.

11 Koma iye amene akhulupilira zinthu izi zimene ndayankhulazi, iye ndidzamuyendera ndi maonetseredwe a Mzimu wanga, ndipo iye adzadziwa ndi kuchitira umboni. Pakuti chifukwa cha Mzimu wanga iye adzadziwa kuti zinthu izi ndizoona; pakuti zimakopa anthu kuchita zabwino.

12 Ndipo chilichonse chokopa anthu kuchita chabwino ndi cha ine; pakuti chabwino sichibwera kupatula chikhale cha ine. Ndine yemweyo amene ndimatsogolera anthu kuchita zabwino zonse; iye amene sadzakhulupilira mawu anga sadzakhulupilira ine—kuti ndine; ndipo iye amene sadzakhulupilira ine sadzakhulupilira Atate amene adandituma ine. Pakuti taonani, ndine Atate, ndine kuwala, ndi moyo, ndi choonadi cha dziko lapansi.

13 Bwerani kwa ine, O inu Amitundu, ndipo ndidzaonetsa kwa inu zinthu zazikulu, chidziwitso chimene chidabisidwa chifukwa cha kusakhulupilira.

14 Bwerani kwa ine, O inu nyumba ya Israeli, ndipo zidzadziwitsidwa kwa inu m’mene zinthu zazikulu Atate aziikira kwa inu, kuchokera ku maziko a dziko lapansi; ndipo sizidafike kwa inu, chifukwa cha kusakhulupilira.

15 Taonani, pamene inu mudzang’amba chophimba cha kusakhulupilira chimene chimakupangitsani inu kukhalabe mu mkhalidwe wanu woipa, ndi kuumitsa mitima, ndi khungu la m’maganizo, pamenepo zinthu zazikulu ndi zodabwitsa zimene zabisidwa kuchokera ku maziko a dziko lapansi kwa inu—inde, pamene inu mudzaitanire pa dzina la Atate mu dzina langa, ndi mtima wosweka ndi mzimu wolapa, pamenepo inu mudzadziwa kuti Atate adakumbukira pangano limene iwo adapanga kwa makolo anu, O nyumba ya Israeli.

16 Ndipo pamenepo mavumbulutso anga amene ndachititsa kuti alembedwe ndi mtumiki wanga Yohane adzavumbulutsidwa m’maso mwa anthu onse. Kumbukira, pamene inu mwawona zinthu izi, mudzadziwa kuti nthawi yayandikira kuti izo zidzawonetseredwa mu chochitikacho.

17 Kotero, pamene iwe udzalandira zolembazi iwe ungathe kudziwa kuti ntchito ya Atate yayambika pamaso ponse pa dziko.

18 Kotero, lapani nonse malekezero a dziko lapansi, ndi kubwera kwa ine, ndi kukhulupilira mu uthenga wanga wabwino, ndi kubatizidwa mu dzina langa; pakuti iye amene akhulupilira ndipo wabatizidwa adzapulumutsidwa; koma iye amene sakhulupilira adzalangidwa; ndipo zizindikiro zidzawatsata iwo amene akhulupilira mu dzina langa.

19 Ndipo odala ndi iye amene wapezeka okhulupirika ku dzina langa pa tsiku lotsiriza, pakuti iye adzakwezedwa kukakhala mu ufumu wokonzedwera kwa iye kuchokera ku maziko a dziko lapansi. Ndipo taonani ndi ine amene ndazinena. Ameni.

Print