Malembo Oyera
Eteri 9


Mutu 9

Ufumu uchokera kwa m’modzi kupita kwa wina kudzera kumtundu, chiwembu ndi kupha—Emeri aona Mwana wa Chilungamo—Aneneri ambiri amafuula kulapa—Chilala ndi njoka za chiphe zizunza anthu.

1 Ndipo tsopano ine, Moroni, ndikupitiriza zolemba zanga. Kotero, taonani, zidachitika kuti chifukwa cha magulu achinsinsi a Akishi ndi amzake, taonani, iwo adagwetsa ufumu wa Omeri.

2 Komabe, Ambuye adali ndi chifundo kwa Omeri, ndiponso kwa ana ake aamuna ndi aakazi amene sadafune kumuwononga iye.

3 Ndipo Ambuye adachenjeza Omeri mu maloto kuti iye anyamuke kuchoka m’dzikolo; kotero Omeri adanyamuka kuchoka m’dzikolo ndi banja lake, ndipo adayenda masiku ambiri, ndipo adafika ndi kudzera ku phiri la Shimu, ndipo adafika pa malo amene Anefi adawonongedwa, ndipo kuchokera pamenepo chakum’mawa, ndipo adafika ku malo amene ankatchedwa Abulomu, pafupi ndi gombe lanyanja, ndipo pamenepo iye adakhoma hema lake, ndiponso ana ake aamuna ndi aakazi, ndi onse amnyumba mwake, kupatula Yaredi ndi banja lake.

4 Ndipo zidachitika kuti Yaredi adadzodzedwa mfumu pa anthuwo, ndi dzanja la woipa ndipo iye adapereka kwa Akishi mwana wake wamkazi kukhala mkazi wake.

5 Ndipo zidachitika kuti Akishi adafuna moyo wa apongozi ake aamuna; ndipo iye adafunsa kwa iwo amene iye adalumbilira ndi lumbilo la akale, ndipo iwo adatenga mutu wa apongozi akewo, pamene iwo adakhala pa mpando wawo wachifumu, akumvetsera anthu awo.

6 Pakuti kwakukulu kudali kufala kwa gulu lachinsinsi ndi loipali mpaka zidaipitsa mitima ya anthu onse; kotero Yaredi adaphedwa pa mpando wake wachifumu, ndipo Akishi adalamulira m’malo mwake.

7 Ndipo zidachitika kuti Akishi adayamba kuchitira nsanje mwana wake wamwamuna, kotero iye adamutsekera mundende ndi kumusunga iye ndi chakudya chochepa kapena osadya kufikira iye adafa.

8 Ndipo tsopano m’bale wa iye amene adafayo (ndipo dzina lake lidali Nimira) adakwiya ndi atate akewo chifukwa cha chimene atate akewo adachita kwa m’bale wake.

9 Ndipo zidachitika kuti Nimira adasonkhanitsa pamodzi chiwerengero chochepa cha anthu, ndipo adathawa kuchoka m’dzikolo, ndi kubwera ndi kudzakhala ndi Omeri.

10 Ndipo zidachitika kuti Akishi adabereka ana ena aamuna, ndipo iwo adakopa mitima ya anthu, posatengera kuti adalumbira kwa iye kuchita chilichonse choipa molingana ndi chimene iye adakhumbira.

11 Tsopano anthu a Akishi ankakhumbira kupindula, monga momwe Akishi ankakhumbira mphamvu; kotero, ana aamuna a Akishi adapereka kwa iwo ndalama, mwa njira imeneyi iwo adakokera mbali yochuluka ya anthu pambuyo pawo.

12 Ndipo kudabuka nkhondo pakati pa ana a Akishi ndi Akishi, imene idatha kwa nthawi ya dzaka zambiri, inde, mpaka kuwononga pafupifupi anthu onse mu ufumuwo, inde, ngakhale onse, kupatula anthu makumi atatu, ndi iwo amene adathawa ndi banja la Omeri.

13 Kotero, Omeri adabwenzeretsedwanso ku dziko la cholowa chake.

14 Ndipo zidachitika kuti Omeri adayamba kukalamba; komabe, mu ukalamba wake iye adabereka Emeri; ndipo adamudzodza Emeri kukhala mfumu yolamula m’malo mwake.

15 Ndipo atangomudzodza Emeri kukhala mfumu iye adaona mtendere mu dzikolo kwa nthawi ya dzaka ziwiri, ndipo iye adamwalira, ataona masiku ochuluka kwambiri, amene adali odzadza ndi chisoni. Ndipo zidachitika kuti Emeri adalamulira m’malo mwake, ndipo adatsatira mapazi a atate ake.

16 Ndipo Ambuye adayambiranso kuchotsa thembelero kuchokera m’dzikolo, ndipo banja la Emeri lidachita bwino kwambiri pansi pa ulamuliro wa Emeri; ndipo kwa nthawi ya dzaka makumi asanu ndi chimodzi ndi mphambu ziwiri iwo adakhala amphamvu kwambiri, kufikira kuti iwo adakhala olemera kwambiri—

17 Pokhala ndi zipatso za mitundu yonse, ndi mbewu, ndi ulusi, ndi nsalu zokongola, ndi golide, ndi siliva, ndi zinthu zamtengo wapatali;

18 Ndiponso mitundu yonse ya ng’ombe, zazimuna zokankha ngolo ndi zazikazi za mkaka, ndi nkhosa, ndi nkhumba, ndi mbuzi, ndiponso mitundu ina yambiri ya nyama zimene zili zofunikira ku chakudya cha munthu.

19 Ndipo iwo adalinso ndi akavalo, ndi abulu, ndipo kudali njovu ndi akurelomu ndi akumomu; zonse zimene zidali zofunikira kwa munthu, ndipo makamaka njovuzo ndi akurelomu ndi akumomu.

20 Ndipo motero Ambuye adatsanulira madalitso awo pa dzikoli, limene lidali losankhika kuposa maiko ena onse; ndipo adalamula kuti aliyense amene adzakhale mu dzikoli akuyenera kukhalamo mwa Ambuye, kapena adzawonongedwa pamene adzakhwima mu zoipa; pakuti pa oterewa, atero Ambuye: Ndidzatsanula chidzalo cha mkwiyo wanga.

21 Ndipo Emeri adagamula chiweruzo mwa chilungamo masiku onse a moyo wake, ndipo iye adabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri; ndipo adabereka Koriyantumu, ndipo iye adadzodza Koriyantumu kuti alamulire m’malo mwake.

22 Ndipo iye atatha kudzodza Koriyantumu kuti alamulire m’malo mwake iye adakhala dzaka zinayi, ndipo adaona mtendere mudzikomo; inde, ndipo iye adaona ngakhale Mwana wa Chilungamo, ndipo adakondwera ndi kulemekeza mu tsiku lake; ndipo adamwalira mu mtendere.

23 Ndipo zidachitika kuti Koriyantumu adayenda m’mapazi a atate ake, ndipo adamanga mizinda yamphamvu yambiri, ndi kuchita chimene chidali chabwino kwa anthu ake m’masiku ake onse. Ndipo zidachitika kuti iye adalibe ana ngakhale kufikira iye adakalamba kwambiri.

24 Ndipo zidachitika kuti mkazi wake adamwalira, pokhala ndi dzaka zana limodzi ndi ziwiri. Ndipo zidachitika kuti Koriyantumu adatenga mkazi, mu ukalamba wake, kamsoti, ndipo adabereka ana aamuna ndi aakazi; kotero iye adakhala kufikira ali ndi dzaka zana limodzi ndi makumi anayi ndi ziwiri.

25 Ndipo zidachitika kuti iye adabereka Komi, ndipo Komi adalamulira m’malo mwake; ndipo iye adalamulira kwa dzaka makumi anayi ndi zisanu ndi zinayi, ndipo adabereka Heti; ndiponso adabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

26 Ndipo anthu adafalikiranso pamaso pa dziko lonselo, ndipo kudayambiranso kukhala kuipa kwakukulu kwambiri pamaso pa dzikolo, ndipo Heti adayamba kugwiritsanso madongosolo achinsinsi akale, kuti awononge atate ake.

27 Ndipo zidachitika kuti iye adachotsa ufumu atate ake, pakuti adawapha ndi lupanga lake lomwe; ndipo iye adalamulira m’malo mwawo.

28 Ndipo kudadza aneneri mudzikolo kachiwiri, kufuula kulapa kwa iwo—kuti iwo athe kukonza njira ya Ambuye kapena kudzakhala thembelero pamaso pa dzikolo; ngakhale kudzakhala chilala chachikulu, mumene iwo akuyenera kudzawonongedwa ngati iwo sadalape.

29 Koma anthuwo sadakhulupilire mawu a aneneriwo, koma adawathamangitsira iwo kunja; ndipo ena mwa iwo adawaponyera m’maenje ndi kuwasiya kuti afe. Ndipo zidachitika kuti adachita zinthu zonsezi molingana ndi malamulo a mfumu, Heti.

30 Ndipo zidachitika kuti kudayamba kukhala njala yayikulu pa dzikolo, ndipo okhalamo adayamba kuwonongedwa mofulumira kwambiri chifukwa cha njala, pakuti kudalibe mvula pamaso pa dziko lapansi.

31 Ndipo kudadza njoka za chiphe pa dzikopo, ndipo zidapha anthu ambiri. Ndipo zidachitika kuti ziweto zawo zidayamba kuthawa pamaso pa njoka zachiphezo, kupita ku dziko lakum’mwera, limene linkatchedwa ndi Anefi Zarahemula.

32 Ndipo zidachitika kuti zidalipo zambiri zimene zidafera mu njira; komabe, zidaliponso zina zimene zidathawira ku dziko la kum’mwera.

33 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adachititsa njokazo kuti zisazithamangitsenso, koma kuti zitchinge njira kuti anthuwo asadutse, kuti amene angayesere kudutsa akathe kufa ndi njoka zachiphezo.

34 Ndipo zidachitika kuti anthu adatsatira njira ya ziwetozo, ndipo ankadya nyama ya zimene zidagwera munjira, kufikira adazidya zonse. Tsopano pamene anthu adaona kuti akuyenera kufa iwo adayamba kulapa ku zoipa zawo ndi kufuula kwa Ambuye.

35 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adadzichipetsa okha mokwanira pamaso pa Ambuye iye adatumiza mvula pamaso pa dziko lapansi; ndipo anthu adayamba kutsitsimukanso, ndipo kudayamba kukhala zipatso ku maiko akumpoto, ndi kumaiko onse ozungulira. Ndipo Ambuye adaonetsa mphamvu yawo kwa iwo powapulumutsa iwo ku njala.

Print