Malembo Oyera
Eteri 13


Mutu 13

Eteri ayankhula za Yerusalemu Watsopano kuti adzamangidwa ku Amerika ndi mbewu ya Yosefe—Iye anenera, athamangitsidwa, alemba mbiri ya Ayaredi, ndipo alosera za chiwonongeko cha Ayaredi—Nkhondo iyambika mu dziko lonse.

1 Ndipo tsopano ine, Moroni, ndikumalizitsa zolemba zanga zokhudzana ndi chiwonongeko cha anthu amene ndakhala ndikulemba.

2 Pakuti taonani, iwo adakana mawu onse a Eteri; pakuti iye adawauzadi iwo zinthu zonse, kuchokera pa chiyambi cha munthu; ndipo kuti atatha madzi kuphwera pamaso pa dziko limeneli lidakhala dziko losankhika kuposa maiko ena onse, dziko losankhika ndi Ambuye; kotero Ambuye adafuna kuti anthu onse awatumikire iwo amene akhala pa dziko limeneli.

3 Ndipo kuti adali malo a Yerusalemu Watsopano, amene adzabwere kuchokera kumwamba, ndi malo oyera opatulika a Ambuye.

4 Taonani, Eteri adaona masiku a Khristu, ndipo adayankhula zokhudzana ndi Yerusalemu Watsopano pa dzikoli.

5 Ndipo iye adayankhulanso zokhudzana ndi nyumba ya Israeli, ndi Yerusalemu kumene Lehi adzachokere—atawonongedwa akuyenera adzamangidwanso kachiwiri, mzinda woyera kwa Ambuye; kotero, sakadakhala Yerusalemu watsopano pakuti adali mu nthawi yakale; koma akuyenera kumangidwanso, ndi kukhala mzinda woyera wa Ambuye; ndipo udzamangidwa kwa nyumba ya Israeli—

6 Ndipo kuti Yerusalemu Watsopano adzamangidwa pa dziko ili, kwa otsalira a mbewu ya Yosefe, pa chimene chinthuchi pali chitsanzo chake.

7 Pakuti Yosefe adabweretsa atate ake kuchokera ku dziko la Igupto, ngakhale choncho iye adafera komweko, kotero, Ambuye adabweretsa otsalira a mbewu ya Yosefe kuchokera ku dziko la Yerusalemu, kuti iye akathe kuchitira chifundo kwa mbewu ya Yosefe kuti iwo asawonongedwe, ngakhale monga iye adachitira chifundo kwa atate a Yosefe kuti asawonongedwe.

8 Kotero, otsalira a nyumba ya Yosefe adzamangidwa pa dziko ili; ndipo lidzakhala dziko la cholowa chawo; ndipo iwo adzamanga mzinda woyera kwa Ambuye, ofanana ndi Yerusalemu wakale; ndipo sadzasokonezedwanso, kufikira chimaliziro chidzafika pamene dziko lapansi lidzatha.

9 Ndipo padzakhala kumwamba kwa tsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo adzakhala ngati akale kupatula kuti akale atha, ndipo zinthu zonse zidzakhala zatsopano.

10 Ndipo kenako adzabwera Yerusalemu Watsopano; ndipo odala ali iwo amene adzakhalamo, pakuti ndi iwo amene zovala zawo ndi zoyera kudzera mu mwazi wa Mwana wa Nkhosa; ndipo ndi iwo amene ali owerengedwa pamodzi ndi otsalira a mbewu ya Yosefe, amene adali a nyumba ya Israeli.

11 Ndipo kenakonso adzabwera Yerusalemu wakale; ndi okhalamo m’menemo, odala ndi iwo, pakuti iwo atsukidwa ndi mwazi wa Mwana wa Nkhosa; ndipo ndi iwo amene adabalalitsidwa ndi kusonkhanitsidwa kuchokera ku zigawo zinayi za dziko lapansi, ndi kuchokera ku maiko a kumpoto, ndipo ali ogawana nawo m’kukwaniritsidwa kwa pangano limene Mulungu adapanga ndi tate wawo, Abrahamu.

12 Ndipo pamene zinthu izi zidza, zidzakwaniritsa malembo oyera amene amati, alipo iwo amene adali oyamba, amene adzakhala omaliza; ndipo alipo iwo amene adali omaliza, amene adzakhala oyamba.

13 Ndipo ine ndidali pafupi kulemba zambiri, koma ndidaletsedwa; koma mauneneri aakulu ndi odabwitsa adali a Eteri; koma iwo adamuyesa iye kukhala wopanda pake, ndipo adamuthamangitsa; ndipo iye ankabisala mu mphanga la mwala kumasana ndipo kumadzulo iye ankapita kuwona zinthu zimene zikuyenera kubwera pa anthuwo.

14 Ndipo pamene iye ankakhala mu mphanga la mwalawo adapanga zotsalira za zolemba izi, poona chiwonongeko chimene chidabwera pa anthuwa, mkati mwausiku.

15 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chomwecho chimene iye adathamangitsidwa kuchoka pakati pa anthuwo kudayamba kukhala nkhondo pakati pa anthu, pakuti adalipo ambiri amene adaukira, amene adali anthu amphamvu, ndipo adafuna kuti amuwononge Koriyantumuri ndi madongosolo awo achinsinsi oipa, amene anenedwa kale.

16 Ndipo tsopano Koriyantumuri, ataphunzira, yekha, mu ukadaulo wa nkhondo ndi kuchenjera konse kwa dziko lapansi, kotero iye adathira nkhondo kwa iwo amene adafuna kumuwononga iye.

17 Koma iye sadalape, ngakhale ana ake aamuna ndi aakazi okongola; ngakhale ana aamuna ndi aakazi okongola a Koho; ngakhale ana aamuna ndi aakazi okongola a Koriho; ndipo pamapeto ake, kudalibe aliyense mwa ana aamuna ndi aakazi okongola pamaso pa dziko lapansi lonse amene adalapa machimo awo.

18 Kotero, zidachitika kuti mu chaka choyamba chimene Eteri adakhala mu mphanga la mwala, kudali anthu ambiri amene adaphedwa ndi lupanga la iwo amagulu azachinsinsi, kumenyana motsutsana ndi Koriyantumuri kuti iwo alande ufumuwo.

19 Ndipo zidachitika kuti ana aamuna a Koriyantumuri adamenya kwambiri ndipo adavulala kwambiri.

20 Ndipo mu chaka cha chiwiri mawu a Ambuye adadza kwa Eteri, kuti iye apite ndi kukanenera kwa Koriyantumuri kuti, ngati iye angalape, ndi onse a banja lake lonse, Ambuye adzapereka kwa iye ufumu wake ndi kupulumutsa anthuwo—

21 Kupanda apo iwo adzawonongedwa, ndi banja lake lonse kupatula iyemwini. Ndipo iye adzakhala moyo kuti aone kukwanilitsidwa kwa mauneneri amene adayankhulidwa okhudzana anthu ena kulandira dzikolo ku cholowa chawo; ndipo Koriyantumuri adzakwiliridwa ndi iwowa; ndipo munthu wina aliyense adzawonongedwa kupatula Koriyantumuri.

22 Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri sadalape, ngakhale banja lake, ngakhale anthuwo; ndipo nkhondozo sizidathe; ndipo iwo adafuna kumupha Eteri, koma iye adathawa kuchoka pamaso pawo ndipo adabisalanso mu mphanga la mwala.

23 Ndipo zidachitika kuti kudabwera Saredi, ndipo iyenso adathira nkhondo kwa Koriyantumuri; ndipo iye adamugonjetsa iye, kufikira kuti mu chaka chachitatu iye adamubweretsa iye mu ukapolo.

24 Ndipo ana aamuna a Koriyantumuri, mu chaka cha chinayi, adamugonjetsa Saredi, ndipo adalanda dzikolo kachiwiri kwa atate awo.

25 Tsopano kudayamba kukhala nkhondo pamaso ponse pa dzikolo, munthu aliyense ndi gulu lake kumenyana pa chimene iye wakhumbira.

26 Ndipo kudali zigawenga, ndipo pamapeto pake, zoipa zamtundu wonse pamaso pa dziko lonselo.

27 Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri adali okwiya kwambiri ndi Saredi, ndipo iye adapita motsutsana naye ndi ankhondo ake kukhondo; ndipo adakumana mu mkwiyo waukulu, ndipo adakumana ku mtsinje wa Giligala; ndipo nkhondoyo idakhala yoopsya kwambiri.

28 Ndipo zidachitika kuti Saredi adamenyana naye kwa nthawi ya masiku atatu. Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri adamugonjetsa iye, ndipo adamuthamangitsa kufikira iye adafika m’zigwa za Heshuloni.

29 Ndipo zidachitika kuti Saredi adamuthiranso nkhondo kachiwiri mu zigwazo; ndipo taonani, iye adamugonjetsa Koriyantumuri, ndipo adamubwenza kachiwiri ku mtsinje wa Giligala.

30 Ndipo Koriyantumuri adamuthiranso nkhondo Saredi kachiwiri mu mtsinje wa Giligala, mumene adamugonjetsa Saredi ndi kumupha.

31 Ndipo Saredi adavulaza Koriyantumuri pa ntchafu yake, mpakana iye sadapitsenso ku nkhondo kwa nthawi ya dzaka ziwiri, mumene m’nthawiyo anthu onse pamaso pa dzikolo adali kukhetsa mwazi, ndipo padalibe owaletsa iwo.

Print