Malembo Oyera
Eteri 2


Mutu 2

Ayaredi akonzekera ulendo wawo wa kudziko la lonjezano—Ndi dziko losankhidwa kumene anthu akuyenera kutumikira Khristu kapena kuthamangitsidwa—Ambuye ayankhula kwa m’bale wa Yaredi kwa maora atatu—Ayaredi amanga mabwato—Ambuye afunsa m’bale wa Yaredi kuti anene m’mene mabwato angawalitsidwire.

1 Ndipo zidachitika kuti Yaredi ndi m’bale wake, ndi mabanja awo, ndiponso abwenzi a Yaredi ndi m’bale wake ndi mabanja awo, adapita ku chigwa chimene chidali chakumpoto, (ndipo dzina la chigwacho lidali Nimrodi, kutchedwa potsatira mlenje wamkuluyo) ndi ziweto zawo zimene adazisonkhanitsa pamodzi, zazimuna ndi zazikazi, za mitundu yonse.

2 Ndipo adatcheranso misampha ndi kugwira mbalame za m’mlengalenga; ndiponso adakonza zotengera, mumene iwo ankatengera nsomba za m’madzi.

3 Ndiponso adanyamula ndi iwo madesereti, amene, mwa tanthauzo lake, ndi njuchi za uchi; ndipo motero iwo adanyamula ndi iwo magulu a njuchi, ndi mitundu yonse ya zimene zidali pamaso pa dzikolo, mbewu za mitundu yonse.

4 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adafika ku chigwa cha Nimrodi Ambuye adatsika ndi kuyankhula ndi m’bale wa Yaredi; ndipo iwo adali m’mitambo, ndipo m’bale wa Yaredi sadawaone.

5 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adawalamula iwo kuti apite ku chipululu, inde, ku chigawo chimene munthu sadafikeko. Ndipo zidachitika kuti Ambuye adapita patsogolo pawo, ndi kuyankhula nawo pamene iwo adaima m’mitambo, ndi kuwapatsa mayendedwe amene iwo angayendere.

6 Ndipo zidachitika kuti iwo adayenda m’chipululumo, ndipo adamanga mabwato, mumene iwo adawolokera madzi ambiri, potsogoleredwa ndi dzanja la Ambuye.

7 Ndipo Ambuye sadalore kuti iwo ayime kutsidya kwa nyanjayo m’chipululu, koma iwo adafuna kuti iwo afike ngakhale ku dziko la lonjezano, limene lidali losankhika kuposa maiko ena onse, limene Ambuye Mulungu adasungira kwa anthu olungama.

8 Ndipo iwo adalumbira mu mkwiyo wake kwa m’bale wa Yaredi, kuti amene adzatenge dziko la lonjezanoli, kuyambira pa nthawi imeneyo kumka mtsogolo ndi kunthawi zosatha, akuyenera kutumikira iwo, Mulungu woona komanso yekhayo, kapena adzathamangitsidwa pamene chidzalo cha mkwiyo wake chidzabwera pa iwo.

9 Ndipo tsopano, tikhonza kuona zilengezo za Mulungu zokhudzana ndi dziko ili. kuti ndi dziko la lonjezano; ndipo dziko linalililonse limene lidzalitenge lidzatumikira Mulungu, kapena adzathamangitsidwa pamene chidzalo cha mkwiyo wake chidzabwera pa iwo. Ndipo chidzalo cha mkwiyo wake chimabwera pa iwo pomwe iwo akwanira m’kusaweruzika.

10 Pakuti taonani, ili ndi dziko limene lili losankhidwa kuposa maiko onse; kotero iye amene adzakhalemo adzatumikira Mulungu, kapena adzathamangitsidwa; pakuti ili ndi lamulo losatha la Mulungu. Ndipo sichiri choncho mpaka kufikira mpaka chidzalo cha mphulupulu pakati pa ana a dzikoli, kuti iwo adzathamangitsidwa.

11 Ndipo izi zibwera kwa inu, O inu Amitundu, kuti inu mukathe kudziwa malamulo a Mulungu—kuti inu mukathe kulapa, ndi kusapitilira m’kusaweruzika kwanu kufikira chidzalocho chitafika, kuti inu musakathe kubweretsa chidzalo cha mkwiyo wa Mulungu pa inu monga okhala mu dzikoli adachitira kufikira tsopano.

12 Taonani, ili ndi dziko losankhika, ndipo mtundu uliwonse umene udzalandira ilo udzakhala omasuka kuchoka ku msinga, ndi kuchoka ku ukapolo, ndi kuchoka ku maiko ena pansi pa thambo, ngati iwo adzatumikira Mulungu wa dzikolo, amene ali Yesu Khristu, amene waonetseredwa ndi zinthu zimene ife tazilemba.

13 Ndipo tsopano ndikupitiriza ndi zolemba zanga; pakuti taonani, zidachitika kuti Ambuye adafikitsa Yaredi ndi abale ake ngakhale ku nyanja yaikuluyo imene idagawa maikowo. Ndipo pamene iwo adafika ku nyanja, adakhoma mahema awo; ndipo adatcha dzina la malowo Moriyankume; ndipo iwo adakhala m’mahema, ndi kukhala m’mahema pa gombe lanyanjayo kwa nthawi ya dzaka zinayi.

14 Ndipo zidachitika kuti kumapeto kwa dzaka zinayi Ambuye adabwera kwa m’bale wa Yaredi, ndikuima m’mitambo ndipo adayankhula naye. Ndipo kwa nthawi ya maora atatu Ambuye adayankhulana ndi m’bale wa Yaredi, ndi kumudzudzula iye chifukwa sadakumbukire kuitanira pa dzina la Ambuye.

15 Ndipo m’bale wa Yaredi adalapa mu zoipa zimene iye adachita, ndipo adaitanira pa dzina la Ambuye m’malo mwa abale ake amene adali naye. Ndipo Ambuye adati kwa iye: Ndikukhululukira iwe ndi abale ako machimo awo; koma iweyo usadzachimwenso, pakuti udzakumbukira kuti Mzimu wanga siudzalimbana ndi munthu nthawi zonse; kotero, ngati udzachimwanso kufikira utakhwima kotheratu udzadulidwa kuchoka pamaso pa Ambuye. Ndipo awa ndi maganizo anga pa dziko limene ndidzakupatseni pa cholowa chanu; pakuti lidzakhala dziko losankhidwa kuposa maiko onse.

16 Ndipo Ambuye adati: Pitani kukagwira ntchito ndi kumanga, potsatira mtundu wa mabwato amene inu mwamanga mpaka pano. Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Yaredi adapita kukagwira ntchito, ndiponso abale ake, ndi kukamanga mabwato potsatira njira imene iwo adamanga, molingana ndi malangizo a Ambuye. Ndipo adali aang’ono, ndipo adali opepuka pamadzi, ngakhale ngati kupepuka kwa mbalame pa madzi.

17 Ndipo adamangidwa potsatira mamangidwe woti adali othina kwambiri, ngakhale kuti iwo ankatha kutunga madzi ngati m’nsengwa, ndipo pansi pake padali pothinana monga ngati nsengwa; ndipo m’mbali mwake mudali mothinana monga ngati nsengwa; ndipo mutsinde mwake mudali mosongoledwa; ndipo pamwamba pake padali pothinana ngati nsengwa; ndipo mulitali wake udali utali wa mtengo; ndipo chitseko chake, chikatsekedwa, chidali chothinana ngati nsengwa.

18 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Yaredi adafuula kwa Ambuye, nati: O Ambuye, ndachita ntchito imene inu mwandilamula ine, ndipo ndapanga mabwato molingana ndi momwe inu mwanditsogolera.

19 Ndipo taonani, O Ambuye, mkati mwake mulibe kuwala; kodi tidzapalasira kuti? Ndiponso ife tidzawonongeka, pakuti mkati mwake sitingathe kupuma, kupatula mpweya wam’menemo; kotero ife tidzawonongeka.

20 Ndipo Ambuye adati, kwa m’bale wa Yaredi; Taona, iwe udzapange bowo pamwamba, ndiponso pansi; ndipo pamene mudzasaukira mpweya, mudzatsegula bowolo ndikulandira mpweya. Ndipo ngati zitadzakhale kuti madzi alowa pa inu, taona, mudzatseka bowolo, kuti musawonongedwe ndi kusefukira kwa madzi.

21 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Yaredi adachita choncho, molingana ndi momwe Ambuye adamulamulira.

22 Ndipo iye adafuulanso kwa Ambuye nati: O Ambuye, taonani ndachita ngakhale momwe inu mudandilamulira ine; ndipo ndakonza mabwato a anthu anga, ndipo taonani mulibe kuwala mkati mwake. Taonani, O Ambuye, kodi mudzalora kuti ife tiwoloke madzi aakuluwa mu mdima?

23 Ndipo Ambuye adati kwa m’bale wa Yaredi: Kodi iwe ukufuna kuti ndichite chiyani kuti inu mukhale ndi kuwala mu mabwato anu? Pakuti taonani, simungakhale ndi mazenera, pakuti adzasweka mzidutswa; ngakhale simungatenge moto ndi inu, pakuti simudzapita ndi kuwala kwa moto.

24 Pakuti taonani, mudzakhala ngati chinsomba pakati pa nyanja; pakuti mafunde am’mapiri adzagwera pa inu. Komabe, ndidzakutulutsaninso kuchokera mkuya kwa nyanja; pakuti mphepozi zatuluka pakamwa panga, ndiponso mvula ndi madzi osefukira ndidazitumiza.

25 Ndipo taonani, ndakukonzekeretsani inu motsutsana ndi zinthu zimenezi; pakuti simungawoloke kuya kwakukulu uku kupatula ine nditakukonzekeretsani inu motsutsana ndi mafunde a panyanjapa, ndi mphepo zimene zapitapo, ndi madzi osefukira amene adzabwere. Kotero kodi mudzafuna chiyani choti ndikukonzereni inu kuti mukakhale ndi kuwala pamene inu mwamezedwa mkuya kwa nyanja?

Print