Buku la Eteri
Zolemba za Ayaredi, zotengedwa kuchokera ku mapale makumi awiri ndi anayi opezedwa ndi anthu a Limuhi m’masiku a Mfumu Mosiya.
Mutu 1
Moroni afupikitsa zolemba za Eteri—M’badwo wa Eteri ukhazikitsidwa—Chiyankhulo cha Ayaredi sichidasokonezedwe pa Nsanja ya Babele—Ambuye alonjeza kuwatsogolera ku dziko losankhika ndi kuwapanga iwo mtundu waukulu.
1 Ndipo tsopano ine, Moroni, ndikupitiliza kupereka nkhani ya anthu akalewo amene adawonongedwa ndi dzanja la Ambuye pamaso pa dziko la kumpotoli.
2 Ndipo ndikutenga nkhani yangayi kuchokera pa mapale makumi awiri ndi anayi amene adapezedwa ndi anthu a Limuhi, imene imatchetdwa Buku la Eteri.
3 Ndipo monga momwe ndikuganizira kuti gawo loyamba la zolembazi, zimene zikukamba zokhudzana ndi chilengedwe cha dziko lapansi, ndiponso cha Adamu, ndi nkhani yochokera pa nthawi imeneyo ngakhale mpaka ku nsanja yayikulu, ndi zinthu zilizonse zimene zidachitika pakati pa ana a anthu kufikira kunthawi imeneyo, zidachitika pakati pa Ayuda—
4 Kotero sindikulemba zinthu izo zimene zidachitika kuchokera ku masiku a Adamu kufikira ku nthawi imeneyo; koma izo zili pa mapalewa; ndipo aliyense amene azipeza, yemweyo adzakhala ndi mphamvu kuti athe kupeza nkhani yonse.
5 Koma taonani, ine sindikupereka nkhani yonse, koma gawo limodzi la nkhaniyi ndipereka, kuchokera ku nsanjayo mpaka kufikira iwo adawonongedwa.
6 Ndipo moteremu ine ndikupereka nkhaniyi. Iye amene adalemba zolembazi adali Eteri, ndipo adali chidzukulu cha Koriyanto.
7 Koriyanto adali mwana wa Morone.
8 Ndipo Morone adali mwana wa Etemu.
9 Ndipo Etemu adali mwana wa Aha.
10 Ndipo Aha adali mwana wa Seti.
11 Ndipo Seti adali mwana wa Shibuloni
12 Ndipo Shibuloni adali mwana wa Komi
13 Ndipo Komi adali mwana wa Koriyantumu.
14 Ndipo Koriyantumu adali mwana wa Amunigada.
15 Ndipo Amunigada adali mwana wa Aroni.
16 Ndipo Aroni adali chidzukulu cha Heti, amene adali mwana wa Heritomu.
17 Ndipo Heritomu adali mwana wa Libi.
18 Ndipo Libi adali mwana wa Kisi.
19 Ndipo Kisi adali mwana wa Koromu.
20 Ndipo Koromu adali mwana wa Levi.
21 Ndipo Levi adali mwana wa Kimu.
22 Ndipo Kimu adali mwana wa Moriyantoni.
23 Ndipo Moriyantoni adali chidzukulu cha Ripulakisi.
24 Ndipo Ripulakisi adali mwana wa Shezi.
25 Ndipo Shezi adali mwana wa Heti.
26 Ndipo Heti adali mwana wa Komi.
27 Ndipo Komi adali mwana wa Koriyantumu.
28 Ndipo Koriyantumu adali mwana wa Emeri.
29 Ndipo Emeri adali mwana wa Omeri.
30 Ndipo Omeri adali mwana wa Shule.
31 Ndipo Shule adali mwana wa Kibi.
32 Ndipo Kibi adali mwana wa Oriha, amene adali mwana wa Yaredi;
33 Yaredi amene adabwera ndi m’bale wake ndi mabanja awo, ndi anthu ena ndi mabanja awo, kuchokera ku nsanja yayikulu, pa nthawi imene Ambuye adasokoneza chiyankhulo cha anthu, ndi kulumbira mu mkwiyo wawo kuti abalalitsidwe pamaso ponse pa dziko lapansi; ndipo molingana ndi mawu a Ambuye anthuwo adabalalitsidwa.
34 Ndipo m’bale wa Yaredi pokhala munthu wojintcha ndi wamphamvu, ndi munthu okonderedwa ndi Ambuye, Yaredi, m’bale wake, adati kwa iye: Fuula kwa Ambuye, kuti iye asatisokoneze ife kuti tisathe kumva mawu athu.
35 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Yaredi adafuula kwa Ambuye, ndipo Ambuye adali ndi chifundo pa Yaredi; kotero iye sadasokoneze chiyankhulo cha Yaredi; ndipo Yaredi ndi m’bale wake sadasokonezedwe.
36 Pamenepo Yaredi adati kwa m’bale wake: Fuula kachiwiri kwa Ambuye, ndipo zingatheke kuti iye adzabwenza mkwiyo wake kwa iwo amene ali abwenzi athu, kuti asasokoneze chiyankhulo chawo.
37 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Yaredi adafuula kwa Ambuye, ndipo Ambuye adachitira chifundo pa abwenzi awo ndi mabanja awonso, kuti iwo sadasokonezeke.
38 Ndipo zidachitika kuti Yaredi adayankhulanso kwa m’bale wake, nati: Pita ndipo ukafunse kwa Ambuye ngati iwo atatithamangitse ife kuchoka mu dzikoli, ndipo ngati iwo atatithamangitse ife ku dzikoli, ufuule kwa iwo kuti tilowere kuti. Ndipo ndani angadziwe koma Ambuye adzatitengera ife ku dziko limene liri losankhika kuposa dziko lonse lapansi? Ndipo ngati zitakhale choncho, tiyeni tikhale okhulupirika kwa Ambuye, kuti tithe kulirandira ilo monga cholowa chathu.
39 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Yaredi adafuula kwa Ambuye molingana ndi chimene chidayankhulidwa ndi pakamwa pa Yaredi.
40 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adamumvera m’bale wa Yaredi, ndipo adamuchitira iye chifundo, ndipo adati kwa iye:
41 Pita ndipo kasonkhanitse pamodzi ziweto zako, zonse zazimuna ndi zazikazi, za mitundu yonse; ndiponso mbewu za mnthaka za mitundu yonse; ndi mabanja anu, ndiponso Yaredi m’bale wako ndi banja lake; ndiponso abwenzi ako ndi mabanja awo, ndi abwenzi a Yaredi ndi mabanja awo.
42 Ndipo pamene iwe wachita izi udzapite patsogolo pawo kupita ku chigwa chimene chili ku mpoto. Ndipo kumeneko ine ndidzakumana nawe, ndipo ndidzapita patsogolo pako ku dziko limene liri losankhika kuposa maiko onse a dziko lapansi.
43 Ndipo ndidzakudalitsa iwe ndi mbewu yako, ndi kudzutsira kwa ine mwa mbewu yako, ndi mbewu ya m’bale wako, ndi iwo amene adzapite nawe, mtundu waukulu. Ndipo kumeneko sikudzakhala wina oposa mtundu umene ndidzautse kwa ine wa mbewu yako, pamaso ponse pa dziko lapansi. Ndipo moteromo ndidzachitira kwa iwe chifukwa nthawi yonseyi iwe wafuulira kwa ine.