Malembo Oyera
Eteri 5


Mutu 5

Mboni zitatu ndi ntchito mwayokha, zidzayima ngati umboni wa choonadi cha Buku la Mormoni.

1 Ndipo tsopano, ine, Moroni, ndalemba mawu amene ndidalamulidwa, molingana ndi chikumbutso changa; ndipo ndakuuzani zinthu zimene ndazimata; kotero musazigwire kuti mukathe kuzimasulira; pakuti chinthu chimenecho mwaletsedwa, kupatula pang’ono ndi pang’ono chidzakhala chanzeru mwa Mulungu.

2 Ndipo taonani, mungathe kukhala ndi mwayi kuti mukathe kuonetsa mapalewo kwa iwo amene adzathandizire kubweretsa ntchito imeneyi.

3 Ndipo kwa atatu zidzawonetseredwa ndi mphamvu ya Mulungu; kotero iwo adzadziwa mwandithu kuti zinthu izi ndi zoona.

4 Ndipo pa kamwa pa mboni zitatu zinthu izi zidzakhazikitsidwa; ndipo umboni wa atatu, ndi ntchito iyi, mumene mudzaonetseredwa mphamvu ya Mulungu ndiponso mawu ake, amene Atate, ndi Mwana, ndi Mzimu Woyera achitira umboni—ndi zonsezi zidzaima ngati umboni motsutsana ndi dziko lapansi pa tsiku lotsiriza.

5 Ndipo ngati zikhale kuti iwo alapa ndi kubwera kwa Atate mu dzina la Yesu, iwo adzalandiridwa mu ufumu wa Mulungu.

6 Ndipo tsopano, ngati ndilibe ulamuliro wa zinthu izi, weruzani; pakuti mudzadziwa kuti ndili ndi ulamuliro pamene inu mudzandiona, ndipo tidzaima pamaso pa Mulungu pa tsiku lotsiriza. Ameni.

Print