Malembo Oyera
Eteri 15


Mutu 15

Mazanazana a Ayaredi aphedwa mu nkhondo—Shizi ndi Koriyantumuri asonkhanitsa anthu onse ku ndewu yophana—Mzimu wa Ambuye usiya kulimbana nawo—Dziko la Ayaredi liwonongedwa kotheratu—Koriyantumiri yekha atsalira.

1 Ndipo zidachitika kuti pamene Koriyantumuri adachira ku mabala ake, iye adayamba kukumbukira mawu amene Eteri adayankhula kwa iye.

2 Iye adaona kuti adaphedwa kale ndi lupanga pafupifupi mazanazana awiri a anthu ake, ndipo iye adayamba kumva chisoni mumtima mwake; inde, adaphedwa mazanazana awiri a anthu amphamvu, ndiponso akazi awo ndi ana awo.

3 Iye adayamba kulapa ku zoipa zake zimene iye adachita, iye adayamba kukumbukira mawu amene adayankhulidwa ndi pakamwa pa aneneri onse, ndipo iye adawaona kuti adakwaniritsidwa kufikira apa, kena kalikonse; ndipo mzimu wake udalira ndi kukana kutonthozedwa.

4 Ndipo zidachitika kuti iye adalemba kalata kwa Shizi, kufuna kuti iye awasiye anthu, ndipo iye adzapereka ufumuwo chifukwa cha miyoyo ya anthuwo.

5 Ndipo zidachitika kuti pamene Shizi adalandira kalata yake iye adalemba kalata kwa Koriyantumuri, kuti ngati iye angadzipereke yekha, kuti iye akathe kumupha ndi lupanga lake lomwe, kuti iye adzasunga miyoyo ya anthuwo.

6 Ndipo zidachitika kuti anthuwo sadalape ku mphulupulu zawo; ndipo anthu a Koriyantumuri adautsidwa ku mkwiyo motsutsana ndi anthu a Shizi, ndipo anthu a Shizi adautsidwa ku mkwiyo motsutsana ndi anthu a Koriyantumuri; kotero, anthu a Shizi adathira nkhondo kwa anthu a Koriyantumuri.

7 Ndipo pamene Koriyantumuri adaona kuti iye adali pafupi kugwa iye adathawanso pamaso pa anthu a Shizi.

8 Ndipo zidachitika kuti iye adafika ku madzi a Ripiliyankumu, amene, mutanthauzo lake, ndi kukula, kapena kuposa onse; kotero, pamene iye adafika ku madzi amenewa adakhoma mahema awo; ndipo Shizi nayenso adakhoma mahena ake pafupi ndi iwo; ndipo kotero m’mawa mwake iwo adabwera kudzamenyana.

9 Ndipo zidachitika kuti iwo adamenyana nkhondo yoopsya kwambiri, pamene Koriyantumuri adavulalanso, ndipo adakomoka ndi kutayika kwa mwazi.

10 Ndipo zidachitika kuti ankhondo a Koriyantumuri adachilimika pa ankhondo a Shizi mpakana iwo adawagonjetsa, mpakana iwo adapangitsa iwo kuthawa pamaso pawo; ndipo iwo adathawira chakumadzulo, ndipo adakhoma mahema awo pa malo amene ankatchedwa Ogati.

11 Ndipo zidachitika kuti ankhondo a Koriyantumuri adakhoma mahema awo pa phiri la Rama; ndipo lidali phiri lomwelo limene atate anga Mormoni adabisa zolemba kwa Ambuye, zimene zidali zopatulika.

12 Ndipo zidachitika kuti iwo adasonkhanitsa pamodzi anthu onse pamaso pa dzikolo, amene sadaphedwe, kupatula Eteri.

13 Ndipo zidachitika kuti Eteri adaona zochita zonse za anthuwo; ndipo iye adaona kuti anthuwo amene adali a Koriyantumuri adasonkhanitsidwa pamodzi ku ankhondo a Koriyantumuri; ndipo anthu amene adali a Shizi adasonkhanitsidwa pamodzi ku ankhondo a Shizi.

14 Kotero, iwo adali kwa nthawi ya dzaka zinayi akusonkhanitsa pamodzi anthuwo, kuti akathe kupeza onse amene adali pamaso pa dzikolo, kuti akathe kulandira mphamvu zimene zidali zothekera kuti akathe kulandira.

15 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adasonkhanitsidwa pamodzi, aliyense ku ankhondo amene akadatha, ndi akazi awo ndi ana awo—onse amuna, akazi, ndi ana kupatsidwa zida za nkhondo, kukhala ndi zishango, chapachifuwa, ndi chisoti chakumutu, ndi kuvekedwa potsatira njira yankhondo—iwo adagubira wina motsutsana ndi mzake ku nkhondo; ndipo adamenyana tsiku lonselo, ndipo sadagonjetsane.

16 Ndipo zidachitika kuti pamene udali usiku iwo adali otopa, ndipo adapumula ku misasa yawo; ndipo atatha kupumula ku misasa yawo iwo adayamba kubuula ndi maliro chifukwa cha kutaika kwa kuphedwa kwa anthu awo; ndipo kwakukulu kudali kulira kwawo, kubuula kwawo ndi maliro awo, mpakana adang’amba mpweya kwambiri.

17 Ndipo zidachitika kuti m’mawa mwake iwo adapitanso ku nkhondo, ndipo lalikulu ndi loopsya lidali tsikulo; komabe, iwo sadagonjetsane, ndipo pamene usiku udafikanso, iwo adan’gamba mpweya ndi kulira kwawo, ndi kubuula kwawo, ndi maliro awo, chifukwa cha kutaika kwa kuphedwa kwa anthu awo.

18 Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri adalemberanso kalata kwa Shizi, kufuna kuti iye asabwerenso kunkhondo, koma kuti iye adzatenge ufumuwo, ndi kusunga miyoyo ya anthuwo.

19 Koma taonani, Mzimu wa Ambuye udasiya kulimbana nawo, ndipo Satana adali ndi mphamvu zonse pa mitima ya anthuwo; pakuti iwo adaperekedwa ku kuuma kwa mitima yawo;, ndi khungu la maganizo awo mpaka kukatha kuwonongedwa; kotero iwo adapitanso kunkhondo.

20 Ndipo zidachitika kuti iwo adamenyana tsiku lonse, ndipo pamene usiku udafika iwo adagonera pa malupanga awo.

21 Ndipo m’mawa mwake iwo adamenyana ngakhale kufikira usiku udafika.

22 Ndipo pamene usiku udafika iwo adaledzera ndi mkwiyo, ngakhale monga munthu amene waledzera ndi vinyo; ndipo adagonanso pa malupanga awo.

23 Ndipo m’mawa mwake iwo adamenyananso; ndipo pamene usiku udafika iwo adali atagwa ndi lupanga kupatula adalipo makumi asanu ndi awiri mwa anthu a Koriyantumuri, ndi makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu zisanu ndi anayi mwa anthu a Shizi.

24 Ndipo zidachitika kuti adagoneranso malupanga awo usiku umenewo, ndipo m’mawa mwake adamenyananso, ndipo iwo adalimbana mwa mphamvu zawo ndi malupanga awo ndi zishango zawo, tsiku lonselo.

25 Ndipo pamene usiku udafika kudali makumi atatu ndi awiri mwa anthu a Shizi, ndi makumi awiri ndi asanu ndi awiri mwa anthu a Koriyantumuri.

26 Ndipo zidachitika kuti iwo adadya ndi kugona, ndi kukonzekera kufa m’mawa mwake. Ndipo iwo adali anthu ojintcha ndi amphamvu monga mwa mphamvu za anthu.

27 Ndipo zidachitika kuti iwo adamenyana kwa nthawi ya maora atatu, ndipo iwo adakomoka ndi kutaika kwa mwazi.

28 Ndipo zidachitika kuti pamene anthu a Koriyantumuri adalandira mphamvu zokwanira kuti iwo angathe kuyenda, iwo adali pafupi kuti athawe chifukwa cha moyo wawo; koma taonani, Shizi adadzuka ndiponso anthu ake, ndipo iye adalumbira mu mkwiyo wake kuti adzapha Koriyantumuri kapena adzafa ndi lupanga.

29 Kotero, iye adawathamangitsa iwo, ndipo m’mawa mwake iye adawapeza, ndipo adamenyananso ndi lupanga. Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adagwa ndi lupanga, kupatula Koriyantumuri ndi Shizi, taonani Shizi adakomoka chifukwa cha kutaika kwa mwazi.

30 Ndipo zidachitika kuti pamene Koriyantumuri adatsamila lupanga lake, mpaka iye adapumula pang’ono, iye adadula mutu wa Shizi.

31 Ndipo zidachitika kuti atadula mutu wa Shizi, kuti Shizi adaimika manja ake ndikugwa, ndipo ataphupha kupuma, iye adafa.

32 Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri adagwa pansi, ndipo adakhala ngati kuti alibe moyo.

33 Ndipo Ambuye adayankhula kwa Eteri, ndipo adati kwa iye: Pita. Ndipo iye adapita, ndi kuona kuti mawu a Ambuye akwaniritsidwa onse; ndipo iye adamaliza zolemba zake; (ndipo gawo la zana sindidalilembe) ndipo iye adazibisa mu njira yakuti anthu a Limuhi adazipeza.

34 Tsopano mawu omaliza amene alembedwa ndi Eteri ndi awa: Ngati Ambuye angafune kuti ndikwatulidwe, kapena ndipilire chifuniro cha Ambuye mu thupi, zilibe kanthu, ngati zili choncho kuti ndapulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu. Ameni.

Print