Malembo Oyera
Eteri 12


Mutu 12

Mneneri Eteri alimbikitsa anthu kuti akhulupilire mwa Mulungu—Moroni akumbukira zozizwitsa ndi zodabwitsa zochitika mwa chikhulupiliro—Chikhulupiliro chidathandiza m’bale wa Yaredi kuti aone Khristu—Ambuye amapereka zofooka kwa anthu kuti iwo athe kudzichepetsa—M’bale wa Yaredi adasuntha Phiri la Zerini mwa Chikhulupiliro—Chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi chikondi ndizofunikira pa chipulumutso—Moroni adaona Yesu maso ndi maso.

1 Ndipo zidachitika kuti masiku a Eteri adali m’masiku a Koriyantumuri; ndipo Koriyantumuri adali mfumu pa dziko lonselo.

2 Ndipo Eteri adali mneneri wa Ambuye; kotero Eteri adabwera mumasiku a Koriyantumuri, ndipo adayamba kunenera kwa anthuwo, pakuti iye sakadaletsedwa chifukwa cha Mzimu wa Ambuye omwe udali naye.

3 Pakuti iye adafuula kuchokera m’mawa, ngakhale mpaka kulowa kwa dzuwa, kulangiza anthuwo kuti akhulupilire mwa Mulungu m’kulapa kuopa iwo angawonongedwe, ponena kwa iwo kuti mwa chikhulupiliro zinthu zonse zakwaniritsidwa—

4 Kotero, aliyense amene amakhulupilira mwa Mulungu angathe kukhala ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha dziko labwino, inde, ngakhale malo pa dzanja la manja la Mulungu, chiyembekezo chimene chimabwera mwa chikhulupiliro, chimapanga nangula ku miyoyo ya anthu, chimene chidzawapange iwo kutsimikizika ndi kukhazikika, nthawi zonse kuchita mochuluka ntchito zabwino, akutsogoleredwa kulemekeza Mulungu.

5 Ndipo zidachitika kuti Eteri adanenera zinthu zazikulu ndi zodabwitsa kwa anthuwo, zimene iwo sadakhulupilire, chifukwa iwo sadazione.

6 Ndipo tsopano, ine, Moroni, ndiyankhulapo zinazake zokhudzana ndi zinthu izi; ndidzaonetsa ku dziko lapansi kuti chikhulupiliro ndi zinthu zimene zimayembekezeredwa koma zosaoneka; kotero, musatsutse chifukwa inu simukuziona, pakuti simulandira umboni kufikira patatha kuyesedwa kwa chikhulupiliro chanu.

7 Pakuti zidali mwa chikhulupiliro kuti Khristu adadzionetsera yekha kwa makolo athu, ataukitsidwa kwa akufa; ndipo iye sadadzionetsere yekha kwa iwo kufikira atatha kukhala ndi chikhulupiliro mwa iye; kotero, zikuyenera kuti ena adali ndi chikhulupiliro mwa iye, pakuti sadadzionetsere yekha ku dziko lapansi.

8 Koma chifukwa cha chikhulupiliro cha anthu iye wadzionetsera yekha ku dziko lapansi, ndipo walemekeza dzina la Atate, ndi kukonzera njira kuti potero ena athe kulandira za mphatso yakumwamba, kuti iwo athe kuyembekezera pa zinthu izo zimene iwo sadazione.

9 Kotero, mungathenso kukhalanso ndi chiyembekezo, ndi kukhala ogawana nawo mphatsoyo, ngati mudzafuna koma kukhala ndi chikhulupiliro.

10 Taonani zidali mwa chikhulupiliro kuti iwo akalewo adaitanidwa potsatira dongosolo loyera la Mulungu.

11 Kotero, mwa chikhulupiliro lamulo la Mose lidaperekedwa. Koma mu mphatso ya Mwana wake Mulungu adakonzera mu njira yabwino koposa; ndipo ndi mwa chifukwa cha chikhulupiliro kuti zakwaniritsidwa.

12 Pakuti ngati pali popanda chikhulupiliro pakati pa ana a anthu Mulungu sangachite chozizwitsa pakati pawo; kotero, iye sadadzionetsere yekha kufikira pambuyo pa chikhulupiriro chawo.

13 Taonani, chidali chikhulupiliro cha Alima ndi Amuleki chimene chidachititsa kuti ndende igwe pansi.

14 Taonani, chidali chikhulupiliro cha Nefi ndi Lehi chimene chidapangitsa kusintha pa Alamani, mpaka iwo adabatizidwa ndi moto ndipo ndi Mzimu Woyera.

15 Taonani, chidali chikhulupiliro cha Amoni ndi abale ake chimene chidapangitsa chozizwitsa chachikulu zedi pakati pa Alamani.

16 Inde, ndipo ngakhale iwo onse adachita zodabwitsa adazichita chifukwa cha chikhulupiliro, ngakhale iwo amene adalipo Khristu asadabadwe ndiponso iwo amene adalipo pambuyo pake.

17 Ndipo chidali chifukwa cha chikhulupiliro kuti ophunzira atatu adapeza lonjezo kuti iwo sadzalawa imfa; ndipo iwo sadalandire lonjezolo kufikira pambuyo pa chikhulupiliro chawo.

18 Ndipo palibe nthawi ina imene zodabwitsa zidachitidwa kufikira chikhulupiliro chawo; kotero iwo adayamba kaye kukhulupilira mwa Mwana wa Mulungu.

19 Ndipo adalipo ambiri amene chikhulupiliro chawo chidali champhamvu kwambiri, ngakhale Khristu asadabwere, amene sakadatha kusungidwa mu kuphimbidwa, koma zoonadi adaona ndi maso awo zinthu zimene iwo adaona ndi maso achikhulupiliro, ndipo iwo adakondwera.

20 Ndipo taonani, ife taona mu zolemba izi kuti m’modzi mwa iwo adali m’bale wa Yaredi; pakuti chachikulu chidali chikhulupiliro chake mwa Mulungu, kuti pamene Mulungu adaika chala chake sakadatha kuchibisa pamaso pa m’bale wa Yaredi, chifukwa cha mawu ake amene adayankhula kwa iye, amene mawuwo adawapeza mwa chikhulupiliro.

21 Ndipo atatha m’bale wa Yaredi kuona chala cha Ambuye, chifukwa cha lonjezo limene m’bale wa Yaredi adalandira mwa chikhulupiliro, Ambuye sakadatha kubisa kanthu pamaso pake; kotero iye adamuonetsa iye zinthu zonse, pakuti sakadatha kusungidwanso mu kuphimbidwa.

22 Ndipo izi ndi chifukwa cha chikhulupiliro kuti atate anga adalandira lonjezo kuti zinthu izi zidzabwere kwa abale awo kudzera mwa Amitundu; kotero Ambuye andilamula ine, inde ngakhale Yesu Khristu.

23 Ndipo ndidanena kwa iye: Ambuye, Amitundu adzanyozera zinthu izi, chifukwa cha kufooka kwa kalembedwe kathu; pakuti Ambuye inu mwatipanga ife amphamvu mu mawu mwa chikhulupiliro, koma inu simudatipange ife amphamvu m’kalembedwe; pakuti inu mwapanga anthu onsewa kuti akathe kuyankhula zambiri, chifukwa cha Mzimu Woyera umene inu mwawapatsa iwo.

24 Ndipo inu mwatipanga ife kuti tikathe kulemba zochepa, chifukwa cha kupepera kwa manja athu. Taonani, inu simudatipange ife a mphamvu m’malembedwe monga m’bale wa Yaredi, pakuti inu mudamupanga iye kuti zinthu zimene iye adalemba zidali zamphamvu ngakhale monga inu mulili, kwa kumugonjetsa munthu kuti aziwerenge.

25 Inu mwapangitsa mawu athu kukhala amphamvu ndi aakulu, ngakhale kuti ife sitingathe kuwalemba; kotero, pamene ife tikulemba timaona kufooka kwathu, ndi kuphonyetsa chifukwa cha kaikidwe ka mawu athu; ndipo ndikuopa kuti Amitundu adzanyozera pa mawu athu.

26 Ndipo pamene ine ndidanena izi, Ambuye adayankhula kwa ine, nati: Opusa amanyoza, koma iwo adzalira; ndipo chisomo changa ndichokwanira kwa ofatsa, kuti iwo sadzatengera mwayi chifukwa cha kufooka kwanu;

27 Ndipo ngati anthu abwera kwa ine ndidzawaonetsa kwa iwo zofooka zawo. Ndimapereka kwa anthu zofooka kuti iwo akathe kudzichepetsa; ndipo chisomo changa ndichokwanira kwa anthu onse amene amadzichepetsa okha pamaso panga; pakuti ngati iwo adzichepetsa okha pamaso panga, ndi kukhala ndi chikhulupiliro mwa ine, kenako ndidzapanga zinthu zofooka kukhala zamphamvu kwa iwo.

28 Taonani, ndidzaonetsa kwa Amitundu zofooka zawo, ndipo ndidzawaonetsa iwo kuti chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi chikondi zimabweretsa kwa ine—kasupe wa chilungamo chonse.

29 Ndipo ine, Moroni, nditamva mawu awa, ndidatonthozedwa, ndipo ndidati: O Ambuye, chilungamo chanu chichitidwe, pakuti ndikudziwa kuti inu mumagwira ntchito kwa ana a anthu molingana ndi chikhulupiliro chawo;

30 Pakuti m’bale wa Yaredi adati kwa phiri la Zerini, Choka—ndipo lidachoka. Ndipo ngati iye akadapanda chikhulupiliro silikadachoka; kotero inu mumagwira ntchito pambuyo pa anthu atakhala ndi chikhulupiliro.

31 Pakuti motero inu mudadzionetsera nokha kwa ophunzira; pakuti atatha iwo kukhala ndi chikhulupiliro, ndi kuyankhula mu dzina lanu, inu mudadzionetsa nokha kwa iwo mu mphamvu zazikulu.

32 Ndiponso ndikukumbukira kuti inu mudanena kuti mwakonzera nyumba ya munthu, inde, ngakhale pakati pa nyumba za Atate anu, mumene munthu akathe kukhalamo ndi chiyembekezo chopambana kwambiri; kotero munthu akuyenera kukhala ndi chiyembekezo, kapena iye sangathe kulandira cholowa mu malo amene inu mwawakonza.

33 Ndiponso, ndikukumbukira kuti inu mwanena kuti inu mwakonda dziko lapansi, ngakhale pakuika pansi moyo wanu chifukwa cha dziko lapansi, kuti inu mukathe kuutenganso kuti mukakonze malo a ana a anthu.

34 Ndipo tsopano ndikudziwa kuti kukonda uku kumene inu mwakhala nako pa ana a anthu ndi chikondi; kotero, pokhapokha anthu adzakhale ndi chikondi iwo sangathe kulandira malo amene inu mwawakonzera mu nyumba ya Atate anu.

35 Kotero, ndikudziwa mwa chinthu ichi chimene inu mwanenachi, kuti ngati Amitundu sangakhale ndi chikondi chifukwa cha zofooka zathu, kuti inu mudzawayesa iwo, ndi kuchotsa luso lawo, inde, ngakhale limene iwo adalandira, ndi kuwapatsa iwo amene adzakhale nazo zochuluka.

36 Ndipo zidachitika kuti ndidapemphera kwa Ambuye kuti adzapereke kwa Amitundu chisomo, kuti akathe kukhala ndi chikondi.

37 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adati kwa ine: Ngati iwo sakhala ndi chikondi zilibe kanthu kwa iwe, iwe wakhala okhulupirika; kotero, zovala zako zayeretsedwa. Ndipo chifukwa iwe waona zofooka zako udzapangidwa kukhala wamphamvu, ngakhale kudzakhala pansi mu malo amene ine ndawakonza mu nyumba ya Atate anga.

38 Ndipo tsopano, Ine Moroni, nditsanzika kwa Amitundu, inde, ndiponso kwa abale anga amene ndimawakonda, kufikira tidzaonane pamaso pa mpando wa chiweruzo wa Khristu, kumene anthu onse adzadziwe kuti zovala zanga zilibe banga ndi mwazi wanu.

39 Ndipo pamenepo mudzadziwa kuti ine ndamuona Yesu, ndipo kuti iye adayankhula ndi ine maso ndi maso, ndipo iye adandiuza ine mu kudzichepetsa poyera, ngakhale monga munthu awuzira wina mu chiyankhulo changa, zokhudzana ndi zinthu izi.

40 Ndipo zochepa zokha ine ndazilemba, chifukwa cha kufooka kwanga m’malembedwe.

41 Ndipo tsopano, ndikukulangizani inu kuti mufunefune Yesu ameneyu amene aneneri ndi atumwi adalemba, kuti chisomo cha Mulungu Atate, ndiponso Ambuye Yesu Khristu, ndi Mzimu Woyera, umene umachitira umboni za iwo, ukhale ndi inu kunthawi zosatha. Ameni.

Print