Malembo Oyera
Eteri 11


Mutu 11

Nkhondo, kusagwirizana, ndi kuipa kutsogolera moyo wa Ayaredi—Aneneri alosera chiwonongeko chotheratu cha Ayaredi pokhapokha iwo atalapa—Anthu akana mawu a aneneri.

1 Ndipo kudadzanso mu masiku a Komi aneneri ochuluka, ndipo adanenera za chiwonongeko cha anthu amphamvuwo pokhapokha iwo atalapa, ndi kubwelera kwa Ambuye, ndi kusiya zokupha ndi zoipa zawo.

2 Ndipo zidachitika kuti aneneriwo adakanidwa ndi anthuwo, ndipo iwo adathawira kwa Komi pa chitetezo, pakuti anthuwo adafuna kuti awawononge iwo.

3 Ndipo iwo adanenera kwa Komi zinthu zambiri; ndipo iye adadalitsidwa mu masiku otsalira ake onse.

4 Ndipo iye adakhala mpaka ukalamba wabwino, ndipo adabereka Shibulomu; ndipo Shibulomu adalamulira m’malo mwake. Ndipo m’bale wa Shibulomu adagalukira motsutsana naye, ndipo kudayamba kukhala nkhondo yaikulu mu dziko lonselo.

5 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Shibulomu adachititsa kuti aneneri onse amene adanenera za chiwonongeko cha anthu aphedwe.

6 Ndipo kudali tsoka lalikulu mu dziko lonselo, pakuti iwo adachitira umboni kuti thembelero lalikulu lidzabwera pa dzikolo, ndiponso pa anthuwo, ndipo kuti kudzakhala chiwonongeko chachikulu pakati pawo, chimene sichidakhalapo pamaso pa dziko lapansi, ndipo mafupa awo adzakhala ngati milu ya dothi pamaso pa dziko lapansi pokhapokha iwo atalapa za kuipa kwawo.

7 Ndipo iwo sadamvere kwa mawu a Ambuye, chifukwa cha magulu awo ankhanza; kotero, kudayamba kukhala nkhondo ndi mikangano mu dziko lonselo, ndiponso zilala zambiri ndi miliri, mpakana kuti kudali chiwonongeko chachikulu, chimene sichidadziwikepo pamaso pa dziko lapansi; ndipo zonsezi zidadza mu masiku a Shibulomu.

8 Ndipo anthu adayamba kulapa ku zoipa zawo; ndipo pamene iwo adatero Ambuye adawachitira chifundo.

9 Ndipo zidachitika kuti Shibulomu adaphedwa, ndipo Seti adatengedwa ukapolo, ndipo adakhala mu ukapolo masiku ake onse.

10 Ndipo zidachitika kuti Aha, mwana wake, adatenga ufumuwo; ndipo adalamulira pa anthuwo masiku ake onse. Ndipo adachita mitundu yonse ya zoipa mu masiku ake, zimene zidapangitsa kukhetsa kwa mwazi kwakukulu; ndipo ochepa adali masiku ake.

11 Ndipo Etemu, pokhala mdzukulu wa Aha, adatenga ufumuwo; ndipo iyenso adachita chimene chidali choipa mu masiku ake.

12 Ndipo zidachitika kuti mu masiku a Etemu kudadza aneneri ambiri, ndipo adaneneranso kwa anthuwo; inde, iwo adanenera kuti Ambuye adzawawononga iwo kuchoka pamaso pa dziko lapansi pokhapokha iwo atalapa zoipa zawo.

13 Ndipo zidachitika kuti anthuwo adalimbitsa mitima yawo, ndipo sadamvetsere kwa mawu awo; ndipo aneneriwo adalira ndi kuchoka pakati pa anthuwo.

14 Ndipo zidachitika kuti Etemu ankagamula ziweruzo moipa masiku ake onse; ndipo adabereka Morone. Ndipo zidachitika kuti Morone adalamulira m’malo mwake; ndipo Morone adachita chimene chidali choipa pamaso pa Ambuye.

15 Ndipo zidachitika kuti kudabuka kupanduka pakati pa anthuwo, chifukwa cha magulu azinsinsi amene adamangidwa kuti apeze mphamvu ndi phindu; ndipo kudabuka munthu wamphamvu pakati pawo mu zoipa, ndipo adathira nkhondo kwa Morone, mumene iye adagwetsa theka la ufumuwo; ndipo iye adatenga theka la ufumuwo kwa dzaka zambiri.

16 Ndipo zidachitika kuti Morone adamugwetsa iye, ndipo adatenganso ufumuwo.

17 Ndipo zidachitika kuti kudabweranso munthu wina wa mphamvu; ndipo adali chidzukulu cha m’bale wa Yaredi.

18 Ndipo zidachitika kuti iye adagwetsa Morone ndi kutenga ufumuwo; kotero, Morone adakhala mu ukapolo mu masiku ake onse otsalira, ndipo adabereka Koriyanto.

19 Ndipo zidachitika kuti Koriyanto adakhala mu ukapolo masiku ake onse.

20 Ndipo mu masiku a Koriyanto kudadzanso aneneri ambiri, ndipo adanenera za zinthu zazikulu ndi zodabwitsa, ndipo adafuula kulapa pa anthuwo, ndipo pokhapokha iwo atalapa Ambuye Mulungu adzachita chiweruzo motsutsana nawo m’kuwonongeka kwawo kotheratu.

21 Ndipo kuti Ambuye Mulungu adzatumiza kapena kubweretsa anthu ena kuti atenge dzikolo, mwa mphamvu yawo, potsatira njira imene iwo adabweretsera makolo awo.

22 Ndipo iwo adakana mawu onse a aneneriwo, chifukwa cha magulu awo azinsinsi ndi zoipa zonyansa.

23 Ndipo zidachitika kuti Koriyanto adabereka Eteri, ndipo adamwalira atakhala mu ukapolo masiku ake onse.

Print