Malembo Oyera
Eteri 6


Mutu 6

Ngalawa za Ayaredi zidakankhidwa ndi mphepo kupita ku dziko la lonjezano—Anthu atamanda Ambuye chifukwa cha ubwino Wake—Oriha asankhidwa mfumu pa iwo—Yaredi ndi m’bale wake amwalira.

1 Ndipo tsopano, ine, Moroni, ndikupitiriza kupereka mbiri ya Yaredi ndi m’bale wake.

2 Pakuti zidachitika kuti potsatira Ambuye kukonza miyala imene m’bale wa Yaredi adainyamula ku phiri, m’bale wa Yaredi adatsika m’phirimo, ndipo adaika miyalayo mu mabwato amene adakonzedwa, umodzi kumbuyo kwa iliyonse; ndipo taonani, idapereka kuwala mu mabwatowo.

3 Ndipo motero Ambuye adachititsa miyalayo kuwala mu mdima, kuti ipereke kuwala kwa abambo, amayi ndi ana, kuti iwo asawoloke madzi aakuluwo mu mdima.

4 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adakonza chakudya chamitundumitundu, kuti potero adye pa madzipo, ndiponso chakudya cha nkhosa ndi ziweto zawo, ndi zilombo zilizonse kapena zinyama kapena mbalame zimene angazinyamule—ndipo zidachitika kuti pamene iwo adachita zinthu zonsezi adakwera mu mabwato awo kapena ngalawa, ndi kuyamba ulendo wapanyanja, kudzipereka okha kwa Ambuye Mulungu wawo.

5 Ndipo zidachitika kuti Ambuye Mulungu adachititsa kuti kukhale mphepo yaukali yowomba pa nkhope ya madziwo, kulunjika ku dziko la lonjezano; ndipo motero iwo adakankhidwa pa mafunde a nyanja ndi pa mphepo.

6 Ndipo zidachitika kuti padali nthawi zambiri pamene iwo adamizidwa mkuya kwa nyanja, chifukwa cha mapiri a mafunde amene adawawomba iwo, ndiponso anamondwe aakulu ndi owopsya amene adachitika ndi ukali wa mphepo.

7 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adamizidwa mkuya padalibe madzi amene akadawavulaza iwo, mabwato awo pokhala othinana ngati nsengwa, ndiponso adali othinana monga ngati chombo cha Nowa; kotero pamene iwo adazunguliliridwa ndi madzi ambiri adafuula kwa Ambuye, ndipo iye adawatulutsanso pamwamba pa madziwo.

8 Ndipo zidachitika kuti mphepo siidasiye kuwomba kulunjika ku dziko la lonjezano pamene iwo adali pamadziwo; ndipo motero iwo adakankhidwa ndi mphepoyo.

9 Ndipo iwo adayimba matamando kwa Ambuye; inde, m’bale wa Yaredi adayimba matamando kwa Ambuye ndipo iye adathokoza ndi kutamanda Ambuye tsiku lonse; ndipo pamene usiku udafika, iwo sadasiye kutamanda Ambuye.

10 Ndipo motero iwo adakankhidwa kutsogolo; ndipo palibe chilombo chapanyanja chikadawathyola iwo, ngakhale chinsomba chimene chikadawavulaza iwo; ndipo iwo adakhala ndi kuwala kosalekeza, kaya padali pamwamba pa madzi kapena pansi pa madziwo.

11 Ndipo motero iwo adakankhidwa kutsogolo, masiku mazana atatu ndi makumi anayi ndi mphambu zinayi pa nyanjapo.

12 Ndipo iwo adafika pa gombe la dziko la lonjezano. Ndipo pamene iwo adaponda mapazi awo pa gombe la dziko la lonjezanolo adadzigwaditsa okha pankhope ya dzikolo, ndi kudzichepetsa okha pamaso pa Ambuye, ndipo adakhetsa misozi ya chisangalalo pamaso pa Ambuye, chifukwa cha zifundo zake zochuluka pa iwo.

13 Ndipo zidachitika kuti iwo adapita pa dzikolo, ndipo adayamba kulima m’nthaka.

14 Ndipo Yaredi adali ndi ana aamuna anayi; ndipo ankatchedwa Yakomu, ndi Giliga, ndi Maha, ndi Oriha.

15 Ndipo m’bale wa Yaredi adabereka ana aamuna ndi aakazi.

16 Ndipo anzake a Yaredi ndi abale ake adali mu chiwerengero pafupifupi miyoyo makumi awiri ndi iwiri; ndipo iwonso adabereka ana aamuna ndi aakazi asadafike ku dziko la lonjezanolo; ndipo kotero adayamba kukhala ambiri.

17 Ndipo adaphunzitsidwa kuyenda modzichepetsa pamaso pa Ambuye; ndipo adaphunzitsidwanso kuchokera kumwamba.

18 Ndipo zidachitika kuti iwo adayamba kumwazikana pa nkhope ya dzikolo, ndi kuyamba kuchulukana ndi kulima nthaka; ndipo adakula mu mphamvu mudzikolo.

19 Ndipo m’bale wa Yaredi adayamba kukalamba, ndipo adaona kuti posachedwa akuyenera kutsikira kumanda; kotero iye adati kwa Yaredi: Tiye tisonkhanitse pamodzi anthu athu kuti tiwawerenge, kuti tithe kudziwa kwa iwo zomwe angakhumbe kwa ife tisadapite ku manda athu.

20 Ndipo mwachilinganizo anthuwo adasonkhanitsidwa pamodzi. Tsopano chiwerengero cha ana aamuna ndi aakazi a m’bale wa Yaredi chidali makumi awiri ndi anthu awiri; ndipo chiwerengero cha ana aamuna ndi aakazi a Yaredi chidali khumi ndi awiri, iye pokhala ndi ana aamuna anayi.

21 Ndipo zidachitika kuti adawerengera anthu awo; ndipo pakutha pakuwawerengako, iwo adakhumba kwa iwo zinthu zimene iwo akufuna kuti achite iwo asadapite kumanda awo.

22 Ndipo zidachitika kuti anthuwo adakhumba kwa iwo kuti adzodze m’modzi mwa ana awo aamuna kuti akhale mfumu pa iwo.

23 Ndipo tsopano taonani, ichi chidali chowawa kwa iwo. Ndipo m’bale wa Yaredi adati kwa iwo: Ndithudi chinthu ichi chimatsogolera ku ukapolo.

24 Koma Yaredi adati kwa m’bale wake: Aloleni iwo kuti athe kukhala ndi mfumu. Ndipo kotero iye adati kwa iwo: Sankhani inu kuchokera pakati pa ana athu mfumu, ngakhale amene mufuna.

25 Ndipo zidachitika kuti iwo adasankha mwana oyamba wa m’bale wa Yaredi; ndipo dzina lake lidali Pagagi. Ndipo zidachitika kuti iye adakana ndipo sadafune kuti akhale mfumu yawo. Ndipo anthuwo adafuna kuti atate ake amukakamize, koma atate ake sadafune; ndipo adawalamula iwo kuti asamakakamize munthu aliyense kuti akhale mfumu yawo.

26 Ndipo zidachitika kuti iwo adasankha azibale ake onse a Pagagi, ndipo iwo sadafune.

27 Ndipo zidachitika kuti ana aamuna a Yaredi sadafunenso, ngakhale onse kupatula m’modzi; ndipo Oriha adadzodzedwa kukhala mfumu pa iwo.

28 Ndipo iye adayamba kulamulira, ndipo anthu adayamba kuchita bwino; ndipo iwo adakhala olemera kwambiri.

29 Ndipo zidachitika kuti Yaredi adamwalira, ndiponso m’bale wake.

30 Ndipo zidachitika kuti Oriha adayenda modzichepetsa pamaso pa Ambuye, ndipo adakumbukira zinthu zazikulu zimene ambuye adazichita kwa atate ake, ndiponso adaphunzitsa anthu ake zinthu zazikulu zimene Ambuye adazichita kwa makolo awo.

Print