Malembo Oyera
Eteri 7


Mutu 7

Oriha alamulira mwa chilungamo—Mkatikati mwa kulanda ndi mkangano, maufumu odana a Shule ndi Koho akhazikitsidwa—Aneneri adzudzula kuipa ndi kupembedza mafano kwa anthu, amene kenako alapa.

1 Ndipo zidachitika kuti Oriha adapereka zigamulo ziweruzo pa dzikolo mwa chilungamo m’masiku ake onse, amene masiku ake adali ochuluka kwambiri.

2 Ndipo iye adabereka ana aamuna ndi aakazi; inde, adabereka makumi atatu ndi m’modzi, mwa iwo mudali ana aamuna makumi awiri ndi atatu.

3 Ndipo zidachitika kuti iye adaberekanso Kibi mu ukalamba wake. Ndipo zidachitika kuti Kibi adalamulira m’malo mwake; ndipo Kibi adabereka Koriho.

4 Ndipo pamene Koriho adali ndi dzaka makumi atatu ndi ziwiri adagalukira motsutsana ndi atate ake, ndipo adapita ndi kukakhala ku dziko la Neho; ndipo adabereka ana aamuna ndi aakazi, ndipo adakhala anthu okongola kwambiri; kotero Koriho adakopa anthu ambiri kumtsatira iye.

5 Ndipo pamene iye adasonkhanitsa pamodzi ankhondo adabwera ku dziko la Morone kumene mfumu imakhala, ndi kuitenga ukapolo, zimene zidakwaniritsa zonena za m’bale wa Yaredi kuti adzabweretsedwa ku ukapolo.

6 Tsopano dziko la Morone, kumene mfumu inkakhala, lidali pafupi ndi dziko limene linkatchedwa Bwinja ndi Anefi.

7 Ndipo zidachitika kuti Kibi adakhala mu ukapolo, ndi anthu ake pansi pa Koriho mwana wake, kufikira iye adakalamba kwambiri; komabe Kibi adabereka Shule mu ukalamba wake, pamene iye adakali mu ukapolo.

8 Ndipo zidachitika kuti Shule adakwiya ndi m’bale wake; ndipo Shule adakula mphamvu, ndi kukhala wadzitho monga mwa nyonga za munthu; ndipo iye adalinso waluntha m’maweruzidwe.

9 Kotero, iye adafika ku phiri la Eferemu, ndipo adasungunula kuchokera m’phirilo, ndi kupangira malupanga kuchokera ku chitsulo kwa iwo amene adakopeka ndi iye; ndipo atatha kuwapatsa malupanga adabwelera ku mzinda wa Neho, ndipo adathira nkhondo kwa m’bale wake Koriho, mwa njira imeneyi iye adalanda ufumuwo ndi kuubwenzeretsa kwa Atate ake Kibi.

10 Ndipo tsopano chifukwa cha chinthu chimene Shule adachita, atate ake adamupatsa iye ufumuwo; kotero iye adayamba kulamulira m’malo mwa atate ake.

11 Ndipo zidachitika kuti iye ankapereka chigamulo mwa chilungamo; ndipo adafalitsa ufumuwo pamaso ponse pa dzikolo, pakuti anthu adakhala ochulukana kwambiri.

12 Ndipo zidachitika kuti Shule adaberekanso ana aamuna ndi aakazi ambiri.

13 Ndipo Koriho adalapa pa zoipa zambiri zimene adachita; kotero Shule adamupatsa mphamvu mu ufumu wake.

14 Ndipo zidachitika kuti Koriho adali ndi ana aamuna ndi aakazi ambiri. Ndipo pakati pa ana aamuna a Koriho padali m’modzi amene dzina lake lidali Nowa.

15 Ndipo zidachitika kuti Nowa adagalukira motsutsana ndi Shule, mfumu, ndiponso atate ake Koriho, ndipo adakopa Koho m’bale wake, ndiponso abale ake onse ndi ambiri mwa anthuwo.

16 Ndipo iye adathira nkhondo kwa Shule, mfumu, m’mene iye adalanda dziko la cholowa chawo choyamba; ndipo iye adakhala mfumu ku gawo limenelo la dzikolo.

17 Ndipo zidachitika kuti iye adathiranso nkhondo kachiwiri kwa Shule, mfumu; ndipo adatenga Shule, mfumu, ndi kuitenga ukapolo ku Morone.

18 Ndipo zidachitika kuti pamene adali pafupi kuti amuphe, ana aamuna a Shule adazembera nyumba ya Nowa mu usiku ndi kumupha, ndipo adaphwanya chitseko cha ndende ndi kutulutsa atate awo, ndi kuwaika pa mpando wawo wachifumu mu ufumu wawo.

19 Kotero, mwana wa Nowa adamanga ufumu wake m’malo mwake; komabe iwo sadapeze mphamvu zina pa Shule mfumuyo, ndipo anthu amene adali pansi pa ulamuliro wa Shule mfumuyo adachita bwino kwambiri ndipo adakulirakulira kwambiri.

20 Ndipo dzikolo lidagawikana; ndipo padali maufumu awiri, ufumu wa Shule, ndi ufumu wa Koho, mwana wa Nowa.

21 Ndipo Koho, mwana wa Nowa, adachititsa kuti anthu ake apite kunkhondo motsutsana ndi Shule, mumene Shule adawagonjetsa ndi kupha Koho.

22 Ndipo tsopano Koho adali ndi mwana amene ankatchedwa Nimurodi; ndipo Nimurodi adapereka ufumu wa Koho kwa Shule, ndipo iye adapeza kukonderedwa m’maso mwa Shule; kotero Shule adapereka zokondera zambiri kwa iye, ndipo iye ankachita mu ufumu wa Shule molingana ndi zokhumba zake.

23 Ndiponso mu ulamuliro wa Shule kudabwera aneneri pakati pa anthu, amene adatumidwa kuchokera kwa Ambuye, kunenera kuti kuipa ndi kupembedza mafano kwa anthu kunkabweretsa thembelero pa dzikolo, ndipo akuyenera kuwonongedwa ngati iwo salapa.

24 Ndipo zidachitika kuti anthu adachitira mwano aneneriwo, ndipo adawanyoza iwo. Ndipo zidachitika kuti mfumu Shule idapereka chigamulo motsutsana ndi onse amene adachitira mwano aneneri.

25 Ndipo iye adaika lamulo kuzungulira dziko lonselo, limene lidapereka mphamvu kwa aneneri kuti adzipita kulikonse akufuna; ndipo pa chifukwa ichi anthu adabweretsedwa m’kulapa.

26 Ndipo chifukwa anthuwo adalapa pa mphulupulu zawo ndi kupembedza mafano Ambuye adawachitira chifundo, ndipo adayamba kuchitanso bwino mudzikolo. Ndipo zidachitika kuti Shule adabereka ana aamuna ndi aakazi mu ukalamba wake.

27 Ndipo kudalibenso nkhondo mu masiku a Shule; ndipo iye adakumbukira zinthu zazikulu zimene Ambuye adawachitira makolo ake mukuwabweretsa iwo kuwoloka kuya kwakukulu kulowa m’dziko lalonjezano; kotero iye adapereka chigamulo mwa chilungamo m’masiku ake onse.

Print