Malembo Oyera
Eteri 10


Mutu 10

Mfumu imodzi ilowa m’malo mwa ina—Mafumu ena ndi olungama; ena ndi oipa—Pamene chilungamo chipitilira, anthu amadalitsidwa ndi kuchititsidwa bwino ndi Ambuye.

1 Ndipo zidachitika kuti Shezi, amene adali mdzukulu wa Heti—pakuti Heti adafa ndi njala, ndi onse abanja lake kupatula Shezi—kotero, Shezi adayamba kulimbikitsanso anthu okhumudwa.

2 Ndipo zidachitika kuti Shezi adakumbukira chiwonongeko cha makolo ake, ndipo adamanga ufumu wolungama; pakuti iye adakumbukira zimene Ambuye adachita pobweretsa Yaredi ndi abale ake kuwombokera kwakuya; ndipo adayenda mu njira za Ambuye; ndipo adabereka ana aamuna ndi aakazi.

3 Ndipo mwana wake wamkulu wamwamuna, amene dzina lake lidali Shezi, adawukira motsutsana naye; komabe, Shezi, adakanthidwa ndi dzanja la chigawenga chifukwa cha chuma chake chambiri, zimene zidabweretsa mtendere kachiwiri kwa atate ake.

4 Ndipo zidachitika kuti atate ake adamanga mizinda yambiri pamaso pa dzikolo, ndipo anthu adayambanso kufalikira pamaso pa dziko lonselo. Ndipo Shezi adakhala kufika pokalamba kwambiri; ndipo adabereka Ripulakisi. Ndipo iye adamwalira, ndipo Ripulakisi adalamulira m’malo mwake.

5 Ndipo zidachitika kuti Ripulakisi sadachite chimene chidali choyenera pamaso pa Ambuye, pakuti iye adali ndi akazi ambiri ndi adzakazi, ndipo adaika pa mapewa a anthu zimene zidali zowawa kuzinyamula; iye ankakhometsa misonkho ndi misonkho yolemetsa; ndipo ndi misonkhoyo iye adamanga nyumba zazikulu.

6 Ndipo iye adadzipangira yekha mpando wachifumu wokongola kwambiri; ndipo adamanga ndende zambiri, ndipo aliyense amene sankafuna kupereka msonkho iye ankawaponya mu ndendemo; ndipo aliyense amene sakadatha kupereka msonkho ankawaponya mundendemo; ndipo iye adapangitsa kuti iwo adzigwira ntchito mosalekeza pakudzithandiza; ndipo aliyense amene ankakana kugwira ntchitoyo iye adapangitsa kuti aphedwe.

7 Kotero iye adapeza ntchito zake zabwino zonse, inde, ngakhale golide wake wabwino iye adapangitsa kuti ayengedwe mu ndende; ndipo ntchito zamitundu yonse iye adapangitsa kuti zidzichitidwa mundendemo. Ndipo zidachitika kuti iye adasautsa anthuwo ndi zigololo zake ndi zonyansa.

8 Ndipo pamene iye adalamulira kwa nthawi ya dzaka makumi anayi ndi ziwiri anthu adamuukira ndikumupandukira motsutsana naye; ndipo mudayambiranso kukhala nkhondo mu dzikolo, kotero kuti Ripulakisi adaphedwa, ndipo adzukulu ake adathamangitsidwa kuchoka mu dzikolo.

9 Ndipo zidachitika kuti patatha nthawi ya dzaka zambiri, Moriyantoni, (iye pokhala chidzukulu cha Ripulakisi) adasonkhanitsa pamodzi ankhondo othamangitsidwa, ndipo adapita ndi kukathira nkhondo kwa anthuwo; ndipo adapeza mphamvu pa mizinda yambiri; ndipo nkhondoyo idakula kwambiri, ndipo idakhalapo kwa nthawi ya dzaka zambiri; ndipo iye adapeza mphamvu pa dziko lonselo, ndi kudzikhazikitsa yekha mfumu pa dziko lonselo.

10 Ndipo pambuyo pakudzikhazikitsa yekha mfumu adapeputsa zolemetsa za anthu, potero iye adapeza kukonderedwa m’maso mwa anthuwo, ndipo adamudzodza iye kuti akhale mfumu yawo.

11 Ndipo iye adachita chilungamo kwa anthuwo, koma osati kwa iye mwini chifukwa cha zigololo zake zambiri; kotero iye adadulidwa kuchoka pamaso pa Ambuye.

12 Ndipo zidachitika kuti Moriyantoni adamanga mizinda yambiri, ndipo anthu adakhala olemera kwambiri pansi pa ulamuliro wake, zonse mu zomangamanga, mu golide ndi siliva, ndi mu kulima mbewu, ndi ziweto, ndi zinyama, ndi zinthu zotero zimene zidabwenzeretsedwa kwa iwo.

13 Ndipo Moriyantoni adakhala kufika pokalamba kwambiri, ndipo kenako adabereka mwana Kimu; ndipo Kimu adalamulira m’malo mwa atate ake; ndipo iye adalamulira dzaka zisanu ndi zitatu, ndipo atate ake adamwalira. Ndipo zidachitika kuti Kimu sadalamulire molungama, kotero iye sadakonderedwe ndi Ambuye.

14 Ndipo m’bale wake adaukira mu kupanduka motsutsana naye, mumene iye adamubweretsa mu ukapolo; ndipo iye adakhalabe mu ukapolo masiku ake onse; ndipo adabereka ana aamuna ndi aakazi mu ukapolo, ndipo mu ukalamba wake iye adabereka Levi; ndipo adamwalira.

15 Ndipo zidachitika kuti Levi adatumikira mu ukapolo pambuyo pa imfa ya atate ake, kwa nthawi ya dzaka makumi anayi ndi ziwiri. Ndipo iye adapanga nkhondo motsutsana ndi mfumu ya dzikolo, mumene iye adapeza kwa iye yekha ufumuwo.

16 Ndipo atatha kutenga kwa iye yekha ufumuwo iye adachita chimene chidali choyenera pamaso pa Ambuye; ndipo anthu adachita bwino mu dzikolo; ndipo iye adakhala mpaka kukalamba bwino, ndipo adabereka ana aamuna ndi aakazi; ndiponso iye adabereka Koromu, amene iye adamudzodza mfumu m’malo mwake.

17 Ndipo zidachitika kuti Koromu adachita chimene chidali chabwino pamaso pa Ambuye masiku ake onse; ndipo adabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri; ndipo iye atatha kuona masiku ochuluka adamwalira, ngakhale ngati aliyense pa dziko lapansi; ndipo Kisi adalamulira m’malo mwake.

18 Ndipo zidachitika kuti Kisi adamwaliranso, ndipo Libi adalamulira m’malo mwake.

19 Ndipo zidachitika kuti Libi adachitanso chimene chidali chabwino pamaso pa Ambuye. Ndipo mumasiku a Libi njoka za chiphe zidawonongedwa. Kotero iwo adapita ku dziko la kum’mwera, kukasaka chakudya cha anthu a dzikolo, pakuti dzikolo lidali lodzadza ndi nyama zakutchire. Ndipo Libi nayenso adakhala mlenje wamkulu.

20 Ndipo adamanga mzinda waukulu palowe popapatiza pa dzikolo, pafupi ndi pamene nyanja idagawikana ndi dzikolo.

21 Ndipo iwo adasungira dziko la kum’mweralo kuti likhale chipululu, kuti adzipezamo nyama. Ndipo dziko la kumpoto lonse lidadzadzidwa ndi anthu.

22 Ndipo iwo adali akatswiri kwambiri, ndipo ankagula ndi kugulitsa katundu wina ndi mzake, kuti iwo apeze phindu.

23 Ndipo ankagwira ntchito ya mitundu yonse ya zitsulo, ndipo iwo adapanga golide, ndi siliva, ndi zitsulo, mkuwa, ndi mitundu yonse ya zitsulo; ndipo ankazikumba kuchokera pa nthaka; kotero, adaunjika milu ya dothi kuti apeze zitsulo, golide, ndi siliva, ndi mkuwa ndi kopa. Ndipo iwo adagwira ntchito zamtundu uliwonse zabwino.

24 Ndipo iwo adali ndi silika, ndi nsalu zopota bwino; ndipo ankapanga ntchito ya mitundu yonse ya zovala, kuti adziveke okha kumaliseche awo.

25 Ndipo ankapanga zipangizo zamitundu yonse zolimira nthaka, zonse zolimira ndi zobzalira, zokololela ndi kusosera ndi kupunthira.

26 Ndipo ankapanga zipangizo zamtundu uliwonse zimene ankagwiritsa ntchito nyama zawo.

27 Ndipo iwo ankapanga mitundu yonse ya zida zankhondo. Ndipo iwo ankagwira ntchito zamtundu uliwonse mwaluso lodabwitsa kwambiri.

28 Ndipo sikudakatha konse kukhala anthu odalitsika kuposa momwe iwo adaliri, ndipo ochititsidwa bwino kwambiri ndi dzanja la Ambuye. Ndipo iwo adali mu dziko losankhika kuposa maiko onse, pakuti Ambuye adayankhula ichi.

29 Ndipo zidachitika kuti Libi adakhala dzaka zambiri, ndipo adabereka ana aamuna ndi aakazi; ndiponso adabereka Heritomu.

30 Ndipo zidachitika kuti Heritomu adalamulira m’malo mwa atate ake. Ndipo pamene Heritomu adalamulira kwa dzaka makumi awiri ndi zinayi, taonani, ufumuwo udalandidwa kwa iye. Ndipo iye adagwira kwa dzaka zambiri mu ukapolo, inde, ngakhale masiku ake onse otsalira.

31 Ndipo iye adabereka Heti, ndipo Heti adakhala mu ukapolo masiku ake onse. Ndipo Heti adabereka Aroni, ndipo Aroni adakhala mu ukapolo masiku ake onse; ndipo adabereka Amunigada, ndipo Amunigada adakhalanso mu ukapolo masiku ake onse; ndipo iye adabereka Koriyantumu, ndipo Koriyantumu adakhala mu ukapolo masiku ake onse, ndipo iye adabereka Komi.

32 Ndipo zidachitika kuti Komi adathawitsa theka la ufumuwo. Ndipo iye adalamulira pa theka la ufumuwo kwa dzaka makumi anayi ndi ziwiri; ndipo iye adapita kukamenya nkhondo motsutsana ndi mfumu, Amigidi, ndipo adamenyana kwa nthawi ya dzaka zambiri, munthawi imeneyi Komi adapeza mphamvu pa Amigidi, ndipo adapeza mphamvu pa ufumu otsalirawo.

33 Ndipo mu masiku a Komi kudayamba kukhala achifwamba mu dzikolo; ndipo iwo adatenga madongosolo akale, ndi kuchita malumbiro potsatira njira ya achikale, ndi kufunanso kuti awononge ufumuwo.

34 Tsopano Komi adamenyana motsutsana nawo kwambiri; komabe, iye sadagonjetse kutsutsana nawoko.

Print