Malembo Oyera
Eteri 14


Mutu 14

Mphulupulu za anthu zibweretsa thembelero pa dziko—Koriyantumuri ayambitsa nkhondo motsutsana ndi Giliyadi, kenako Libi, ndipo kenako Shizi—Mwazi ndi infa ziphimba dzikolo.

1 Ndipo tsopano kudayambika kukhala thembelero lalikulu pa dziko lonse chifukwa cha mphulupulu za anthuwo, mumene, ngati munthu angayike chipangizo chake kapena lupanga lake pa alumali, kapena pa malo amene iye angasungile, taonani, m’mawa mwake, samalipeza, lalikulu lidali thembeleroli pa dzikolo.

2 Kotero munthu wina aliyense adakakamila pa icho chimene chidali chake, ndi manja ake, ndipo sakadabwereketsa kapena kubwereka; ndipo munthu wina aliyense ankasunga chigwiliro cha lupanga lake m’dzanja lake lamanja, potetezera chuma chake ndi moyo wake womwe ndi akazi ake ndi ana ake.

3 Ndipo tsopano, patatha nthawi ya dzaka ziwiri, ndipo atamwalira Saredi, taonani, kudabwera m’bale wa Saredi ndipo iye adathira nkhondo kwa Koriyantumuri, mumene Koriyantumuri adamugonjetsa iye ndi kumuthamangitsira iye m’chipululu cha Akishi.

4 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Saredi adamuthira nkhondo mu chipululu cha Akishi; ndipo nkhondoyo idakhala yoopsya kwambiri, ndipo zikwi zambiri zidagwa ndi lupanga.

5 Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri adazungulira chipululucho; ndipo m’bale wa Saredi adaguba kutuluka m’chipululumo nkati mwa usiku, ndipo adapha gawo la ankhondo a Koriyantumuri, pamene iwo adaledzera.

6 Ndipo iye adafika ku dziko la Morone, ndi kudzikhazika yekha pa mpando wachifumu wa Koriyantumuri.

7 Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri adakhala ndi ankhondo ake m’chipululu kwa nthawi ya dzaka ziwiri, mumene iye adalandira mphamvu zazikulu ku ankhondo ake.

8 Tsopano m’bale wa Saredi, amene dzina lake lidali Giliyadi, nayenso adalandira mphamvu zazikulu ku ankhondo ake, chifukwa cha magulu azachinsinsi.

9 Ndipo zidachitika kuti wamkulu wa ansembe wake adamupha iye pamene iye adakhala pa mpando wake wachifumu.

10 Ndipo zidachitika kuti m’modzi wa gulu la zachinsinsi adamupha iye mu njira yachinsinsi, ndipo adadzitengera paiye yekha ufumuwo; ndipo dzina lake lidali Libi; Libi adali munthu wamtali kwambiri, kuposa munthu aliyense pakati pa anthu onse.

11 Ndipo zidachitika kuti m’chaka choyamba cha Libi, Koriyantumuri adabwera ku dziko la Morone, ndipo adathira nkhondo kwa Libi.

12 Ndipo zidachitika kuti iye adamenyana ndi Libi, mumene Libi adamukantha pa mkono mpakana iye adavulala; komabe, ankhondo a Koriyantumuri adapita chitsogolo pa Libi, mpakana iye adathawira ku malire ndi gombe la nyanja.

13 Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri adamuthamangitsa; ndipo Libi adamuthira nkhondo pa gombe lanyanjalo.

14 Ndipo zidachitika kuti Libi adakantha ankhondo a Koriyantumuri, mpakana iwo adathawiranso ku chipululu cha Akishi.

15 Ndipo zidachitika kuti Libi adamuthamangitsa iye kufikira iye adafika ku chigwa cha Agosi. Ndipo Koriyantumuri adatenga anthu onse ndi iye pamene iye ankathawa pamaso pa Libi mu gawo limenelo la dziko lomwe iye adathawira.

16 Ndipo pamene iye adafika mu chigwa cha Agosi iye adathira nkhondo kwa Libi, ndipo adakantha iye kufikira adafa; komabe, m’bale wa Libi adabwera motsutsana ndi Koriyantumuri m’malo mwake, ndipo nkhondoyo idakhala yoopsya kwambiri, pamene Koriyantumuri adathawa kachiwiri pamaso pa ankhondo a m’bale wa Libi.

17 Tsopano dzina la m’bale wa Libi linkatchedwa Shizi. Ndipo zidachitika kuti Shizi adathamangitsa Koriyantumuri, ndipo iye adagwetsa mizinda yambiri, ndipo iye adapha onse amayi ndi ana omwe, ndipo adawotcha mizindayo.

18 Ndipo kudali kuopedwa kwa Shizi ku maiko onse ozungulira, mfuu udafika kuzungulira dzikolo—Ndani angayime pamaso pa Shizi? Taonani, iye akusesa dziko lapansi pamaso pake!

19 Ndipo zidachitika kuti anthuwo adayamba kusonkhana pamodzi m’magulu ankhondo, kuzungulira dziko lonselo.

20 Ndipo iwo adagawikana; ndipo ena mwa iwo adathawira kwa ankhondo a Shizi, ndi ena mwa iwo adathawira kwa ankhondo a Koriyantumuri.

21 Ndipo yaikulu ndi yokhalitsa idali nkhondoyo, ndipo aatali adali maonekedwe a kukhetsa mwazi ndi kuphana, mpakana nkhope yonse ya dzikolo idaphimbidwa ndi matupi a anthu okufa.

22 Ndipo yachangu komanso yofulumira idali nkhondoyo mpakana kudalibe wina otsala kuti akwilire omwalira, koma iwo adaguba kuchoka kokhetsa mwazi kupitanso kokhetsa mwazi, kusiya matupi a onse amuna, akazi, ndi ana atangoponyedwa pamaso pa dzikolo, kuti akhale zodyedwa ndi mphutsi za mthupi.

23 Ndipo fungo lake lidafika pa dziko lonse, ngakhale pa nkhope yonse ya dzikolo; kotero anthu adavutika usana ndi usiku, chifukwa cha fungo lakelo.

24 Komabe, Shizi sadasiye kuthamangitsa Koriyantumuri; pakuti iye adalumbira kuti adzabwenzera yekha pa Koriyantumuri mwazi wa m’bale wake, amene adaphedwa, ndipo mawu a Ambuye amene adabwera kwa Eteri kuti Koriyantumuri sadzagwa ndi lupanga.

25 Ndipo motero tikuona kuti Ambuye adawayendera mu chidzalo cha mkwiyo wake, ndipo zoipa ndi zonyansa zidakonzera njira ya chiwonongeko chawo chosatha.

26 Ndipo zidachikita kuti Shizi adathamangitsabe Koriyantumuri chakum’mawa, ngakhale kumalire a gombe lanyanja, ndipo kumeneko adathirana nkhondo kwa nthawi ya masiku atatu.

27 Ndipo choopsya chidali chiwonongeko pakati pa ankhondo a Shizi kuti anthu adayamba kuchita mantha, ndipo adayamba kuthawa pamaso pa ankhondo a Koriyantumuri; ndipo iwo adathawira ku dziko la Koriho, ndipo adasesako okhalamo pamaso pawo, onse amene sadafune kugwirizana nawo.

28 Ndipo iwo adakhoma mahema awo mu mtsinje wa Koriho; ndipo Koriyantumuri adakhoma mahena ake mu mtsinje wa Shure. Tsopano mtsinje wa Shure udali pafupi ndi phiri la Komuno; kotero Koriyantumuri adasonkhanitsa ankhondo ake pamodzi pa phiri la Komuno, ndipo iye adaliza lipenga kwa ankhondo a Shizi kuwaitana iwo ku nkhondo.

29 Ndipo zidachitika kuti iwo adabwera, koma adathamangitsidwanso; ndipo adabweranso kachiwiri, ndipo iwo adathamangitsidwanso kachiwiri. Ndipo zidachitika kuti adabweranso kwa nthawi yachitatu, ndipo nkhondoyo idakhala yoopsya kwambiri.

30 Ndipo zidachitika kuti Shizi adamukantha Koriyantumuri mpakana kuti adamupatsa iye mabala aakulu; ndipo Koriyantumuri, potaya mwazi wambiri, adakomoka, ndipo adanyamulidwa ngati kuti wafa.

31 Tsopano kutayika kwa amuna, aakazi ndi ana ku mbali zonse kudali kwakukulu mpakana Shizi adalamula anthu ake kuti asathamangitsenso ankhondo a Koriyantumuri; kotero, iwo adabwelera ku msasa wawo.

Print