Malembo Oyera
Eteri 8


Mutu 8

Pali ndeu ndi mikangano ya ufumu—Akishi apanga gulu la zachinsinsi lomangidwa ndi lumbiro kuti aphe mfumu—Magulu a zachinsinsi ndi a mdyerekezi ndipo amabweretsa chiwonongeko ku maiko—Amitundu atsopano akuchenjezedwa motsutsana ndi gulu la zachinsinsi limene lidzafune kugwetsa ufulu wa mafuko ndi maiko onse.

1 Ndipo zidachitika kuti iye adabereka Omeri, ndipo Omeri adalamulira m’malo mwake. Ndipo Omeri adabereka Yaredi; ndipo Yaredi adabereka ana aamuna ndi aakazi.

2 Ndipo Yaredi adagalukira motsutsana ndi atate ake, ndipo iye adabwera ndi kukhala mu dziko la Heti. Ndipo zidachitika kuti iye adanyengelera anthu ambiri, chifukwa cha kuchenjera kwa mawu ake, kufikira kuti adapeza theka la ufumuwo.

3 Ndipo pamene iye adakopa theka la ufumuwo adathira nkhondo kwa atate ake, ndipo iye adatenga atate ake ku ukapolo, ndipo adapangitsa iwo kuti agwire ntchito mu ukapolo.

4 Ndipo tsopano, mu masiku a ulamuliro wa Omeri adali mu ukapolo theka la masiku ake. Ndipo zidachitika kuti iye adabereka ana aamuna ndi aakazi, pakati pawo padali Esilomu ndi Koriyantumuri;

5 Ndipo iwo adali okwiya kwambiri chifukwa cha zochita za Yaredi m’bale wawo, mpakana kuti iwo adadzutsa ankhondo ndi kuthira nkhondo kwa Yaredi. Ndipo zidachitika kuti iwo adamuthira nkhondoyo mu usiku.

6 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adapha ankhondo a Yaredi, adalinso pafupi kumupha iye; ndipo iye adachondelera nawo kuti asamuphe, ndipo adzapereka ufumuwo kwa atate ake. Ndipo zidachitika kuti adamupatsa iye moyo wake.

7 Ndipo tsopano Yaredi adakhala wachisoni kwambiri chifukwa cha kutayika kwa ufumuwo, pakuti iye adaika mtima wake pa ufumuwo ndi pa ulemelero wa dziko lapansi.

8 Tsopano mwana wamkazi wa Yaredi pokhala katswiri kwambiri, ndi poona zisoni za atate ake, adaganiza zopanga dongosolo limene iye angathe kuwombola ufumuwo kwa atate ake.

9 Tsopano mwana wamkazi wa Yaredi adali wokongola kwambiri. Ndipo zidachitika kuti adayankhula ndi atate ake, ndi kunena kwa iwo: Pati pamene atate anga ali ndi chisoni chachikuluchi? Kodi iwo sadawerenge nkhani imene makolo athu adabweletsa kuwolotsa pakuya kwambiri? Taonani, kodi palibe nkhani yokhudzana ndi iwo akale, kuti iwo kudzera ku madongosolo achinsinsi adapeza maufumu ndi ulemelero waukulu?

10 Ndipo tsopano, kotero, lolani atate anga aitane Akishi, mwana wa Kimuno; ndipo taonani, ndine wokongola, ndipo ndidzavina pamaso pake, ndipo ndidzamukondweretsa,kuti adzafuna ine kuti ndikhale mkazi wake; kotero ngati adzafune kwa inu kuti mumupatse ine kukhala mkazi wake, pamenepo inu mudzati: Ndimupereka iye ngati inu mungabweretse kwa ine mutu wa atate anga, mfumuyo.

11 Ndipo tsopano Omeri adali bwenzi wa Akishi; kotero, pamene Yaredi adatumiza kukaitana Akishi, mwana wamkazi wa Yaredi adavina kwa iye mokuti adamukondweretsa iye, kufikira kuti iye adamkhumbira kukhala mkazi wake. Ndipo zidachitika kuti iye adati kwa Yaredi: Ndipatse iye kuti akhale mkazi wanga.

12 Ndipo Yaredi adati kwa iye: Ndimpereka iye kwa iwe, ngati ungabweretse kwa ine mutu wa atate anga, mfumuyo.

13 Ndipo zidachitika kuti Akishi adasonkhanitsa ku nyumba ya Yaredi achibale ake onse, ndipo adati kwa iwo: Kodi mulumbira kwa ine kuti mudzakhala okhulupirika kwa ine mu chinthu chimene ndingafune kwa inu?

14 Ndipo zidachitika kuti iwo onse adalumbira kwa iye, mwa Mulungu wakumwamba, ndiponso mwa kumwamba ndiponso mwa dziko lapansi, ndi pa mitu yawo, kuti aliyense angasemphane ndi chithandizo chimene Akishi adakhumba adzataya mutu wake; ndipo aliyense amene angaulure chinthu chilichonse Akishi adawadziwitsa iwo, yemweyo adzataya moyo wake.

15 Ndipo zidachitika kuti motero iwo adagwirizana ndi Akishi. Ndipo Akishi adapereka kwa iwo malumbiro amene adaperekedwa ndi iwo akale amenenso ankafuna mphamvu, amene adapatsidwa kuchokera ngakhale kwa Kaini, amene adali wokupha kuyambira pa chiyambi.

16 Ndipo adasungidwa mwa mphamvu ya mdyerekezi kupereka malumbiro amenewa kwa anthu, kuti awasunge mu mdima, kuwathandizira iwo ofuna mphamvu kuti apeze mphamvu, ndi kupha, ndi kulanda, ndi kunama, ndi kuchita zoipa zamitundu yonse ndi zadama.

17 Ndipo adali mwana wamkazi wa Yaredi amene adachiika mumtima mwake kuti afufuze zinthu izi za kale; ndipo Yaredi adachiika mumtima mwa Akishi; kotero, Akishi adachipereka kwa abale ake ndi anzake, kuwasocheretsa iwo mwa malonjezo abwino kuti achite chilichonse chomwe iye adakhumba.

18 Ndipo zidachitika kuti iwo adapanga gulu la zachinsinsi, ngakhale monga iwo akale; limene gulu lake ndi lonyansa kwambiri ndi loipa kuposa onse, pamaso pa Mulungu;

19 Pakuti Ambuye sagwira ntchito mumagulu azachinsinsi, ngakhale iwo safuna kuti munthu akhetse mwazi, koma mu zinthu zonse adaletsa icho, kuyambira pachiyambi cha munthu.

20 Ndipo tsopano ine, Moroni, sindilemba njira ya malumbirowo ndi zachinsinsizo, pakuti zadziwitsidwa kwa ine kuti zidakalipo pakati pa anthu onse, ndipo zidakalipo pakati pa Alamani.

21 Ndipo iwo apangitsa kuwonongeka kwa anthu awa amene ndikuyankhula tsopano, ndiponso chiwonongeko cha anthu a Nefi.

22 Ndipo dziko linalililonse litadzagwiritsitse magulu achinsinsi oterowa, kuti lipeze mphamvu ndi phindu, kufikira iwo atafalikira padziko, taonani, iwo adzawonongedwa; pakuti Ambuye sadzalora kuti mwazi wa oyera mtima ake, umene udzakhetsedwe ndi iwo, udzakhalebe ukulira kwa iwo kuchokera kufumbi kuti abwenzere chilango pa iwo ndipo komabe iwo sadzawabwenzera iwo chilango.

23 Kotero, O inu Amitundu, ndi chanzeru mwa Mulungu kuti zinthu izi ziwonetseredwe kwa inu, kuti potero muthe kulapa pamachimo anu, ndipo osalora kuti magulu akuphawa adzakhale pamwamba panu, amene amamangidwa kuti apeze mphamvu ndi phindu—ndi ntchito, inde, ngakhale ntchito ya chiwonongeko ibwera kwa inu, inde, ngakhale lupanga la chilungamo la Mulungu wa Muyaya lidzagwera pa inu, ku chigonjetso ndi chiwonongeko chanu ngati inu mudzalora zinthu izi kuti zikhale.

24 Kotero, Ambuye akukulamulani inu, pamene mudzaona zinthu izi zikubwera pakati panu kuti mudzachangamuka ku lingaliro la nyengo yanu yowopsa, chifukwa cha gulu la zachinsinsi limene lidzakhala pakati panu; kapena tsoka kukhala kwa ilo, chifukwa cha mwazi wa iwo amene aphedwa; pakuti iwo akulira kuchokera ku fumbi kuti abwenzere chilango pa ichi, ndiponso pa iwo amene adalimanga ilo.

25 Pakuti zimachitika kuti amene amalimanga amafuna kugonjetsa ufulu wa maiko ndi mafuko onse; ndipo limabweretsa chiwonongeko cha anthu onse, pakuti limamangidwa ndi mdyerekezi, amene ali tate wa mabodza onse; ngakhale wabodza yemweyo amene adanyenga makolo athu oyamba, inde, ngakhale wabodza yemweyo amene adachititsa munthu kuti adzipha kuyambira pachiyambi; amene adalimbitsa mitima ya anthu kuti adapha aneneri, ndi kuwagenda miyala, ndi kuwathamangitsa kuyambira pachiyambi.

26 Kotero, ine, Moroni, ndalamulidwa kuti ndilembe zinthu izi kuti zoipa zithe, ndipo kuti nthawi ithe kubwera imene Satana asathe kukhala ndi mphamvu pa mitima ya ana a anthu, koma kuti akakamizidwe kuchita zabwino mosalekeza, kuti akathe kubwera ku kasupe wa chilungamo chonse ndi kupulumutsidwa.

Print