Malembo Oyera
Eteri 3


Mutu 3

M’bale wa Yaredi aona chala cha Ambuye pamene iye agwira miyala khumi ndi isanu ndi umodzi—Khristu aonetsa thupi Lake la uzimu kwa m’bale wa Yaredi—Iwo amene ali ndi chidziwitso chonse sangaletsedwe mu chophimba—Omasulira aperekedwa kuti abweretse zolemba za Ayaredi poyera.

1 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Yaredi, (tsopano chiwerengero cha mabwato amene adakonzedwa chidali asanu ndi atatu) adapita ku phiri, limene iwo adalitchula phiri la Shelemu, chifukwa cha kutalika kwake kopambana, ndipo adasungunula kuchokera muthanthwe miyala khumi ndi isanu ndi umodzi; ndipo iyo idali yoyera ndi yowonekera, ngakhale yowonekera ngati kalilore; ndipo iye adainyamula m’manja mwake pamwamba pa phirilo, ndipo adafuulanso kwa Ambuye nati:

2 O Ambuye, inu mwanena kuti tikuyenera kudzazingidwa ndi madzi osefukira Tsopano taonani, O Ambuye, ndipo musakwiye ndi mtumiki wanu chifukwa cha zofooka zake pamaso panu; pakuti tikudziwa kuti inu ndi oyera ndipo mumakhala kumwamba, ndipo kuti ife sitili oyenera pamaso panu; chifukwa cha kugwa chilengedwe chathu chakhala choipa mosalekeza; komabe, O Ambuye, inu mwatipatsa ife lamulo kuti tikuyenera kuyitanira pa inu, kuti kuchokera kwa inu tikathe kulandira molingana ndi zokhumba zathu.

3 Taonani, O Ambuye, inu mwatikantha ife chifukwa cha mphulupulu zathu, ndipo mwatithamangitsa ife, ndipo pa dzaka zambiri zimenezi takhala tili mu chipululu; komabe, inu mwakhala achifundo kwa ife. O Ambuye, ndiyang’aneni ine mwachisoni, ndi kutembenuza mkwiyo wanu kwa anthu anu awa, ndipo musalore kuti iwo apite kudutsa mu mdima oopsya uwu; koma taonani zinthu izi zimene ine ndasungunula kuchokera ku thanthwe.

4 Ndipo ndikudziwa, O Ambuye, kuti inu muli ndi mphamvu zonse, ndipo mukhonza kuchita chilichonse chimene mufuna m’kuthandizira kwa munthu; kotero khudzani miyalayi, O Ambuye, ndi chala chanu, ndi kuyikonzekeretsa iyo kuti iwale mu mdima; ndipo idzawalira kwa ife mubwato limene ife takonza, kuti tikhale ndi kuwala pamene tikuwoloka nyanja.

5 Taonani, O, Ambuye, Inu mukhonza kuchita ichi. Tikudziwa kuti inu mutha kuonetsa mphamvu zazikulu, zimene zimaoneka zazing’ono m’kumvetsa kwa anthu.

6 Ndipo zidachitika kuti pamene m’bale wa Yaredi adayankhula mawu amenewa, taonani, Ambuye adatambasula dzanja lawo ndi kukhudza miyalayo umodzi ndi umodzi ndi chala chawo. Ndipo chophimba chidachotsedwa m’maso mwa m’bale wa Yaredi, ndipo iye adaona chala cha Ambuye; ndipo chidali ngati chala cha munthu, monga kwa mnofu ndi mwazi; ndipo m’bale wa Yaredi adagwa pamaso pa Ambuye, pakuti iye adagwidwa ndi mantha.

7 Ndipo Ambuye adaona kuti m’bale wa Yaredi adagwa pansi; ndipo Ambuye adati kwa iye: Dzuka, chifukwa chiyani wagwa?

8 Ndipo iye adati kwa Ambuye: Ndaona chala cha Ambuye, ndipo ndidaopa kuti iye andikantha ine; pakuti sindimadziwa kuti Ambuye ali ndi mnofu ndi mwazi.

9 Ndipo Ambuye adati kwa iye: Chifukwa cha chikhulupiliro chako iwe waona kuti ndidzadzitengera pa ine thupi ndi mwazi; ndipo palibe munthu amene adadza pamaso panga ndi chikhulupiliro chachikulu monga iwe wachitira; pakuti pakadapanda kutero iwe siukadaona chala changa. Kodi waona zoposera zimenezi?

10 Ndipo iye adayankha: Ayi; Ambuye, zionetsereni kwa ine.

11 Ndipo Ambuye adati kwa iye: Kodi ukukhulupilira mawu amene ine ndidzayankhula?

12 Ndipo adayankha: Inde, Ambuye, ndikudziwa kuti inu mumayankhula choonadi, pakuti inu ndi Mulungu wa choonadi, ndipo simunganame.

13 Ndipo pamene iye adanena mawu awa, taonani, Ambuye adadzionetsera kwa iye, ndipo adati: Chifukwa iwe ukudziwa zinthu izi, wawomboledwa m’kugwa; kotero wabwenzeretsedwa pamaso panga; kotero ndizionetsera kwa iwe.

14 Taona, ndine amene ndidakonzedwa kuyambira pa maziko a dziko lapansi kuwombola anthu anga. Taona, ndine Yesu Khristu. Taona, ndine Atate ndi Mwana. Mwa ine anthu onse adzakhala ndi moyo, ndipo kuti kwamuyaya, ngakhale iwo amene adzakhulupilira mu dzina langa; ndipo adzakhala ana anga aamuna ndi aakazi.

15 Ndipo sindidadzionetserepo kwa munthu amene ndidamulenga, pakuti palibe munthu amene adakhulupilira mwa ine monga iwe wachitira. Waona kodi kuti iwe udalengedwa m’chifaniziro changa? Inde, ngakhale anthu onse adalengedwa pachiyambi potengera chifaniziro changa.

16 Taona, thupi ili, limene ukulionali, ndi thupi la mzimu wanga; ndipo munthu ndamulenga potengera thupi la mzimu wanga; ndipo ngakhale momwe ndikuonekera kwa iwe kukhala mu uzimu ndidzaonekera kwa anthu anga mu thupi.

17 Ndipo tsopano, pamene ine, Moroni, ndati sindingapange nkhani yonse ya zinthu izi zimene zalembedwa, kotero ndizokwanira kwa ine kunena kuti Yesu adadzionetsera kwa munthu uyu mu uzimu, ngakhale potengera mchitidwe ndi maonekedwe a thupi lomwelo ngati limene adadzionetsera yekha kwa Anefi.

18 Ndipo iye adatumikira kwa iye monga ngati iye adatumikira kwa Anefi; ndipo zonsezi kuti munthu uyu adziwe kuti iye adali Mulungu, chifukwa cha ntchito zazikulu zambiri zimene Ambuye adamuonetsera iye.

19 Ndipo chifukwa cha chidziwitso cha munthu uyu sadaletsedwe kuti aone kuchokera mu chophimbacho; ndipo iye adaona chala cha Yesu, chimene, pamene iye adaona, adagwa pansi ndi mantha; pakuti iye adadziwa kuti chidali chala cha Ambuye; ndipo adalibenso chikhulupiliro, pakuti adadziwa, popanda kukaikira kanthu.

20 Potero, atakhala ndi chidziwitso chonse cha Mulungu, iye sakadatha kusungidwa mkati mwa chophimba; kotero iye adaona Yesu; ndipo adatumikira kwa iye.

21 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adati kwa m’bale wa Yaredi: Toana, usadzalore kuti zinthu izi zimene iwe waona ndi kuzimva kuti zipite ku dziko lapansi, kufikira nthawi idze imene ndidzalemekeza dzina langa mu thupi; kotero, iwe udzasunge zinthu izi zimene waziona ndi kuzimva, ndipo usazionetse kwa munthu.

22 Ndipo taona, pamene udzabwera kwa ine, udzazilemba ndi kuzimata, kuti palibe angazimasulire; pakuti udzazilemba mu chiyankhulo choti sizingawerengedwe.

23 Ndipo taona, miyala iwiri iyi ndidzaipereka kwa iwe, ndipo iwe udzaimatanso ndi zinthu zimene udzazilembe.

24 Pakuti taona, chiyankhulo chimene udzachilembe ine ndachisokoneza; kotero ndidzachititsa mu nthawi yanga kuti miyala iyi idzakulitsa ku maso a anthu zinthu izi zimene iwe udzazilembe.

25 Ndipo pamene Ambuye adanena mawu awa, iwo adaonetsa kwa m’bale wa Yaredi anthu onse okhala mu dziko lapansi amene adakhala, ndiponso onse amene adzakhale; ndipo sadawabise pamaso pake, ngakhale kumalekezero a dziko lapansi.

26 Pakuti iye adanena kwa iye kale, kuti ngati iye adzakhulupilira mwa iye adzatha kuwonetsera kwa iye zinthu zonse—zikuyenera kuonetseredwa kwa iye; kotero Ambuye sakadabisa kanthu kwa iye, pakuti iye adadziwa kuti Ambuye akhonza kumuonetsa zinthu zonse.

27 Ndipo Ambuye adati kwa iye; Lemba zinthu izi ndi kuzimata: ndipo ndidzaonetsa izo mu nthawi yanga kwa ana a anthu.

28 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adalamula iye kuti amate miyala iwiri imene iye adalandira, ndi kusayionetsa, kufikira Ambuyewo adzaionetsere kwa ana a anthu.

Print