Malembo Oyera
1 Nefi 19


Mutu 19

Nefi apanga mapale a miyala ndi kulemba mbiri ya anthu ake—Mulungu wa Israeli adzabwera zaka mazana asanu ndi limodzi kuchokera pamene Lehi adachoka ku Yerusalemu—Nefi afotokoza za mazunzo ndi kupachikidwa pa mtanda kwake—Ayuda adzanyozedwa ndi kubalalitsidwa mpaka m’masiku otsiriza. adzabwelera kwa Ambuye. Mdzaka dza pafupifupi 588–570 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adandilamulira ine, kotero, ndidapanga mapale a miyala kuti ndizokote pa iwo zolemba za anthu anga. Ndipo pa mapale amene ndidapanga ndidalemba zolemba za atate anga, ndiponso maulendo athu m’chipululu, ndi mauneneri a atate anga; ndiponso ambiri a mauneneri anga ine ndidazokota pa iwo.

2 Ndipo sindidadziŵe pa nthawi imene ndidawapanga kuti ndikuyenera kudzalamulidwa ndi Ambuye kupanga mapale awa; kotero zolemba za atate anga, ndi m’badwo ya makolo awo; ndi mbali yochuluka ya zochitika zathu zonse m’chipululu zalembedwa pa mapale oyamba aja amene ndayankhula; kotero, zinthu zimene zidachitika ndisadapange mapale amenewa, ziri zoonadi, makamaka zidatchulidwa pa mapale oyamba.

3 Ndipo nditapanga mapalewa mwa njira ya lamulo, ine, Nefi, ndidalandira lamulo kuti utumiki ndi mauneneri, womveka bwino kwambiri ndi magawo amtengo wapatali a iwo, alembedwe pa mapale amenewa; ndi kuti zinthu zimene zidalembedwa zikuyenera kusungidwa ku chilangizo cha anthu anga, amene adzalandira dzikolo, ndiponso chifukwa cha zolinga zina zanzeru, zolinga zomwe zimadziwika kwa Ambuye.

4 Kotero, ine, Nefi, ndidapanga zolemba pa mapale ena, omwe amapereka nkhani, kapena omwe amapereka mbiri yochulukirapo ya nkhondo ndi mikangano ndi chiwonongeko cha anthu anga. Ndipo ndidachita izi, ndipo ndidawalamula anthu anga zimene adzachite ndikadzachoka ine; ndipo kuti mapale awa akuyenera kuperekedwa kuchokera ku m’badwo umodzi kupita ku umzake; kapena kuchokera kwa mneneri wina kupita kwa wina, mpaka malamulo ena a Ambuye ataperekedwa.

5 Ndipo nkhani ya kupanga kwanga kwa mapale amenewa idzaperekedwa mtsogolo muno; ndipo tsopano, taonani, ndipitilira malingana ndi izo ndayankhula; ndipo izi ndikuchita kuti zinthu zopatulika kwambiri zisungidwe ku chidziwitso cha anthu anga.

6 Komabe, sindilemba kalikonse pa mapale kupatula kuti ndikuganiza kuti ndi zopatulika. Ndipo tsopano, ngati ine ndilakwitsa, ngakhale iwo akale adalakwitsa; osati kuti ndikudziwiringulira ndekha chifukwa cha anthu ena, koma chifukwa cha chofowoka chiri mwa ine, molingana ndi thupi, ndikadati ndidzilungamitse ndekha.

7 Pakuti zinthu zimene anthu ena amaziona kuti ndi zamtengo wapatali, kwa thupi ndi moyo womwe, ena amazipondereza ndi kuzipondaponda. Inde, ngakhale Mulungu wa Israeli yu anthu amamupondaponda pansi pa mapazi awo; ndikuti, kumuponda pansi pa mapazi awo koma ndiyankhula m’mawu ena—amamunyoza, ndipo samamvera mawu a uphungu wake.

8 Ndipo taonani akubwera, monga mwa mau a mngelo, m’dzaka mazana asanu ndi amodzi kuyambira nthawi imene atate anga adachoka ku Yerusalemu.

9 Ndipo dziko lapansi, chifukwa cha kusaweruzika kwawo, lidzamuweruza iye kukhala kanthu kopanda pake; kotero adamukwapula, ndipo adalolera; ndipo adamukantha iye, ndipo adalolera. Inde, iwo adalavulira pa iye, ndipo iye adalolera izo, chifukwa cha kukoma mtima kwa chikondi kwake ndi kupilira kwake pa ana a anthu.

10 Ndipo Mulungu wa makolo athu, amene adatsogozedwa kuchoka mu Igupto, kuchoka mu ukapolo, ndiponso adatetezedwa m’chipululu ndi iye, inde, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo, adzipereka yekha, monga mwa mawu a mngelo, monga munthu, m’manja mwa anthu oipa, kuti akwezedwe, monga mwa mau a Zenoki, ndi kupachikidwa, monga mwa mau a Nemu, ndi kuikidwa m’manda, monga mwa mawu a Zenosi, amene adakamba zokhudzana ndi masiku atatu a mdima, chimene chiyenera kukhala chizindikiro choperekedwa cha imfa yake kwa iwo amene adzakhale muzilumba za nyanja, makamaka kuperekedwa kwa iwo amene ali a nyumba ya Israeli.

11 Pakuti adanena motero mneneri: Ambuye Mulungu ndithu adzayendera nyumba yonse ya Israeli tsiku limenelo, ena ndi mawu ake, chifukwa cha chilungamo chawo, ku chisangalalo chawo chachikulu ndi chipulumutso, ndi ena ndi mabingu ndi mphezi za mphamvu yake; ndi mkuntho, ndi moto, ndi utsi, ndi nthunzi wamdima, ndi kutseguka kwa dziko lapansi, ndi mapiri amene adzanyamulidwe.

12 Ndipo zinthu zonsezi zikuyenera kubwera ndithu, akutero mneneri Zenosi. Ndipo miyala ya dziko lapansi idzang’ambika; ndipo chifukwa cha kubuula kwa dziko lapansi, ambiri a mafumu a zilumba za nyanja adzagwidwa ndi Mzimu wa Mulungu, kufuula: Mulungu wa chilengedwe azunzika.

13 Ndipo kwa iwo amene ali ku Yerusalemu, atero mneneri, iwo adzazunzidwa ndi anthu wonse, chifukwa iwo adapachika Mulungu wa Israeli, ndi kutembenuzira mitima yawo kumbali, kukana zizindikiro ndi zodabwitsa, ndi mphamvu ndi ulemelero wa Mulungu wa Israeli.

14 Ndipo chifukwa iwo atembenuzira mitima yawo kumbali, akutero mneneri, ndipo anyoza Woyera wa Israeli, iwo adzayendayenda m’thupi, ndipo adzawonongeka, ndipo adzakhala mphekesera ndi nthano, ndipo adzadedwa pakati pa mitundu yonse.

15 Komabe, pamene tsiku limenelo lidzafika, akutero mneneri, kuti iwo sadzatembenuziranso kumbari mitima yawo kwa Woyera wa Israeliyo, pamenepo iye adzakumbukira mapangano amene iye adapanga kwa makolo awo.

16 Inde, pamenepo adzakumbukira zilumba za nyanja; inde, ndipo anthu onse amene ali a nyumba ya Israeli, ndidzawasonkhanitsa, atero Ambuye, monga mwa mawu a mneneri Zenosi, kuchokera ku ngodya zinayi za dziko lapansi.

17 Inde, ndipo dziko lonse lapansi lidzaona chipulumutso cha Ambuye, atero mneneri; dziko lililonse, fuko, chinenero ndi anthu adzadalitsidwa.

18 Ndipo ine, Nefi, ndalemba zinthu izi kwa anthu anga, kuti mwina ndikawakope kuti akumbukire Ambuye Mombolo wawo.

19 Kotero, ndi kuyankhula kwa nyumba yonse ya Israeli, ngati kuli kuti adzalandira zinthu izi.

20 Pakuti taonani, ndiri nazo ntchito mu mzimu, zimene zimanditopetsa ine ngakhale kuti mafundo anga onse afowoka, kwa iwo amene ali ku Yerusalemu; pakuti Ambuye akadapanda kukhala wachifundo, kuonetsera kwa ine zokhudzana ndi iwo, ngakhale ngati adachitira aneneri akale, ndikadawonongekanso.

21 Ndipo ndithudi iye adaonetsa kwa aneneri akale zinthu zonse zokhudzana ndi iwo; ndiponso iye adawonetsa kwa ambiri zokhudza ife; kotero, zikuyenera kuti tidziwe za iwo pakuti alembedwa pa mapale a mkuwa.

22 Tsopano zidachitika kuti ine, Nefi, ndidaphunzitsa abale anga zinthu izi; ndipo zidachitika kuti ndidawerenga zinthu zambiri kwa iwo, zomwe zidazokotedwa pa mapale a mkuwa, kuti athe kudziwa zokhudzana ndi zochita za Ambuye m’maiko ena, pakati pa anthu akale.

23 Ndipo ndidawerenga zinthu zambiri kwa iwo zomwe zidalembedwa m’mabuku a Mose; koma kuti ndithe kuwakopa mokwanira kuti akhulupilire mwa Ambuye Momboli wawo ndidawerenga kwa iwo zimene zidalembedwa ndi mneneri Yesaya; pakuti ndidafanizira malemba oyera onse kwa ife; kuti zikhale zopindulitsa ndi kuphunzira kwathu.

24 Kotero ndidayankhula nawo, nati: Imvani mawu a mneneri, inu otsalira a nyumba ya Israeli, nthambi imene yathyoledwa; mverani mawu a mneneri, olembedwa kwa nyumba yonse ya Israeli, ndipo afanizireni kwa inu nokha, kuti mukhale ndi chiyembekezo monganso abale anu amene mudadulidwa kwa iwo; pakuti mneneri adalemba motero.

Print