Malembo Oyera
1 Nefi 16


Mutu 16

Oipa amatenga chilungamo kukhala chovuta—Ana a Lehi aamuna akwatira ana aakazi a Ismaeli—Liyahona itsogolera njira m’chipululu—Mauthenga ochokera kwa Ambuye alembedwa pa Liyahona kwa nthawi ndi nthawi—Ismaeli amwalira; banja lake ling’ung’udza chifukwa cha masautso. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti ine, Nefi, nditamaliza kuyankhula ndi azibale anga, taonani iwo adati kwa ine: iwe watidziwitsa ife zinthu zovuta, kuposa m’mene tingathe kukwanitsa.

2 Ndipo zidachitika kuti ine ndidati kwa iwo kuti ndidadziwa kuti ndayankhula zinthu zovuta motsutsana ndi oipa, molingana ndi choonadi; ndi olungama ndawalungamitsa, ndi kuchitira umboni kuti iwo adzakwezedwe pa tsiku lomaliza; kotero, anthu olakwa ndi amene amatenga chilungamo kukhala chovuta, chifukwa chimawacheka iwo pakati penipeni.

3 Ndipo tsopano azibale anga, ngati mudakakhala olungama ndipo mudali ofunitsitsa kumvetsera ku choonadi, ndi kumvera icho, kuti inu mungayende mowongoka pamaso pa Mulungu, ndiye simukadang’ung’udza chifukwa cha choonadi, ndi kunena kuti: Iwe wayankhula zinthu zovuta zotsutsa ife.

4 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidachondelera abale anga, ndi khama lonse, kuti adzisunga malamulo a Ambuye.

5 Ndipo zidachitika kuti iwo adadzichepetsa okha pamaso pa Ambuye, kotero kuti ine ndidasangalala ndipo ndidali ndi ziyembekezo zazikulu za iwo, kuti adzayenda mu njira za chilungamo.

6 Tsopano, zinthu zonsezi zidakambidwa ndi kuchitidwa pamene bambo ankakhala mu msasa mu chigwa chimene iwo adachitcha Lemueli.

7 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidatenga m’modzi wa ana aakazi a Ismaeli kukhala mkazi wanga; ndiponso, abale anga adatenga ana aakazi a Ismaeli kukhala akazi awo; ndiponso Zoramu adatenga mwana wa wamkazi wamkulu wa Ismaeli kukhala mkazi wake.

8 Ndipo kotero atate anga adali atakwaniritsa malamulo onse a Ambuye amene adaperekedwa kwa iwo. Ndiponso, ine, Nefi, ndidadalitsidwa ndi Ambuye kwambiri.

9 Ndipo zidachitika kuti mawu a Ambuye adayankhula kwa atate anga pa usiku, ndikuwalamula kuti m’mawa akuyenera kuyamba ulendo kupita m’chipululu.

10 Ndipo zidachitika kuti pamene atate anga adadzuka mam’mawa, ndikupita ku khomo la hema, mu kuzizwa kwawo kwakukulu adaona pansi mpira wozungulira wamapangidwe opatsa chidwi, ndipo udali wamkuwa wabwino. Ndipo nkati mwa mpirawo mudali mivi iwiri; ndipo wina umaloza njira imene tiyenera kupita m’chipululu.

11 Ndipo zidachitika kuti tidasonkhanitsa pamodzi chinthu chinachilichonse chomwe tikadanyamula m’chipululu, ndi zonse zotsalira za zakudya zathu zonse zimene Ambuye adatipatsa; ndipo tidatenga mbewu za mitundu yonse kuti ife tithe kunyamula m’chipululu.

12 Ndipo zidachitika kuti ife tidanyamula mahema athu ndikunyamuka kupita m’chipululu, kuowoloka mtsinje wa Lamani.

13 Ndipo zidachitika kuti tidayenda kwa nthawi ya masiku anayi, moyandikira mbali yoloza chakum’mwera-kumwera chakum’mawa, ndipo tidakhomanso mahema athu; ndipo tidawatcha dzina la malowo kuti Shazeri.

14 Ndipo zidachitika kuti tidatenga mauta athu ndi mivi yathu, ndikupita mchipululu kukapha chakudya cha mabanja athu; ndipo titapha chakudya cha mabanja athu tidabwelera ku mabanja athu mchipululu, kumalo a Shazeri. Ndipo tidapitanso kachiwiri mchipululu, kutsata njira yomweyo, kusunga malo anthaka yachonde amchipululu, amene adali m’malire ndi Nyanja Yofiira.

15 Ndipo zidachitika kuti tidayenda kwa masiku ambiri, kupha chakudya munjira, ndi mauta athu ndi mivi yathu ndi miyala yathu ndi malegeni athu.

16 Ndipo tidayenda motsogozedwa ndi mpirawo, umene umatitsogolera ku magawo a malo anthaka yachonde kwambiri m’chipululu.

17 Ndipo titayenda kwa masiku ambiri, tidakhoma mahema athu kwakanthawi, kuti tithe kupumulanso ndi kupeza chakudya cha mabanja athu.

18 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidapita kukapha chakudya, taonani ndidathyola uta wanga, umene udali opangidwa ndi chitsulo chabwino; ndipo nditathyola utawo, taonani, abale anga adakwiya nane chifukwa cha kutayika kwa uta wanga, pakuti sitidapeze chakudya.

19 Ndipo zidachikita kuti tidabwelera opanda chakudya kwa mabanja athu, ndipo pokhala otopa kwambiri, chifukwa cha ulendo wawo, adavutika kwambili chifukwa chakusowa kwa chakudya.

20 Ndipo zidachitika kuti Lamani ndi Lemueli ndi ana aamuna a Ismaeli adayamba kung’ung’udza kwambiri, chifukwa cha kuvutika ndi masautso awo m’chipululu; ndiponso atate anga adayamba kung’ung’udza motsutsana ndi Ambuye Mulungu wawo; inde, ndipo onse adali ndi chisoni chochuluka, ngakhale kuti adayamba kung’ung’udza motsutsana ndi Ambuye.

21 Tsopano zidachitika kuti ine, Nefi, nditasautsidwa ndi abale anga chifukwa cha kutayika kwa uta wanga, ndipo mauta awo atakhwefuka, zidayamba kukhala zovuta kwambiri, inde mpaka kuti sitinathe kupeza chakudya.

22 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidayankhula kwambiri kwa abale anga chifukwa iwo adali ataumitsa mitima yawo kachiwiri, mpaka kudandaula motsutsana ndi Ambuye Mulungu wawo.

23 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidapanga uta kuchokera ku mtengo, ndipo kuchokera ku ndodo yoongoka, ndidapanga muvi; kotero, ndidanyamula uta ndi muvi, ndi legeni ndi miyala. Ndipo ndidati kwa bambo anga: Kodi ndilowere kuti, kuti ndikapeze chakudya?

24 Ndipo zidachitika kuti iwo adafunsa kwa Ambuye, pakuti adadzichepetsa okha chifukwa cha mawu anga; pakuti ndidayankhula kwa iwo zinthu zambiri mu mphamvu za moyo wanga.

25 Ndipo zidachitika kuti mawu a Ambuye adabwera kwa bambo anga; ndipo adadzudzulidwadi chifukwa cha kung’ung’udza motsutsana ndi Ambuye, kwambiri kuti adatsitsidwa mu chisoni chozama.

26 Ndipo zidachitika kuti mawu a Ambuye adati kwa iwo: Yang’ana pa mpirawo, ndipo ona zinthu zomwe zalembedwa.

27 Ndipo zidachitika kuti pamene bambo anga adaona zinthu zimene zidalembedwa pa mpirawo, adachita mantha ndi kunjenjemera kwambiri, ndiponso abale anga ndi ana aamuna a Ismaeli ndi azikazi awo.

28 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidaona mivi imene idali mumpiramo, kuti imagwira ntchito molingana ndi chikhulupiliro ndi khama ndi kumvera kumene tidapeleka kwa iwo.

29 Ndipo padalembedwanso mawu atsopano pamenepo, amene adali osavuta kuwerenga, amene adatipatsa ife kumvetsa zokhudzana ndi njira za Ambuye; ndipo zidalembedwa ndi kusinthidwa kwa nthawi ndi nthawi, molingana ndi chikhulupiliro ndi khama limene ife tidapereka kwa ichi. Ndipo motero tikuona kuti kudzera mu zinthu zazing’ono Ambuye amabweretsa zinthu zazikulu.

30 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidapita pamwamba pa phiri, molingana ndi chitsogozo chimene chidapelekedwa pa mpirawo.

31 Ndipo zidachitika kuti ndidapha zinyama zakutchire, kotero kuti ndidapeza chakudya cha mabanja athu.

32 Ndipo zidachitika kuti ndidabwelera ku mahema athu, nditanyamula zinyama zomwe ndidapha; ndipo tsopano ataona kuti ndapeza chakudya, chisangalalo chawo chidali chachikulu motani nanga! Ndipo zidachitika kuti adadzichepetsa pamaso pa Ambuye, ndipo adathokoza kwa iye.

33 Ndipo zidachitika kuti tidayambanso kuyenda ulendo wathu, kuyenda pafupifupi njira yomwe tidayambira; ndipo titayenda kwa kanthawi ka masiku ambiri, tidakhomanso mahema athu, kuti tikhaleko kwa ka nthawi.

34 Ndipo zidachitika kuti Ismaeli adamwalira, ndipo adayikidwa pa malo otchedwa Nahomu.

35 Ndipo zidachitika kuti ana aakazi a Ismaeli adalira kwambiri, chifukwa cha imfa ya atate awo, ndi chifukwa cha masautso awo mchipululu; ndipo adang’ung’udza motsutsana ndi bambo anga, chifukwa adawabweretsa iwo kuchoka ku dziko la Yerusalemu, adati: Atate athu amwalira; inde, ndipo tayendayenda kwambiri m’chipululu, ndipo tazunzika masautso aakulu, njala, ludzu ndi kutopa; ndipo pakutha pa kuzunzika konseku tikuyenera kufa ndi njala mchipululu.

36 Ndipo umo ndi momwe adang’ung’udzira motsutsana ndi bambo anga, ndiponso motsutsana ndi ine; ndipo adafuna kuti abwelere ku Yerusalemu.

37 Ndipo Lamani adati kwa Lemueli ndinso kwa ana aamuna a Ismaeli; Taonani, tiyeni tiwaphe atate athu, ndiponso m’bale wathu Nefi, amene wadzitengera yekha kukhala otilamulira ndi mphunzitsi wa ife, okhala azikulu ake.

38 Tsopano, iye akuti Ambuye ayankhula naye, ndiponso kuti angelo amutumikira iye. Koma taonani, ife tikudziwa kuti iye akutinamiza; ndipo amatiuza ife zinthu izi, ndi kuchita zinthu zambiri mwa luso lakuchenjera kwake, kuti apusitse maso athu, kuganiza kuti, mwina, angatitsogolere ife ku chipululu china chachilendo; ndipo akadzatitsogolera ife, akufuna kudzadzipanga yekha kukhala mfumu ndi olamulira pa ife, kuti achite nafe mogwirizana ndi chifuniro chake ndi zomusangalatsa. Ndipo motere ndi momwe m’bale wanga Lamani adatakasa mkwiyo ku mitima yawo.

39 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adali ndi ife, inde, ngakhale mawu a Ambuye adadza ndi kuyankhula mawu ambiri kwa iwo, ndipo adawadzudzula kwambiri; ndipo atadzudzulidwa ndi mawu a Ambuye adabweza mkwiyo wawo, ndipo adalapa machimo awo, kotero kuti Ambuye adatidalitsanso ndi chakudya ndipo ife sitidawonongeke.