Malembo Oyera
1 Nefi 7


Mutu 7

Ana aamuna a Lehi abwelera ku Yerusalemu ndi kukaitana Ismaeli ndi banja lake kuti atsagane nawo pa ulendo wawo—Lamani ndi ena apanduka—Nefi awalimbikitsa abale ake kuti akhale ndi chikhulupiliro mwa Ambuye—Am’manga ndi zingwe, nakonza chiwonongeko chake—Iye amasulidwa ndi mphamvu ya chikhulupiliro—Abale Ake apempha chikhululukiro—Lehi ndi gulu lake apereka nsembe ndi zopereka zopsereza. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano ndikufuna kuti mudziwe, kuti atate anga, Lehi, atatsiriza kunenera za mbewu yawo, zidachitika kuti Ambuye adayankhula kwa iwo kachiwiri, nanena kuti sikudali koyenera kwa iwo, Lehi, kuti atengere banja lawo lokha kuchipululu; koma kuti ana awo aamuna atenge ana aakazi akhale akazi awo, kuti adzutse mbeu kwa Ambuye m’dziko la lonjezano.

2 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adawulamulira iwo kuti ine, Nefi, ndi abale anga, kuti tibwelere ku dziko la Yerusalemu, ndi kubweretsa Ismaeli ndi banja lake kuchipululu.

3 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndi abale anga, tidapitanso m’chipululu kupita ku Yerusalemu.

4 Ndipo zidachitika kuti tidapita ku nyumba ya Ismaeli, ndipo tidapeza kukonderedwa pamaso pa Ismaeli, kotero kuti tidalankhula kwa iye mau a Ambuye.

5 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adafewetsa mtima wa Ismaeli, ndiponso a m’banja lake, moti adanyamuka ulendo wawo ndi ife m’chipululu ku chihema cha atate athu.

6 Ndipo zidachitika kuti pamene timayenda m’chipululu, taonani Lamani ndi Lemueli, ndi awiri a ana akazi a Ismaeli, ndi ana amuna awiri a Ismaeli ndi mabanja awo, adapandukira ife; inde, motsutsana nane ine, Nefi, ndi Samu, ndi abambo awo, Ismaeli, ndi mkazi wake, ndi ana ake aakazi ena atatu.

7 Ndipo zidachitika kuti mukupanduka kumeneku, iwo adakhumba kubwelera ku dziko la Yerusalemu.

8 Ndipo tsopano ine, Nefi, pakumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo, kotero ndidayankhula kwa iwo, nati, inde, ngakhale kwa Lamani ndi kwa Lemueli: Taonani ndinu abale anga akulu, ndipo ndi chifukwa chiyani muli owuma kwambiri m’mitima yanu, ndi akhungu chotere m’malingaliro mwanu, kuti mukusowekera kuti ine, mng’ono wanu, ndilankhule kwa inu, inde, ndi kupeleka chitsanzo kwa inu?

9 Nanga bwanji simudamvera mau a Ambuye?

10 Mudaiwala bwanji kuti mudaona mngelo wa Ambuye?

11 Inde, ndipo zili bwanji kuti mwaiwala zinthu zazikulu zimene Ambuye watichitira ife, m’kupulumutsa ife kuchokera m’manja mwa Labani, ndiponso kuti ife titenge zolemba?

12 Inde ndipo n’chifukwa chiyani kuti mwaiwala kuti Ambuye ali wakutha kuchita zinthu zonse monga mwa chifuniro chake, kwa ana a anthu, ngati iwo akhulupilira mwa iye? Choncho tiyeni tikhale okhulupilika kwa iye.

13 Ndipo ngati tikhala okhulupilika kwa iye, tidzalandira dziko la lonjezano; ndipo mudzadziwa m’nyengo ina yamtsogolo kuti mawu a Ambuye adzakwaniritsidwa ponena za chiwonongeko cha Yerusalemu; pakuti zinthu zonse zimene Ambuye wanena zokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu ziyenera kukwaniritsidwa.

14 Pakuti taonani, Mzimu wa Ambuye adzaleka posachedwapa kulimbana nawo; pakuti taonani, akana aneneri, ndipo Yeremiya adamponya m’ndende. Ndipo adafuna kutenga moyo wa atate anga, kotero kuti adawathamangitsa iwo m’dziko.

15 Tsopano taonani, ndinena kwa inu kuti ngati mungabwelere ku Yerusalemu inunso mudzawonongedwa ndi iwo. Ndipo tsopano, ngati muli nako kusankha, pitani ku dzikolo, ndi kukumbukira mawu amene ine ndikulankhula kwa inu, kuti ngati inu mupita inunso mudzawonongedwa; pakuti motere Mzimu wa Ambuye wandikakamiza ine kuti ndilankhule.

16 Ndipo zidachitika kuti pamene ine, Nefi ndidayankhula mawu awa kwa abale anga, iwo adandikwiyira ine. Ndipo zidachitika kuti adayika manja awo pa ine, pakuti taonani, iwo adali okwiya kwambiri, ndipo adandimanga ine ndi zingwe, pakuti iwo adafuna kutenga moyo wanga, kuti andisiye ine m’chipululu kuti ndidyedwe ndi zilombo zakuthengo.

17 Koma zidachitika kuti ndidapemphera kwa Ambuye, nati: Inu Ambuye, monga mwa chikhulupiliro changa chomwe chiri mwa inu, kodi mudzandipulumutsa ine kuchoka m’manja mwa abale anga; inde, ngakhale kundipatsa mphamvu kuti ndidule zingwe izi zimene ndamangidwa nazo.

18 Ndipo zidachitika kuti pamene ndidanena mawu awa, taonani, zingwezo zidamasuka kuchokera m’manja mwanga ndi m’mapazi anga, ndipo ndidaima pamaso pa abale anga, ndipo ndidayankhula kwa iwo kachiwiri.

19 Ndipo zidachitika kuti iwo adakwiya ndi ine kachiwiri, ndipo adafuna kuyika manja pa ine; koma taonani, m’modzi wa ana aakazi a Ismaeli, inde, ndiponso amake, ndi mmodzi wa ana aamuna a Ismaeli, adachondelera abale anga, kotero kuti adafewetsa mitima yawo; ndipo iwo adasiya kuyesetsa kuchotsa moyo wanga.

20 Ndipo zidachitika kuti iwo adali achisoni, chifukwa cha zoipa zawo, kotero kuti adagwada pamaso panga; ndipo adandidandaulira kuti ndiwakhululukire zomwe adandichitira.

21 Ndipo zidachitika kuti ndidawakhululukira moona mtima zonse zimene adachita, ndipo ndidawalimbikitsa kuti apemphere kwa Ambuye Mulungu wawo kuti awakhululukire. Ndipo zidachitika kuti iwo adachita momwemo. Ndipo atatha kupemphera kwa Ambuye tidayendanso ulendo wathu wopita ku chihema cha atate athu.

22 Ndipo zidachitika kuti ife tidafika ku chihema cha atate athu. Ndipo Ine ndi abale anga ndi nyumba yonse ya Ismaeli titabwera ku chihema cha atate anga, iwo adathokoza kwa Ambuye Mulungu wawo; ndipo adapereka nsembe ndi zopereka zopsereza.