Malembo Oyera
1 Nefi 20


Mutu 20

Ambuye avumbulutsa zolinga Zake kwa Israeli—Israeli wasankhidwa m’ng’anjo ya masautso ndipo adzatuluka kuchokera ku Babulo—Fananizani Yesaya 48. Mdzaka dza pafupifupi 588–570 Yesu asadabadwe.

1 Mvetserani ndi kumva izi, inu a nyumba ya Yakobo, amene amatchedwa ndidzina la Israeli, ndipo atuluka m’madzi a Yuda, kapena m’madzi a ubatizo, amene amalumbira pa dzina la Ambuye, ndipo amatchula Mulungu wa Israeli, koma samalumbira muchoonadi kapena muchilungamo.

2 Ngakhale zili choncho, amadzitcha okha a mumzinda woyera, koma sakhazikika pa Mulungu wa Israeli, amene ali Ambuye wa makamu; Inde, Ambuye wa makamu ndilo dzina lake.

3 Taonani, ndidanena zinthu zakale kuyambira pachiyambi; ndipo zidatuluka m’kamwa mwanga, ndipo ndidazionetsa. Ndidazionetsa modzidzimutsa.

4 Ndipo ndidazichita popeza ndidadziwa kuti uli wouma khosi, ndi khosi lako ndi mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako ndi mkuwa;

5 Ndipo ngakhale kuyambira pa chiyambi ndidakufotokozerani; zisadachitike ndidakuonetsani; ndipo ndidakuonetsani pa kuwopa kuti munganene—Fano langa lazichita, ndi fano langa losema; ndi chifaniziro changa chosungunula chazilamulira.

6 Inu mwaona ndi kumva zonsezi; simuzilengeza a kodi? Ndipo kuti ndakuwonetsani zinthu zatsopano kuyambira tsopano, ngakhale zinthu zobisika, ndipo simudazidziwe.

7 Zalengedwa tsopano, ndipo osati kuchokera ku chiyambi, ngakhale lisadadze tsiku limene iwe sudazimve izo zidalengezedwa kwa iwe, kuti ungadzanene kuti—Taonani ndidazidziwa.

8 Inde, ndipo iwo sudamve; inde, iwe sudadziwe; inde, kuyambira nthawi imeneyo khutu lako lidali lisadatseguke; pakuti ndidadziwa kuti udzachita zachinyengo kwambiri, ndipo udatchedwa wolakwa kuyambira m’mimba.

9 Komabe, chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndipo chifukwa cha matamando anga ndidzadziletsa kwa iwe, kuti ndisakuchotse pamaso panga.

10 Pakuti, taona, ndakuyenga, ndakusankha iwe mung’anjo ya masautso.

11 Chifukwa cha ine, inde, chifukwa cha Ine ndidzachita izi, pakuti sindidzalola dzina langa kuti liyipitsidwe, ndipo sindidzapereka ulemelero wanga kwa wina.

12 Mvetserani ine, Yakobo, ndi Israeli oitanidwa anga, pakuti Ine ndine; Ine ndine woyamba, ndipo inenso ndine wotsiriza.

13 Dzanja langanso lidaika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja latambasula kumwamba. Ndimaziitana ndipo zimaimilira pamodzi.

14 Nonse inu, sonkhanani nokha; ndi kumva; ndani mwa iwo adalengeza izi kwa iwo? Ambuye wamkonda; inde, ndipo adzakwaniritsa mawu ake omwe adalengezetsa kudzera mwa iwo; ndipo adzachita zomkondweretsa pa Babulo, ndipo mkono wake udzafika pa Akaldeya.

15 Ndiponso, atero Ambuye; Ine Ambuye, inde, ndayankhula; inde, ndamuitana kuti anene, Ndabwera naye, ndipo adzakometsa njira yake.

16 Bwerani pafupi ndi Ine; Sindidayankhule mwachinsinsi; kuyambira pachiyambi, kuyambira nthawi imene chidanenedwa ndayankhula; ndipo Ambuye Mulungu, ndi Mzimu wake, wandituma.

17 Ndipo akutero Ambuye, Muwomboli wako, Woyera wa Israeli; Ndamutuma, Ambuye Mulungu wanu, amene amakuphunzitsani kuti mupindule, amene amakutsogolerani m’njira imene mukuyenera kuyendamo, wachita izi.

18 O kuti ukadamvera malamulo anga—pamenepo mtendere wako ukadakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako ngati mafunde a nyanja.

19 Mbewu yakonso idakhala ngati mchenga; ana a m’mimba mwako ngati miyala yake; dzina lake silidayenera kuchotsedwa kapena kuwonongedwa pamaso panga.

20 Tulukani inu mu Babulo, thawani kwa Akaldeya, ndi mawu oyimbira lengezani, nenani izi, nenani kumathero a dziko; nenani; Ambuye wawombola mtumiki wake Yakobo.

21 Ndipo sadamve ludzu; adawatsogolera m’zipululu; adapangitsa madzi kuti atuluke muthanthwe chifukwa cha iwo; adang’amba thanthwe ndipo madzi adatuluka.

22 Ndipo ngakhale iye wachita zonse izi, ndipo zazikulunso, palibe mtendere, atero Ambuye, kwa oipa.