Malembo Oyera
1 Nefi 17


Mutu 17

Nefi alamulidwa kuti amange ngalawa—Abale ake atsutsana naye—Awalimbikitsa iwo pakufotokoza za mbiri ya zochita za Mulungu ndi Israeli—Nefi adzadzidwa ndi mphamvu ya Mulungu—Abale ake aletsedwa kumukhudza iye, kuwopa kuti angafote ngati bango louma. Mdzaka dza pafupifupi 592–591 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti tidanyamukanso ulendo wathu wa m’chipululu; ndipo tidayenda kufupi ndi chakum’mawa kuyambira nthawi imeneyo. Ndipo tidayenda ndi kudutsa zosautsa zambiri mu chipululu; ndipo akazi athu adabala ana mchipululu.

2 Ndipo aakulu adali madalitso a Ambuye pa ife, kuti pamene tidali kukhala ndi moyo pa nyama yaiwisi m’chipululu, akazi athu adayamwitsa ana awo mochuluka, ndipo adali amphamvu, inde, ngakhale ngati amuna; ndipo adayamba kuyenda ulendo wawo mopanda zong’ung’udza.

3 Ndipo kotero ife tikuona kuti malamulo a Mulungu ayenera kukwaniritsidwa. Ndipo ngati ziri kuti ana a anthu asunga malamulo a Mulungu iye amawasamalira iwo, ndi kuwalimbitsa iwo, ndi kupereka njira imene iwo angathere kukwaniritsira chinthu chimene iye adawalamulira iwo; kotero, adatipatsa njira pamene tidali kukhala m’chipululu.

4 Ndipo tidakhala kwa nthawi ya zaka zambiri, inde, ngakhale zaka zisanu ndi zitatu mu chipululu.

5 Ndipo tidafika ku dziko limene tinkalitcha Lochuluka, chifukwa cha zipatso zake zambiri komanso uchi wa kuthengo; ndipo zinthu zonsezi zidakonzedwa ndi Ambuye kuti ife tisawonongeke. Ndipo tidaona nyanja, imene tidaitcha Ireyantumu, imene, kuyitanthauzira, ndi madzi ambiri.

6 Ndipo zidachitika kuti tidakhoma mahema athu pafupi ndi gombe la nyanja; ndipo ngakhale tidavutika ndi masautso ambiri ndi zovuta zambiri, inde, ngakhale zochuluka kotero kuti sitingathe kuzilemba zonse, tidakondwera kwakukulu pamene tidafika ku gombe la nyanja, ndipo malowo tidawatcha Lochuluka, chifukwa cha zipatso zake zambiri.

7 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, nditakhala m’dziko Lochuluka kwa nthawi ya masiku ambiri, mawu a Ambuye adadza kwa ine, kuti; Nyamuka, ndipo ukwere m’phiri. Ndipo zidachitika kuti ndidanyamuka ndikukwera m’phiri, ndipo ndidalilira kwa Ambuye.

8 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adayankhula kwa ine, kuti: Iwe udzamanga ngalawa, motsatira njira imene ine ndidzakusonyeze iwe, kuti ine ndidzathe kunyamula anthu ako kuwoloka madzi awa.

9 Ndipo ine ndidati: Ambuye, ndipite kuti, kuti ndikapeze miyala yoti ndisungunule, kuti ndipange zida zomangira ngalawayo motsatira njira yomwe mwandiwonetserayi?

10 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adandiuza kumene ine ndikuyenera kupita kukapeza miyala, kuti ine ndithe kupanga zida zogwilira ntchito.

11 Ndipo zidachitika kuti Ine, Nefi, ndidapanga mvuvu wouzira moto wa zikopa za nyama; ndipo nditapanga mvuvu, kuti ndikhale ndi pouzilira moto, ndidamenyetsa miyala iwiri pamodzi kuti ndiyatse moto.

12 Pakuti Ambuye adali asadatilore kuti tisonkhe moto wochuluka, pamene tidali kuyenda m’chipululu; pakuti adati, Ndidzachititsa chakudya chanu kukhala chokoma, kuti musamachiphike;

13 Ndipo ndidzakhalanso kuunika kwanu m’chipululu; ndipo ndidzakonza njira pamaso panu, ngati kuli kuti mudzasunga malamulo anga; pamene inu mudzasunga malamulo anga inu mudzatsogozedwa kupita ku dziko lolonjezedwa; ndipo mudzadziwa kuti ndi Ine amene mukutsogozedwa naye.

14 Inde, ndipo Ambuye adanenanso kuti, Mukadzafika m’dziko lolonjezedwa, mudzadziwa kuti Ine, Ambuye, ndine Mulungu; ndi kuti Ine, Ambuye, ndidawombola inu ku chiwonongeko; inde, kuti ndidakutulutsani m’dziko la Yerusalemu.

15 Kotero, Ine, Nefi, ndidalimbika kusunga malamulo a Ambuye, ndipo ndidawalimbikitsa abale anga ku kukhulupirika ndi khama.

16 Ndipo zidachitika kuti ndidapanga zida zogwilira ntchito za mwala umene ndidausungunula kuchokera m’thanthwe.

17 Ndipo pamene abale anga adaona kuti ndidali pafupi kupanga ngalawa, adayamba kung’ung’udza motsutsana nane, kuti: M’bale wathu ndi wopusa, chifukwa akuganiza kuti akhoza kupanga ngalawa; inde, ndipo iye akuganizanso kuti akhoza kuwoloka madzi aakulu awa.

18 Ndipo motero abale anga adadandaula motsutsa ine, ndipo adakhumba kuti asagwire ntchito, pakuti sadakhulupilire kuti ndingamange ngalawa; kapena sadakhulupilire kuti ndidalangizidwa ndi Ambuye.

19 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidali wachisoni kwambiri chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo; ndipo tsopano pamene iwo anawona kuti ndidayamba kukhala wachisoni adasekera m’mitima yawo, moti adakondwera chifukwa cha ine, kuti: Ife tidadziwa kuti iwe sukadatha kupanga ngalawa, pakuti ife tidadziwa kuti iwe udaperewera mu chiweruzo; kotero, iwe sungathe kukwaniritsa ntchito yaikulu chonchi.

20 Ndipo uli ngati atate athu, osocheretsedwa ndi zolingalira zopusa za mtima wawo; inde, atitsogolera ife kuchokera m’dziko la Yerusalemu, ndipo tayenda m’chipululu zaka zambirizi; ndipo akazi athu agwira ntchito, kukhala ali ndi pakati papakulu; ndipo adabala ana m’chipululu ndi kuvutika zinthu zonse, kupatula imfa; ndipo kukadakhala bwino kuti iwo amwalire asadatuluke mu Yerusalemu kusiyana ndi kuvutika zowawa izi.

21 Taonani, zaka zambiri izi ife takhala tikuvutika mu chipululu, nthawi yomwe ife tikadatha kumasangalala ndi chuma chathu ndi dziko la cholowa chathu; inde, ndipo tikadatha kukhala okondwa.

22 Ndipo tikudziwa kuti anthu amene adali m’dziko la Yerusalemu adali anthu wolungama; pakuti adasunga malamulo ndi ziweruzo za Ambuye, ndi malamulo ake onse, monga mwa chilamulo cha Mose; kutero, tikudziwa kuti iwo ali anthu wolungama; ndipo atate athu awaweruza, ndi kutisokeretsa ife chifukwa tidamvera mawu awo; inde, ndipo m’bale wathu ali monga iwo. Ndipo pa kayankhulidwe kotere abale anga adang’ung’udza ndi kudandaula motsutsana nafe.

23 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidayankhula kwa iwo, nati: Kodi mukukhulupilira kuti makolo athu, omwe adali ana a Israeli, akadatsogozedwa kuchokera m’manja mwa Aigupto ngati sadamvere mawu a Ambuye?

24 Inde, kodi mukuganiza kuti akadatsogozedwa kutuluka mu ukapolo, ngati Ambuye sadalamulire Mose kuti awatsogolere kutuluka mu ukapolo?

25 Tsopano mukudziwa kuti ana a Israeli adali mu ukapolo; ndipo mukudziwa kuti adalemedwa ndi ntchito, zomwe zidali zowawa kuti zigwilidwe; kotero, mukudziwa kuti chikuyenera kukhala chinthu chabwino kwa iwo, kuti atulutsidwe mu ukapolo.

26 Tsopano inu mukudziwa kuti Mose adalamulidwa ndi Ambuye kuchita ntchito yaikulu imeneyo; ndipo mukudziwa kuti ndi mawu ake madzi a Nyanja Yofiira adagawanika uku ndi uko, ndipo adawoloka pouma.

27 Koma inu mukudziwa kuti Aigupto adamizidwa mu Nyanja Yofiira, amene adali ankhondo a Farao.

28 Ndipo inu mukudziwa kuti iwo adadyetsedwa ndi mana m’chipululu.

29 Inde, ndipo inunso mukudziwa kuti Mose, ndi mawu ake molingana ndi mphamvu ya Mulungu imene idali mwa iye, adakantha thanthwe, ndipo madzi adatuluka, kuti ana a Israeli athe kuthetsa ludzu lawo.

30 Ndipo ngakhale iwo amatsogozedwa, Ambuye Mulungu wawo, Muwomboli wawo, akupita patsogolo pawo, akuwatsogolera iwo usana ndi kupereka kuwala kwa iwo usiku, ndi kuchita zinthu zonse kwa iwo zimene zidali zoyenera kuti munthu alandire, iwo adaumitsa mitima yawo ndipo adachititsa khungu malingaliro awo, ndi kunyoza Mose ndi Mulungu woona ndi wamoyo.

31 Ndipo zidachitika kuti molingana ndi mawu ake adawawononga; ndipo molingana ndi mawu ake adawatsogolera; ndipo molingana ndi mawu ake adawachitira iwo zinthu zonse; ndipo palibe kanthu kadachitidwa koma mwa mawu ake.

32 Ndipo atawoloka mtsinje wa Yordani adawapanga iwo amphamvu pakuthamangitsa ana a dzikolo, inde pa kuwabalalitsa iwo ku chiwonongeko.

33 Ndipo tsopano, kodi mukuganiza kuti ana a dzikoli, amene adali m’dziko la lonjezano, amene adathamangitsidwa ndi makolo athu, kodi mukuganiza kuti adali wolungama? Taonani, ndinena kwa inu, Ayi.

34 Mukuganiza kuti makolo athu akadakhala osankhidwa mochuluka kuposa iwo akadakhala wolungama? Ndinena kwa inu, Ayi.

35 Taonani, Ambuye amaona anthu onse kukhala amodzi; amene ali olungama amakondedwa ndi Mulungu. Koma taonani, anthu awa adali atakana mawu aliwonse a Mulungu, ndipo iwo adali atakhwima mu kusaweruzika; ndipo chidzalo cha mkwiyo wa Mulungu chidali pa iwo; ndipo Ambuye adatembelera dziko motsutsana ndi iwo, ndipo adalidalitsa kwa makolo athu; inde, iye adatembelera ilo motsutsana ndi iwo ku chiwonongeko chawo, ndipo iye adadalitsa ilo kwa makolo athu kuti apeze mphamvu pa ilo.

36 Taonani, Ambuye adalenga dziko lapansi kuti likhalidwemo; ndipo adalenga ana ake kuti likhale lawo.

37 Ndipo iye amadzutsa mtundu wolungama, nawononga mitundu ya woipa.

38 Ndipo amatsogoza olungama ku maiko a mtengo wapatali, ndipo oipa amawawononga, ndi kutembelera dziko chifukwa cha iwo.

39 Amalamulira kumwamba, chifukwa ndi mpando wake wachifumu, ndipo dziko lapansili ndi popondera mapazi ake.

40 Ndipo amakonda iwo amene akufuna kuti iye akhale Mulungu wawo. Taonani, adakonda makolo athu, ndipo adapanga pangano ndi iwo, inde, ngakhale Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo; ndipo adakumbukira mapangano amene adapanga; kotero, adawaturutsa m’dziko la Igupto.

41 Ndipo adawapsinja m’chipululu ndi ndodo yake; pakuti adaumitsa mitima yawo, monganso inu mwaumitsira; ndipo Ambuye adawapsinja chifukwa cha kusaweruzika kwawo. Adatumiza njoka zamoto zouluka pakati pawo; ndipo pamene adalumidwa adakonza njira yoti achiritsidwe; ndipo ntchito imene adayenera kuichita idali kuyang’ana; ndipo chifukwa cha kuphweka kwa njirayo, kapena kusavuta kwake, padali ambiri amene adawonongeka.

42 Ndipo iwo adaumitsa mitima yawo nthawi ndi nthawi, ndipo adanyoza Mose, ndiponso Mulungu; komabe, mukudziwa kuti adatsogozedwa ndi mphamvu yake yosayerekezereka kulowa m’dziko la lonjezano.

43 Ndipo tsopano, zitachitika zinthu zonsezi, nthawi yafika yoti iwo akhala oipa, inde, pafupifupi kupsa; ndipo sindikudziwa, koma ali patsikuli pafupi kuwonongedwa; pakuti ndikudziwa kuti tsikulo likuyenera ndithudi kubwera lomwe iwo akuyenera kuwonongedwa, kupatula ochepa okha, amene adzatsogozedwa kupita ku ukapolo.

44 Kotero, Ambuye adalamula atate anga kuti apite kuchipululu; ndipo Ayuda adafunanso kuchotsa moyo wawo; inde, ndipo inunso mwafuna kutenga moyo wawo; kotero, muli akupha m’mitima mwanu ndipo muli ngati iwo.

45 Muli ofulumira kuchita mphulupulu, koma ochedwa kukumbukira Ambuye Mulungu wanu. Inu mwaona mngelo, ndipo adayankhula nanu; inde, mudamva mawu ake ku nthawi ndi nthawi; ndipo adayankhula ndi inu m’mawu aang’ono onong’oneza, koma mudasiya kumva, kotero kuti simudamve mawu ake; kotero, iye wayankhula kwa inu ngati mawu a bingu, limene lidapangitsa dziko lapansi kugwedezeka ngati kuti lidukane pakati.

46 Ndipo inunso mukudziwa kuti ndi mphamvu ya mawu ake amphamvu zonse akhonza kuchititsa dziko lapansi kutha; inde, ndipo mukudziwa kuti ndi mawu ake atha kupangitsa malo onyambalaza kusalazika, ndi malo osalazika adzasweka. Kodi, ndiye, nchifukwa chiyani kuti inu muli owuma mitima yanu?

47 Taonani, moyo wanga wang’ambika ndi zowawitsa chifukwa cha inu, ndipo mtima wanga ukuwawa; Ndikuopa kuti mungadzatayidwe kwamuyaya. Taonani, ndadzadzidwa ndi Mzimu wa Mulungu, kotero kuti thupi langa lilibe mphamvu.

48 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene ndidayankhula mau awa adandikwiyira, nafuna kundiponya m’kuya kwa nyanja; ndipo pamene adabwera kudzaika manja awo pa ine ndidayankhula kwa iwo, nati: M’dzina la Mulungu Wamphamvu zonse, ndikukulamulirani kuti musandikhudze, pakuti ndadzadzidwa ndi mphamvu ya Mulungu, ngakhale mpaka kugwira thupi langa; ndipo iye amene adzaika manja ake pa ine adzafota ngakhale monga bango louma; ndipo adzakhala ngati wopanda pake pamaso pa mphamvu ya Mulungu, pakuti Mulungu adzamkantha iye.

49 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidanena kwa iwo kuti sakuyenera kung’ung’udzanso motsutsa atate awo; kapena kukana kundigwilira ntchito ine, pakuti Mulungu adandilamulira ine kuti ndipange ngalawa.

50 Ndipo Ndidati kwa iwo: ngati Mulungu akadandilamula ine kuchita zinthu zonse ndikadazichita. Ngati angandilamulire ine kuti ndinene kwa madzi awa, khala dothi, adzakhala dothi; ndipo ngati ndingazinene, zingachitike.

51 Ndipo tsopano, ngati Ambuye ali ndi mphamvu yaikulu yotere, ndipo wachita zozizwitsa zambiri pakati pa ana a anthu, nanga bwanji kuti sangandiphunzitse ine kuti ndimange ngalawa?

52 Ndipo zidachitika kuti Ine, Nefi, ndidanena zinthu zambiri kwa abale anga, kotero kuti iwo adagonjetsedwa ndipo sadathe kutsutsana nane; kapena sadayerekeze kuika manja awo pa ine, kapena kundikhudza ine ndi dzala dzawo, ngakhale kwa nthawi ya masiku ambiri. Tsopano iwo sadayerekeze kuchita izi kuopa kuti angafote pamaso panga, udali wamphamvu kwambiri Mzimu wa Mulungu; ndipo kotero izo zidawachitikira iwo.

53 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adati kwa ine, Tatambasuliranso dzanja lako kwa abale ako, ndipo sadzafota pamaso pako, koma ndidzawagwira nyesi, adatero Ambuye, ndipo ndidzachita izi, kuti adziwe kuti Ine ndine Ambuye Mulungu wawo.

54 Ndipo zidachitika kuti ndidatambasulira dzanja langa kwa abale anga, ndipo sadafote pamaso panga; koma Ambuye adawagwedeza, monga mwa mawu amene adanena.

55 Ndipo tsopano, iwo adati: Ife tikudziwa ndithu kuti Ambuye ali ndi iwe, pakuti ife tikudziwa kuti ndi mphamvu ya Ambuye yomwe yatigwedeza. Ndipo iwo adagwa pansi pamaso panga, ndipo adali pafupi kundilambira ine, koma ine sindidawalore iwo, nanena: Ine ndine m’bale wanu, inde, ngakhale mng’ono wanu; kotero, lambirani Ambuye Mulungu wanu, ndipo lemekezani atate wanu ndi amayi wanu, kuti masiku anu achuluke m’dziko limene Ambuye Mulungu wanu adzakupatsani inu.