Malembo Oyera
1 Nefi 6


Mutu 6

Nefi alemba za zinthu za Mulungu—Cholinga cha Nefi ndi kukopa anthu kuti abwere kwa Mulungu wa Abrahamu ndi kupulumutsidwa. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano ine, Nefi, sindikupeleka mbiri ya chibadwidwe cha makolo anga m’gawo ili la zolemba zanga; ndipo sindikupeleka pa nthawi iliyonse imene ndikulemba pa mapalewa; pakuti ikuperekedwa mu zolembedwa zimene zasungidwa ndi atate anga; kotero, sindilemba mu ntchito iyi.

2 Pakuti kwandikwanira kunena kuti ndife ana a Yosefe.

3 Ndipo zilibe kanthu kwa ine kuti ine ndiri wapadera kuti ndipereke mbiri yokwanira ya zinthu zonse za atate anga, pakuti izo sizingalembedwe pa mapale amenewa, pakuti ndikhumba malo kuti ndilembemo za zinthu za Mulungu.

4 Pakuti chidzalo cha cholinga changa ndi chakuti ndikope anthu kuti abwere kwa Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, kuti apulumutsidwe.

5 Pachifukwa ichi, zomwe zimakondweretsa dziko lapansi sindilemba, koma zomwe zimakondweretsa Mulungu ndi kwa iwo omwe sali a dziko lapansi.

6 Kotero, ndidzapereka lamulo kwa mbewu yanga, kuti iwo sadzaika m’mapale amenewa zinthu zimene siziri zofunikira kwa ana a anthu.