Malembo Oyera
1 Nefi 11


Mutu 11

Nefi aona Mzimu wa Ambuye ndipo aonetsedwa masomphenya a mtengo wa moyo—Aona mayi wa Mwana wa Mulungu ndi kuphunzira za kudzichepetsa kwa Mulungu—Aona ubatizo, utumiki, ndi kupachikidwa pa mtanda kwa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu—Aonanso maitanidwe ndi utumiki wa atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Pakuti zidachitika kuti nditatha kukhumbira kudziwa za zinthu zomwe bambo anga adaona, ndi kukhulupilira kuti Ambuye akhonza kundidziwitsa ine za zimenezi, pamene ndidakhala ndikulingalira mumtima mwanga ndidagwidwa ndi mzimu wa Ambuye, inde kuphiri lalitali, lomwe sindidalionepo, ndipo limene sindidaikepo phanzi langa.

2 Ndipo Mzimu udati kwa ine: Taona, kodi ukukhumba chiyani?

3 Ndipo ndidati: Ndikhumba kuona zinthu zomwe bambo anga adaona.

4 Ndipo Mzimu udati kwa ine: Kodi ukukhulupilira kuti bambo ako adaona mtengo omwe akunenawo?

5 Ndipo ndidati: Inde, inu mukudziwa kuti ine ndimakhulupilira mawu onse abambo anga.

6 Ndipo pamene ndidayankhula mawu awa, Mzimu udafuula ndi mawu okweza, nati: Hosana kwa Ambuye, Mulungu wam’mwambamwamba: pakuti iye ali Mulungu wadziko lonse lapansi, inde ngakhale pamwamba pa onse. Ndipo odala ndi iwe, Nefi, chifukwa umakhulupilira mwa Mwana wa Mulungu wam’mwambamwamba: kotero, iwe udzaona zinthu zimene wazikhumba.

7 Ndipo taona chinthu ichi chidzapatsidwa kwa iwe ngati chizindikiro, kuti utatha kuona mtengo umene udabala chipatso chomwe bambo ako adalawa, udzaonanso munthu akutsika kuchoka kumwamba, ndipo iwe udzamuchitira umboni, ndipo ukadzamuchitira umboni, udzachitira umboni kuti iye ndi Mwana wa Mulungu.

8 Ndipo zidachitika kuti Mzimu adati kwa ine: Yang’ana! Ndipo ndidayang’ana ndi kuona mtengo; ndipo udali ngati mtengo omwe bambo anga adaona; ndipo kukongola kwake kudali kwapatali kwambiri, inde kukongola koposa zonse; ndipo kuyera kwake kudaposa kuyera kwa matalala.

9 Ndipo zidachitika kuti nditaona mtengowo, ndidati kwa Mzimuwo: Ndaona kuti mwandionetsa mtengo umene uli wapatali kuposa yonse.

10 Ndipo adati kwa ine: Kodi ukukhumba chiyani?

11 Ndipo ine ndidati kwa iye: kudziwa tanthauzo lake—pakuti ndinkayankhula naye ngati mmene amayankhulira munthu; pakuti ndidaona kuti iye adali m’maonekedwe a munthu: komabe, ndidadziwa kuti udali Mzimu wa Ambuye; ndipo udayankhula kwa ine ngati munthu akuyankhula ndi munthu mzake.

12 Ndipo zidachitika kuti iye adati kwa ine: Yang’ana! Ndipo ndidayang’ana ngati kuti ndikumuyang’ana iye, koma sindidamuone: pakuti adali atachoka pamaso panga.

13 Ndipo zidachitika kuti ndidayang’ana ndipo ndidaona mzinda waukulu wa Yerusalemu, komanso mizinda ina. Ndipo ndidaona mzinda wa Nazareti; ndipo mumzinda wa Nazareti ndidaonamo namwali, ndipo adali wokongola ndi oyera ndithu.

14 Ndipo zidachitika kuti ndidaona kumwamba kukutseguka: ndipo mngelo adabwera ndikuima pamaso panga; ndipo adati kwa ine: Nefi, kodi ukuona chiyani?

15 Ndipo ine ndidati kwa iye: Namwali, okongola kwambiri ndi oyera kuposa anamwali onse.

16 Ndipo adati kwa ine: kodi ukudziwa kudzichepetsa kwa Mulungu?

17 Ndipo ine ndidati kwa iye: Ndikudziwa kuti amakonda ana ake; komabe, sindidziwa tanthauzo la zinthu zonse.

18 Ndipo iye adati kwa ine: Taona, namwali amene ukumuonayo ndi mayi wa Mwana wa Mulungu, monga mwa thupi.

19 Ndipo zidachitika kuti ndidaona kuti adanyamulidwa mu Mzimu; ndipo atanyamulidwa mu Mzimu kwa kanthawi, mngelo adayankhula nane, nati: Yang’ana!

20 Ndipo ndidayang’ana ndikuona namwali kachiwiri, atanyamula mwana m’manja mwake.

21 Ndipo mngelo adati kwa ine: Taona Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, inde, ngakhale Mwana wa Atate wa Muyaya! Kodi ukudziwa tanthauzo la mtengo omwe bambo ako adaona?

22 Ndipo ndidamuyankha iye, nati: Inde, ndichikondi cha Mulungu, chimene chidzitsanulira chokha m’mitima ya ana a anthu, kotero, ndichinthu chokhumbirika kuposa zinthu zonse.

23 Ndipo iye adayankhula kwa ine, nati: Inde, ndi chosangalatsa kwambiri kwa moyo.

24 Ndipo atatha kunena mawu awa, adati kwa ine: Yang’ana! Ndipo ndidayang’ana, ndipo ine ndidaona Mwana wa Mulungu akuyenda pakati pa ana a anthu; ndipo ndidaona ambiri akugwa pa mapazi ake ndi kumulambira.

25 Ndipo zidachitika kuti ndidaona kuti ndodo ya chitsulo, imene bambo anga adayiona, adali mawu a Mulungu, amene adatsogolera ku kasupe wamadzi amoyo, kapena ku mtengo wa moyo; amene madzi ake ali chithunzithunzi cha chikondi cha Mulungu; ndiponso ndidaona kuti mtengo wa moyo udali chithunzithunzi cha chikondi cha Mulungu.

26 Ndipo mngelo adati kwa ine kachiwiri: Yanga’ana ndipo taona kudzichepetsa kwa Mulungu!

27 Ndipo ndidayang’ana ndipo ndidaona Muwomboli wa dziko lapansi, amene bambo anga adakamba za iye; ndiponso ndidaona mneneri amene adzakonze njira iye asadafike. Ndipo Mwana wa Nkhosa wa Mulungu adapita ndi kubatizidwa ndi iye; ndipo atatha kubatizidwa, ndidaona kumwamba kutatseguka, ndipo Mzimu Woyera adatsika kuchoka kumwamba ndikukhala pa iye ngati nkhunda.

28 Ndipo ndidaona kuti adayamba kutumikira kwa anthu, ndi mphamvu ndi ulemelero waukulu; ndipo khwimbi la anthu lidasonkhana pamodzi ndikumvera iye; ndipo ndidaona kuti adamuthamangitsa pakati pawo.

29 Ndipo ndidaonanso ena khumi ndi awiri akumutsata iye. Ndipo zidachitika kuti adatengedwa mu Mzimu kuchoka pamaso panga, ndipo sindidawaonenso.

30 Ndipo zidachitika kuti mngelo adayankhula nanenso, nati: Yang’ana! Ndipo ndidayang’ana, ndipo ine ndidaona kumwamba kutatseguka kachiwiri, ndipo ndidaona angelo akutsikira pa ana a anthu; ndipo adawatumikira iwo.

31 Ndipo adayankhula kwa ine kachiwiri, nati: Yang’ana! Ndipo ndidayang’ana, ndipo ndidaona Mwana wa Nkhosa wa Mulungu akuyenda pakati pa ana a anthu. Ndipo ndidaona khwimbi la anthu amene ankadwala, ndi omwe amene ankasautsika ndi mitundu yonse ya matenda, ndi ziwanda ndi mizimu yonyansa; ndipo mngelo adayankhula ndi kuonetsa zinthu zonsezi kwa ine. Ndipo adachilitsidwa ndi mphamvu ya Mwana wa Nkhosa wa Mulungu; ndipo ziwanda ndi mizimu yonyansa zidatulutsidwa.

32 Ndipo zidachitika kuti mngelo adayankhula nane kachiwiri, nati: Yang’ana! Ndipo ndidayang’ana ndipo ine ndidaona mwana wa Nkhosa wa Mulungu, kuti adatengedwa ndi anthu; inde, Mwana wa Mulungu wosatha adaweruzidwa ndi dziko lapansi; ndipo ndidaona ndikuchitira umboni.

33 Ndipo ine, Nefi, ndidaona kuti adapachikidwa pa mtanda ndi kuphedwa chifukwa cha machimo adziko lapansi.

34 Ndipo ataphedwa ndidaona khwimbi la mdziko lapansi, kuti adali atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi atumwi a Mwana wa Nkhosa; pakuti makumi awiri ndi asanu wo adatchedwa choncho ndi mngelo wa Ambuye.

35 Ndipo khwimbi la dziko lidasonkhana pamodzi; ndipo ndidaona kuti lidali mu chinyumba chachikulu komanso chotakasuka, ngati chinyumba chomwe bambo anga adaona. Ndipo mngelo wa Ambuye adayankhula nane kachiwiri, nati: Taonani dziko lapansi ndi nzeru zake; inde, taonani nyumba ya Israeli yasonkhana pamodzi kuti imenyane ndi atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa.

36 Ndipo zidachika kuti ndidaona ndi kuchitira umboni, kuti chinyumba chachikulu ndi chotakasuka chidali kudzikweza kwa dziko lapansi; ndipo chidagwa, ndipo kugwa kwake kudali kwakukulu. Ndipo mngelo wa Ambuye adayankhula kwa ine kachiwiri, nati: Kumeneku kudzakhala kugwa kwa maiko, mitundu, zinenero ndi anthu, amene adzamenyane ndi atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa.