Malembo Oyera
1 Nefi 13


Mutu 13

Nefi aona m’masomphenya mpingo wa mdyerekezi utayikidwa pakati pa Amitundu, Kutulukira ndi kulamulira dziko la Amerika, kutayika kwa zigawo zomveka komanso zamtengo wapatali za mu Baibulo, zotsatila zake za mpatuko wa amitundu, kubwenzeretsedwa kwa uthenga wabwino, Kubwera kwa malembo oyera a masiku otsiriza, ndi kumangidwa kwa Ziyoni. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti mngelo adayankhula nane, nati: Yang’ana! Ndipo ndidayang’ana ndikuona maiko ndi maufumu.

2 Ndipo mngelo adati kwa ine: Kodi ukuona chiyani? Ndipo ndidati: Ndikuona maiko ndi maufumu.

3 Ndipo iye adati kwa ine: Awa ndiwo maiko ndi maufumu a Amitundu.

4 Ndipo zidachitika kuti ndidaona pakati pa maiko a Amitundu kupangidwa kwa mpingo waukulu.

5 Ndipo mngelo adati kwa ine: Taona kupangidwa kwa mpingo umene uli wonyasa kuposa mipingo ina yonse, umene umapha oyera mtima a Mulungu, inde, ndikuwazunza ndi kuwamanga iwo, ndi kuwasenzetsa goli la chitsulo, ndikuwatengera iwo ku ukapolo.

6 Ndipo zidachitika kuti ndidaona mpingo wonyasa waukuluwu, ndipo ndidaona mdyerekezi kuti iye adali woyambitsa wake.

7 Ndipo ndidaona golide, ndi siliva ndi silika, ndi nsalu zofiira, ndi nsalu zopota bwino, ndi zovala zamtengo wapali zamitundu yonse ndipo ndidaona achigololo ambiri.

8 Ndipo mngelo adayankhula nane, nati: Taona golide, ndi siliva, ndi silika, ndi nsalu zofiira, ndi nsalu zopota bwino, ndi zovala zamtengo wapali, ndi achigololo, ndizo zokhumba za mpingo waukulu ndi woyipitsitsa.

9 Ndiponso kuti atamandidwe ndi dziko lapansi, iwo amaononga oyera mtima a Mulungu, ndi kuwapititsa mu ukapolo.

10 Ndipo zidachitika kuti ndidayang’ana ndikuona madzi ambiri; ndipo adagawanitsa Amitundu kwa mbewu ya azibale anga.

11 Ndipo zidachitika kuti mngelo adati kwa ine: Taona mkwiyo wa Mulungu uli pa mbewu ya abale ako.

12 Ndipo ndidayang’ana ndikuona munthu pakati pa Amitundu, amene adalekanitsidwa kwa mbewu ya abale anga ndi madzi ambiri; ndipo ndidaona Mzimu wa Mulungu, kuti udatsika ndikum’khudza munthuyo; ndipo adayenda pa madzi ambiriwo, ngakhale kwa mbewu ya abale anga, amene adali ku dziko la lonjezano.

13 Ndipo zidachitika kuti ndidaona mzimu wa Mulungu, kuti udakhudza Amitundu; ndipo adatuluka mu ukapolo, kudzera m’madzi ambiri.

14 Ndipo zidachitika kuti, ndidaona makamu ambiri Amitundu pa dziko la lonjezano ndipo ndidaona mkwiyo wa Mulungu, umene udali pa mbewu ya abale anga; ndipo iwo adamwazikana kwa Amitundu ndipo adakanthidwa.

15 Ndipo ndidaona Mzimu wa Ambuye, kuti udali pa Amitundu, ndipo adachita bwino ndi kutenga dzikolo ngati cholowa chawo; ndipo ndidaona kuti adali oyera, ndi abwino kwambiri ndi okongola ngati m’mene adali anthu anga asadaphedwe.

16 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidaona kuti Amitundu amene adatuluka mu ukapolo adadzichepetsa pamaso pa Ambuye; ndipo mphamvu ya Ambuye idali mwa iwo.

17 Ndipo ndidaona kuti manthu wa Amitundu adasonkhanitsidwa pamodzi pamadzi, ndiponso pamtunda, kuti amenyane nawo.

18 Ndipo ndidaona kuti mphamvu ya Mulungu idali ndi iwo, ndiponso mkwiyo wa Mulungu udali pa onse amene adasonkhana pamodzi kumenyana nawo.

19 Ndipo ine, Nefi, ndidaona kuti Amitundu amene adachoka ku ukapolo adapulumutsidwa ndi mphamvu ya Mulungu kuchoka m’manja mwa maiko ena onse.

20 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidaona kuti iwo adachita bwino m’dzikolo; ndipo ndidaona buku, ndipo lidanyamulidwa pakati pawo.

21 Ndipo mngelo adati kwa ine: Kodi ukudziwa tanthauzo la bukulo?

22 Ndipo ndidati kwa iye: Sindikudziwa.

23 Ndipo iye adati: Taona likutuluka m’kamwa mwa Myuda. Ndipo ine, Nefi, ndidaliona, ndipo iye adati kwa ine: Buku lomwe ukulionali ndi zolemba za Ayuda limene muli mapangano a Ambuye, amene iye adapanga ndi nyumba ya Israeli; ndipo lirinso ndi maulosi ambiri a aneneri oyera; ndipo ndi zolemba ngati zozokotedwa zimene zili pa mapale a mkuwa, koma kuti sali ochuluka; komabe, ali ndi mapangano a Ambuye, amene adapanga ndi nyumba ya Israeli; kotero ndi amtengo wapatali kwambiri kwa Amitundu.

24 Ndipo mngelo wa Ambuye adati kwa ine: Iwe waona kuti bukulo lidatuluka kuchokera m’kamwa mwa Myuda; ndipo pamene lidatuluka kuchokera m’kamwa mwa Myuda, lidali ndi chidzalo cha uthenga wa Ambuye, amene atumwi khumi ndi awiri amachitira umboni; ndipo akuchitira umboni molingana ndi choonadi chimene chili mwa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu.

25 Kotero, zinthu izi zidachoka kwa Ayuda zili m’chiyero kupita kwa Amitundu, molingana ndi choonadi chimene chili mwa Mulungu.

26 Ndipo zitapita ndi dzanja la atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa; kuchokera kwa Ayuda kupita kwa Amitundu, ukuona kupangidwa kwa mpingo waukulu ndi wonyansa, umene uli wonyansa kuposa mipingo yonse; pakuti taonani, achotsa mu uthenga wabwino wa Mwana wa Nkhosa magawo ambiri amene ali omveka komanso amtengo wapatali; ndiponso mapangano ambiri a Ambuye achotsamo.

27 Ndipo zonsezi azichita kuti apotoze njira zolondola za Ambuye, kuti achititse khungu maso ndi kulimbitsa mitima ya ana a anthu.

28 Kotero, ukuona kuti bukuli litapita kudzera m’manja mwa mpingo wonyansa waukulu, kuti pali zomveka komanso zamtengo wapatali zambiri zimene zachotsedwa kuchoka m’bukuli, limene liri buku la Mwana wa Nkhosa wa Mulungu.

29 Ndipo zitachotsedwa zomveka komanso zamtengo wapatali zimenezi, lidapita kwa maiko onse a Amitundu; ndipo, litapita choncho kwa maiko a Amitundu, inde, ngakhale kuoloka madzi ambiri amene iwe wawaona pa modzi ndi Amitundu amene achoka ku ukapolo, iwe ukuona—chifukwa chakuti zomveka komanso zamtengo wapatali zachotsedwamo mu bukulo, zimene zidali zomveka mu kumvetsetsa kwa ana a anthu, monga mwa kumveka kumene kuli mwa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu—chifukwa cha zinthu izi zomwe zachotsedwa mu uthenga wabwino wa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, ambiri ochuluka kwambiri apunthwa, inde, mwakuti mpaka satana amakhala ndi mphamvu kwa iwo.

30 Komabe, iwe waona kuti Amitundu amene achoka ku ukapolo, ndipo akwezedwa ndi mphamvu ya Mulungu kuposa maiko ena onse, pankhope ya dziko lomwe liri losankhika kuposa maiko ena onse, limene liri dziko limene Ambuye Mulungu adapangana pangano ndi atate ako kuti mbewu yawo akhale nalo monga dziko la cholowa chawo; kotero, ukuwona kuti Ambuye Mulungu sadzalola kuti Amitundu awononge kotheratu kusakanizikana kwa mbewu yako, yomwe ili pakati pa abale ako.

31 Kapena iye sadzalora kuti Amitundu adzaononge mbewu ya abale ako.

32 Ngakhalenso Ambuye Mulungu sadzalora kuti Amitundu adzakhalebe m’chikhalidwe choopsa cha khungu, chimene iwe waona kuti adakali, chifukwa cha kuchotsedwa kwa zomveka komanso zamtengo wapatali za uthenga wabwino wa Mwana wa Nkhosa zimene zichotsedwa ndi mpingo wonyansa ndi waukulu umenewo, umene mapangidwe ake iwe waona kale.

33 Kotero atero Mwana wa Nkhosa wa Mulungu: Ndidzakhala ndi chifundo kwa Amitundu, ndikuwayendera otsalira a nyumba ya Israeli mu chiweruzo chachikulu.

34 Ndipo zidachitika kuti mngelo wa Ambuye adayankhula nane, nati: Taona, atero Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, Nditatha kuyendera otsalira a nyumba ya Israeli—ndipo otsalira awa amene ndikunena ndi mbewu ya atate ako—kotero, nditatha kuwayendera iwo m’chiweruzo, ndi kuwakantha iwo ndi dzanja la Amitundu, ndipo Amitundu akadzapunthwa kwakukulu, chifukwa cha kuchotsedwa kwa zomveka komanso zamtengo wapatali za uthenga wabwino wa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu ndi mpigo wonyansa ndi waukulu, umene uli kholo la achigololo, atero Mwana wa Nkhosa—ndidzakhala ndi chifundo kwa Amitundu mtsikulo, kotero kuti ndidzabweretsa kwa iwo kudzera mu mphamvu yanga, uthenga wabwino wochuluka, umene udzakhale omveka bwino ndi wamtengo wapatali, atero Mwana wa Nkhosa.

35 Pakuti taonani, atero Mwana wa Nkhosa: Ndidzadzionetsera ndekha kwa mbewu yako, kuti iwo adzalemba zambiri zimene ine ndidzatumikira kwa iwo, zimene zidzakhala zomveka bwino komanso zamtengo wapatali; ndipo mbewu yako ikadzaonongedwa, ndi kucheperachepera mukusakhulupilira, ndiponso mbewu ya abale ako, taona, zinthu izi zidzabisidwa, kuti zidzabwere kwa Amitundu, ndi mphatso komanso mphamvu ya Mwana wa Nkhosa.

36 Ndipo m’menemo mudzalembedwa uthenga wabwino, atero Mwana wa nkhosa, ndi thanthwe langa ndi chipulumutso changa.

37 Ndipo odala ndi iwo amene adzafune kubweretsa Ziyoni wanga pa tsikulo, pakuti adzakhala ndi mphatso komanso mphamvu ya Mzimu Woyera; ndipo ngati iwo adzapilire mpaka pamapeto adzakwezedwa pa tsiku lomaliza, ndipo adzapulumutsidwa mu ufumu wosatha wa Mwana wa Nkhosa; ndipo amene adzalengeze mtendere, inde uthenga wa chisangalalo chachikulu, n’lokongola bwanji phiri lomwe iwo adzakhale.

38 Ndipo zidachitika kuti ndidaona otsalira a mbewu ya abale anga, ndiponso buku la Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, limene lidachoka m’kamwa mwa Myuda, kuti lidatuluka kuchokera kwa Amitundu kupita kwa otsalira a mbewu ya azibale anga.

39 Ndipo litabwera kwa iwo, ndidaona mabuku ena, amene adabwera ndi mphamvu ya Mwana wa Nkhosa, kuchokera kwa Amitundu kupita kwa iwo, kwa kutsimikizira Amitundu ndi otsalira a nyumba ya abale anga, komanso a Yuda amene adamwazikana pa nkhope ya dziko lonse lapansi, kuti zolemba za aneneri ndi atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa ndi zoona.

40 Ndipo mngelo adayankhula nane, nati: Zolemba izi zomaliza, zomwe iwe waziona pakati pa Amitundu, zidzakhazikitsa choonadi cha zoyamba, zimene zili za atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa, Ndipo zidzadziwitsa zinthu zomveka komanso zamtengo wapatali zomwe zidachotsedwa kuchoka m’menemo; ndipo zidzadziwitsa kwa maiko, zinenero ndi anthu, kuti Mwana wa Nkhosa wa Mulungu ndiye Mwana wa Atate wa Muyaya, ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi; ndipo kuti anthu onse akuyenera kubwera kwa iye, apo ayi sangathe kupulumutsidwa.

41 Ndipo akuyenera kubwera molingana ndi mawu amene adzakhazikitsidwe kuchokera pakamwa pa Mwana wa Nkhosa; ndi mawu a Mwana wa Nkhosa adzadziwitsidwa m’malemba a mbewu yako, komanso m’malemba a atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa; kotero onsewo adzakhazikitsidwa pamodzi; pakuti pali Mulungu m’modzi, ndi M’busa m’modzi kwa dziko lonse lapansi.

42 Ndipo nthawi ilinkudza imene adzadzionetsera yekha kwa maiko onse, kwa a Yuda ndiponso Amitundu; ndipo akadzadzionetsera yekha kwa Ayuda ndinso kwa Amitundu, pamenepo adzadzionetsera kwa Amitundu ndiponso kwa Ayuda, ndipo omaliza adzakhala oyamba ndi oyamba adzakhala omaliza.