Malembo Oyera
1 Nefi 8


Mutu 8

Lehi aona masomphenya a mtengo wa moyo—Adya chipatso chake ndipo afunitsitsa kuti banja lake lichite chimodzimodzi—Aona ndodo ya chitsulo, njira yolunjika ndi yopapatiza, ndi nkhungu zamdima zomwe zimaphimba anthu—Sariya, Nefi, ndi Samu adya chipatsocho, koma Lamani ndi Lemueli akana. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti tidasonkhanitsa pamodzi mitundu yonse ya mbewu zosiyanasiyana, zonse za chimanga ya mtundu onse ndiponso mbewu za zipatso za mitundu yonse.

2 Ndipo zidachitika kuti pamene bambo anga adali kukhala mchipululu adayankhula ndi ife, nati: Taonani, ndalota loto; kapena, m’mawu ena, ine ndaona masomphenya.

3 Ndipo taonani, chifukwa cha chinthu chomwe ndaona, ndili ndi chifukwa chosangalalira mwa Ambuye chifukwa cha Nefi ndiponso cha Samu: pakuti ndili ndi chifukwa choganizira kuti iwo, ndiponso ambiri a mbewu zawo, adzapulumutsidwa.

4 Koma taonani, Lamani ndi Lemueli, ndili ndi mantha aakulu chifukwa cha inu; pakuti taonani, ndikuganiza kuti ndaona m’maloto, chipululu chamdima ndi choopsya.

5 Ndipo zidachitika kuti ndidaona munthu, ndipo adavala mwinjiro woyera; ndipo adabwera ndi kuima pamaso panga.

6 Ndipo zidachitika kuti adayankhula kwa ine, ndikundiuza ine kuti nditsatire iye.

7 Ndipo zidachitika kuti pamene ndinkamutsatira iye ndidadziona ndekha kuti ndidali mu mdima wandiweyani komanso wodetsa nkhawa.

8 Ndipo nditayenda kwa nthawi ya maora ochuluka mu mdima, ndidayamba kupemphera kwa Ambuye kuti andichitire chifundo, monga mwa zifundo zake zochuluka.

9 Ndipo zidachitika kuti nditatha kupemphera kwa Ambuye ndidaona bwalo lalilkulu ndi lotakasuka.

10 Ndipo zidachitika kuti ndidaona mtengo, omwe chipatso chake chidali chosililika ndi kumupangitsa munthu kusangalala.

11 Ndipo zidachitika kuti ndidapita chitsogolo ndi kudya chipatso chakecho; ndipo ndidaona kuti chidali chokoma kwambiri, kuposera zonse zimene ndidalawapo. Inde, ndipo ndidaona kuti chipatso chake chidali choyera, kuposa kuyera komwe ine ndidakuonapo.

12 Ndipo pamene ndidadya chipatso chakecho, chidadzadza moyo wanga ndi chisangalalo chachikulu: kotero, ndidayamba kufunitsitsa kuti banja langa lidyenso; pakuti ndidadziwa kuti chidali chosililika kuposa zipatso zina zonse.

13 Ndipo pamene ndidaponya maso anga mozungulira, kuti mwina ndingapeze banja langanso, ndidaona mtsinje wa madzi; ndipo umadutsira mothamanga, ndipo udali pafupi ndi mtengo umene ine ndidali kudya chipatsocho.

14 Ndipo ndidayang’ana kuti ndione kumene umachokera; ndipo ndidaona mutu wake patali pang’ono; ndipo chakumutu kwake ndidaona mayi anu Sariya, ndi Samu, ndi Nefi; ndipo adayima ngati kuti sakudziwa kumene akuyenera kupita.

15 Ndipo zidachitika kuti ndidawakodola iwo; ndipo ndidati kwa iwo ndi mawu ofuula kuti abwere kwa ine, ndikudzadya chipatso, chomwe chidali chosilirika kuposa chipatso china chirichonse.

16 Ndipo zidachitika kuti iwo adabwera kwa ine ndikudyanso chipatsocho.

17 Ndipo zidachitika kuti ndidakhumbira kuti Lamani ndi Lemueli abwere ndikudyanso chipatsocho; kotero, ndidaponya maso anga cha kumutu kwa mtsinje, kuti mwina ndingawaone.

18 Ndipo zidachitika kuti ndidawaona, koma sadafune kubwera kwa ine ndikudya chipatsocho.

19 Ndipo ndidaona ndodo ya chitsulo, ndipo idatambasukira mphepete mwa mtsinje, ndi kulondolera ku mtengo omwe ine ndidaima.

20 Ndiponso ndidaona njira yolunjika ndi yopapatiza, imene idalunjika limodzi ndi ndodo ya chitsulo, ngakhale ku mtengo omwe ine ndidaima; ndipo idatsogozedwanso ndi mutu wa kasupe, ku bwalo lalikulu ndi lotakasuka, ngati kuti lidali dziko.

21 Ndipo ndidaona khwimbi la anthu osawerengeka, ambiri mwa iwo amene ankayenda chitsogolo, kuti akathe kupeza njira yomwe imatsogolera ku mtengo omwe ine ndidayima.

22 Ndipo zidachitika kuti adabweradi chitsogolo, ndikuyamba kuyenda mnjira yomwe imatsogolera ku mtengo.

23 Ndipo zidachitika kuti pamenepo padauka nkhungu ya mdima; inde, ngakhale nkhungu ya mdima waukulu kwambiri, kwambiri kotero kuti iwo amene adayamba kuyenda mnjirayi adataya njira yawo, mpaka kuti adasochera ndi kutaika.

24 Ndipo zidachitika kuti ndidaona ena akupitabe chitsogolo, ndipo adafika ndi kugwira nsonga ya ndodo ya chitsulo; ndipo adapitabe chitsogolo kudzera mu nkhungu ya mdima, kukangamira ku ndodo ya chitsulo, mpakana adafika chitsogolo ndi kudya chipatso cha mu mtengowo.

25 Ndipo atatha kudya chipatso cha mu mtengowo adaponya maso awo uku ndi uku ngati kuti akuchita manyazi.

26 Ndipo inenso ndidaponya maso anga mozungulira, ndipo ndidaona, kutsidya lina la mtsinje wa madzi, chinyumba chachikulu ndi chotakatasuka; ndipo chidaima ngati mmalele, pamwamba pa nthaka.

27 Ndipo mudadzadza ndi anthu, onse aakulu ndi aang’ono, onse aamuna ndi aakazi; ndipo mavalidwe awo adali okongola kwambiri; ndipo adali mchikhalidwe chonyoza ndi kuloza dzala kwa iwo amene adabwera ndi kumadya chipatso.

28 Ndipo atatha kulawa chipatsocho adachita manyazi, chifukwa cha iwo amene amawanyoza iwo; ndipo adagwera mnjira zoletsedwa ndipo adatayika.

29 Ndipo tsopano ine Nefi, sindiyankhula mawu onse abambo anga.

30 Koma, kukhala mwachidule polemba, taonani, adaona khwimbi likupitabe chitsogolo; ndipo adabwera ndikugwiritsa nsonga ya ndodo ya chitsulo; ndipo adachilimika chitsogolo mnjira yawo, kupitiliza kugwira ndodo ya chitsulo kosalekeza, mpakana adafika patsogolo ndi kugwa pansi, ndi kudya chipatso cha mu mtengo.

31 Ndipo adaonanso khwimbi lina likumvelera njira yawo molunjika ku chinyumba chachikulu ndi chotakasuka chija.

32 Ndipo zidachitika kuti ambiri adamizidwa mu m’kuya kwa kasupe; ndipo ena adataika m’maso mwawo, akuyendayenda njira zachilendo.

33 Ndipo lochuluka lidali khwimbi lomwe lidalowa m’chinyumba chachilendocho. Ndipo atatha kulowa m’chinyumbacho, adaloza dzala zonyoza kwa ine ndiponso kwa iwo amene ankadya chipatso, koma ife sitidawamvere.

34 Awa ndi mawu a bambo anga: Pakuti ambiri amene adamvera iwo, adagwa.

35 Ndipo Lamani ndi Lemueli sadadye chipatsocho, adatero bambo anga.

36 Ndipo zidachitika kuti bambo anga atatha kuyankhula mawu onse a maloto ndi masomphenya awo, amene adali ambiri, adati kwa ife, chifukwa cha zinthu izi zimene adaona m’masomphenya, adachita mantha kwambiri chifukwa cha Lamani ndi Lemueli; inde, adaopa kuti angachotsedwe pamaso pa Ambuye.

37 Ndipo adawalimbikitsa iwo pamenepo ndi kumvelera konse kwa kholo lachikondi, kuti iwo amvetsere mawu awo, kuti mwina Ambuye adzawachitire chifundo iwo, ndikusawataya iwo; inde, bambo anga adalalika kwa iwo.

38 Ndipo atatha kuwalalikira iwo, ndinso kulosera kwa iwo zinthu zambiri, adawauza iwo kuti asunge malamulo a Ambuye; ndipo adasiya kuyankhula kwa iwo.