Malembo Oyera
1 Nefi 12


Mutu 12

Nefi aona masomphenya a dziko la lonjezano; chiyero, kusaweruzika, ndi kugwa kwa anthu okhalamo; kubwera kwa mwana wa Nkhosa wa Mulungu pakati pa iwo; m’mene Ophunzira Khumi ndi Awiri ndi Atumwi Khumi ndi Awiri adzaweruzire Israeli; ndi khalidwe loipa ndi lonyansa la iwo amene akuchepa m’kusakhulupilira. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti mngeloyo adati kwa ine: Yang’ana, ndipo taona mbewu yako, ndiponso mbewu ya azibale ako. Ndipo ndidayang’ana ndikuona dziko la lonjezano; ndipo ndidaona khwimbi la anthu, inde ngakhale lochuluka ngati mchenga wa ku nyanja.

2 Ndipo zidachitika kuti ndidaona khwimbi litasonkhana pamodzi kumenyana, kutsutsana wina ndi mnzake; ndipo ndidaona nkhondo ndi mbiri za nkhondo, ndi kuphana kwakukulu ndi lupanga pakati pa anthu anga.

3 Ndipo zidachitika kuti ndidaona mibadwo yambiri ikudutsa, mwanjira ya nkhondo ndi mikangano m’dziko; ndipo ndidaona mizinda yambiri, inde ngakhale kuti sindidathe kuiwerenga.

4 Ndipo zidachitika kuti ndidaona nkhungu ya mdima pa nkhope ya dziko la lonjezano; ndipo ndidaona ziphaliwali, ndi kumva mabingu, ndi zibvomerezi, ndi maphokoso owopsa mosiyanasiyana; ndipo ndidaona nthaka ndi mathanthwe kuti zidang’ambika, ndipo ndidaona mapiri akugumuka mzidutswa; ndipo ndidaona zigwa za dziko zikuphwanyika; ndipo ndidaona mizinda yochuluka ikumizidwa; ndipo ndidaona ambiri amene adaotchedwa ndi moto; ndipo ndidaona ambiri amene adagwa pansi chifukwa cha chibvomerezi.

5 Ndipo zidachitika kuti nditaona zinthu izi, ndidaona nthunzi wa mdima, kuti udachoka pa nkhope ya dziko lapansi; ndipo taonani, ndidaona khwimbi limene silidagwe chifukwa cha zigamulo zazikulu ndi zoopsya za Ambuye.

6 Ndipo ndidaona kumwamba kukutseguka, ndipo mwana wa Nkhosa wa Mulungu akutsika kuchokera kumwamba; ndipo adabwera pansi ndikuzionetsera yekha kwa iwo.

7 Ndipo inenso ndidaona ndi kuchitira umboni kuti Mzimu Woyera udagwera kwa ena khumi ndi awiri, ndipo adadzodzedwa ndi Mulungu ndi kusankhidwa.

8 Ndipo mngeloyo adayankhula nane, nati: Taona otsatira khumi ndi awiri a mwana wa nkhosa, amene asankhidwa kutumikira kwa mbewu yako.

9 Ndipo iye adati kwa ine: Kodi ukuwakumbukira atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa? Taonani, ndi iwo amene adzaweruze mafuko khumi ndi awiri a Israeli; kotero, atumiki khumi ndi awiri a mbewu yako adzaweruzidwa ndi iwo; pakuti ndinu a nyumba ya Israeli.

10 Ndipo atumiki khumi ndi awiri amene ukuwaonawa adzaweruza mbewu yako. Ndipo, taona, ndi olungama mpaka muyaya; pakuti chifukwa cha chikhulupiliro chawo mwa mwana wa Nkhosa wa Mulungu zovala zawo zidzayeretsedwa ndi mwazi wake.

11 Ndipo mngelo adati kwa ine: Yang’ana! Ndipo ndidayang’ana, ndipo ndidaona mibadwo itatu ikupita mu chilungamo; ndipo zovala zawo zidali zoyera ngati za mwana wa Nkhosa wa Mulungu. Ndipo mngelo adati kwa ine: Awa ayeretsedwa mu mwazi wa Mwana wa Nkhosa, chifukwa cha chikhulupiliro chawo mwa iye.

12 Ndipo ine Nefi, ndidaonanso ambiri a m’badwo wachinayi amene adamwalira m’chilungamo.

13 Ndipo zidachitika kuti ndidaona khwimbi la dziko lapansi litasonkhana pamodzi.

14 Ndipo mngeloyo adati kwa ine: Taona mbewu yako, ndiponso mbewu ya azibale ako.

15 Ndipo zidachika kuti, ndidayang’ana ndikuona anthu a mbewu yanga atasonkhanitsidwa pamodzi mu khwimbi motsutsana ndi mbewu ya azibale anga; ndipo adasonkhanitsidwa pamodzi kuti amenyane.

16 Ndipo mngelo adayankhula nane, nati: Taona kasupe wa madzi onyansa amene bambo ako adaona; inde, ngakhale mtsinje omwe iwo adayankhula; ndipo kuya kwake ndiko kuya kwa gahena.

17 Ndipo nkhungu za mdima ndi mayesero a mdyerekezi, amene amapangitsa khungu maso, ndi kuumitsa mitima ya ana a anthu, ndikuwatsogolera ku njira zotakasuka, kuti aonongeke ndi kutayika.

18 Ndipo nyumba yaikulu ndi yotakata, imene bambo ako adaona, ndi malingaliro opanda pake ndi kunyada kwa ana a anthu. Ndipo phompho lalikulu ndi loopsya likuwagawaniza iwo; inde ngakhale mawu a chilungamo cha Mulungu wa Muyaya, ndi Mesiya amene ali Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene Mzimu Woyera amachitira umboni, kuchokera pachiyambi cha dziko lapansi kufikira nthawi ino, ndi kuchokera nthawi ino mpaka muyaya.

19 Ndipo pamene mngelo ankayankhula mawu awa, ndidaona ndi kupenya mbewu ya azibale anga ikulimbana ndi mbewu yanga, monga mwa mawu a mngelo; ndi chifukwa cha kunyada kwa mbewu yanga, ndi mayesero a mdyerekezi, ndidaona kuti mbewu ya abale anga idapambana anthu a mbewu yanga.

20 Ndipo zidachitika kuti ndidaona, ndi kupenya anthu a mbewu ya azibale anga kuti adagonjetsa mbewu yanga; ndipo adapita m’makamu pa nkhope ya dziko lapansi.

21 Ndipo ndidaona iwo atasonkhanitsidwa pamodzi m’makamu; ndipo ndidaona nkhondo ndi mbiri za nkhondo pakati pawo; ndipo mu nkhondo ndi mbiri za nkhondo zomwe ndidaona mibadwo yambiri ikupita.

22 Ndipo mngelo adati kwa ine: Taona awa adzacheperachepera mu kusakhulupilira.

23 Ndipo zidachitika kuti ndidaona, atacheperachepera mu kusakhulupilira adakhala anthu amdima ndi onyasa, ndi aumve, odzala ndi ulesi ndi kuchita mitundu yonse ya zonyansa.

Print