Malembo Oyera
1 Nefi 18


Mutu 18

Ngalawa imalizidwa—Kubadwa kwa Yakobo ndi Yosefe kutchulidwa—Khamu la anthu linyamuka kupita ku dziko lolonjezedwa—Ana aamuna a Ismaeli ndi akazi awo agwirizana m’kusemphana ndi kupanduka—Nefi amangidwa, ndipo ngalawa ibwenzedwa ndi chimphepo chowopsya—Nefi amasulidwa, ndipo mwa pemphero lake chimphepo chileka—Anthu afika m’dziko lolonjezedwa. Mdzaka dza pafupifupi 591–589 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti iwo adalambira Ambuye, ndipo adapita nane; ndipo tidapanga matabwa opangidwa mwaluso. Ndipo Ambuye adandionetsa ine nthawi ndi nthawi m’mene ndiyenera kugwilitsira ntchito matabwa angalawayi.

2 Tsopano ine, Nefi, sindidagwire matabwawa motsata ndondomeko yomwe idaphunziridwa ndi anthu; koma ndidaimanga motsatira dongosolo limene Ambuye adandisonyeza; kotero, siidali monga mwa chikhalidwe cha anthu.

3 Ndipo ine, Nefi, ndidapita kuphiri kawirikawiri, ndipo ndidapemphera kawirikawiri kwa Ambuye; kotero Ambuye adandionetsa ine zinthu zazikulu.

4 Ndipo zidachitika kuti nditamaliza ngalawa, monga mwa mawu a Ambuye, abale anga adawona kuti idali yabwino, ndi kuti mapangidwe ake adali abwino kwambiri; kotero, iwo adadzichepetsanso pamaso pa Ambuye.

5 Ndipo zidachitika kuti mawu a Ambuye adabwera kwa atate anga, kuti tinyamuke ndikuti tikwere m’ngalawamo.

6 Ndipo zidachitika kuti mawa lake, titakonza zinthu zonse, zipatso zambiri ndi nyama yochokera kuchipululu, ndi uchi wambiri, ndi zakudya monga mwa zimene Ambuye adatilamulira, tidakwera m’ngalawamo ndi katundu wathu yense ndi mbewu zathu, ndi chirichonse chimene tidabwera nacho ife, aliyense monga mwa msinkhu wake; kotero, tonse tidakwera m’ngalawamo, ndi akazi athu ndi ana athu.

7 Ndipo tsopano, atate anga adabala ana amuna awiri m’chipululu; wamkulu adali Yakobo ndipo wamng’ono adali Yosefe.

8 Ndipo zidachitika kuti titakwera ife tonse m’ngalawa, ndi kutenga zakudya zathu ndi zinthu zimene zidalamuliridwa kwa ife, tidakalowa mnyanja ndipo tidakankhidwira patsogolo ndi mphepo kupita ku dziko lolonjezedwa.

9 Ndipo titakankhidwa ndi mphepo kwa nthawi ya masiku ambiri; taonani, abale anga ndi ana aamuna a Ismaeli komanso akazi awo adayamba kukondwera, moti adayamba kuvina, ndi kuimba, ndi kuyankhula mwa mwano kwambiri, inde, ngakhale kuti adaiwala ndi mphamvu yomwe iwo adabweretsedwa kumeneko; inde, adadzikuza pa kuchita mwano kwambiri.

10 Ndipo Ine, Nefi, ndidayamba kuchita mantha kwambiri kuti mwina Ambuye angakwiyire ife, ndi kutikantha chifukwa cha kusaweruzika kwathu, kuti timezedwe m’kuya kwa nyanja; kotero Ine, Nefi, ndidayamba kuyankhula kwa iwo modekha kwambiri; koma taonani adandikwiyira, nati: Sitikufuna kuti mb’ale wathu wamng’ono akhale wotilamulira ife.

11 Ndipo zidachitika kuti Lamani ndi Lemueli adanditenga ndi kundimanga ndi zingwe, ndipo adandichitira nkhanza zambiri; komabe, Ambuye adalolera izi kuti awonetse mphamvu yake, mu kukwaniritsidwa kwa mawu ake amene iye adayankhula ponena za oipa.

12 Ndipo zidachitika kuti atandimanga ine kotero kuti sindikadatha kusuntha, kampasi, yomwe idali itakonzedwa ndi Ambuye, idasiya kugwira ntchito.

13 Kotero, iwo sadadziwe kumene akuyenera kupititsa ngalawayo, mwakuti kudabuka namondwe wamkulu, inde, namondwe wamkulu ndi oopsa, ndipo tidabwenzedwa m’mbuyo pa madzi kwa nthawi ya masiku atatu; ndipo adayamba kuchita mantha kwambiri kuti angamizidwe m’nyanja; koma sadandimasule.

14 Ndipo pa tsiku lachinayi, limene tidabwenzeredwa m’mbuyo, namondwe adayamba kukhala woopsa kwambiri.

15 Ndipo zidachitika kuti tidatsala pang’ono kumizidwa m’kuya kwa nyanja. Ndipo titabwenzedwa m’mbuyo pa madzi kwa nthawi ya masiku anayi, abale anga adayamba kuona kuti ziweruzo za Mulungu zidali pa iwo, ndi kuti akuyenera kuwonongeka malire ake alape mphulupulu zawo; kotero, adabwera kwa ine, nandimasula zingwe zomwe zidali pa manja anga, ndipo taonani adali atatupa kwambiri; ndipo zidendene zanga zidatupa kwambiri, ndipo zidali zikupweteka kwambiri.

16 Komabe Ndidayang’ana kwa Mulungu wanga, ndipo ndidamlemekeza tsiku lonse; ndipo sindidang’ung’udze motsutsana ndi Ambuye chifukwa cha masautso anga.

17 Tsopano atate anga, Lehi, adali atanena zinthu zambiri kwa iwo, ndiponso kwa ana aamuna a Ismaeli; koma, taonani, adatulutsa ziwopsezo zambiri motsutsa aliyense amene angandiyankhulire; ndipo makolo anga adali atakula kwambiri, ndipo adali atazunzika ndi chisoni chochuluka chifukwa cha ana awo, iwo adagonekedwa pansi, inde, ngakhale pa makama awo odwala.

18 Chifukwa cha ululu wa mu mtima ndi chisoni chawo chachikulu, ndi kusaweruzika kwa abale anga, adawabweretsa pafupi kuti awatulutse kuti akakumane ndi Mulungu wawo; inde, imvi zawo zidali pafupi kuikidwa pansi m’fumbi; inde, ngakhale iwo adali pafupi kuponyedwa ndi chisoni m’manda amadzi.

19 Ndipo Yakobo ndi Yosefenso, pokhala ana ang’ono, okuti adafunika chisamaliro chambiri, adamva chisoni chifukwa cha masautso a amayi wawo; ndiponso mkazi wanga ndi misonzi yake ndi mapemphero ake, ndiponso ana anga, sizidafewetse mitima ya abale anga kuti andimasula ine.

20 Ndipo padalibe kalikonse koma mphamvu ya Mulungu, imene idawawopseza ndi chiwonongeko, ikadatha kufewetsa mitima yawo; kotero, poona kuti atsala pang’ono kumizidwa m’kuya kwa nyanja, adalapa pa chinthu chimene adachita, kotero kuti adandimasula.

21 Ndipo zidachitika atandimasula, taonani, ndidatenga kampasiyo, ndipo idagwira kumene ndidafuna. Ndipo zidachitika kuti ndidapemphera kwa Ambuye; ndipo nditapemphera mphepo idaleka, ndipo namondwe adaleka, ndipo padali bata lalikulu.

22 Ndipo zidachitika kuti Ine, Nefi, ndidaongolera ngalawayo, kuti tidanyamukanso kupita ku dziko lolonjezedwa.

23 Ndipo zidachitika kuti titayenda panyanja kwa nthawi ya masiku ambiri tidafika ku dziko lolonjezedwa; ndipo tidapita kumtunda, ndipo tidakhoma mahema athu; ndipo ife tidalitcha ilo dziko lolonjezedwa.

24 Ndipo zidachitika kuti tidayamba kulima m’nthaka, ndipo tidayamba kudzala mbewu; inde, tidayika mbewu zathu zonse m’nthaka, zimene tidatenga kuchokera ku dziko la Yerusalemu. Ndipo zidachitika kuti izo zidakula kwambiri; kotero, tidadalitsidwa mochuluka.

25 Ndipo zidachitika kuti tidapeza pa dziko la malonjezo, pamene tidali kuyenda m’chipululu, kuti mudali zilombo m’nkhalango zamitundumitundu, ng’ombe zazimuna, ndi ng’ombe zazikazi, ndi bulu, ndi akavalo, ndi mbuzi ndi mbuzi zakuthengo, ndi mitundu yonse ya nyama zakuthengo, zimene zidali zogwiritsa ntchito anthu. Ndipo tidapeza mitundu yonse ya miyala, yonse ya golidi, ndi siliva, ndi yakopa.

Print