Mutu 15
Mbewu ya Lehi idzalandira uthenga wabwino kuchokera kwa Amitundu m’masiku otsiriza—Kusonkhanitsidwa kwa Israeli kukufanizidwa ndi mtengo wa azitona umene nthambi zake zachilengedwe zidzamezetsanidwa kachiwiri—Nefi amasulira masomphenya a mtengo wa moyo ndipo ayankhula za chilungamo cha Mulungu pa kulekanitsa oipa ndi olungama. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, nditatha kunyamulidwa mu Mzimu, ndi kuona zinthu zonsezi, ndidabwelera ku chihema cha atate anga.
2 Ndipo zidachitika kuti, ndidaona abale anga, ndipo adali akutsutsana wina ndi mzake zokhudzana ndi zinthu zimene atate anga adayankhula kwa iwo.
3 Pakuti zoona iwo adayankhula zinthu zazikulu zambiri kwa iwo, zimene zidali zovuta kuzimvetsa, pokhapokha munthu atafunsa kwa Ambuye; ndipo chifukwa cha kuumitsa mtima kwawo, chotero sadayang’ane kuyang’ana kwa Ambuye, monga akadachitira.
4 Ndipo ine, Nefi, ndidali ndi chisoni chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo, ndiponso chifukwa cha zinthu zimene ndidaona, ndipo ndidadziwa kuti zikuyenera kudzakwaniritsidwa mosapeweka chifukwa cha kuipa kwakukulu kwa ana a anthu.
5 Ndipo zidachitika kuti ine ndidagonjetsedwa chifukwa cha masautso, pakuti ndidaganizira kuti masautso anga adali aakulu kuposa onse, chifukwa cha kuonongedwa kwa anthu anga, pakuti ndidaona kugwa kwao.
6 Ndipo zidachitika kuti nditalandira mphamvu ndidayankhula kwa abale anga, kufunitsitsa kuti ndidziwe za iwo chifukwa cha kukangana kwawo.
7 Ndipo adati: Taona ife sitikumvetsa mawu amene atate athu ayankhula zokhudzana ndi nthambi zachilengedwe za mtengo wa azitona, komanso zokhudzana ndi Amitundu.
8 Ndipo ine ndidati kwa iwo: Kodi mwafunsa kwa Ambuye?
9 Ndipo iwo adati kwa ine: Sitidafunse; pakuti Ambuye samatidziwitsa ife zinthu zotere.
10 Taonani, Ine ndidati kwa iwo: Kodi ndi chifukwa chiyani inu simusunga malamulo a Ambuye? Kodi n’chifukwa chiyani kuti inu mudzaonongeke chifukwa cha kuumitsa mitima yanu?
11 Kodi inu simukumbukira zinthu zimene Ambuye adanena?—Ngati inu simudzalimbitsa mitima yanu, ndi kundifunsa mwa chikhulupiliro, kukhulupilira kuti mudzalandira, ndi khama pa kusunga malamulo anga, ndithudi zinthu zimenezi zidzadziwitsidwa kwa inu.
12 Taonani, ndinena kwa inu, kuti nyumba ya Israeli idafanizidwa ndi mtengo wa azitona, mwa mzimu wa Ambuye umene udali mwa atate athu: ndipo taonani ife sitidathyoledwe ku nyumba ya Israeli, ndipo ife si nthambi ya nyumba ya Israeli?
13 Ndipo tsopano, chinthu chimene atate athu akutanthauza zokhudzana ndi kumezanitsa mu nthambi zachilengedwe kudzera mu chidzalo cha Amitundu, ndi, kuti m’masiku otsiriza, pamene mbewu yathu idzakhala itachepa mu kusakhulupilira, inde, kwa nthawi ya dzaka zambiri, ndipo mibadwo yambiri Mesiya akadzadzionetsera yekha mu thupi kwa ana a anthu, pamenepo chidzalo cha uthenga wabwino wa Mesiya chidzabwera kwa Amitundu, ndipo kuchokera kwa Amitundu kufikira kwa otsalira a mbewu yathu—
14 Ndipo patsikulo, otsalira a mbewu yathu adzadziwa kuti iwo ndi a nyumba ya Israeli, ndipo kuti iwo ndi anthu apangano a Ambuye; ndipo pamenepo adzadziwa ndi kufika pa chidziwitso cha makolo awo, ndiponso chidziwitso cha uthenga wabwino wa Muwomboli wawo, umene udatumikiridwa kwa makolo awo ndi iye; kotero, adzafika ku chidziwitso cha Muwomboli wawo ndinso mfundo zenizeni za chiphunzitso chake, kuti adziwe m’mene angabwelere kwa iye ndi kupulumutsidwa.
15 Ndipo patsikulo kodi iwo sadzasangalala ndikuyamika kwa Mulungu wawo wamuyaya, thanthwe lawo ndi chipulumutso chawo? Inde, patsikulo, kodi iwo sadzalandira mphamvu ndi chakudya kuchokera kwa Mpesa weniweni? Inde, kodi iwo sadzabwera ku khola loona la Mulungu?
16 Taonani, ndinena ndi inu, Inde; iwo adzakumbukiridwanso pakati pa a nyumba ya Israeli; adzalumikizanitsidwa mkati, pokhala nthambi ya chilengedwe ya mtengo wa azitona, mumtengo weniweni wa azitona.
17 Ndipo izi ndizimene atate anthu akutanthauza; ndipo akutanthauza kuti izi sizidzachitika mpakana adzalumikizanitsidwa ndi Amitundu; ndipo akutanthauza kuti zidzabwera kupyolera mwa Amitundu, kuti Ambuye adzaonetse mphamvu zawo kwa Amitundu, pachifukwa chomwechi adzakanidwa ndi Ayuda, kapena a nyumba ya Israeli.
18 Kotero, atate athu sadayankhule za mbewu yathu yokha, komanso za onse a nyumba ya Israeli, kuloza ku pangano limene liyenera kudzakwaniritsidwa m’masiku otsiriza; pangano limene Ambuye adapanga kwa atate athu Abrahamu, nati: Mwa mbewu yako mafuko onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.
19 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidayankhula zokhudzana ndi zinthu izi; inde, ndidayankhula kwa iwo zokhudzana ndi kubwezeretsedwa kwa Ayuda m’masiku otsiriza.
20 Ndipo ndidabwerezanso kwa iwo mawu a Yesaya, amene adayankhula zokhudzana ndi kubwezeretsedwa kwa Ayuda, kapena a nyumba ya Israeli; ndipo atabwezeretsedwa sadzanyazitsidwanso, ngakhalenso kumwazikana kachiwiri. Ndipo zidachitika kuti ndidayankhula mawu ambiri kwa abale anga, mpakana adakhazikika ndi kudzichepetsa okha pamaso pa Ambuye.
21 Ndipo zidachitikita kuti adayankhulanso kwa ine, nati: kodi nanga zikunthauza chiyani zimene atate athu adaona mu maloto? Tanthauzo la mtengo omwe adaona ndi chiyani?
22 Ndipo ndidati kwa iwo: Udali chithunzithunzi cha mtengo wa moyo.
23 Ndipo iwo adati kwa ine: Nanga zimatanthauza chiyani za ndodo ya chitsulo imene abambo athu adaona, imene imatsogolera ku mtengo?
24 Ndipo ndidati kwa iwo kuti adali mawu a Mulungu: ndipo amene amvera mawu a Mulungu, ndi kuwagwiritsa, sadzawonongeka; ngakhalenso mayesero ndi mivi yoyaka moto ya mdani sizidzawagonjetsa iwo mpaka kuwapatsa khungu, kuti awasocheretse ku chionongeko.
25 Kotero, ine, Nefi ndidawalimbikitsa iwo kuti amvetsere mawu a Ambuye; inde, ndidawadandaulira ndi mphamvu za moyo wanga onse, ndi luso langa lonse lomwe ndidali nalo, kuti amvetsere mawu a Mulungu ndi kukumbukira kusunga malamulo ake nthawi zonse mu zinthu zonse.
26 Ndipo iwo adati kwa ine: Nanga umatanthauza chiyani mtsinje wa madzi omwe atate athu adaona?
27 Ndipo ine ndidati kwa iwo kuti madzi amene atate anga adaona ndi zonyasa; ndipo kwambiri maganizo awo adamezedwa mu zinthu zina zomwe iwo adaona kotero sadaone kunyasa kwa madziwo.
28 Ndipo ndidati kwa iwo kuti chidali chiphompho choopsya, chimene chidasiyanitsa oipa ku mtengo wa moyo, ndiponso kwa oyera mtima a Mulungu.
29 Ndipo ndidati kwa iwo kuti chidali chithunzithunzi cha gahena woopsya uja, amene mngelo adanena kwa ine kuti adakonzedwa chifukwa cha oipa.
30 Ndipo ndidanena kwa iwo kuti atate athu adaonanso kuti chilungamo cha Mulungu chidagawanso oipa ndi olungama; ndipo kuwala kwake kudali ngati kuwala kwa malawi a moto, amene amakwera m’mwamba kwa Mulungu kwa muyaya ndipo alibe malire.
31 Ndipo iwo adati kwa ine: Kodi izi zikunthauza kuzunzika kwa thupi m’masiku oyesedwera, kapena zikutanthauza mkhalidwe omalizira wa munthu akadzamwalira ku thupi, kapena zikunena za zinthu zomwe zili za kuthupi?
32 Ndipo zidachitika kuti ine ndidati kwa iwo kuti zidali chithunzithunzi cha zinthu zonse za kuthupi komanso za uzimu: pakuti tsiku likudza kuti iwo ayenera kuweruzidwa chifukwa cha ntchito zawo, inde ngakhale ntchito zimene zidachitidwa ku thupi pa masiku awo oyesedwera.
33 Kotero, ngati adzamwalire akadali m’machimo akuyeneranso kudzatayidwa, monga mwa zinthu zimene zili za uzimu, zimene zili zokhudzana ndi chilungamo; kotero, akuyenera kubweretsedwa kudzayima pamaso pa Mulungu, kudzaweruzidwa pa ntchito zawo; ndipo ngati ntchito zawo zidali zonyasa, akuyenera kukhala onyasa, ndipo ngati ali onyasa ndiye kuti sangakhale mu ufumu wa Mulungu; ngati zili choncho, ndiye kuti ufumu wa Mulungu ndi onyasanso.
34 Koma taonani, ndikunena ndi inu, ufumu wa Mulungu si onyasa, ndipo palibe chinthu china chilichonse chodetsedwa chimene chingalowe mu ufumu wa Mulungu; kotero, pakuyenera kukhala malo anyansi amene akonzedwa chifukwa cha zimene zili zonyasa.
35 Ndipo pali malo amene akonzedwa, inde, ngakhale gahena woopsya amene ndakamba, ndipo mdyerekezi ndi amene adakonza malowo; kotero mkhalidwe wotsiliza wa miyoyo ya anthu ndiko kuti adzakhale mu ufumu wa Mulungu, kapena kudzatulutsidwa chifukwa cha chilungamo chimene ndakamba.
36 Kotero, oipa amakanidwa kuchoka kwa olungama, ndiponso kuchoka ku mtengo wa moyo umenewo, umene chipatso chake ndi chamtengo wapatali ndi chosililika kuposa zipatso zina zonse, inde, ndipo ndi chachikulu pa mphatso zonse za Mulungu. Ndipo umo ndi mmene ndidayankhulira kwa abale anga. Ameni.