Malembo Oyera
1 Nefi 5


Mutu 5

Sariya ang’ung’udza motsutsana ndi Lehi—Onse akondwera pa kubwelera kwa ana awo aamuna—Apereka nsembe—Mapale a mkuwa ali ndi zolemba za Mose ndi aneneri—Mapale azindikiritsa Lehi kuti ndi mbadwa ya Yosefe—Lehi alosera ponena za mbewu yake ndi kusungidwa kwa mapale. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti titabwelera kuchipululu kwa atate athu, taonani, iwo adadzadzidwa ndi chisangalalo, ndiponso amayi anga, Sariya, adali okondwa mopambana chifukwa adalira chifukwa cha ife.

2 Pakuti iwo adaganiza kuti ife tidawonongeka m’chipululu; ndipo iwonso adali atadandaula motsutsana ndi atate anga, powauza iwo kuti iwo adali munthu wamasomphenya; nati: Taonani, mwatitulutsa m’dziko la cholowa chathu, ndipo ana anga kulibenso, ndipo tikuwonongeka m’chipululu.

3 Ndipo m’kulankhula kotere amayi anga adandaula motsutsana ndi atate anga.

4 Ndipo zidachitika kuti atate anga adanena nawo, nati: Ndikudziwa kuti ndine munthu wamasomphenya; pakuti ndikadapanda kuwona zinthu za Mulungu m’masomphenya sindikadadziwa ubwino wa Mulungu, koma ndikadakhala ku Yerusalemu, ndipo ndikadaonongeka pamodzi ndi abale anga.

5 Koma taonani, ndalandira dziko la lonjezano, limene ndikondwera nalo; inde, ndipo ndidziwa kuti Ambuye adzapulumutsa ana anga aamuna kuchokera m’manja mwa Labani; ndi kuwabweretsanso kwa ife m’chipululu.

6 Ndipo m’kulankhula kotere atate anga, Lehi, adatonthoza amayi anga, Sariya, ponena za ife; pamene ife tinkayenda m’chipululu kupita ku dziko la Yerusalemu, kuti tikatenge zolemba za Ayuda.

7 Ndipo pamene tidabwelera ku hema ya atate anga, taonani chisangalalo chawo chidadzadza, ndipo mayi anga adatonthonzedwa.

8 Ndipo adanena, kuti: Tsopano ndidziwa ndithu kuti Ambuye adalamulira mwamuna wanga kuthawira kuchipululu; Inde, ndikudziwanso motsimikiza kuti Ambuye wateteza ana anga aamuna, ndipo adawawombola iwo kuchoka m’manja mwa Labani, ndi kuwapatsa iwo mphamvu yomwe iwo angathere kukwaniritsa chinthu chimene Ambuye adawalamulira iwo. Ndipo m’kulankhula kotere iwo adayankhula.

9 Ndipo zidachitika kuti adakondwera koposa, ndipo adapereka nsembe ndi zopereka zopsereza kwa Ambuye; ndipo adayamika Mulungu wa Israeli.

10 Ndipo atapereka mayamiko kwa Mulungu wa Israeli, atate anga, Lehi, adatenga zolemba zimene zidazokotedwa pa mapale a mkuwa, ndipo iwo adazisakatula izo kuchokera pachiyambi.

11 Ndipo adaona kuti iwo adali ndi mabuku asanu a Mose, amene adapereka mbiri ya chilengedwe cha dziko lapansi, ndiponso ya Adamu ndi Hava, amene adali makolo athu oyamba;

12 Ndiponso mbiri ya Ayuda kuchokera pachiyambi, ngakhale mpaka koyambilira kwa ufumu wa Zedekiya, mfumu ya Yuda;

13 Ndiponso mauneneri a aneneri oyera, kuchokera pa chiyambi, ngakhale mpaka ku chiyambi cha ulamuliro wa Zedekiya; ndiponso maulosi ambiri amene adayankhulidwa pakamwa pa Yeremiya.

14 Ndipo zidachitika kuti atate anga, Lehi, nawonso adapeza pa mapale a mkuwa chibadwidwe cha makolo awo; kotero adadziwa kuti adali m’badwo wa Yosefe; inde, Yosefe wake yemwe uja mwana wa Yakobo, amene adagulitsidwa ku Igupto, amene adatetezedwa ndi dzanja la Ambuye, kuti ateteze atate ake, Yakobo, ndi banja lake lonse kuti asawonongeke ndi njala.

15 Ndipo iwo adatsogozedwanso kuchoka mu ukapolo ndi kutuluka m’dziko la Igupto, ndi Mulungu yemweyo amene adawateteza

16 Ndipo motero atate anga, Lehi, adapeza mbiri ya chibadwidwe cha makolo awo. Ndipo Labani nayenso adali mbadwa ya Yosefe, kotero iye ndi makolo ake adasunga zolembazo.

17 Ndipo tsopano pamene atate anga adaona zinthu zonsezi, adadzadzidwa ndi Mzimu, ndipo adayamba kulosera ponena za mbewu yawo—

18 Kuti mapale a mkuwawa ayenera kupita kwa mayiko onse, mafuko, zinenero, ndi anthu amene adali a mbewu yawo.

19 Kotero, adanena kuti mapale a mkuwa awa sakuyenera kuwonongeka; ngakhale sakuyenera kudetsedwanso ndi nthawi. Ndipo iwo adanenera zinthu zambiri zokhudza mbewu yawo.

20 Ndipo zidachitika kuti kufikira pamenepa ine ndi atate anga tidasunga malamulo amene Ambuye adatilamulira ife.

21 Ndipo ife tidali titalandira zolemba zomwe Ambuye adatilamulira ife, ndipo tidazisakatula izo ndipo tidapeza kuti zidali zofunika; inde, angakhale za mtengo waukulu kwa ife, kotero kuti ife tikadatha kuteteza malamulo a Ambuye kwa ana athu.

22 Kotero, zidali nzeru mwa Ambuye kuti tinyamuke nazo, pamene tikuyenda m’chipululu kupita ku dziko la lonjezo.