Malembo Oyera
1 Nefi 2


Mutu 2

Lehi atengela banja lake m’chipululu kudzera Nyanja Yofiira—Asiya chuma chawo—Lehi apereka nsembe kwa Ambuye ndipo aphunzitsa ana ake aamuna kusunga malamulo—Lamani ndi Lemueli ang’ung’udza motsutsana ndi atate awo—Nefi amvera ndi kupemphera m’chikhulupiliro; Ambuye alankhula naye, ndipo asankhidwa kuti alamulire abale ake. Mdzaka dza pafupifupi 600 Yesu asadabadwe.

1 Pakuti taonani, zidachitika kuti Ambuye adayankhula kwa atate anga, inde, ngakhale mu loto, ndipo adati kwa iwo: Odalitsidwa ndiwe Lehi, chifukwa cha zinthu zimene iwe wachita; ndipo chifukwa iwe wakhala okhulupirika ndi kulengeza kwa anthu awa zinthu zimene ndidakulamulira iwe, taona, iwo akufuna kuchotsa moyo wako.

2 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adalamulira atate anga, ngakhale mu loto, kuti atenge banja lawo ndi kunyamuka kupita kuchipululu.

3 Ndipo zidachitika kuti iwo adamvera mawu a Ambuye, kotero adachita monga Ambuye adawalamulira iwo.

4 Ndipo zidachitika kuti iwo adapita kuchipululu. Ndipo adasiya nyumba yawo, ndi dziko la cholowa chawo, ndi golidi wawo, ndi siliva wawo, ndi zinthu zawo zamtengo wapatali, ndipo sadatenge kanthu, koma banja lawo, ndi zakudya, ndi mahema, ndipo adapita kuchipululu.

5 Ndipo adatsikira ku malire a mphepete mwa Nyanja Yofiira; nayenda m’chipululu m’malire ali pafupi ndi Nyanja Yofiira; Ndipo iwo adayenda m’chipululu ndi banja lawo, limene lidali la amayi anga, Sariya, ndi abale anga aakulu, amene adali Lamani, Lemueli, ndi Samu.

6 Ndipo zidachitika kuti pamene adayenda masiku atatu m’chipululu, adakhoma hema lawo m’chigwa m’mbali mwa mtsinje wa madzi.

7 Ndipo zidachitika kuti iwo adamanga guwa la nsembe la miyala, napereka nsembe kwa Ambuye, ndipo adayamika Ambuye Mulungu wathu.

8 Ndipo zidachitika kuti adatchula dzina la mtsinjewo, Lamani, ndipo umakhuthulira mu Nyanja Yofiira; ndipo chigwacho chinali m’malire a kukamwa kwake.

9 Ndipo pamene atate anga adaona kuti madzi a mtsinje amakhuthulira m’kasupe wa Nyanja Yofiira, adayankhula kwa Lamani, nati: O kuti iwe ukhale wonga mtsinje uwu, kuthamangira mosalekeza m’kasupe wa chilungamo chonse!

10 Ndipo iwo adayankhulanso kwa Lemueli: O kuti iwe ukhale monga chigwa ichi, olimba ndi okhazikika, ndi osasunthika m’kusunga malamulo a Ambuye!

11 Tsopano izi adayankhula chifukwa cha kusamva kwa Lamani ndi Lemueli; pakuti taonani iwo adang’ung’udza mu zinthu zambiri motsutsana ndi atate awo, chifukwa iwo adali munthu wamasomphenya, ndipo adawatsogolera iwo kuchokera m’dziko la Yerusalemu, kusiya dziko la cholowa chawo, ndi golide wawo, ndi siliva wawo, ndi zinthu zawo zamtengo wapatali, kuti adzawonongeke m’chipululu. Ndipo ichi adanena kuti adachita chifukwa cha zolingalira zopusa za mtima wawo.

12 Ndipo motero Lamani ndi Lemueli, pokhala aakulu, adang’ung’udza motsutsana ndi atate awo. Ndipo adang’ung’udza chifukwa chakuti sankadziwa zochita za Mulungu amene adawalenga.

13 Komanso sadakhulupilire kuti Yerusalemu, mzinda waukuluwo, ukhoza kuwonongedwa mogwirizana ndi mawu a aneneri. Ndipo adali ngati Ayuda amene adali ku Yerusalemu, amene ankafuna kuchotsa moyo wa atate anga.

14 Ndipo zidachitika kuti atate anga adayankhula kwa iwo mu chigwa cha Lemueli, ndi mphamvu, atadzadzidwa ndi Mzimu, mpaka matupi awo adagwedezeka pamaso pake. Ndipo adawagonjetsa iwo, kuti sadayelekeze kunena zotsutsa iwo; kotero, iwo adachita monga adawalamulira iwo.

15 Ndipo atate anga adakhala muchihema.

16 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, pokhala wamng’ono kwambiri, komabe pokhala wamkulu mu msinkhu, ndiponso ndidali ndi zikhumbo zazikulu kuti ndidziwe za zinsinsi za Mulungu, kotero ndidafuula kwa Ambuye; ndipo taonani iye adandiyendera ine, ndipo adafewetsa mtima wanga kuti ndidakhulupilira mawu onse amene adayankhulidwa ndi atate anga; kotero, sindidapandukire iwo ngati abale anga.

17 Ndipo ine ndidayankhula kwa Samu, kumudziwitsa iye zinthu zimene Ambuye adandiwonetsera ine mwa Mzimu wake Woyera. Ndipo zidachitika kuti adakhulupilira mawu anga.

18 Koma, taonani, Lamani ndi Lemueli sadamvere mawu anga; ndipo pokhala wachisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo ndidalira kwa Ambuye chifukwa cha iwo.

19 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adayankhula kwa ine, nati: Wodala uli iwe, Nefi, chifukwa cha chikhulupiliro chako, chifukwa wandifunafuna molimbikira, ndi kudzichepetsa kwa mtima.

20 Ndipo pamene udzasunga malamulo anga, udzapambana, ndipo udzatsogozedwa ku dziko la lonjezo; inde, ngakhale dziko limene ndakonzera iwe; inde, dziko limene lili losankhidwa pamwamba pa maiko ena onse.

21 Ndipo pamene abale ako adzakupandukira iwe, iwo adzachotsedwa pamaso pa Ambuye.

22 Ndipo pamene udzasunga malamulo anga, udzapangidwa wolamulira ndi mphunzitsi wa abale ako.

23 Pakuti taona, m’tsiku limene adzandipandukira, ndidzawatembelera ngakhale ndi thembelero loŵaŵa, ndipo sadzakhala ndi mphamvu pa mbewu yako, pokhapokha adzandipandukire inenso.

24 Ndipo ngati zidzachitike kuti andipandukira ine, iwo adzakhala chikwapu kwa mbewu yako, chowachangamutsa iwo m’njira za chikumbutso.