Malembo Oyera
1 Nefi 22


Mutu 22

Israeli adzabalalitsidwa pamaso padziko lapansi—Amitundu adzasamala ndi kudyetsa Israeli ndi uthenga wabwino m’masiku omaliza—Israeli adzasonkhanitsidwa ndi kupulumutsidwa, ndipo oipa adzawotchedwa ngati chiputu—Ufumu wa mdyerekezi udzawonongedwa, ndipo Satana adzamangidwa. Mdzaka dza pafupifupi 588–570 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti nditatha ine, Nefi, kuwerenga zinthu izi zimene zidali zozokotedwa pa mapale a mkuwa, abale anga adabwera kwa ine ndipo adati kwa ine: Kodi zinthu izi zimene inu mwawerenga zikutanthauza chiyani? Taonani, kodi izo zikuyenera kumvetsetsedwa molingana ndi zinthu zomwe ziri zauzimu, zomwe zidzachitike molingana ndi mzimu ndipo osati kuthupi?

2 Ndipo ine, Nefi, ndidati kwa iwo: Taonani izo zidawonetseredwa kwa mneneri ndi mawu a Mzimu; pakuti mwa Mzimu zinthu zonse zimadziwika kwa aneneri, zimene zidzafike pa ana a anthu molingana ndi thupi.

3 Kotero, zinthu zimene ine ndawerenga ndi zinthu zokhudzana ndi zinthu zonse zakuthupi ndi zauzimu; pakuti zikuwoneka kuti nyumba ya Israeli, posachedwa kapena kutsogoloku, idzabalalitsidwa pamaso pa dziko lapansi, ndiponso pakati pa mitundu yonse.

4 Ndipo taonani, pali ambiri amene asowa kale ku chidziwitso cha iwo amene ali ku Yerusalemu. Inde, ochuluka a mafuko onse atsogozedwa kutali; ndipo amwazikana uku ndi uko pazilumba za nyanja; ndipo kumene iwo ali palibe m’modzi wa ife akudziwa, kupatula kuti ife tikudziwa kuti iwo atsogozedwa kutali.

5 Ndipo popeza iwo adatsogozedwa kutali, zinthu izi zidaloseredwa zokhudzana ndi iwo, komanso zokhudzana ndi onse amene pambuyo pake adzabalalitsidwa ndi kusokonezedwa; chifukwa cha Woyera wa Israeli; pakuti adzaumitsa mitima yawo motsutsana naye; kotero, adzabalalitsidwa pakati pa maiko onse, ndipo adzadedwa ndi anthu onse.

6 Komabe, atasamalidwa ndi Amitundu, ndipo Ambuye atakweza dzanja lake pa Amitundu, ndi kuwakweza ngati mbendera, ndipo ana awo adanyamula m’manja mwawo, ndipo ana awo aakazi kunyamulidwa pa mapewa awo, taonani zinthu izi zomwe zimayankhulidwa ziri zakuthupi; pakuti otere ali mapangano a Ambuye ndi makolo athu; ndipo zikutanthauza ife m’masiku alinkudza, ndiponso abale athu onse amene ali a nyumba ya Israeli.

7 Ndipo zikutanthauza kuti nthawi idzafika kuti pamene nyumba yonse ya Israeli idzabalalitsidwa ndi kusokonezedwa, kuti Ambuye Mulungu adzadzutsa fuko lamphamvu pakati pa Amitundu, inde, ngakhale pamaso pa dziko lino; ndipo mwa iwo mbewu zathu zidzabalalitsidwa.

8 Ndipo mbewu yathu itabalalitsidwa Ambuye Mulungu adzapitiriza kuchita ntchito yodabwitsa pakati pa Amitundu, imene idzakhala ya mtengo wapatali kwa mbewu yathu; kotero, ikufanizidwa ngati ndi kudyetsedwa kwawo ndi Amitundu ndi kunyamulidwa m’manja mwawo ndi pa mapewa awo.

9 Ndipo idzakhalanso yoyenera kwa Amitundu; ndipo si kwa Amitundu okha koma kwa nyumba yonse ya Israeli, pa kuwazindikiritsa za mapangano a Atate a kumwamba kwa Abrahamu, okuti: Mumbewu yako mafuko onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.

10 Ndipo ine ndikadakonda, abale anga, kuti mudziwe kuti mafuko onse a dziko lapansi sangathe kudalitsidwa pokhapokha iye atavumbulutsa mkono wake pamaso pa maiko.

11 Kotero, Ambuye Mulungu adzavumbulutsa nkono wake pamaso pa amitundu wonse, pokwaniritsa mapangano ake ndi uthenga wabwino wake kwa iwo amene ali a nyumba ya Israeli.

12 Kotero, adzawatulutsanso kuchoka mu ukapolo, ndi kudzasonkhanitsidwa pamodzi ku maiko a cholowa chawo; ndipo adzatulutsidwa kuchoka mu kusadziwa ndi kuchoka mu mdima; ndipo adzadziwa kuti Ambuye ndiye Mpulumutsi wawo ndi Muwomboli wawo, Wamphamvu wa Israeli.

13 Ndipo mwazi wa mpingo waukulu ndi wonyansa umenewo, umene uli wachigololo wa dziko lonse lapansi, udzatembenukira pa mitu yawo yomwe; pakuti adzachita nkhondo mwa iwo wokha, ndipo lupanga la manja awo womwe lidzagwa pa mitu yawo yomwe, ndipo iwo adzaledzera ndi mwazi wawo.

14 Ndipo mtundu uliwonse umene udzamenyana ndi inu, O nyumba ya Israeli, udzatembenukirana wina ndi mnzake, ndipo udzagwa m’dzenje limene adakumba kuti akole anthu a Ambuye. Ndipo onse omenyana ndi Ziyoni adzawonongedwa, ndipo mkazi wachiwerewere wamkulu uja, amene wapotoza njira zolungama za Ambuye, inde, mpingo waukulu ndi wonyansa umenewo, udzagwetseredwa ku fumbi ndipo kwakukulu kudzakhala kugwa kwa iwo.

15 Pakuti tawonani, atero mneneri, nthawi ilinkudza mofulumira kuti Satana sadzakhalanso ndi mphamvu pa mitima ya ana a anthu; pakuti tsiku likudza posachedwa kuti onse onyada ndi iwo amene amachita zoipa adzakhala ngati chiputu; ndipo tsiku likudza limene iwo ayenera kuwotchedwa.

16 Pakuti nthawi ilinkudza posachedwa kuti chidzalo cha mkwiyo wa Mulungu chidzatsanuliridwa pa ana onse a anthu; pakuti sadzalora kuti oipa awononge olungama.

17 Kotero, adzateteza olungama ndi mphamvu yake; ngakhale kudzakhala kuti chidzalo cha mkwiyo wake chikuyenera kubwera, ndipo olungama adzatetezedwa, ngakhale ku chiwonongeko cha adani awo ndi moto. Kotero, olungama sakuyenera kuchita mantha; pakuti atero mneneri, iwo adzapulumutsidwa, ngakhale kudzakhala ngati ndimoto.

18 Taonani, abale anga, ndikunena kwa inu, kuti zinthu izi zikuyenera kubwera posachedwa; inde, ngakhale mwazi, ndi moto, ndi nthunzi wa utsi zikuyenera kudza; ndipo zikuyenera kukhala pamaso pa dziko lapansili; ndipo zidzabwera kwa anthu monga mwa kuthupi ngati kudzakhala kuti adzaumitsa mitima yawo motsutsana ndi Woyera wa Israeli.

19 Pakuti taonani, wolungama sadzawonongedwa; pakuti nthawi ikuyeneradi kudza kuti onse amene akumenyana ndi Ziyoni adzachotsedwa.

20 Ndipo Ambuye adzakonzera ndithu njira anthu ake; kuti mawu a Mose akwaniritsidwe, amene adanena, kuti: Mneneri ngati ine Ambuye Mulungu wanu adzawutsa kwa inu; mudzamvera iye mu zinthu ziri zonse zimene adzanena kwa inu. Ndipo zidzachitika kuti onse amene sadzamvera mneneri ameneyo adzachotsedwa pakati pa anthu.

21 Ndipo tsopano, ine, Nefi, ndikulengeza kwa inu, kuti mneneri uyu amene Mose adayankhula za iye adali Woyera wa Israeli; kotero, adzachita chiweruzo m’chilungamo.

22 Ndipo olungama sakuyenera kuopa, pakuti iwo ndi amene sadzachita manyazi. Koma uli ufumu wa mdyerekezi, umene udzamangidwa pakati pa ana a anthu, ufumu umene ukukhazikika pakati pa iwo amene ali akuthupi—

23 Pakuti nthawi idzafika mwa msanga kuti mipingo yonse yomangidwa kuti ipindule, ndi yonse yomangidwa kuti ikhale ndi mphamvu pa thupi; ndi iyo imene imamangidwa kuti ikhale yotchuka m’maso mwa dziko lapansi, ndipo iyo imene imatsata zilakolako za thupi ndi zinthu za dziko lapansi; ndi kuchita mitindu yonse ya zoyipa; inde, pamapeto pake, onse amene ali mu ufumu wa mdyerekezi ali iwo amene akuyenera kuchita mantha, ndi kunthunthumira, ndi kunjenjemera; ndiwo amene akuyenera kutsitsidwa m’fumbi; ndiwo amene adzathedwa ngati ziputu; ndipo izi ziri monga mwa mawu a mneneri.

24 Ndipo nthawi ilinkudza msanga kuti olungama atsogoledwe ngati ana a ng’ombe a m’khola; ndipo Woyera wa Israeli akuyenera kulamulira mu ulamuliro, ndi molimbika; ndi mwa mphamvu, ndi ulemelero waukulu.

25 Ndipo asonkhanitsa ana ake ku ngodya zinayi za dziko lapansi; ndipo awerenga nkhosa zake, ndipo zimudziwa iye; ndipo padzakhala khola limodzi ndi m’busa m’modzi; ndipo adzadyetsa nkhosa zake, ndipo mwa iye zidzapeza msipu.

26 Ndipo chifukwa cha chilungamo cha anthu ake, Satana alibe mphamvu; kotero, sangathe kumasulidwa kwa dzaka zambiri; pakuti alibe mphamvu pa mitima ya anthu; pakuti iwo akhala m’chilungamo, ndipo Woyera wa Israeli alamulira.

27 Ndipo tsopano taonani, ine, Nefi, ndikunena kwa inu, kuti izi zonse zikuyenera kubwera molingana ndi kuthupi.

28 Koma, taonani, maiko onse, mafuko, zinenero, ndi anthu adzakhala motetezeka mwa Woyera wa Israeli ngati atadzakhale kuti adzalapa.

29 Ndipo tsopano ine, Nefi, ndipanga mapeto; pakuti sindiyankhulanso mopitiriza zokhudzana ndi zinthu izi.

30 Kotero, abale anga, ndikufuna kuti muganizire kuti zinthu zimene zidalembedwa pa mapale a mkuwa ndi zoona; ndipo zimachitira umboni kuti munthu akuyenera kukhala omvera malamulo a Mulungu.

31 Kotero, simuyenera kuganiza kuti ine ndi atate anga ndife tokha amene tachitira umboni, ndi kuphunzitsa izo. Kotero, ngati mudzakhala omvera malamulo, ndi kupilira kufikira chimaliziro, mudzapulumutsidwa pa tsiku lomaliza. Ndipo zili choncho. Ameni.

Print