Malembo Oyera
1 Nefi 1


Buku Loyamba la Nefi

Ulamuliro ndi Utumiki Wake

Nkhani ya Lehi ndi mkazi wake Sariya, ndi ana ake aamuna anayi, akutchedwa, (kuyambira pa wamkulu) Lamani, Lemueli, Samu, ndi Nefi. Ambuye achenjeza Lehi kuti achoke m’dziko la Yerusalemu, chifukwa iye amalosera kwa anthu ponena za kusaweruzika kwawo ndipo afuna kuwononga moyo wake. Ayenda ulendo wa masiku atatu m’chipululu pamodzi ndi banja lake. Nefi atenga abale ake nabwelera ku dziko la Yerusalemu kukatenga mbiri ya Ayuda. Nkhani za mazunzo awo. Atenga ana aakazi a Ismaeli kukhala akazi awo. Atenga mabanja awo ndi kupita kuchipululu. Mazunzo ndi zowawa zawo m’chipululu. Njira ya maulendo awo. Iwo afika ku madzi aakulu. Abale ake a Nefi amupandukira. Awagonjetsa, namanga ngalawa. Iwo awatcha dzina la malowo Chuluka. Iwo awoloka madzi aakulu kupita ku dziko lolonjezedwa, ndi zina zotero. Izi ziri molingana ndi nkhani ya Nefi; kapena m’mawu ena, ine, Nefi, ndidalemba mbiri iyi.

Mutu 1

Nefi ayamba zolemba za anthu ake—Lehi awona m’masomphenya mzati wa moto ndipo awerenga kuchokera m’buku la ulosi—Atamanda Mulungu, alosera za kudza kwa Mesiya, nalosera za chiwonongeko cha Yerusalemu—Iye azunzidwa ndi Ayuda. Mdzaka dza pafupifupi 600 Yesu asadabadwe.

1 Ine, Nefi, pobadwa kwa makolo abwino, choncho ndidaphunzitsidwa pena pake m’maphunziro onse a atate anga; ndipo powona zisautso zambiri m’kupita kwa masiku anga, komabe, pokhala okonderedwa kwambiri ndi Ambuye m’masiku anga onse; inde, pokhala ndi chidziwitso chachikulu cha ubwino ndi zinsinsi za Mulungu, choncho ndikupanga zolemba zanga m’masiku anga.

2 Inde, ndilemba m’chinenero cha atate anga, chimene chili ndi zophunzira za Ayuda ndi chinenero cha Aigupto.

3 Ndipo ndidziwa kuti zolembedwa zomwe ndipange zili zoona; ndipo ndipanga ndi dzanja langa; ndipo ndichita monga mwa kudziwa kwanga.

4 Pakuti zidachitika mu kuyambilira kwa chaka choyamba cha ulamuliro wa Zedekiya, mfumu ya Yuda, (atate anga, Lehi, atakhala ku Yerusalemu m’masiku awo onse); ndipo m’chaka chomwecho munadza aneneri ambiri, akunenera kwa anthu kuti ayenera kulapa, kapena mzinda waukulu Yerusalemu uyenera kuwonongedwa.

5 Kotero zidachitika kuti atate anga, Lehi, pamene adali kuyenda adapemphera kwa Ambuye, inde, ngakhale ndi mtima wawo wonse, mmalo mwa anthu awo.

6 Ndipo zidachitika kuti pakupemphera kwa Ambuye, mzati wa moto udadza, nakhala pa thanthwe pamaso pawo; ndipo adaona, ndi kumva zambiri; ndipo chifukwa cha zinthu zimene adaziwona ndi kuzimva adathunthumira ndi kunjenjemera kwakukulu.

7 Ndipo zidachitika kuti adabwelera kunyumba kwawo ku Yerusalemu; ndipo adadzigwetsa pakama pawo, nagonjetsedwa ndi Mzimu ndi zinthu zimene adaziwona.

8 Ndipo pakugonjetsedwa ndi Mzimu kotero, iwo adatengedwa m’masomphenya, ngakhale kuti adaona kumwamba kutatseguka, ndipo iwo adaganiza kuti iwo adaona Mulungu atakhala pa mpando wake wachifumu, atazunguliridwa ndi magulu osawerengeka a angelo mu chikhalidwe cha kuyimba ndi kutamanda Mulungu wawo.

9 Ndipo zidachitika kuti iwo adaona M’modzi akutsika kuchokera pakati pa thambo, ndipo iwo adaona kuti kuwala kwake kudali koposa kwa dzuwa ku masana.

10 Ndipo adaonanso khumi ndi awiri akumtsata, ndi kuwala kwawo kudaposa kwa nyenyezi za mlengalenga.

11 Ndipo adatsika, natulukira pa nkhope ya dziko lapansi; ndipo woyamba adadza nayima pamaso pa atate anga, nawapatsa iwo buku, nawauza iwo kuti awerenge.

12 Ndipo zidachitika kuti pamene ankawerenga adadzadzidwa ndi Mzimu wa Ambuye.

13 Ndipo adawerenga, nati: Tsoka, tsoka, Yerusalemu, pakuti ndaona zonyansa zako! Inde, ndinso zinthu zambiri zimene atate anga adawerenga ponena za Yerusalemu—kuti iye adzawonongedwa, ndi anthu okhalamo; ambiri adzawonongeka ndi lupanga, ndipo ambiri adzatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo.

14 Ndipo zidachitika kuti atate anga atawerenga ndi kuona zinthu zambiri zazikulu ndi zodabwitsa, adafuula zinthu zambiri kwa Ambuye; monga: Zazikulu ndi zozizwitsa ziri ntchito zanu, Inu Ambuye Mulungu Wa mphamvu zonse! Mpando wanu wachifumu uli kumwamba, ndipo mphamvu yanu, ndi ubwino wanu, ndi chifundo zili pa onse okhala padziko lapansi; ndipo, chifukwa inu muli wachifundo, inu simudzalola iwo amene adza kwa inu kuti awonongeke!

15 Ndipo chotere chidali chinenelo cha atate anga m’kutamanda Mulungu wawo; pakuti moyo wawo udakondwera, ndipo mtima wawo wonse udadzadzidwa, chifukwa cha zinthu zimene iwo adaona, inde, zimene Ambuye adawonetsa kwa iwo.

16 Ndipo tsopano ine, Nefi, sindilemba nkhani zonse zimene atate anga adalemba, pakuti iwo adalemba zinthu zambiri zimene adaona m’masomphenya ndi m’maloto; ndipo iwo adalembanso zinthu zambiri zimene adalosera ndi kulankhula kwa ana awo, zimene sindidzalemba nkhani zonse.

17 Koma ndidzalemba nkhani za zochita zanga m’masiku anga. Taonani, ndipanga chidule cha zolemba za atate anga, pa mapale amene ndapanga ndi manja anga; kotero, ndikadzamaliza kufupikitsa mbiri ya atate anga ndidzapanga zolemba nkhani za moyo wanga.

18 Kotero, ndimafuna kuti mudziwe, kuti Ambuye atasonyeza zinthu zodabwitsa zambiri kwa atate anga, Lehi, inde, ponena za chiwonongeko cha Yerusalemu, tawonani iwo adapita pakati pa anthu, ndipo adayamba kulosera ndi kulengeza kwa iwo ponena za zinthu zimene adaziwona ndi kuzimva.

19 Ndipo zidachitika kuti Ayuda adawanyoza chifukwa cha zinthu zomwe adachitira umboni za iwo; pakuti iwo adachitira umboni moona za kuipa kwawo ndi zonyansa zawo; ndipo iwo adachitira umboni kuti zinthu zimene iwo adaziwona ndi kuzimva, ndiponso zinthu zimene iwo adaŵerenga m’buku, zidasonyeza momveka bwino za kudza kwa Mesiya, ndiponso chiwombolo cha dziko.

20 Ndipo pamene Ayuda adamva izi adakwiya nawo; inde, monga ndi aneneri akale, amene adawathamangitsa, nawaponya miyala, ndi kuwapha; ndipo iwonso adafuna moyo wawo, kuti auchotse. Koma taonani, ine, Nefi, ndidzawonetsa kwa inu kuti zifundo za Ambuye ziri pa onse amene iye adawasankha, chifukwa cha chikhulupiliro chawo, kuti awapangitse iwo amphamvu ngakhale mpaka ku mphamvu ya chipulumutso.