Malembo Oyera
1 Nefi 21


Mutu 21

Mesiya adzakhala kuunika kwa Amitundu ndipo adzamasula am’ndende—Israeli adzasonkhanitsidwa ndi mphamvu m’masiku omaliza—Mafumu adzakhala atate awo owalera—Fananizani ndi Yesaya 49. Mdzaka dza pafupifupi 588–570 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo kachiwiri: Mvetserani, O inu a nyumba ya Israeli, inu nonse amene mwathyoledwa ndi kupirikitsidwa chifukwa cha kuipa kwa abusa a anthu anga; inde, inu nonse othyoledwa, amene mudabalalikana kunja, amene muli mwa anthu anga, nyumba ya Israeli. Tamverani, inu zilumba, kwa Ine, ndipo mvetserani inu anthu akutali; Ambuye wandiitana ine kuchokera muchiberekero; kuchokera m’mimba mwa amayi anga adatchula dzina langa.

2 Ndipo wapanga pakamwa panga ngati lupanga lakuthwa; mumthunzi wa dzanja lake adandibisa, nandipanga mtengo wopukutidwa; m’phodo lake adandibisa;

3 Ndipo adati kwa ine, Ndiwe mtumiki wanga, Israeli, mwa amene ndidzalemekezedwa.

4 Kenako ndidati, Ndagwira ntchito pachabe, ndagwiritsa ntchito mphamvu yanga pachabe ndi popanda pake; Ndithu, kuweruzidwa kwanga kuli ndi Ambuye, ndipo ntchito yanga ili kwa Mulungu wanga.

5 Ndipo tsopano, atero Ambuye, amene adandiumba kuyambira m’mimba kuti ndikhale mtumiki wake, kuti ndibweretsenso Yakobo kwa iye, ngakhale Israeli sadasonkhanitsidwe, koma ine ndidzakhala waulemelero pamaso pa Ambuye, ndipo Mulungu wanga adzakhala mphamvu zanga.

6 Ndipo iye adati: Ndichinthu chopepuka kuti ukhale mtumiki wanga ndi kuukitsa mafuko a Yakobo, ndi kubwenzeretsa otetezedwa a Israeli. Ndidzakuperekanso iwe ngati kuunika kwa Amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa kufikira kumapeto a dziko lapansi.

7 Akutero Ambuye, Mombolo wa Israeli, Woyera wake, kwa iye amene anthu amamunyoza, kwa iye amene maiko amanyansidwa naye, kwa watchito wa olamulira: Mafumu adzaona ndi kudzaimilira, akalonga nawonso adzalambira, chifukwa cha Ambuye amene ali okhulupirika.

8 Akutero Ambuye: Mu nthawi yovomerezeka ndidamva inu, O inu zilumba za m’nyanja, ndipo pa tsiku la chipulumutso didzakuthandizani; ndipo ndidzakutetezani, ndi kukupatsani mtumiki wanga kuti akhale pangano la anthu; kukakhazikitsa dziko lapansi, kupangitsa kuti alandire zolowa zabwinja;

9 Kuti ukauze am’ndende, Pitani; kwa iwo akukhala mumdima: Dziwonetseni. Adzadya munjira, ndi abusa awo adzakhala m’malo okwezeka onse.

10 Sadzamva njala kapena ludzu, ngakhale kutentha kapena dzuwa sizidzawakantha; pakuti iye wakuwachitira chifundo adzawatsogolera, ngakhale ku akasupe a madzi adzawatsogolera.

11 Ndipo ndidzapangitsa mapiri anga onse kukhala njira. ndipo misewu yanga idzakwezeka.

12 Ndipo kenako, O nyumba ya Israeli, taona, awa adzachokera kutali; ndipo taona, awa ochokera kumpoto ndi kumadzulo; ndi awa ochokera ku dziko la Sinimu.

13 Imbani, O kumwamba; ndipo sangalala, O dziko lapansi; pakuti mapazi a iwo ali kum’mawa adzakhazikika; ndi kuyamba kuyimba, O mapiri; pakuti sadzakanthidwanso; pakuti Ambuye watonthoza anthu ake, ndipo adzachitira chifundo wosautsidwa ake.

14 Koma, taonani, Ziyoni adati: Ambuye anditaya ine, ndipo Ambuye anga andiiwala ine—koma adzasonyeza kuti sadatero.

15 Pakuti kodi mkazi angaiwale mwana wake oyamwa, kuti iye sangachitire chifundo mwana womubala iye? Inde, akhonza kuiwala, koma Ine sindidzakuiwala iwe, O nyumba ya Israeli.

16 Taona, ndakulemba pa zikhato za manja anga; makoma ako ali pamaso panga kosalekeza.

17 Ana ako adzafulumira motsutsana ndi okuwononga; ndipo iwo amene adakupasula adzatuluka mwa iwe.

18 Kweza maso ako mozungulira ndipo taona; onsewa adzasonkhana pamodzi, ndipo adzabwera kwa iwe. Ndipo monga ndiri ndimoyo, atero Ambuye, ndithu iwe udzabvala ndi iwo onse; ngati ndi chokongoletsera, ndi kuwamanga ngakhale ngati mkwatibwi.

19 Pakuti malo ako opasuka ndi abwinja, ndi dziko lachiwonongeko chako, lidzakhala lopapatiza kwambiri chifukwa cha okhalamo; ndipo iwo amene adakumeza iwe adzakhala kutali.

20 Ana amene udzakhala nawo, utataya woyamba, adzanenanso m’makutu mwako: Malowa andipanikiza kwambiri; ndipatseni malo kuti ndikhale.

21 Pamenepo udzanena mumtima mwako: Ndani wandibalira ine awa, powona ndataya ana anga, ndipo ndine bwinja, kapolo, woyendayenda uku ndi uko? Ndipo ndi ndani wawalera awa? Taonani, ndidasiyidwa ndekha; awa, kodi adali kuti?

22 Akutero Ambuye Mulungu, Taonani, ndidzakwezera dzanja langa kwa Amitundu, ndi kukweza mbendera yanga kwa anthu; ndipo adzabwera nawo ana ako aamuna m’manja mwawo, ndi ana ako akazi adzanyamulidwa paphewa pawo.

23 Ndipo mafumu adzakhala atate ako okulera, ndi mfumukazi zawo azimayi okuyamwitsa; adzakugwadirani ndi nkhope zawo pansi, ndi kudzanyambita fumbi la kumapazi anu; ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Ambuye; pakuti sadzachita manyazi amene adikilira ine.

24 Kodi zofunkha zidzalandidwa kwa wamphamvu, kapena akapolo ovomerezeka adzalanditsidwa?

25 Koma akutero Ambuye, ngakhale am’nsinga a wamphamvu adzatengedwa, ndi zofunkha za woopsa zidzapulumutsidwa; pakuti ndidzatsutsana ndi iye amene atsutsana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako.

26 Ndipo ndidzadyetsa iwo akupondereza inu ndi thupi lawo lomwe; adzaledzera ndi mwazi wawo omwe ngati ndi vinyo wotsekemera; ndipo anthu onse adzadziwa kuti Ine, Ambuye, ndine Mpulumutsi wako ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.