Malembo Oyera
1 Nefi 3


Mutu 3

Ana aamuna a Lehi abwelera ku Yerusalemu kuti akatenge mapale a mkuwa—Labani akana kupeleka mapale—Nefi alangiza molimbika ndi kulimbikitsa abale ake—Labani aba katundu wawo ndi kuyesera kuwapha—Lamani ndi Lemueli akantha Nefi ndi Samu ndipo adzudzulidwa ndi mngelo. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti, Ine, Nefi, ndidabwelera kuchokera kolankhula ndi Ambuye, ku chihema cha atate anga.

2 Ndipo zidachitika kuti adanena kwa ine, nati; Taona, ndalota maloto, amene Ambuye adandiuza ine, kuti iwe ndi abale ako mubwelere ku Yerusalemu.

3 Pakuti taona, Labani ali ndi zolembedwa za Ayuda ndinso m’badwo wa makolo anga, ndipo n’zozokotedwa pa mapale a mkuwa.

4 Kotero, Ambuye wandilamulira ine kuti iwe ndi abale ako mupite ku nyumba ya Labani, ndi kukafunafuna zolembazo, ndi kuzibweretsa izo muno mu chipululu.

5 Ndipo tsopano, tawona, abale ako akung’ung’udza, kunena kuti ndi chinthu chovuta chimene ndafuna kwa iwo; koma taonani sindidachifune kwa iwo, koma ndi lamulo la Ambuye.

6 Choncho pita, mwana wanga, ndipo Ambuye adzakukomera mtima, chifukwa sudang’ung’udze.

7 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidati kwa atate anga: Ndidzapita ndi kukachita zinthu zimene Ambuye adalamulira, pakuti ndidziwa kuti Ambuye sapereka malamulo kwa ana a anthu, koma iye adzawakonzera iwo njira kuti akwaniritse chinthu chimene adawalamulira.

8 Ndipo zidachitika kuti pamene atate anga adamva mawu awa adali okondwa kwambiri, pakuti adadziwa kuti ndidali nditadalitsidwa ndi Ambuye.

9 Ndipo ine, Nefi, ndi abale anga tidayamba ulendo wathu m’chipululu, ndi mahema athu, kuti tipite ku dziko la Yerusalemu.

10 Ndipo zidachitika kuti pamene tidapita ku dziko la Yerusalemu, ine ndi abale anga tidakambirana wina ndi mzake.

11 Ndipo tidachita maere—ndani wa ife alowe m’nyumba ya Labani. Ndipo zidachitika kuti maere adagwera Lamani; ndipo Lamani adalowa m’nyumba ya Labani, ndipo adayankhula naye pamene adakhala m’nyumba mwake.

12 Ndipo adakhumba kwa Labani zolembedwa zimene zidali zolembedwa pa mapale a mkuwa, zimene zidali ndi m’badwo wa atate anga.

13 Ndipo taonani, zidachitika kuti Labani adakwiya, ndipo adamponyera iye kunja kumuchotsa pa maso pake; ndipo sadafune kuti iye akhale nazo zolembazo. Kotero, adati kwa iye: Taona ndiwe wakuba, ndipo ndikupha iwe.

14 Koma Lamani adathawa kuchoka pamaso pake, ndipo adatiuza zinthu zimene Labani adachita, kwa ife. Ndipo tidayamba kukhala achisoni kwambiri, ndipo abale anga adali pafupi kubwelera kwa atate anga m’chipululu.

15 Koma taonani ndidanena kwa iwo kuti: Ngati Ambuye ali moyo, ndipo ngati ife tili moyo, ife sitidzatsikira kwa atate athu m’chipululu mpaka ife titakwaniritsa chinthu chimene Ambuye adatilamulira ife.

16 Kotero, tiyeni tikhale okhulupilika m’kusunga malamulo a Ambuye; kotero, tiyeni titsikire ku dziko la cholowa cha atate athu, pakuti taonani adasiya golide ndi siliva, ndi chuma chamtundu uliwonse. Ndipo zonsezi adachita chifukwa cha malamulo a Ambuye.

17 Pakuti iye ankadziwa kuti Yerusalemu ayenera kuwonongedwa, chifukwa cha kuipa kwa anthu.

18 Pakuti taonani, iwo akana mawu a aneneri. Kotero, ngati atate anga akadakhala m’dzikomo atalamulidwa kuti athawe m’dzikolo, taonani, iwonso akadaonongeka. Kotero, zimayenera kuti athawe m’dzikolo.

19 Ndipo taonani, ndi nzeru mwa Mulungu kuti titenge zolemba izi, kuti tisunge kwa ana athu chinenero cha makolo athu;

20 Ndiponso kuti ife tiwasungile mawu amene adayankhulidwa mkamwa mwa aneneri onse oyera, amene adaperekedwa kwa iwo mwa Mzimu ndi mphamvu ya Mulungu, kuyambira chiyambi cha dziko, ngakhale mpakana nthawi ino.

21 Ndipo zidachitika kuti m’kuyankhula mwa mtundu uwumenewu ndidakopa abale anga, kuti akhale okhulupilika m’kusunga malamulo a Mulungu.

22 Ndipo zidachitika kuti ife tidapita ku dziko la cholowa chathu, ndipo tidasonkhanitsa pamodzi golide wathu, ndi siliva wathu, ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.

23 Ndipo titasonkhanitsa zinthu izi pamodzi, tidapita ku nyumba ya Labani.

24 Ndipo zidachitika kuti ife tidapita kwa Labani, ndipo tidamupempha iye kuti atipatse ife zolemba zomwe zidalembedwa pa mapale a mkuwa, zimene ife tidakaperekera kwa iye golide wathu, ndi siliva wathu, ndi zinthu zathu zonse za mtengo wapatali.

25 Ndipo zidachitika kuti pamene Labani adaona chuma chathu, ndi kuti chidali chambiri kwambiri, adachikhumba, moti adatithamangitsira kunja, ndipo adatumiza antchito ake kuti atiphe, kuti atenge chuma chathu.

26 Ndipo zidachitika kuti tidathawa pamaso pa antchito a Labani, ndipo tidakakamizika kusiya chuma chathu, ndipo chidagwera m’manja mwa Labani.

27 Ndipo zidachitika kuti tidathawira kuchipululu, ndipo antchito a Labani sadatipeze, ndipo tidabisala m’phanga la thanthwe.

28 Ndipo zidachitika kuti Lamani adakwiya ndi ine, ndi atate anga; ndi Lemueli nayenso, pakuti adamvera mawu a Lamani. Kotero Lamani ndi Lemueli adayankhula mawu ambiri ovuta kwa ife, abale awo aang’ono, ndipo adatikantha ngakhale ndi ndodo.

29 Ndipo zidachitika kuti pamene adali kutimenya ndi ndodo, taonani, mngelo wa Ambuye adadza, naima pamaso pawo, nanena nawo, nati: Nanga bwanji mukumkantha mng’ono wanu ndi ndodo? Kodi simukudziwa kuti Ambuye adamusankha kuti akhale olamulira wanu, ndipo zimenezi chifukwa cha mphulupulu zanu? Taonani mudzapitanso ku Yerusalemu, ndipo Ambuye adzapereka Labani m’manja mwanu.

30 Ndipo mngelo atatha kuyankhula nafe, adachoka.

31 Ndipo atachoka mngeloyo, Lamani ndi Lemueli adayambanso kung’ung’udza, kuti: Kodi ndi zotheka bwanji kuti Ambuye apereke Labani m’manja mwathu? Taonani, iye ndi munthu wamphamvu, ndipo akhonza kulamula makumi asanu, inde, ngakhale akhonza kupha makumi asanu; ndiye kuli bwanji ife?