Malembo Oyera
1 Nefi 10


Mutu 10

Lehi alosera kuti Ayuda adzatengedwa ku ukapolo ndi Ababulo—Akamba za kubwera kwa Mesiya pakati pa Ayuda, Mpulumutsi, Muwomboli—Lehi akambanso za m’modzi yemwe adzabatize Mwana wa Nkhosa wa Mulungu—Lehi akamba za imfa ndi chiukitso cha Mesiya—Afananiza kubalalitsidwa ndi kusonkhanitsidwa kwa Israeli ndi mtengo wa azitona—Nefi ayankhula za Mwana wa Mulungu, ndi mphatso ya Mzimu Woyera, ndi kufunikira kwa chilungamo. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, Ine Nefi, ndikupitiliza kupereka mbiri ili pa mapale awa ya zochitika zanga, ndi ulamuliro wanga, ndi utumiki wanga; kotero, kuti ndipitilize ndi mbiri yanga, ndikuyenera kuyankhula zina za zinthu za bambo anga, ndiponso za abale anga.

2 Pakuti taonani, zidachitika kuti bambo anga atatha kumaliza kuyankhula za mawu a loto lawo, ndiponso kuwalimbikitsa iwo mu khama lonse, adayankhula kwa iwo zokhudzana ndi Ayuda—

3 Kuti akadzatha kuonongedwa, ngakhale mzinda uja waukulu wa Yerusalemu, ndipo ambiri adzatengedwa mu ukapolo ku Babulo, molingana ndi nthawi yake yoyikika ya Ambuye, adzabweleranso, inde angakhale kubweretsedwa kuchoka ku ukapolo; ndipo akadzabweretsedwa kuchokera ku ukapolo adzatenganso malo a cholowa chawo.

4 Inde, ngakhale dzaka mazana asanu ndi chimodzi kuchokera m’nthawi yomwe bambo anga adachoka ku Yerusalemu, mneneri Ambuye Mulungu adzadzutsa pakati pa Ayuda—ngakhale Mesiya, kapena m’mawu ena, Mpulumutsi wa dziko lapansi.

5 Ndipo adayankhulanso zokhudzana ndi aneneri, za mmene ambiri adachitira umboni za zinthu izi, zokhudzana ndi Mesiya ameneyu, amene za iye adayankhula, kapena uyu Muwomboli wa dziko lapansi.

6 Kotero, anthu onse adali mu m’khalidwe wokugwa ndi wotayika, ndipo adzakhalabe choncho pokhapokha atadalira mwa Muwomboliyu.

7 Ndipo adayankhulanso zokhudzana ndi za mneneri amene akuyenera kubwera Mesiya asadafike, kudzakonza njira ya Ambuye.

8 Inde, ngakhale iye adzayenda ndi kukalira mchipululu: Konzani njira ya Ambuye, ndi kupanga njira zake zoongoka; pakuti pali wina wayima mmodzi pakati panu amene simukumudziwa; ndipo ali wamphamvu kuposa ine, amene zingwe za nsapato zake sindili oyenera kuzimasula. Ndipo zambiri adayankhula bambo anga zokhudzana ndi chinthu ichi.

9 Ndipo bambo anga adati iye akuyenera kubatiza mu Batabara, kutsidya la Yordani; ndipo adatinso kuti iye akuyenera kubatiza ndi madzi; ngakhale kuti akuyenera kum’batiza Mesiya ndi madzi.

10 Ndipo akadzatha kubatiza Mesiya ndi madzi, iye akuyenera kuona ndi kuchitira umboni kuti adabatiza Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, amene adzachotse machimo a dziko lapansi.

11 Ndipo zidachikita kuti bambo anga atatha kuyankhula mawu awa, adayankhula kwa abale anga zokhudzana ndi uthenga wabwino umene ukuyenera kulalikidwa pakati pa Ayuda, ndiponso zokhudzana ndi kupinimbira kwa Ayuda mu kusakhulupilira. Ndipo akadzapha Mesiya, amene akuyenera kudzabwera, ndipo akadzaphedwa, iye akuyenera kudzauka kwa akufa, ndipo akuyenera kudzadzionetsera yekha, mwa Mzimu Woyera, kwa Amitundu.

12 Inde, ngakhale bambo anga adayankhula zambiri zokhudzana ndi Amitundu, ndiponso zokhudzana ndi nyumba ya Israeli, kuti akuyenera kudzafanizidwa ngati mtengo wa azitona, umene mthambi zake zathyoledwa ndi kumwazidwa pa nkhope ya dziko lonse lapansi

13 Kotero, iwo adati, pali kufunika ndithu kuti ife tikuyenera kutsogololedwa mu umodzi kulowa dziko la lonjezano, m’kukwaniritsa kwa mawu a Ambuye, kuti tikuyenera kumwazikana pa nkhope ya dziko lonse lapansi.

14 Ndipo atamwazidwa a nyumba ya Israeli, akuyenera kudzasonkhanitsidwanso; kapena kunena kwabwino, Amitundu akadzalandira chidzalo cha uthenga wabwino, nthambi zachilengedwe za mtengo wa azitona, kapena otsalira a nyumba ya Israeli, adzaphatikizidwa nawo, kapena adzabwera ku chidziwitso cha Mesiya woona, Ambuye wawo ndi Muwomboli wawo.

15 Monga mwa chilankhulo chotere, bambo anga adalosera ndi kuyankhula kwa abale anga, ndiponso zinthu zambiri zimene sindikulemba mu buku ili; pakuti ndalemba zambiri za izo monga zidali zofunikira kwa ine mu buku langa lina.

16 Ndipo zinthu zonsezi, zimene ndayankhulazi, zidachitika pamene bambo anga adakhala muchihema, mu chigwa cha Lemueli.

17 Ndipo zidachitika kuti atamaliza, ine Nefi, nditamva za mawu onsewa a bambo anga, zokhudzana ndi zinthu zimene iwo adaona mu masomphenya, ndiponso zinthu zimene adayankhula ndi mphamvu ya Mzimu Woyera, mphamvu imene adalandira mwa chikhulupiliro pa Mwana wa Mulungu—ndipo Mwana wa Mulungu adali Mesiya amene adzabwere—Ine, Nefi, ndidali ndi chikhumbo choti nane ndione, ndi kumva, ndi kudziwa zinthu zonsezi, mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, imene ili mphatso ya Mulungu kwa onse amene alimbikira kumusaka iye, momwemonso mu nthawi za kale ngati mu nthawi yomwe iye adzadzionetsera yekha kwa ana a anthu.

18 Pakuti iye ali yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse; ndipo njira yakonzedwa kwa anthu onse kuchokera kumaziko a dziko lapansi, ngati iwo angalape ndi kubwera kwa iye.

19 Pakuti iye amene afunafuna mwa khama adzapeza; ndipo zinsinsi za Mulungu zidzaululidwa kwa iye, mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, monga mwa nthawi zatsopano, ngati mu nthawi yakale, ndipo monga mwa nthawi zakale ngati mnthawi ilinkudza; kotero, njira ya Ambuye ndikuzungulira kumodzi kwamuyaya.

20 Chotero kumbukira, O munthu, pakuti pazochita zako zonse udzabweretsedwa ku chiweruzo.

21 Kotero, ngati wafuna kuchita zoipa m’masiku a m’kuyesedwa kwako, pamenepo udzapezeka odetsedwa pamaso pa mpando wa chiweruzo wa Mulungu; ndipo palibe chinthu chodetsedwa chomwe chidzakhale ndi Mulungu; kotero, inu mukuyenera kutayidwa kwa muyaya.

22 Ndipo Mzimu Woyera wapeleka ulamuliro kuti ndiyankhule zinthu izi, ndipo osazikana ayi.