Malembo Oyera
1 Nefi 9


Mutu 9

Nefi apanga magawo awiri a zolemba—Iliyonse itchedwa mapale a Nefi—Mapale aakulu muli mbiri ya zamdziko; ndi mapale aang’ono agona kwambiri pa zinthu zopatulika. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zinthu zonsezi bambo anga adaona, ndi kumva, ndipo adayankhula, pamene amakhala muchihema, mu chigwa cha Lemueli, ndiponso zinthu zina zazikulu zambiri, zimene sizingalembedwe pa mapale awa.

2 Ndipo tsopano, monga ndayankhula zokhudzana ndi mapale awa, taonani, simapale amene ine ndakonza nkhani yonse ya mbiri ya anthu anga; pakuti mapale awa amene ndakonzapo nkhani yonse ya anthu anga ndaatchula dzina loti Nefi; kotero, akutchedwa kuti mapale a Nefi, kuchokera ku dzina langa lomwe; ndipo mapale awanso akutchedwa kuti mapale a Nefi.

3 Komabe, ndalandira lamulo la Ambuye kuti ndikonze mapale awa, pa cholinga chapadera choti pakuyenera kukhala mbiri yozokotedwa ya utumiki wa anthu anga.

4 Pamapale ena pakuyenera kuzokotedwa mbiri ya ulamuliro wa mafumu, ndi nkhondo ndi mikangano ya anthu anga; kotero mapale awa ali pa gawo lalikulu la utumiki; ndi mapale ena ali pa gawo lalikulu la ulamuliro wa mafumu ndi nkhondo ndi mikangano ya anthu anga.

5 Kotero, Ambuye andilamula kuti ndipange mapale awa ndi cholinga chanzeru mwa iye, chimene cholinga chake sindikuchidziwa.

6 Koma Ambuye amadziwa zinthu zonse kuyambira pachiyambi; kotero, iye amakonza njira kuti akwaniritse ntchito zake zonse pakati pa ana a anthu; pakuti taonani, iye ali ndi mphamvu zonse za kukwaniritsa mawu ake onse. Ndipo zili chomwechi. Amen.