Malembo Oyera
1 Nefi 4


Mutu 4

Nefi apha Labani pa kulamula kwa Ambuye ndipo kenako atenga mapale a mkuwa mwa ukathyali—Zoramu asankha kupita ndi banja la Lehi m’chipululu. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti ndidayankhula kwa abale anga, nati: Tiyeni tipite ku Yerusalemu, ndipo tiyeni tikhale okhulupilika m’kusunga malamulo a Ambuye; pakuti taonani iye ali wamphamvu kuposa dziko lonse lapansi, ndiye asakhale bwanji wamphamvu kuposa Labani ndi makumi asanu ake, inde, kapena ngakhale makumi a zikwi zake?

2 Kotero tiyeni tipite; tiyeni tikhale amphamvu monga Mose; pakuti zoonadi iye adayankhula kwa madzi a Mnyanja Yofiira ndipo adagawanika uku ndi uku, ndipo makolo athu adadutsa, kuchokera mu ukapolo, pa nthaka youma, ndipo magulu ankhondo a Farao adatsatira ndipo adamira m’madzi a Nyanja Yofiira.

3 Tsopano taonani inu mukudziwa kuti izi ndi zoona; ndipo mukudziwanso kuti mngelo walankhula ndi inu; mukukaikira bwanji? Tiyeni tipite; Ambuye angathe kutilanditsa ife, monga makolo athu, ndi kuononga Labani, monganso Aigupto.

4 Tsopano pamene ine ndidanena mawu awa, iwo adakwiyabe, ndipo adapitirizabe kung’ung’udza; komabe iwo adanditsatira mpaka tidafika kunja kwa makoma a Yerusalemu.

5 Ndipo udali usiku; ndipo ndidawachititsa kuti abisale kunja kwa makomawo. Ndipo atabisala, ine, Nefi, ndidakwawira mu mzindawo ndipo ndidapita cha ku nyumba ya Labani.

6 Ndipo ndidatsogozedwa ndi Mzimu, osadziwatu zimene ndiyenera kuchita.

7 Komabe ndidapita, ndipo pamene ndidafika pafupi ndi nyumba ya Labani ndidaona munthu, ndipo adagwa pansi patsogolo panga, pakuti adali ataledzera ndi vinyo.

8 Ndipo pamene ndidafika kwa iye, ndidapeza kuti ndi Labani.

9 Ndipo ndidaona lupanga lake, ndipo ndidalisolola m’chimake; ndipo chogwilira chake chidali cha golidi weniweni, ndipo mapangidwe ake adali abwino kwambiri, ndipo ndidaona kuti mpeni wake udali wa chitsulo chamtengo wapatali.

10 Ndipo zidachitika kuti ndidakakamizidwa ndi Mzimu kuti ndiphe Labani; koma ndidati mumtima mwanga: Sindidakhetsepo mwazi wa munthu. Ndipo ndidafooka, ndi kufuna kuti ndisamuphe.

11 Ndipo Mzimu udati kwa ine kachiwiri: Ona Ambuye wampereka iye m’manja mwako. Inde, ndipo ine ndidadziwanso kuti iye adafuna kutenga moyo wanga; inde, ndipo sadamvere malamulo a Ambuye; ndipo adatilandanso chuma chathu.

12 Ndipo zidachitika kuti Mzimu udanena kwa ine kachiwiri: Muphe, pakuti Ambuye wampereka m’manja mwako;

13 Taona, Ambuye amapha oipa kuti abweretse zolinga zake zolungama. Ndi bwino kuti munthu mmodzi aonongeke kusiyana ndi kuti dziko lichepe muchikhulupiliro ndi kuwonongeka.

14 Ndipo tsopano, pamene ine, Nefi, ndidamva mawu amenewa, ndidakumbukira mawu a Ambuye amene adayankhula kwa ine m’chipululu, kunena kuti: Pamene mbewu yako idzasunga malamulo anga, idzachita bwino m’dziko la lonjezo.

15 Inde, ndipo ndidaganizanso kuti sakadasunga malamulo a Ambuye molingana ndi lamulo la Mose, pokhapokha akhale ndi lamulolo.

16 Ndipo ndidadziwanso kuti lamulo lidali lolembedwa pa mapale a mkuwa.

17 Ndiponso, ndidadziwa kuti Ambuye adali atapereka Labani m’manja mwanga kaamba ka chifukwa chimenechi—kuti ine ndikatenge zolembazo molingana ndi malamulo ake.

18 Kotero, ndidamvera liwu la Mzimu, ndipo ndidagwira Labani ndi tsitsi la pamutu, ndipo ndidadula mutu wake ndi lupanga lake lomwe.

19 Ndipo nditadula mutu wake ndi lupanga lake lomwe, ndidatenga zovala za Labani, ndi kuzivala pathupi langa; inde, ngakhale gawo lirilonse; ndipo ndidamanga chida cha m’chiuno mwake m’chiuno mwanga.

20 Ndipo nditachita izi, ndidapita m’malo mosungiramo chuma cha Labani. Ndipo pamene ndidapita ku malo osungiramo chuma cha Labani, taonani, ndidaona wantchito wa Labani amene adali ndi mfungulo za mosungiramo chuma. Ndipo ndidamulamulira iye m’mawu a Labani, kuti apite ndi ine mosungiramo chuma.

21 Ndipo iye adaganiza kuti ndidali mbuye wake, Labani, pakuti adaona zovala komanso lupanga lomangidwa m’chiwuno mwanga.

22 Ndipo iye adayankhula kwa ine zokhudzana ndi akulu a Ayuda, iye adali kudziwa kuti mbuye wake, Labani, adali atatuluka usiku pakati pawo.

23 Ndipo ndidayankhula kwa iye ngati kuti ndidali Labani.

24 Ndipo ndidayankhulanso kwa iye kuti ndinyamule zozokotedwa, zimene zidali pa mapale a mkuwa, kwa abale anga aakulu, amene adali kunja kwa makoma.

25 Ndipo ndidamuuzanso kuti anditsate.

26 Ndipo iye, poganiza kuti ndimalankhula za abale a mpingo, ndi kuti ndidalidi Labani amene ndidamupha, kotero adanditsatira.

27 Ndipo adayankhula kwa ine kambirimbiri ponena za akulu a Ayuda, pamene ine ndimapita kwa abale anga, amene adali kunja kwa makoma.

28 Ndipo zidachitika kuti pamene Lamani adandiwona iye adawopa kwambiri, komanso Lemueli ndi Samu. Ndipo adathawa pamaso panga; iwo adaganiza kuti adali Labani, ndi kuti adandipha ine ndipo adafuna kutenga miyoyo yawonso.

29 Ndipo zidachitika kuti ndidawaitana, ndipo adandimvera; kotero iwo adasiya kuthawa pamaso panga.

30 Ndipo zidachitika kuti pamene wantchito wa Labani adaona abale anga adayamba kunjenjemera, ndipo adali pafupi kuthawa pamaso panga ndi kubwelera ku mzinda wa Yerusalemu.

31 Ndipo tsopano ine, Nefi, pokhala munthu wamkulu msinkhu, ndipo ndidalandiranso mphamvu zambiri kwa Ambuye, kotero ndidamugwira watchito wa Labani, ndipo ndidamugwira kuti asathawe.

32 Ndipo zidachitika kuti ndidayankhula naye, kuti akamvera mau anga, ngati Ambuye ali wa moyo, ndi inenso ndiri wamoyo, kotero kuti akamvera mau athu, timusiira moyo wake.

33 Ndipo ndidayankhula naye, angakhale ndi lumbiro, kuti asaope; kuti akhala mfulu monga ife ngati adzapita m’chipululu pamodzi ndi ife.

34 Ndipo ndidayankhulanso kwa iye, kuti: Zoonadi Ambuye watilamulira ife kuchita chinthu ichi; ndipo kodi tisakhale akhama m’kusunga malamulo a Ambuye? Kotero, ngati iwe upita ku chipululu kwa atate anga udzakhala ndi malo ndi ife.

35 Ndipo zidachitika kuti Zoramu adalimbika mtima pa mawu amene ndidayankhula. Tsopano Zoramu lidali dzina la wantchitoyo; ndipo adalonjeza kuti adzapita kuchipululu kwa atate wathu. Inde, ndipo iye adalumbiranso kwa ife kuti adzakhala ndi ife kuchokera nthawi imeneyo kupita m’tsogolo.

36 Tsopano ife tidafuna kuti akhale nafe pa chifukwa ichi, kuti Ayuda asadziwe za kuthawira kwathu m’chipululu, kuti angatitsatire ndi kutiwononga.

37 Ndipo zidachitika kuti pamene Zoramu adachita lumbiro kwa ife, mantha athu okhudzana ndi iye adachoka.

38 Ndipo zidachitika kuti tidatenga mapale a mkuwa ndi wantchito wa Labani, ndipo tidapita m’chipululu, ndipo tidayenda kupita ku chihema cha atate athu.

Print