Malembo Oyera
1 Nefi 14


Mutu 14

Mngelo auza Nefi za madalitso ndi matembelero amene adzagwera pa Amitundu—Pali mipingo iwiri yokha basi: Mpingo wa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu ndi mpingo wa mdyerekezi—Oyera mtima a Mulungu m’maiko onse azunzidwa ndi mpingo wonyansa waukulu—Mtumiki Yohane adzalemba zokhudzana ndi kutha kwa dziko lapansi. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidzachitika, kuti ngati Amitundu adzamvera kwa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu mtsiku limene iye adzadzionetsere yekha kwa iwo m’mau, komanso mu mphamvu, ndi ntchito zake kufikira kuchotsa zopunthwitsa zawo—

2 Ndi kusaumitsa mitima yawo motsutsana ndi Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, iwo adzawerengedwa pamodzi ndi mbewu ya bambo ako; inde, iwo adzawerengedwa pamodzi ndi a nyumba ya Israeli; ndipo iwo adzakhala anthu odalitsidwa mu dziko la lonjezano kwa muyaya; sadzatengedwanso kupita ku ukapolo; ndipo nyumba ya Israeli sidzagonjetsedwanso.

3 Ndipo dzenje lalikululo, limene lidakumbidwa chifukwa cha iwo ndi mpingo wonyansa waukulu, umene udakhazikitsidwa ndi mdyerekezi ndi ana ake, kuti iye atsogolere miyoyo ya anthu ku gahena—inde, dzenje lalikulu lomwe lidakumbidwa kuti awononge anthu, lidzazadza ndi iwo amene adalikumba, mpaka kuchionongeko chawo chonse, atero Mwana wa Nkhosa wa Mulungu; osati kuonongedwa kwa mzimu, koma kuti kuponyedwa kwake ku gahena imene ilibe malire.

4 Pakuti taonani, izi ndi monga mwa ukapolo wa mdyerekezi, ndiponso monga mwa chilungamo cha Mulungu, pa onse amene adzachita ntchito zakuipa ndi zonyansa pamaso pake.

5 Ndipo zidachitika kuti mngelo adayankhula kwa ine Nefi, nati: Iwe waona kuti ngati Amitundu alapa zidzakhala bwino kwa iwo; ndipo iwenso ukudziwa zokhudzana ndi mapangano a Ambuye kwa nyumba ya Israeli; ndipo iwenso wamva kuti amene salapa akuyenera kutayika.

6 Potero, tsoka kwa Amitundu ngati zikhale kuti iwo alimbitsa mitima yawo motsutsana ndi Mwana wa Nkhosa wa Mulungu.

7 Pakuti ikudza nthawi, Akutero Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, imene ndidzagwire ntchito yayikulu ndi yodabwitsa pakati pa ana a anthu; ntchito imene idzakhala yamuyaya, kaya kudzanja ili kapena dzanja linali—kapena pakuwatsimikizira iwo za mtendere ndi moyo wamuyaya, kapena ku chiombolo cha iwo pakulimbitsa mitima yawo ndi khungu la m’maganizo awo mpaka kuwabweretsa ku ukapolo, ndiponso kuchionongeko, zonse mwa thupi ndi mwauzimu, monga mwa ukapolo wa mdyerekezi, umene ine ndayankhula.

8 Ndipo zidachitika kuti mngelo atayankhula mawu awa, adati kwa ine: ukukumbukira iwe zamapangano a Atate kwa nyumba ya Israeli? Ndipo ndidati kwa iye, inde.

9 Ndipo zidachitika kuti iye adati kwa ine: Yang’ana, ndipo ndidaona kuti mpingo waukulu ndi wonyansa, umene ndi manthu wa zonyansa, amene mtsogoleri wake ndi mdyerekezi.

10 Ndipo adati kwa ine: Taona pali mipingo iwiri yokha; umodzi ndi wa mwana wa Nkhosa wa Mulungu, ndipo wina ndi mpingo wa mdyerekezi; kotero iye amene sali wa mpingo wa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu ali mu mpingo waukuluwo, umene uli manthu wa zonyansa; ndipo iye ndiye wachigololo wa dziko lapansi.

11 Ndipo zidachitika kuti ndidapenya ndikuona wachigololo wa dziko lapansi, ndipo adali atakhala pa madzi ambiri, ndipo adali ndi ulamuliro padziko lonse lapansi, pakati pa maiko, mafuko, zinenero, ndi anthu.

12 Ndipo zidachitika kuti ndidaona mpingo wa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, ndipo chiwerengero chake chidali chochepa chifukwa cha uchimo ndi zonyansa za wachigololo amene adakhala pa madzi ambiri; komabe, ndidaona kuti mpingo wa Mwana wa Nkhosa, amene adali oyera mtima a Mulungu, udalinso pa nkhope ya dziko lonse lapansi; ndipo maulamuliro awo adali pankhope ya dziko lapansi udali wochepa, chifukwa cha kuipa kwa wa chigololo amene ndidamuona.

13 Ndipo zidachitika kuti ndidaona manthu wankulu wa zonyansa kuti adasonkhanitsa pamodzi makamu pankhope ya dziko lonse lapansi, pakati pa mafuko onse a Amitundu, kuti amenyane ndi Mwana wa Nkhosa wa Mulungu.

14 Ndipo zidachitika kuti ine, Nefi, ndidaona mphamvu ya Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, kuti idatsikira kwa oyera mtima a mpingo wa Mwana wa Nkhosa, ndi pa anthu apangano a Ambuye, amene adamwazikana pa nkhope yonse ya dziko lapansi; ndipo adali ndi zida za chilungamo, ndi mphamvu ya Mulungu mu ulemelero waukulu.

15 Ndipo zidachitika kuti ndidaona kuti mkwiyo wa Mulungu udatsanulidwa kwa mpingo woyipitsitsa waukulu, kuti kudali nkhondo ndi mbiri za nkhondo pakati pa mayiko onse ndi mafuko a padziko lapansi.

16 Ndipo pamene padayamba nkhondo ndi mbiri za nkhondo pakati pa mafuko amene adali a manthu wa zonyasa, mngelo adayankhula nane, nati: Taona, mkwiyo wa Mulungu uli pa manthu wachigololo; ndipo taona, iwe ukuona zinthu zonsezi—

17 Ndipo tsiku likadzafika limene mkwiyo wa Mulungu watsanulidwa kwa manthu wachigololo, amene ali mpingo wonyasa waukulu wa dziko lonse lapansi, umene mtsogoleri wake ndi mdyerekezi, kenako, pa tsikulo, ntchito ya Atate idzayambika, yokonza njira yokwaniritsira mapangano, amene iye adapanga kwa anthu ake amene ali a nyumba ya Israeli.

18 Ndipo zidachitika kuti mngelo adayankhula nane, nati: Yang’ana!

19 Ndipo ndidayang’ana ndi kuona munthu, ndipo adali atavala mwinjiro woyera.

20 Ndipo mngelo adati kwa ine: Taona m’modzi mwa atumwi khumi ndi awiri a Mwana wa Nkhosa.

21 Taona, iye adzaona ndi kulemba zotsalira za zinthu izi; inde, ndi zinthu zina zambiri zimene zachitika.

22 Ndipo adzalembanso zokhudzana ndi kutha kwa dziko lapansi.

23 Kotero, zinthu zomwe iye adzalembe ndi zolungama ndi zoona; ndipo taona zidalembedwa mu buku limene iwe waliona likuchokera pakamwa pa Myuda: ndipo panthawiyo zidzatuluka pakamwa pa Myuda, kapena panthawi imene zinkatuluka pakamwa pa Myuda, zinthu zimene zidalembedwa zidali zomveka komanso zoyera, ndi zamtengo wapatali, ndi zosavuta kumvetsetseka kwa anthu onse.

24 Ndipo taona, zinthu zimene mtumwi wa Mwana wa Nkhosayu adzalembe ndi zimene iwe waziona; ndipo taona, zotsalira udzaziona.

25 Koma zinthu zimene iwe udzaziona kuchoka pano siudzazilemba; pakuti Ambuye Mulungu adadzodza mtumwi wa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu kuti iye adzazilembe.

26 Ndiponso ena amene adakhalako, kwa iwo adaonetsera zinthu zonse, ndipo adazilemba izo; ndipo zasindikizidwa kuti zidzatuluke mu chiyero, monga mwa choonadi chimene chili mwa Mwana wa Nkhosa, mu nthawi yake yoikika ya Ambuye, kwa nyumba ya Israeli.

27 Ndipo ine, Nefi, ndidamva ndi kuchitira umboni, kuti dzina la mtumwi wa Mwana wa Nkhosa lidali Yohane, monga mwa mawu a mngelo.

28 Ndipo taonani, ine, Nefi, ndaletsedwa kuti ndilembe zotsalira za zinthu zimene ndidaona ndi kuzimva; kotero zinthu zimene ndalemba ndizokwanira kwa ine; ndipo ndalemba koma gawo lochepa la zinthu zomwe ndidaziona.

29 Ndipo ndikuchitira umboni kuti ndidaona zinthu zimene atate anga adaona, ndi mngelo wa Ambuye adadziwitsa izi kwa ine.

30 Ndipo tsopano ine ndikumaliza kuyankhula zokhudzana ndi zinthu zimene ndidaona pamene ndidanyamulidwa mu Mzimu; ndipo ngati zinthu zonse zomwe ndidaona sizidalembedwe, zomwe ndalembazo ndizoona. Ndipo zili choncho. Ameni.