Malembo Oyera
Mormoni 8


Mutu 8

Alamani afunafuna ndi kuwononga Anefi—Buku la Mormoni lidzabwera ndi mphamvu ya Mulungu—Matsoka anenedweratu pa iwo amene apumira mkwiyo ndi kudana ndi ntchito ya Ambuye—Zolembedwa za Anefi zidzabwera mu tsiku la kuipa, kucheperachepera, ndi mpatuko. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 400–421.

1 Taonani ine, Moroni, ndikumaliza zolemba za atate anga, Mormoni. Taonani, ndili nazo koma zinthu zochepa zoti ndilembe, zinthu zimene ndalamulidwa ndi atate anga.

2 Ndipo tsopano zidachitika kuti itatha nkhondo yayikulu ndi yopambana pa Kumora, taonani, Anefi amene adathawira ku dziko lakum’mwera adasakidwa ndi Alamani, kufikira onse adawonongedwa.

3 Ndipo atate anganso adaphedwa ndi iwo, ndipo ngakhale ine ndidatsala ndekha kuti ndilembe nkhani yachisoni ya chiwonongeko cha anthu anga. Koma taonani, iwo apita, ndipo ndikukwaniritsa lamulo la atate anga. Ndipo ngati adzandiphe, sindikudziwa.

4 Kotero ndidzalemba ndi kubisa zolembazi m’nthaka; ndipo komwe ndikulowera zilibe kanthu.

5 Taonani, atate anga adapanga zolemba izi, ndipo iwo adalembanso cholinga chake. Ndipo taonani, ndikadachilembanso ngati ndikadakhala ndi malo pa mapalewa, koma ndilibe; ndipo miyala yosungunula ndilibe, pakuti ndili ndekha. Atate anga aphedwa kunkhondo, ndi abale anga onse, ndipo ndilibe anzanga kapena komwe ndingapite; ndipo ndi kotalika bwanji Ambuye adzalora kuti ndikhale moyo sindikudziwa.

6 Taonani, dzaka mazana anayi zatha chibwelereni Ambuye ndi Mpulumutsi wathu.

7 Ndipo taonani, Alamani asaka anthu anga, Anefi, kuchokera mzinda ndi mzinda ndi kuchokera ku malo ndi malo, ngakhale kufikira onse atha; ndipo kwakukulu kwakhala kugwa kwawo; inde, chachikulu ndi chodabwitsa chakhala chiwonongeko cha anthu anga, Anefi.

8 Ndipo taonani, ndi dzanja la Ambuye lomwe lachita izi. Ndipo taonaninso, Alamani ali pa nkhondo wina ndi mzake; ndipo nkhope yonse ya dzikoli ndi lozungulilidwa ndi kuphana ndi kukhetsa mwazi; ndipo palibe amene akudziwa mapeto ankhondoyi.

9 Ndipo tsopano, taonani, sindinenanso zokhudzana ndi iwo, pakuti palibe ena kupatula Alamani ndi achiwembu amene alipo pa nkhope ya dzikoli.

10 Ndipo palibe ena amene akudziwa Mulungu weniweni kupatula ophunzira a Yesu, amene adali naye mu dzikoli kufikira kuipa kwa anthu kudali kwakukulu mpaka Ambuye sadalore iwo kukhalabe ndi anthu, ndipo kaya ali pankhope yadzikoli palibe munthu akudziwa.

11 Koma taonani, atate anga ndi ine tawaona iwo, ndipo atitumikira ife.

12 Ndipo aliyense amene adzalandire zolemba izi, ndipo sadzaziweruza chifukwa cha zolakwika zimene zili m’menemo, yemweyo adzadziwa za zinthu zazikulu zoposera zimenezi. Taonani, Ine ndine Moroni; ndipo kukadakhala kotheka, ndikadadziwitsa zinthu zonse kwa inu.

13 Taonani, ndikumaliza kuyankhula zokhudzana ndi anthu awa. Ndine Mwana wa Mormoni, ndipo atate anga adali chidzukulu cha Nefi.

14 Ndipo ndine yemweyo amene ndidabisa zolembazi kwa Ambuye; mapale akewo ndiopanda phindu chifukwa cha lamulo la Ambuye. Pakuti zoona iye adati pasadzakhale woti akhale nawo kuti apindule; koma zolemba zakezo ndizamtengo wapatali; ndipo amene adzazibweretse m’kuwala, ameneyo Ambuye adzamudalitsa.

15 Pakuti palibe angakhale ndi mphamvu yozibweretsa m’kuwala kupatula zitapatsidwa kwa iye ndi Mulungu; pakuti Mulungu akufuna kuti zidzachitike ndi diso lolunjika ku ulemelero wake, kapena ubwino wa anthu apangano akale ndi obalalitsidwa kalekale a Ambuye.

16 Ndipo odala akhale iye amene adzabweretse chinthu ichi m’kuwala; pakuti chidzabweretsedwa kuchokera ku mdima kufika m’kuwala, molingana ndi mawu a Mulungu; inde, chidzabweretsedwa kuchokera ku nthaka, ndipo chidzawalira kuchokera ku mdima, ndi kubwera m’kuzindikirika kwa anthu; ndipo zidzachitika ndi mphamvu ya Mulungu.

17 Ndipo ngati padzakhale zolakwika zidzakhala zolakwika za munthu. Koma taonani, ife sitikudziwa zolakwikazo; komabe Mulungu amadziwa zinthu zonse; kotero, iye amene akutsutsa, muloleni azindikire kuopa angakhale wopalamula gahena wamoto.

18 Ndipo iye onena kuti; Ndionetse ine, kapena udzakanthidwa—muloleni akhale ochenjera kuopa kuti angalamule icho chimene chili choletsedwa ndi Ambuye.

19 Pakuti taonani, yemweyo oweruza mofulumira adzaweruzidwanso mofulumira; pakuti molingana ndi ntchito zake mphotho yake idzakhala; kotero, iye amene akantha adzakanthidwanso, ndi Ambuye.

20 Taonani zimene malembo oyera amanena—munthu asadzakanthe, ngakhale kuweruza; pakuti kuweruza ndi kwanga, atero Ambuye, ndipo kubwenzera ndi kwanganso, ndipo ndidzabwenza.

21 Ndipo iye amene adzapumira mkwiyo ndi ndewu motsutsana ndi ntchito ya Ambuye, ndi kutsutsana ndi anthu apangano a Ambuye amene ali nyumba ya Israeli, ndipo adzati: Tiwononga ntchito ya Ambuye, ndipo Ambuye sadzakumbukira pangano ili limene wapanga ndi nyumba ya Israeli—yemweyo ali pangozi yodulidwa ndi kuponyedwa mu moto.

22 Pakuti zolinga zamuyaya za Ambuye zidzapitilira, kufikira malonjezano ake onse adzakwaniritsidwe.

23 Fufuzani mauneneri a Yesaya. Taonani, sindingawalembe. Inde, taonani ndikunena ndi inu, kuti awo oyera mtima amene adatsogola, amene adali mdziko ili, adzalira, inde, ngakhale kuchokera ku fumbi adzalira kwa Ambuye; ndipo monga Ambuye ali wamoyo adzakumbukira pangano limene adapanga ndi iwo.

24 Ndipo iye akudziwa mapemphero awo, kuti adali m’malo mwa azibale awo. Ndipo akudziwa chikhulupiliro chawo, pakuti mu dzina lake iwo ankatha kuchotsa mapiri; ndipo mu dzina lake ankatha kuchititsa nthaka kugwedezeka; ndipo ndi mphamvu ya mawu ake ankatha kuchititsa ndende kugwa pansi; inde, ngakhale moto woopsya sukadatha kuwavulaza iwo, ngakhale zilombo kapena njoka zachiphe, chifukwa cha mphamvu ya mawu ake.

25 Ndipo taonani, mapemphero awo adalinso m’malo mwa iye amene Ambuye adzamulole kuti adzabweretse zinthu izi.

26 Ndipo palibe m’modzi anganene kuti izi sizidzabwera, pakuti zidzabwera ndithu, pakuti ambuye anena chimenechi; pakuti kuchokera pansi pamthaka zidzabwera, ndi dzanja la Ambuye, ndipo palibe angachiletse; ndipo chidzabwera mu tsiku limene zidzanenedwa kuti zozizwitsa zidatha; ndipo chidzabwera ngakhale monga ngati kuti wina akuyankhula kuchokera kwa kufa.

27 Ndipo idzabwera mu tsiku limene mwazi wa oyera mtima udzafuula kwa Ambuye, chifukwa cha magulu achinsinsi ndi ntchito za mdima.

28 Inde, idzabwera mu tsiku limene mphamvu ya Mulungu idzakanidwa, ndi mipingo idzadetsedwa ndi kukwezedwa m’kunyada kwa mitima yawo; inde, ngakhale mu tsiku limene atsogoleri a mipingo ndi aphunzitsi adzadzuka m’kunyada kwa mitima yawo, ngakhale m’kuchitira nsanje iwo amene ali m’mipingo yawo.

29 Inde, idzabwera mu tsiku limene kudzamveka za moto, ndi anamondwe, ndi nthunzi wa utsi kumaiko akunja;

30 Ndipo kudzamvekanso za nkhondo, ndi mphekesera za nkhondo, ndi zivomelezi mu malo osiyanasiya.

31 Inde, idzabwera mu tsiku limene kudzakhale kuipitsa kwakukulu pa nkhope ya dziko lapansi; kudzakhala kuphana, ndi kuberana, ndi kunamizana,ndi kunyengana, ndi zigololo, ndi zonyansa zamitundu yonse; pamene kudzakhala ambiri amene adzidzati, Chita ichi, kapena chita icho, ndipo zilibe kanthu, pakuti Ambuye adzavomereza zotero pa tsiku lotsiliza. Koma tsoka kwa otere, pakuti ali mu ndulu yowawa ndi mu nsinga za uchimo.

32 Inde, zidzabwera mu tsiku limene kudzakhala mipingo yomangidwa imene idzidzati: Bwerani kwa ine, ndipo ndi ndalama zanu mudzakhululukidwa machimo anu.

33 O inu ankhanza ndi okhota ndi anthu osamva, n’chifukwa chiyani mukumanga mipingo kwa inu nokha kuti mupeze phindu? N’chifukwa chiyani mwasintha mawu oyera a Mulungu, kuti mubweretse chiwonongeko pa miyoyo yanu? Taonani, yang’anani ku mavumbulutso a Mulungu; pakuti taonani, nthawi ilinkudza pa tsiku limene zinthu zonsezi zikuyenera kukwaniritsidwa.

34 Taonani, Ambuye aonetsera kwa ine zinthu zazikulu ndi zodabwitsa zokhudzana ndi izo zimene zikuyenera kubwera posachedwa, pa tsikulo limene zinthu zimenezi zidzabwera pakati panu.

35 Taonani, ndikuyankhula kwa inu ngati kuti mudali pomwepo, koma inu palibe. Koma taonani, Yesu Khristu wandionetsera inu kwa ine, ndipo ndikudziwa zochita zanu.

36 Ndipo ndikudziwa kuti mumayenda m’kunyada kwa mitima yanu; ndipo kulibe ena kupatula ochepa amene samadzikweza okha m’kunyada kwa mitima yawo, pakuvala zovala zabwino kwambiri, ku kaduka, ndi mikangano, ndi dumbo, ndi kuzunzana, ndi mitundu yonse ya kusaweruzika; ndi mipingo yanu, inde, ngakhale yonse, yakhala yoipitsidwa chifukwa cha kudzikuza kwa mitima yanu.

37 Pakuti taonani, mumakonda ndalama, ndi chuma chanu, ndi zovala zanu zabwino, ndi kukongoletsa mipingo yanu, kuposera m’mene mumakondera osauka, ndi osowa, odwala ndi osautsidwa.

38 O inu oyipitsa, inu achinyengo, inu aphunzitsi, amene mumazigulitsa nokha pa zomwe zidzaole, n’chifukwa chiyani mwayipitsa mpingo oyera wa Mulungu? N’chifukwa chiyani mukuchita manyazi kutenga pa inu dzina la Khristu? N’chifukwa chiyani simuganiza kuti waukulu ndi mtengo wa chimwemwe chosatha kuposera chisoni chimene sichidzafa—chifukwa cha matamando a dziko lapansi?

39 N’chifukwa chiyani mumadziveka nokha ndi zimene zilibe moyo, ndipo koma mumalora anjala, ndi osowa, ndi amaliseche, ndi odwala ndi asautsidwa kuti akudutseni, ndipo simumawalabadira?

40 Inde, n’chifukwa chiyani mukukhazikitsa magulu anu achinsinsi onyansa kuti mupeze phindu, ndi kuchititsa akazi amasiye kuti alire pamaso pa Ambuye, ndiponso ana amasiye kuti alire pamaso pa Ambuye, ndiponso mwazi wa makolo awo ndi azimuna awo kuti ufuule kwa Ambuye kuchokera pansi pa nthaka, pakubwenzera pa mitu yanu?

41 Taonani, lupanga lobwenzera lalendekera pa inu; ndipo posachedwa nthawi ilinkudza imene iye adzabwenzera mwazi wa oyera mtima pa inu, pakuti iye sadzalora kulira kwawo kupitilire.

Print