Malembo Oyera
Mormoni 9


Mutu 9

Moroni ayitana iwo amene sakukhulupilira mwa Khristu kuti alape—Iye alengeza Mulungu wa zozizwitsa, amene amapereka mavumbulutso ndi kutsanulira mphatso ndi zizindikiro pa okhulupirika—Zozizwitsa zimasiya chifukwa cha kusakhulupilira—Zizindikiro zimatsata iwo amene amakhulupilira—Anthu alangizidwa kuti akhale ndi nzeru ndi kusunga malamulo. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401–421.

1 Ndipo tsopano, ndiyankhulanso zokhudzana ndi iwo amene samakhulupilira mwa Khristu.

2 Taonani, kodi mudzakhulupilira mu tsiku lakuyenderedwa kwanu—taonani, pamene Ambuye adzabwera, inde, ngakhale tsiku lalikululo limene dziko lapansi lidzapindidwa pamodzi ngati mpukutu, ndipo zinthu zidzanyeta ndi kutentha kwakukulu, inde, mu tsiku lalikululo limene mudzabweretsedwe kuti muime pamaso pa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu—ndeno mudzanena kuti kulibe Mulungu?

3 Kenako mudzapilitiliza kumukana Khristu, kapena mungathe kuona Mwana wa Nkhosa wa Mulungu? Kodi mukuganiza kuti mudzakhala pansi pa chikumbumtima cha kulakwa kwanu? Kodi mukuganiza kuti mudzatha kukhala osangalala kukhala ndi Munthu woyera, pamene mitima yanu yakhudzidwa ndi chikumbumtima cha kulakwa komwe inu mwagwiritsira mosayenera malamulo ake?

4 Taonani, ndikunena kwa inu kuti mudzakhala achisoni kwambiri kukhala ndi Mulungu woyera ndi wolungama, pansi pa chikumbumtima cha zonyansa zanu pamaso pake, kuposa kukhala ndi mizimu yoweruzidwa mu gahena.

5 Pakuti taonani, pamene inu mudzabweretsedwa kuti muone umaliseche wanu pamaso pa Mulungu, ndiponso ulemelero wa Mulungu, ndi kuyera kwa Yesu Khristu, zidzayatsa lawi la moto osazimitsika pa inu.

6 O ndiye inu osakhulupilira, tembenukirani kwa Ambuye; fuulani mwamphamvu kwa Atate mu dzina la Yesu kuti mwina mungathe kupezeka opanda banga, oyera, mutayeretsedwa ndi mwazi wa Mwana wa Nkhosa, pa tsiku lalikulu ndi lomalizalo.

7 Ndipo kachiwiri ndikuyankhula ndi inu amene mumakana mavumbulutso a Mulungu, ndi kunena kuti adalekeka, kuti kulibe mavumbulutso, kapena mauneneri, kapena mphatso, kapena machilitso, kapena kuyankhula ndi malilime, ndi kutanthauzira malilime;

8 Taonani ndikunena ndi inu, iye amene amakana zinthu izi sadziwa uthenga wabwino wa Khristu; inde, sadawerenge malembo oyera; ngati n’choncho, iye sadawamvetse.

9 Pakuti kodi sitiwerenga kuti Mulungu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse, ndipo mwa iye mulibe kusiyana ngakhale kusintha pang’ono?

10 Ndipo tsopano, ngati inu mwaganizira kwanokha mulungu amene amasintha, ndi mwa amene muli kusintha pang’ono, ndiye mwaganiza kwanokha mulungu amene sali Mulungu wa zozizwitsa.

11 Koma taonani, ndikuonetsani kwa inu Mulungu wa zozizwitsa, ngakhale Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo; ndipo ndi Mulungu yemweyo amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zinthu zonse zimene zili m’menemo.

12 Taonani, iye adalenga Adamu, ndipo kudzera mwa Adamu kudabwera kugwa kwa munthu. Ndipo chifukwa cha kugwa kwa munthu kudabwera Yesu Khristu, ngakhale Atate ndi Mwana; ndipo chifukwa cha Yesu Khristu kudabwera chiwombolo cha munthu.

13 Ndipo chifukwa cha chiwombolo cha munthu, chimene chidabwera ndi Yesu Khristu, iwo adabwezeretsedwanso pamaso pa Ambuye, umu ndi momwe anthu onse adawomboledwera, chifukwa imfa ya Khristu imabweretsa chiukitso, chimene chimabweretsa chiwombolo kuchokera ku tulo losatha, kumene tulo take anthu onse adzadzutsidwa ndi mphamvu ya Mulungu pamene lipenga lidzalira; ndipo iwo adzatulukira, onse aang’ono ndi aakulu, ndipo adzaima pamaso pa bwalo lake, atawomboledwa ndi kumasulidwa ku zingwe za muyaya za imfa, imene imfa yake ndi yakuthupi.

14 Ndipo kenako kudzabwera chiweruzo cha Oyerayo pa iwo; ndipo kenako nthawi idzafika imene iye amene ali wonyansa adzakhala wonyansabe; ndipo iye amene ali wolungama adzakhala wolungamabe; iye amene ali wosangalala adzakhala wosangalalabe; ndi iye amene ali wosasangalala adzakhala wosasangalalabe.

15 Ndipo tsopano, O inu nonse amene mwaganizira kwanokha mulungu amene sangachite zozizwitsa, ndikufunsani, kodi zinthu zonsezi zachitika, zimene ine ndayankhulazi? Kodi mapeto afika kale? Taonani, ndinena kwa inu, Ayi; ndipo Mulungu sadasiye kukhala Mulungu wa zozizwitsa.

16 Taonani, kodi zinthu zomwe Mulungu wachita sizodabwitsa m’maso mwathu? Inde, ndipo ndani amene angazindikire ntchito za Mulungu?

17 Ndani anganene kuti sichidali chozizwitsa kuti ndi mawu ake kumwamba ndi dziko lapansi zikhale; ndipo ndi mphamvu ya mawu ake munthu adalengedwa ku fumbi la mnthaka; ndipo ndi mphamvu ya mawu ake zozizwitsa zachitidwa?

18 Ndipo ndani anganene kuti Yesu Khristu sadachite zozizwitsa zamphamvu zambiri? Ndipo padali zozizwitsa zamphamvu zambiri zochitidwa ndi manja a atumwi.

19 Ndipo ngati kudachitidwa zozizwitsa nthawi imeneyo, n’chifukwa chiyani Mulungu wasiya kukhala Mulungu wa zozizwitsa ndipo chonsecho iye ndi Munthu wosasintha? Ndipo taonani, ndikunena kwa inu iye samasintha; ngati ndi choncho akadasiya kukhala Mulungu; ndipo iye sadasiye kukhala Mulungu, ndipo ndi Mulungu wa zozizwitsa.

20 Ndipo chifukwa chimene iye amasiya kuchita zozizwitsa pakati pa ana a anthu ndi chifukwa choti iwo acheperachepera mu kusakhulupilira, ndi kuchoka mu njira yolondora, ndipo sadziwa Mulungu amene akuyenera kum’khulupilira.

21 Taonani, ndikunena kwa inu kuti aliyense amene akhulupilira mwa Khristu, kusakayikira kanthu, chilichonse chimene iye adzapempha Atate mu dzina la Khristu chidzapatsidwa kwa iye; ndipo lonjezo limeneli liri kwa onse, ngakhale kumalekezero a dziko lapansi.

22 Pakuti taonani, atero Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, kwa ophunzira ake amene atakhalebe, inde, ndiponso kwa ophunzira ake onse, mu kumvetsera kwa unyinjiwo, Pitani inu ku dziko lapansi, ndi kukalalikira uthenga wabwino kwa zolengedwa zonse.

23 Ndipo iye amene akakhulupilire ndi kubatizidwa adzapulumuka, koma iye amene sadzakhulupilira adzaweruzidwa;

24 Ndipo izi ndi zizindikiro zomwe zidzawatsate amene akhulupilira—mu dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzayankhula ndi malilime atsopano; adzaponda zinkhanira; ndipo ngati adzamwe chinthu chokupha chilichonse sichidzawavulaza iwo; adzasanjika manja pa odwala ndipo adzachira;

25 Ndipo aliyense amene adzakhulupilire mu dzina langa, kusakayikira kanthu, kwa iye ndidzatsimikizira mawu anga onse, ngakhale kumalekezero a dziko lapansi.

26 Ndipo tsopano taonani, ndani angaime motsutsana ndi ntchito za Ambuye? Ndani angakane zonena zake? Ndani amene adzaime motsutsana ndi Ambuye wamphamvu zonse? Ndani amene adzanyoze ntchito za Ambuye? Ndani amene adzanyoze ana a Khristu? Taonani, inu nonse amene muli onyoza ntchito za Ambuye, pakuti mudzadabwa ndi kuwonongeka.

27 O ndiyeno musanyoze, ndipo musadabwe, koma mumvetsere ku mawu a Ambuye, ndi kupempha Atate mu dzina la Yesu pa zinthu zilizonse zomwe mudzafune. Musakayikire, koma khulupilirani, ndi kuyamba monga mu nthawi yakale, ndi kubwera kwa Ambuye ndi mtima wanu onse, ndipo limbitsani chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera pamaso pake.

28 Khalani anzeru mu masiku anu a nthawi yoyeseredwa; dzivuleni nokha ku zonse zonyansa; musapemphe, kuti muchiwonongere pa zilakolako zanu, koma pemphani mosagwedezeka, kuti musadzipereke ku mayesero, koma kuti mudzatumikire Mulungu weniweni ndi wa moyo.

29 Onani kuti simudabatizidwe muli wosayenera; onani kuti simukudya mgonero wa Khristu muli wosayenera; koma onani kuti mukuchita zinthu zonsezi muli oyenera, ndipo muchite izi mu dzina la Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo; ndipo ngati muchita izi, ndi kupilira kufikira chimaliziro, simudzaponyedwa mwanjira iliyonse kunja ayi.

30 Taonani, ndikuyankhula kwa inu monga ngati ndikuyankhula kuchokera kwa akufa; pakuti ndikudziwa kuti mudzakhala ndi mawu anga.

31 Musandiweruze chifukwa cha zolakwa zanga, ngakhale atate anga, chifukwa cha zolakwa zawo, ngakhale iwo amene alemba ine ndisadabwere; koma m’malo mwake muthokoze kwa Mulungu kuti wadziwitsa kwa inu zolakwa zathu, kuti mukathe kuphunzira kukhala anzeru kuposa m’mene ife takhalira.

32 Ndipo tsopano, taonani, ife talemba zolemba izi molingana ndi chidziwitso chathu, mu zolemba zimene zimatchedwa pakati pa anthu athu Chi igupto chokonzedwanso, kuperekedwa ndi kusinthidwa ndi ife, molingana ndi kayankhulidwe kathu.

33 Ndipo akadakhala kuti mapale athuwa adali aakulu mokwanira tikadalemba mu Chihebri; koma Chihebri chasinthidwanso ndi ife; ndipo tikadalemba mu Chihebri, taonani simukadakhala ndi zolakwika mu zolemba zathu.

34 Koma Ambuye akudziwa zinthu zimene ife tazilemba, ndiponso kuti palibe anthu ena akudziwa chiyankhulo chathu; ndipo chifukwa choti palibe anthu ena akudziwa chiyankhulo chathuchi, kotero iye wakonza njira ya kumasulira kwake.

35 Ndipo zinthu izi zalembedwa kuti ife tichotse zovala zathu mwazi wa abale athu, amene acheperachepera mu kusakhulupilira.

36 Ndipo taonani, zinthu izi zimene ife takhumbira zokhudzana ndi abale athu, inde, ngakhale kubwenzeretsedwa kwa chidziwitso cha Khristu, zili molingana ndi mapemphero a oyera mtima onse amene adakhalapo m’dzikoli.

37 Ndipo Ambuye Yesu Khristu apangitse kuti mapemphero awo akathe kuyankhidwa molingana ndi chikhulupiliro chawo; ndipo Mulungu Atate akathe kukumbukira pangano limene iye adapanga ndi nyumba ya Israeli; ndipo iye akathe kuwadalitsa iwo kunthawi zosatha, kudzera mu chikhulupiliro pa dzina la Yesu Khristu. Ameni.

Print